Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 36

NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

“Muzichita Zimene Mawu Amanena”

“Muzichita Zimene Mawu Amanena”

“Muzichita zimene mawu amanena.”YAK. 1:22.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kuti tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso tiziwaganizira ndi kuwagwiritsa ntchito pa moyo wathu.

1-2. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti atumiki a Mulungu azisangalala? (Yakobo 1:​22-25)

 YEHOVA ndi Mwana wake wokondedwa amafuna kuti tizisangalala. Wolemba Salimo 119:2 ananena kuti: “Osangalala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake, amene amamufunafuna ndi mtima wawo wonse.” Yesu ananenanso kuti: “Osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga.”Luka 11:28.

2 N’chifukwa chiyani anthu amene timalambira Mulungu timakhala osangalala? Pali zifukwa zambiri, koma chifukwa chimodzi n’chakuti timawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndipo timayesetsa kutsatira zimene timaphunzira.—Werengani Yakobo 1:​22-25.

3. Kodi kugwiritsa ntchito zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu kumatithandiza bwanji?

3 ‘Kuchita zimene Mawu’ a Mulungu amanena kumatithandiza m’njira zambiri. Choyamba, tikamachita zimene timaphunzira timasangalatsa Yehova. Ndipo tikadziwa kuti tikusangalatsa Yehova timasangalala. (Mlal. 12:13) Tikamagwiritsa ntchito zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu timakhala ndi mabanja abwino komanso timagwirizana ndi Akhristu anzathu. N’kutheka kuti inunso mwaona kale kuti zimenezi ndi zoona. Kuwonjezera pamenepo, timapewa mavuto amene anthu omwe satsatira mfundo za Yehova amakumana nawo. Timagwirizana ndi zimene Mfumu Davide inanena. Atanena za malamulo ndi zigamulo za Yehova, anamaliza nyimbo yake ndi mawu akuti: “Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”—Sal. 19:​7-11.

4. N’chifukwa chiyani kuchita zimene Mawu a Mulungu amanena n’kovuta?

4 Kunena zoona, kuchita zimene Mawu a Mulungu amanena si kophweka. Ngakhale kuti timatanganidwa, tiyenera kuwerenga komanso kuphunzira Baibulo n’cholinga choti tizimvetsa zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Tiyeni tikambirane mfundo zina zimene zingatithandize kuti tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Tionanso zimene tingachite kuti tiziganizira zimene tawerenga komanso mmene tingazigwiritsire ntchito pa moyo wathu.

MUZIPEZA NTHAWI YOWERENGA MAWU A MULUNGU

5. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe timatanganidwa nazo?

5 Anthu a Yehova ambiri amatanganidwa. Nthawi yambiri timakhala tikusamalira maudindo athu mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena. Mwachitsanzo, ambiri amagwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wawo ndi wa banja lawo. (1 Tim. 5:8) Akhristu ambiri amasamalira achibale awo okalamba kapena amene akudwala. Komanso tonsefe timafunika nthawi yambiri yosamalira thanzi lathu. Kuwonjezera pa zonsezi, timapatsidwa zochita kumpingo. Ndipo ntchito ina yofunika kwambiri yomwe timafunika kugwira nawo ndi yolalikira. Ndiye ngakhale kuti timatanganidwa chonchi, kodi tingatani kuti tizipeza nthawi yowerenga Baibulo, kuganizira zimene tawerenga komanso kumazigwiritsa ntchito?

6. Kodi mungatani kuti muziona kuti kuwerenga Baibulo n’kofunika kwambiri? (Onaninso chithunzi.)

6 Kuwerenga Baibulo ndi chimodzi mwa ‘zinthu zofunika kwambiri’ kwa Akhristufe choncho tiyenera kuyesetsa kuti tiziliwerenga. (Afil. 1:10) Ponena za munthu wosangalala, salimo loyamba limanena kuti: “Amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama chilamulocho masana ndi usiku.” (Sal. 1:​1, 2) Izi zikutanthauza kuti tiyenera kumapeza nthawi yowerenga Baibulo. Koma kodi nthawi yabwino yoliwerenga ndi iti? Aliyense angasankhe nthawi yomwe ili yabwino kwa iyeyo. Mwachidule, tingati ndi nthawi imene mukhoza kukwanitsa kumawerenga nthawi zonse. M’bale wina dzina lake Victor ananena kuti: “Ine ndimakonda kuwerenga Baibulo m’mamawa. Ngakhale kuti sindikonda kudzuka m’mawa kwambiri, ndimaona kuti pa nthawiyi zosokoneza zimakhala zochepa. Ndimakhala tcheru ndipo ndimatha kuika maganizo pa zimene ndikuwerenga.” Kodi ndi mmene inunso mumaonera? Mungadzifunse kuti, ‘Kodi nthawi yabwino kwa ineyo yoti ndiziwerenga Baibulo ndi iti?’

Kodi ndi nthawi iti yomwe ingakhale yabwino kuwerenga Baibulo, nanga ndi nthawi iti yomwe mungakwanitse kumawerenga nthawi zonse? (Onani ndime 6)


MUZIGANIZIRA ZIMENE MWAWERENGA

7-8. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kupindula ndi zimene tawerenga? Perekani chitsanzo.

