Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi pali zinthu 4 ziti zimene zingatithandize kuti tiziimba bwino?

Tiziima bwino n’kukweza buku la nyimbo. Tizikoka mpweya wokwanira komanso kutsegula kwambiri pakamwa kuti tizitha kuimba mokweza. Kenako tiziimba mokweza kwambiri.​—w17.11, tsa. 5.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti malo amene kunali mizinda yothawirako komanso misewu yopitako zinali zochititsa chidwi?

Mizinda 6 yothawirako inali m’malo osiyanasiyana ku Isiraeli ndipo misewu yopita kumizindayi inali yokonzedwa bwino. Izi zinathandiza kuti munthu azithawirako mwamsanga komanso mosavuta.​—w17.11, tsa. 14.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti mphatso ya Mulungu ya nsembe ya Yesu ndi yabwino kwambiri?

Imatithandiza kukhalabe ndi moyo ndiponso kumasuka ku uchimo ndi imfa. Ngakhale kuti ndife ochimwa, Yehova amatikonda ndipo anapereka Yesu kuti atiwombole.​—wp17.6, tsa. 6-7.

Kodi lemba la Salimo 118:22 linalosera bwanji za kuukitsidwa kwa Yesu?

Anthu anakana kuti Yesu ndi Mesiya ndipo anamupha. Choncho kuti akhale “mwala wofunika kwambiri wapakona” anafunika kuukitsidwa.​—w17.12, tsa. 9-10.

Kodi nthawi zonse mwana woyamba kubadwa ndi amene ankakhala mumzere wa makolo a Mesiya?

Anthu ena amene anali mumzere wa makolo a Mesiya anali oyamba kubadwa koma osati onse. Davide sanali mwana woyamba wa Jese koma anali mumzerewu.​—w17.12, tsa. 14-15.

Kodi m’Baibulo muli mfundo zina ziti zokhudza zaumoyo?

Chilamulo cha Mose chinkati anthu odwala matenda ena ankayenera kukhala kwaokha. Anthu akagwira thupi la munthu wakufa ankayenera kusamba komanso kuchapa zovala. Chilamulocho chinkati chimbudzi cha munthu chiyenera kukwiriridwa pansi kutali ndi anthu. Mwana wamwamuna ankayenera kudulidwa akakwanitsa masiku 8 chifuwa pa nthawiyi magazi ake sankachedwa kuundana.​—wp18.1, tsa. 7.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti si kulakwa kuti Mkhristu azidzikonda moyenerera?

Tiyenera kukonda mnzathu mmene timadzikondera tokha. (Maliko 12:31) Amuna ayeneranso ‘kukonda akazi awo monga matupi awo.’ (Aef. 5:28) Koma n’zoona kuti munthu angayambe kudzikonda mopitirira malire.​—w18.01, tsa. 23.

Kodi tingatani kuti tikule mwauzimu?

Tiziphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kuganizira kwambiri zimene taphunzira. Tizitsatiranso zimene taphunzirazo. Tizilola kuti mzimu woyera uzititsogolera komanso tizitsatira malangizo a anthu ena.​—w18.02, tsa. 26.

N’chifukwa chiyani okhulupirira nyenyezi komanso olosera sangathandize kuti mudziwe zam’tsogolo?

Pali zifukwa zingapo koma chifukwa chachikulu n’chakuti Baibulo limaletsa kuchita zimenezi.​—wp18.2, tsa. 4-5.

Tikaitanidwa kukadya kwa anthu ena n’kuvomera, kodi tiyenera kuchita chiyani?

Ngati tavomera kupita kwa munthu winawake, tiyenera kuyesetsa kuti tisasinthe. (Sal. 15:4) Si bwino kungosintha mwachisawawa. Anthu amene atiitanawo ayenera kuti agwira ntchito mwakhama kuti akonze chakudya.​—w18.03, tsa. 18.

Kodi akulu ndi atumiki othandiza angaphunzire chiyani kwa Timoteyo?

Timoteyo ankakonda anthu komanso kuwaganizira. Ankaikanso zinthu zauzimu pamalo oyamba. Iye ankatumikira mwakhama ndipo ankatsatira zimene waphunzira. Ankapitirizanso kudziphunzitsa komanso ankadalira mzimu wa Yehova. Akulu komanso abale ena angachite bwino kutsatira chitsanzo chake.​—w18.04, tsa. 13-14.