Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akanatha Kusangalatsa Mulungu

Akanatha Kusangalatsa Mulungu

TONSEFE timatumikira Yehova ndipo timafunitsitsa kuti tizimusangalatsa. Koma kodi Mulungu amadalitsa ndiponso kusangalala ndi anthu otani? Yehova anasangalala ndi anthu ena a m’Baibulo ngakhale kuti anthuwo anali atachitapo machimo aakulu. Panalinso anthu ena amene poyamba Mulungu ankasangalala nawo koma kenako anachita zinthu zimene zinamukhumudwitsa. Choncho tingadzifunse kuti, “Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala anthu otani?” Chitsanzo cha Rehobowamu, yemwe anali mfumu ya Yuda, chingatithandize kuyankha funsoli.

SANAYAMBE BWINO

Bambo ake a Rehobowamu anali Solomo, ndipo analamulira Aisiraeli kwa zaka 40. (1 Maf. 11:42) Solomo anamwalira m’chaka cha 997 B.C.E. Kenako Rehobowamu anapita kumpoto kwa Yerusalemu ku Sekemu kuti akadzozedwe kukhala mfumu. (2 Mbiri 10:1) Kodi mukuganiza kuti mwina ankaopa kukhala mfumu pambuyo pa Solomo yemwe anali wanzeru kwambiri? Atangokhala mfumu, Rehobowamu anakumana ndi vuto lalikulu ndipo anayenera kusonyeza ngati anali wanzeru kapena ayi.

Aisiraeli ankaponderezedwa ndipo anatumiza anthu kuti akalankhule ndi Rehobowamu. Iwo anamuuza kuti: “Bambo anu anaumitsa goli lathu. Tsopano inuyo mufewetse ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”​—2 Mbiri 10:3, 4.

Rehobowamu ayenera kuti anavutika kusankha zochita pa nkhaniyi. Zinali choncho chifukwa chakuti ngati akanachita zimene anthuwo anapempha, iye, banja lake ndiponso anthu ena okhala m’nyumba ya mfumu sakanatha kupeza zinthu zapamwamba zimene anazolowera. Koma ngati akanakana kuchita zimene anthuwo ankafuna, mwina iwo akanamuukira. Kodi Rehobowamu anasankha kuchita chiyani? Poyamba anafunsira malangizo kwa amuna achikulire omwe anali alangizi a Solomo. Koma kenako anapemphanso malangizo kwa achinyamata anzake. Iye anasankha kutsatira malangizo a achinyamatawo ndipo anasankha kuchitira nkhanza anthuwo. Iye anayankha kuti: “Ine ndidzakusenzetsani goli lolemera kwambiri, ndipo ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”​—2 Mbiri 10:6-14.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Nthawi zambiri ndi bwino kumvera malangizo a anthu achikulire omwe ndi olimba mwauzimu. Popeza iwo akumana ndi zambiri pa moyo wawo, akhoza kudziwa zimene tingakumane nazo tikasankha zinazake ndipo angatipatse malangizo abwino.​—Yobu 12:12.

“ANAMVERA MAWU A YEHOVA”

Anthu atachoka mu ufumu wake, Rehobowamu anasonkhanitsa asilikali ake. Koma Yehova anatumiza mneneri Semaya kuti akamuuze kuti: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli. Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”​—1 Maf. 12:21-24. *

Rehobowamu ayenera kuti anavutika kwambiri kutsatira zimene Mulungu ananenazi chifukwa chodera nkhawa zimene Aisiraeliwo angaganize. Iye anali atanena kuti awalanga ndi “zikoti zaminga.” Ndiye kodi Aisiraeliwo akanaganiza bwanji ataona kuti sakuchita chilichonse pamene iwo ankachoka mu Ufumu wake? (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 13:7.) Ngakhale zinali choncho, mfumuyo ndiponso asilikali ake “anamvera mawu a Yehova n’kubwerera kwawo.”

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kumvera Mulungu ngakhale pamene tikuona kuti anthu atinyoza chifukwa chochita zimenezi. Tikamamvera Mulungu, iye adzasangalala nafe komanso kutidalitsa.​—Deut. 28:2.

Rehobowamu anamveradi Mulungu ndipo anasiya mapulani ake okamenyana ndi ufumu watsopanowo. Kenako anayamba kumanga mizinda m’mafuko a Yuda ndi Benjamini omwe ankawalamulirabe. Iye ‘analimbitsanso kwambiri’ mizinda yochuluka. (2 Mbiri 11:5-12) Koma chofunika kwambiri n’chakuti kwa nthawi ndithu anamvera malamulo a Yehova. Anthu a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 umene unkalamuliridwa ndi Yerobowamu anayamba kulambira mafano. Choncho ambiri anapita ku Yerusalemu ‘kukalimbikitsa Rehobowamu’ komanso kukasonyeza kuti anali kumbali ya kulambira koona. (2 Mbiri 11:16, 17) Apatu Rehobowamu analimbitsa ufumu wake chifukwa chomvera Yehova.