7 Kunena zoona, tikhoza kumawerenga zinthu zambiri koma osazimvetsa bwinobwino. Kodi munawerengapo nkhani inayake koma pasanapite nthawi yaitali n’kuiwala zimene mwawerenga? Tonsefe zimenezi zinatichitikirapo. N’zomvetsa chisoni kuti zimenezi zikhoza kuchitikanso powerenga Baibulo. Mwina munasankha kuti muziwerenga machaputala angapo pa tsiku. Ngati ndi choncho munachita bwino. Tiyenera kukhala ndi zolinga n’kumayesetsa kuzikwaniritsa. (1 Akor. 9:26) Koma kungowerenga Baibulo ndi chiyambi chabe, ndipo n’chiyambi chabwino. Pamafunika zambiri kuti tizipindula tikamawerenga Mawu a Mulungu.

8 Taganizirani chitsanzo ichi: Zomera zambiri zimafuna mvula. Koma ngati mvula yambiri itagwa pa nthawi yochepa, nthaka ingadzadze madzi. Zikatero mvula yambiri imakhala yosathandiza. Pamafunika nthawi kuti madzi alowe munthaka n’kusungika kuti zomera zigwiritse ntchito. Ifenso tiyenera kupewa kuwerenga Baibulo mofulumira kwambiri mpaka kufika polephera kuganizira zomwe tikuwerengazo, kuzikumbukira komanso kuzigwiritsa ntchito.—Yak. 1:24.

Mofanana ndi nthaka yomwe imafunika nthawi yokwanira kuti isunge madzi a mvula komanso kuwagwiritsa ntchito, ifenso timafunika nthawi yokwanira kuti tiganizire komanso kugwiritsa ntchito zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu (Onani ndime 8)


9. Kodi tingatani ngati tayamba chizolowezi chowerenga Baibulo mofulumira kwambiri?

9 Kodi nthawi zina mumaona kuti mumawerenga Baibulo mofulumira kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi muyenera kuchita chiyani? Muyenera kuchepetsa liwiro. Muziyesetsa kuganizira zimene mukuwerenga kapena zimene mwawerenga. Kuchita zimenezi si kovuta. Mukhoza kuwonjezera nthawi imene mumaphunzira kuti muzipeza nthawi yoganizira zimene mwawerenga. Mungathenso kusankha kuti muziwerenga mavesi ochepa n’kugwiritsa ntchito nthawi yotsalayo kuti muganizire zimene mwawerenga. Victor amene tamutchula kumayambiriro uja ananena kuti: “Ndimangowerenga kwa nthawi yochepa, mwina chaputala chimodzi. Popeza ndimawerenga m’mawa kwambiri, tsiku lonse ndimaganizira zimene ndawerengazo.” Kaya mutsatira njira yotani, chofunika kwambiri ndi chakuti muziwerenga pa liwiro limene lingakuthandizeni kupindula ndi zimene mukuwerenga.—Sal. 119:97; Onani bokosi lakuti “ Mafunso Ofunika Kuwaganizira.”

10. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwaphunzira. (1 Atesalonika 5:​17, 18)

10 Kaya mumawerenga Baibulo nthawi yanji kapena kwa nthawi yaitali bwanji, muzionetsetsa kuti mukupeza njira yogwiritsa ntchito zomwe mwawerenga. Mukawerenga kachigawo kenakake ka Mawu a Mulungu, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji zimenezi panopa kapena m’tsogolo?’ Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuwerenga Baibulo pa 1 Atesalonika 5:​17, 18. (Werengani.) Pambuyo powerenga mavesi awiriwa, mukhoza kuima n’kuganizira ngati mumapemphera pafupipafupi komanso kuchokera pansi pa mtima. Mukhoza kuganiziranso zinthu zimene inuyo mumayamikira. Mwina mukuganizira zinthu zitatu zimene Yehova wakuchitirani ndipo mukufuna mumuthokoze. Ngati mutamachita zimenezi ngakhale kwa nthawi yochepa, mukhoza kukhala munthu amene amamva Mawu a Mulungu n’kumawachita. Mukhoza kupindula kwambiri mukamachita zimenezi tsiku lililonse pa mavesi a m’Baibulo amene mumawerenga. Mukatero mudzakhala munthu amene amachita zimene Mawu a Mulungu amanena. Koma kodi mungatani ngati pali zinthu zambiri zomwe mukuyenera kusintha?

