Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupatsana Moni N’kothandiza Kwambiri

Kupatsana Moni N’kothandiza Kwambiri

“MULI bwanji?”

N’zosachita kufunsa kuti nthawi zambiri mumanena mawu amenewa popereka moni. Mwinanso mumanena mawuwa mutagwirana dzanja ndi munthuyo. Anthu amapatsana moni m’njira zosiyanasiyana malinga ndi chikhalidwe chawo. Ndipo munthu akapanda kupereka kapena kuyankha moni, anthu ena angamuone kuti alibe chikondi komanso ulemu.

Koma si onse amene amakonda kupereka moni. Ena amalephera kuchita zimenezi chifukwa cha manyazi kapena kudzikayikira. Pomwe ena amavutika kupatsa moni anthu amene amasiyana nawo mtundu, chikhalidwe kapena zinthu zina. Koma ngakhale kungonena mawu ochepa popereka moni kwa munthu, kungakhale kothandiza kwambiri.

Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi kupereka moni n’kothandiza bwanji? Nanga Mawu a Mulungu amanena zotani pa nkhaniyi?’

TIZIPEREKA MONI KWA ANTHU “KAYA AKHALE AMTUNDU WOTANI”

Munthu woyamba yemwe sanali Myuda ndipo anali wosadulidwa, dzina lake Koneliyo, atalowa mumpingo wachikhristu, mtumwi Petulo anamulandira. Kenako Petulo anati: “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Nthawi ina Petulo analembanso kuti Mulungu “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Poyamba mwina tingaone kuti malemba amenewa ndi othandiza anthu amene akuphunzira Baibulo. Koma Petulo anauzanso Akhristu kuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale.” (1 Pet. 2:17) Choncho tingachite bwino kumapereka moni kwa anthu onse mosaganizira mtundu wawo, chikhalidwe chawo kapena kumene amachokera. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timawalemekeza komanso kuwakonda.

Mtumwi Paulo anauza anthu amumpingo wa ku Roma kuti: “Landiranani, monga mmene Khristu anatilandirira.” (Aroma 15:7) Paulo anayamikira kwambiri abale amene ‘anamuthandiza ndiponso kumulimbikitsa.’ Masiku ano abale ndi alongo amafunika kulimbikitsidwa kuposa kale chifukwa Satana akulimbana kwambiri ndi anthu a Mulungu.​—Akol. 4:11; Chiv. 12:12, 17.

Zitsanzo za m’Malemba zimasonyeza kuti kupatsana moni kumathandiza m’njira zosiyanasiyana.

TIKAMAPEREKA MONI TIMALIMBIKITSA ANTHU KOMANSO KUSONYEZA CHIKONDI

Pamene nthawi inakwana kuti Mulungu asamutse moyo wa Mwana wake n’kuuika m’mimba mwa Mariya, anatumiza mngelo kuti akalankhule ndi Mariyayo. Mngeloyo anayamba ndi kupereka moni ponena kuti: “Mtendere ukhale nawe, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.” Mariya sankadziwa chifukwa chake mngeloyo ankamulankhula ndipo ‘anadabwa kwambiri.’ Poona zimenezi, mngeloyo anati: “Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomera mtima.” Iye anamufotokozera kuti Mulungu anali ndi cholinga choti Mariyayo abereke Mesiya. Atanena zimenezi, Mariya anasiya kuda nkhawa ndipo anati: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.”​—Luka 1:26-38.

Unali mwayi waukulu kuti mngeloyo akapereke uthenga wa Yehova. Koma sanadzione kuti anali wapamwamba moti n’kulephera kulankhula ndi munthu amene si wangwiro. Monga taonera, mngeloyo anayamba ndi kupereka moni. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kukhala ofunitsitsa kupereka moni kwa anthu komanso kuwalimbikitsa. Mawu ochepa okha angathandize munthu kuona kuti ndi wofunika m’gulu la Yehova.

Paulo ankadziwa anthu ambiri m’mipingo ya ku Asia Minor ndi ku Europe. Ndipo m’makalata ake, anapereka moni kwa anthu osiyanasiyana. Mwachitsanzo, pa Aroma 16, Paulo anapereka moni kwa Akhristu ambiri. Iye anatchula “mlongo wathu Febe” ndipo analimbikitsa abale kuti ‘amulandire mwa Ambuye mmene ankalandirira oyerawo, ndi kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo lawo.’ Paulo anaperekanso moni kwa Purisika ndi Akula ndipo analemba kuti: ‘Si ine ndekha amene ndikuwayamikira, komanso mipingo yonse ya anthu a mitundu ina.’ Iye anaperekanso moni kwa anthu ena amene masiku ano sadziwika bwinobwino. Mwachitsanzo, anapereka moni kwa ‘wokondedwa wake Epeneto’ ndiponso “Turufena ndi Turufosa, akazi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye.” Apa zikuonekeratu kuti Paulo ankakonda kupereka moni kwa abale ndi alongo ake.​—Aroma 16:1-16.