ANACHIMWA KOMA ANALAPA

Ufumu wake utalimba, Rehobowamu anachita zinthu zosayembekezereka. Iye anasiya kumvera malamulo a Yehova ndipo anayamba kulambira milungu yonyenga. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mwina anatsatira mayi ake, omwe anali Muamoni. (1 Maf. 14:21) Koma kaya anayamba kulambira milunguyo pa chifukwa chotani, Aisiraeli ambiri anamutsatira. Choncho Yehova analola kuti Mfumu Sisaki ya Iguputo ilande mizinda yambiri ya ku Yuda ngakhale kuti Rehobowamu anali atailimbitsa.​—1 Maf. 14:22-24; 2 Mbiri 12:1-4.

Zinthu zinafika poipa kwambiri pamene Sisaki anabwera ku Yerusalemu kumene Rehobowamu ankalamulira. Pa nthawiyi, mneneri Semaya anauza Rehobowamu ndi akalonga ake uthenga wochokera kwa Mulungu wakuti: “Inuyo mwandisiya, choncho inenso ndakusiyani ndipo ndakuperekani m’manja mwa Sisaki.” Kodi Rehobowamu anachita chiyani atamva uthengawu? Iye anachita zinthu mwanzeru. Baibulo limanena kuti: “Akalonga a Isiraeliwo ndi mfumuyo atamva zimenezi, anadzichepetsa n’kunena kuti: ‘Yehova ndi wolungama.’” Choncho Yehova anapulumutsa Rehobowamu komanso Yerusalemu moti sanawonongedwe.​—2 Mbiri 12:5-7, 12.

Kenako Rehobowamu anapitiriza kulamulira ufumu wakum’mwera. Ndiyeno asanamwalire, anapereka mphatso zambiri kwa ana ake aamuna. N’kutheka kuti anachita zimenezi pofuna kuti anawo asaukire mchimwene wawo Abiya, yemwe anadzalowa ufumu. (2 Mbiri 11:21-23) Apa Rehobowamu anasonyeza nzeru zimene analephera kusonyeza poyamba.

KODI ANALI WABWINO KAPENA WOIPA?

Ngakhale kuti anachita zinthu zina zabwino, Rehobowamu analephera kusangalatsa Mulungu. Paja Baibulo limanena za ulamuliro wake kuti: “Iye anachita zoipa chifukwa sanatsimikize kufunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.”​—2 Mbiri 12:14.

Mayi a Mfumu Rehobowamu komanso alangizi ake anachititsa kuti ayambe kulambira mafano

Tangoganizirani zimene zinachitika. Rehobowamu ankamvera Mulungu nthawi zina ndipo ankachita zinthu zina zothandiza anthu a Yehova. Koma analephera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumusangalatsa. Choncho anayamba kuchita zinthu zolakwika komanso kulambira milungu yonyenga. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Pamene Rehobowamu ankamvera malangizo a Yehova, kodi ankalapadi kuchokera pansi pa mtima komanso kufunitsitsa kuti asangalatse Mulungu? Kapena kodi ankangotsatira zimene anthu ena ankamuuza?’ (2 Mbiri 11:3, 4; 12:6) Mulimonse mmene zinalili, atakula anayambanso kuchita zinthu zoipa. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene Mfumu Davide, yemwe anali agogo ake, anachita. N’zoona kuti Davide analakwitsa zinthu zina, koma pa moyo wake anasonyeza kuti ankakonda Yehova, ankafunitsitsa kumulambira moyenera komanso ankalapa machimo ake mochokera pansi pa mtima.​—1 Maf. 14:8; Sal. 51:1, 17; 63:1.

Tikhoza kuphunzira zambiri pa nkhani ya Rehobowamu. Anthu amachita bwino akamasamalira mabanja awo komanso akamayesetsa kuchita zinthu zabwino. Koma kuti tisangalatse Mulungu, nthawi zonse tiyenera kuika kulambira Yehova pamalo oyamba.

Tikhoza kuchita zimenezi ngati tingapitirize kukonda Yehova ndi mtima wonse. Kuti moto usazime, munthu ayenera kupitiriza kuusonkhezera. Chimodzimodzinso ndi kukonda Yehova. Kuti tipitirize kukonda Yehova ndi mtima wonse, tiyenera kumaphunzira Mawu ake nthawi zonse, kuganizira mozama zimene taphunzira komanso kulimbikira kupemphera. (Sal. 1:2; Aroma 12:12) Tikamakonda Yehova tidzakhala ndi mtima wofuna kumusangalatsa nthawi zonse. Komanso ngati tachimwa tidzalapa kuchokera pansi pa mtima. Mosiyana ndi Rehobowamu, tikamachita zimenezi tidzapitiriza kulambira Yehova mokhulupirika.​—Yuda 20, 21.

^ ndime 9 Mulungu anali ataneneratu kuti ufumuwo udzagawanika chifukwa Solomo anachita zinthu mosakhulupirika.​—1 Maf. 11:31.