Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA

Muzikhala Okonzeka Kuphunzira Zinthu Zatsopano

Muzikhala Okonzeka Kuphunzira Zinthu Zatsopano

Mukamakonzekera kuphunzira mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndikuyembekezera kuphunzirapo chiyani?’ Ngakhale kuti mungadziwiretu zimene muphunzire, muzikumbukira kuti pangakhalenso zinthu zina zatsopano zimene Yehova angakuphunzitseni. Ndiye kodi mungatani kuti muzikhala okonzeka kuphunzira zinthu zatsopano?

Muzipempha nzeru. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa zimene akufuna kuti muphunzire panopa. (Yak. 1:5) Musamangokhutira ndi zimene munadziwa kale.—Miy. 3:​5, 6.

Muzikumbukira kuti Baibulo ndi lamphamvu. “Mawu a Mulungu ndi amoyo.” (Aheb. 4:12) “Mawu” a Mulungu omwe ndi amoyo angatithandize m’njira zosiyanasiyana nthawi iliyonse imene tikuwawerenga. Komatu izi zingatheke ngati tili okonzeka kuphunzira zinthu zatsopano pa zimene tikuwerengazo.

Muziyamikira zilizonse zomwe Yehova amakuphunzitsani. Chakudya chauzimu chili ngati “phwando la zakudya zabwino kwambiri.” (Yes. 25:6) Choncho muzipewa kusala “zakudya” zimene mumaona kuti sizikusangalatsani. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti mukhale munthu wabwino komanso muzisangalala kwambiri mukamaphunzira.