Tangoganizirani mmene anthuwo ankamvera podziwa kuti Paulo ankawakumbukira ndiponso kuwakonda. Ayenera kuti nawonso anayamba kukonda kwambiri Paulo komanso Akhristu anzawo. Akhristu enanso ataona kuti Paulo anapereka moni kwa anthu onsewo ayenera kuti analimbikitsidwa komanso chikhulupiriro chawo chinalimba. Tikamapatsana moni kuchokera pansi pa mtima ndiponso kusonyeza kuti timayamikira abale ndi alongo athu, timayamba kugwirizana nawo kwambiri.

Paulo atafika ku Potiyolo n’kuyamba ulendo wopita ku Roma, Akhristu ena anabwera kudzamuchingamira. Paulo ataona abalewo akubwera, “anayamika Mulungu, ndipo analimba mtima.” (Mac. 28:13-15) Nthawi zina timatha kungopereka moni pomwetulira kapena kubayibitsa munthu. Koma ngakhale zimenezi zikhoza kulimbikitsa munthu amene ali ndi nkhawa kapena chisoni.

MONI AMATHANDIZA KUTI TIYAMBE KUKAMBIRANA BWINO

Pa nthawi ina, Yakobo anafunika kupereka malangizo amphamvu. Akhristu ena anali achigololo mwauzimu chifukwa chakuti ankachita zinthu mogwirizana ndi dzikoli. (Yak. 4:4) Koma taonani mmene Yakobo anayambira kalata yake.

Iye anati: “Ine Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikupereka moni kwa mafuko 12 amene ali obalalika.” (Yak. 1:1) Anthu amene anawerenga kalatayi ayenera kuti analandira bwino malangizo a Yakobo ataona moni wake. Tikutero chifukwa chakuti moni wakeyo anasonyeza kuti iye ankaona kuti iyeyo ndi Akhristuwo anali ofanana pamaso pa Mulungu. Izi zikusonyeza kuti kupereka moni modzichepetsa kungathandize kuti muyambe kukambirana ndi anthu ngakhale nkhani zovuta.

Koma moni wathu angathandize anthu pokhapokha ngati tapereka mwachikondi komanso kuchokera pansi pa mtima. Kupereka moni chonchi kungathandize ngakhale anthu amene akuoneka ngati sanamve moni wathuwo. (Mat. 22:39) Mwachitsanzo, tsiku lina mlongo wina wa ku Ireland anafika mochedwa ku Nyumba ya Ufumu ndipo anapeza misonkhano itayamba. Polowa muholo m’bale wina anamwetulira n’kunena kuti: “Takulandirani. Ndasangalala kukuonani.” Mlongoyo sanayankhe ndipo anangokakhala.

Patapita milungu ingapo. Mlongoyo anauza m’bale amene anamupatsa moniyo kuti iye wakhala akuvutika ndi mavuto enaake kunyumba. Kenako anamuuza kuti: “Tsiku lija ndinakhumudwa kwambiri moti ndinatsala pang’ono kuti ndisapite ku Nyumba ya Ufumu. Sindikukumbukira zambiri zimene zinanenedwa pamisonkhanoyo koma ndikukumbukira kuti munandipatsa moni. Zinandithandiza kumva kuti ndalandiridwadi. Zikomo kwambiri.”

M’baleyo sanadziwe kuti moni wake analimbikitsa kwambiri mlongoyo. Iye anati: “Atandiuza kuti anamva bwino nditamupatsa moni, ndinasangalala ndipo ndinalimbikitsidwanso.”

Solomo analemba kuti: “Tumiza mkate wako pamadzi, chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.” (Mlal. 11:1) Tikamakonda kupereka moni kwa anthu, makamaka Akhristu anzathu, timalimbikitsa anthu ena ndipo nafenso timalimbikitsidwa. Choncho tizikumbukira nthawi zonse kuti kupatsana moni n’kothandiza kwambiri.