MUZIKHALA NDI ZOLINGA ZOMWE MUNGAZIKWANIRITSE

11. N’chiyani chomwe chingachititse kuti nthawi zina tizikhumudwa? Perekani chitsanzo.

11 Nthawi zina mukamawerenga Baibulo mukhoza kukhumudwa chifukwa choona kuti pali zinthu zambiri zimene mukufunika kusintha. Tiyerekeze kuti lero mwawerenga Baibulo ndipo mwapeza malangizo okhudza kupewa tsankho. (Yak. 2:​1-8) Ndiyeno mukuganizira mmene mumachitira zinthu ndi anthu ena ndipo mukuona kuti mufunika kusintha. Apo ndiye kuti mwachita bwino. Kenako mawa lake mukuwerenga nkhani yosonyeza kufunika kodziletsa polankhula. Mukuzindikira kuti nthawi zina simulankhula bwino. (Yak. 3:​1-12) Ndiye mukuganiza kuti muzilankhula molimbikitsa nthawi zonse. Tsiku lotsatira mukuwerenga m’Baibulo malangizo oti tizipewa kukhala pa ubwenzi ndi dziko. (Yak. 4:​4-12) Mukuzindikira kuti muyenera kusankha bwino zosangalatsa. Pofika tsiku la 4, mukhoza kukhumudwa mukaganizira kuchuluka kwa zinthu zimene mukufunika kusintha.

12. N’chifukwa chiyani simuyenera kukhumudwa ngati powerenga Baibulo mwaona kuti muyenera kusintha zinthu zina? (Onaninso mawu a m’munsi.)

12 Ngati mwapeza kuti pali zinthu zambiri zimene muyenera kusintha, musamakhumudwe. Umenewo ndi umboni wakuti muli ndi mtima wabwino. Munthu amene ndi wodzichepetsa komanso woona mtima, amawerenga Malemba n’cholinga choti aone zinthu zimene ayenera kusintha. a Kumbukiraninso kuti kuvala “umunthu watsopano” sikutha. (Akol. 3:10) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kuchita zimene Mawu a Mulungu amanena?

13. Kodi mungatani kuti mudziikire zolinga zimene mungazikwaniritse? (Onaninso chithunzi.)

13 M’malo moyesa kusintha zinthu zonse nthawi imodzi, muzisankha zolinga zingapo zimene mungazikwaniritse. (Miy. 11:2) Mungayese kuchita izi: Muzilemba zimene mukufuna kusintha ndipo kenako muzisankha chimodzi kapena ziwiri zimene mungayambirire, n’kusiya zinazo kuti mudzazichite pa nthawi ina. Ndiye kodi mungayambe ndi zolinga ziti?

Mogwirizana ndi zimene mwawerenga m’Baibulo, m’malo moyesa kusintha zonse nthawi imodzi, muziyesa kusankha zolinga zimene mungazikwaniritse. Mungasankhe cholinga chimodzi kapena ziwiri (Onani ndime 13-14)


14. Kodi mungayambe ndi zolinga ziti?

14 Mungayambe ndi cholinga chimene mukuona kuti ndi chosavuta kuchikwaniritsa. Kapena mungayambe ndi zinthu zimene mukuona kuti mukufunika kusintha kwambiri. Mukapeza cholinga chimene mukufuna kuchikwaniritsa muzifufuza m’mabuku athu, mwina pogwiritsa ntchito Watch Tower Publications Index kapena Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Muzipempherera cholinga chanucho ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.” (Afil. 2:13) Kenako muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo. Mukayesetsa kukwaniritsa cholinga chanu choyamba zidzakulimbikitsani kuti muyambenso kusintha zinthu zina. Ndipotu mukakwanitsa kusintha khalidwe linalake, zidzakhalanso zosavuta kuti musinthe zinthu zina.

MUZILOLA KUTI MAWU A MULUNGU ‘AZIGWIRA NTCHITO MWA INU’

15. Kodi anthu a Yehova amasiyana bwanji ndi anthu ena amene amawerenganso Baibulo? (1 Atesalonika 2:13)

15 Anthu ena amanena kuti awerengapo Baibulo maulendo ambirimbiri. Koma kodi amakhulupirira zimene limanena? Kodi amagwiritsa ntchito zimene awerenga komanso kulola kuti zisinthe moyo wawo? N’zomvetsa chisoni kuti satero. Izitu ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu a Yehova amachita. Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, timaona Baibulo ‘mmene lililidi, monga mawu a Mulungu.’ Komanso timayesetsa kutsatira malangizo ake pa moyo wathu.—Werengani 1 Atesalonika 2:13.

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichita zimene Mawu a Mulungu amanena?

16 Si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuwerenga komanso kugwiritsa ntchito zimene tawerenga m’Mawu a Mulungu. Nthawi zina zingamativute kuti tipeze nthawi yoti tiwerenge. Apo ayi tikhoza kumawerenga mofulumira kwambiri n’kulephera kupeza nthawi yoganizira zimene tawerenga. Mwinanso tikhoza kukhumudwa tikaganizira kuchuluka kwa zinthu zimene tikufunika kusintha. Choncho kaya inu mukulimbana ndi vuto lotani, dziwani kuti mungathe kuligonjetsa. Yehova angakuthandizeni. Choncho tiyeni tizilola kuti atithandize kuti tisakhale anthu ongomva n’kuiwala koma amene amachita zimene Mawu a Mulungu amanena. N’zosachita kufunsa kuti tikamawerenga kwambiri komanso kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pa moyo wathu, m’pamenenso timakhala osangalala kwambiri.—Yak. 1:25.

NYIMBO NA. 94 Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake