Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu

Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu

“Ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.”​—SAL. 119:99.

NYIMBO: 127, 88

1. Kodi chinthu chimodzi chimene chimasiyanitsa anthu ndi nyama n’chiyani?

CHINTHU chimodzi chimene chimasiyanitsa anthu ndi nyama n’chakuti anthu ali ndi chikumbumtima. Anthu akhala ali ndi chikumbumtima kungoyambira pamene analengedwa. Mwachitsanzo, Adamu ndi Hava ataphwanya lamulo la Yehova anabisala. Zimenezi zikusonyeza kuti chikumbumtima chawo chinkawavutitsa.

2. Kodi chikumbumtima chimafanana bwanji ndi kampasi? (Onani chithunzi choyambirira.)

2 Anthu amene chikumbumtima chawo sichinaphunzitsidwe bwino amakhala ngati munthu woyendetsa sitima yapamadzi amene kampasi yake sikugwira bwino ntchito. * Ndipo munthu akhoza kusochera ngati akuyenda panyanja opanda kampasi yolondola. Mphepo komanso mafunde zingachititse kuti sitimayo iyambe kulowera kolakwika. Koma kampasi yomwe ikugwira bwino ntchito ingathandize woyendetsa sitima kuti asasochere. Chikumbumtima chathu chilinso ngati kampasi yothandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Chimakhala ngati munthu wathu wamkati amene amatiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika ndipo chingatithandize kuti tizichita zinthu zoyenera. Koma kuti chikumbumtimacho chizitithandiza, tiyenera kuchiphunzitsa bwino.

3. Kodi chimachitika n’chiyani ngati munthu sanaphunzitse bwino chikumbumtima chake?

3 Ngati munthu sanaphunzitse bwino chikumbumtima chake, sichingamuletse kuchita zoipa. (1 Tim. 4:1, 2) Zikatero, munthuyo akhoza kuyamba kuona kuti ‘zoipa ndi zabwino.’ (Yes. 5:20) Yesu anauza otsatira ake kuti: “Nthawi ikubwera pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu.” (Yoh. 16:2) Izi n’zimene zinachitika pa nthawi imene anthu anapha Sitefano komanso atumiki ena a Mulungu. (Mac. 6:8, 12; 7:54-60) N’zodabwitsa kuti anthu amene amati ndi opembedza amachita zoipa ngati zimenezi n’kumaphwanya malamulo a Mulungu amene amanena kuti amamupembedzayo. (Eks. 20:13) Apa zikuonekeratu kuti chikumbumtima chingathe kusocheretsa munthu.

4. Kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chisamatisocheretse?

4 Kodi tingatani kuti chikumbumtima chathu chisamatisocheretse? Malamulo komanso mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu n’zothandiza “pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.” (2 Tim. 3:16) Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo mwakhama, kuganizira mozama zimene taphunzira komanso kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu. Tikatero chikumbumtima chathu chimayendera maganizo a Mulungu ndipo chimatithandiza kuchita zinthu zabwino. Tsopano tiyeni tikambirane mmene malamulo komanso mfundo za Yehova zingatithandizire kuti tiziphunzitsa chikumbumtima chathu.

ZIMENE TINGACHITE KUTI MALAMULO A MULUNGU AZITITHANDIZA

5, 6. Kodi timapindula bwanji tikamatsatira malamulo a Mulungu?

5 Kuti malamulo a Mulungu azitithandiza, tiyenera kuchita zambiri osati kungowawerenga n’kuwadziwa. Tiziwakonda kwambiri komanso kuwalemekeza. Paja Mawu a Mulungu amati: “Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Chofunika ndi kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Tiyerekeze kuti muli ndi vuto losowa tulo. Kenako dokotala akukuuzani kuti muzichita masewera olimbitsa thupi, muzidya zakudya zabwino komanso musinthe zinthu zina pa moyo wanu. Ndiyeno mutatsatira malangizowo mukuona kuti mwayamba kupeza tulo bwinobwino. Mukhoza kuthokoza kwambiri dokotalayo chifukwa chokuthandizani.

6 Nayenso Mlengi wathu watipatsa malamulo otithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso tisamakumane ndi mavuto chifukwa cha uchimo. Tangoganizirani mmene timapindulira tikamatsatira malamulo a m’Baibulo pa nkhani ya kunama, chiwembu, kuba, chiwerewere, chiwawa ndiponso kuchita zamizimu. (Werengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikazindikira ubwino woyenda m’njira za Yehova, timayamba kumukonda kwambiri komanso kukonda malamulo ake.

7. Kodi kuwerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo kungatithandize bwanji?

7 Sikuti tiyenera kuphunzira nkhwangwa ili m’mutu kenako n’kuyamba kuona ubwino wotsatira malamulo a Mulungu. Koma tikhoza kuphunzirapo kanthu pa zimene anthu ena otchulidwa m’Baibulo analakwitsa. Lemba la Miyambo 1:5 limati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” Tikamawerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo zimene zinachitikadi timapeza malangizo abwino kwambiri ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Davide zinamupwetekera ataphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita chigololo ndi Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Mukamawerenga nkhaniyi mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo chifukwa chochita chigololo ndi Bati-seba? Kodi ineyo nditakumana ndi mayesero ngati amenewo ndingalimbe? Kodi ndidzathawa ngati Yosefe kapena ndidzakopeka ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Tikamaganizira mavuto amene tingakumane nawo chifukwa chochita tchimo, tikhoza kutsimikiza mumtima mwathu kuti ‘tizidana ndi zoipa.’

8, 9. (a) Kodi chikumbumtima chimatithandiza bwanji? (b) Kodi chikumbumtima chathu chimagwira bwanji ntchito mogwirizana ndi mfundo za Yehova?

8 N’kutheka kuti timapeweratu kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Koma nanga bwanji pa nkhani zimene palibe lamulo lake m’Baibulo? Kodi tingadziwe bwanji zimene Mulungu angasangalale nazo pa nkhani ngati zimenezi? Apa tsopano m’pamene chikumbumtima chophunzitsidwa mfundo za m’Baibulo chingatithandize.

9 Yehova amatikonda ndipo watipatsa mfundo zimene zingatithandize kuti chikumbumtima chathu chizisankha zinthu mwanzeru. Paja iye ananena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.” (Yes. 48:17, 18) Tikamaganizira kwambiri mfundo za m’Baibulo mumtima mwathu timakhala ngati tikuphunzitsa komanso kuumba chikumbumtima chathu. Zimenezi zimathandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru.

MFUNDO ZA MULUNGU ZIZIKUTSOGOLERANI

10. Kodi mfundo za Mulungu n’chiyani, nanga Yesu ankazigwiritsa ntchito bwanji?

10 Mfundo za Mulungu ndi mfundo zachoonadi zomwe zingagwire ntchito pa nkhani zosiyanasiyana ndipo zimathandiza kuti munthu aganizire bwino nkhani inayake kapena asankhe zochita mwanzeru. Kumvetsa mfundo, kumathandiza kuti munthu amvetsenso maganizo a amene anapereka mfundozo komanso zifukwa zimene anaperekera. Pa utumiki wake wonse, Yesu ankaphunzitsa mfundo zimene zikanathandiza ophunzira ake kuti adziwe mavuto amene angakumane nawo ngati ali ndi maganizo enaake kapena ngati atachita zinazake. Mwachitsanzo, anawaphunzitsa kuti mkwiyo ungayambitse chiwawa ndipo kusirira kungapangitse munthu kuchita chigololo. (Mat. 5:21, 22, 27, 28) Kuti tikhale ndi chikumbumtima chophunzitsidwa bwino, tiyenera kulola kuti mfundo za Mulungu zizititsogolera ndipo tikamatero timalemekeza Mulunguyo.​—1 Akor. 10:31.

Mkhristu wolimba mwauzimu amaganizira chikumbumtima cha anthu ena (Onani ndime 11 ndi 12)

11. Kodi Akhristu achikumbumtima chophunzitsidwa bwino angasiyane bwanji pa nkhani zina?

11 Koma pali nkhani zina zimene Akhristu awiri achikumbumtima chophunzitsidwa bwino akhoza kusankha zochita mosiyana. Nkhani ya mowa ndi imodzi mwa nkhani zimenezi. Baibulo sililetsa kumwa mowa mosapitirira malire. Koma limaletsa kumwa kwambiri kapena kuledzera. (Miy. 20:1; 1 Tim. 3:8) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ngati Mkhristu amamwa mosapitirira malire ndiye kuti palibenso mfundo zina zoyenera kuziganizira pa nkhaniyi? Ayi. Mkhristu ayenera kuganiziranso chikumbumtima cha anthu ena ngakhale pa nkhani zimene chikumbumtima chake sichikumutsutsa.

12. Kodi mawu a pa Aroma 14:21 angatithandize bwanji kuti tizilemekeza chikumbumtima cha anthu ena?

12 Posonyeza kufunika koganizira chikumbumtima cha anthu ena, Paulo analemba kuti: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.” (Aroma 14:21) Tiyerekeze kuti muli ndi ufulu wochita zinthu zinazake koma munthu wina akhoza kukhumudwa nazo, kodi mungalolere kuti musazichite? N’zosakayikitsa kuti mungapewe kuchita zinthuzo. Mwachitsanzo, abale athu ena asanakhale a Mboni ankamwa mowa mopitirira malire ndipo panopa safuna kumwa ngakhale pang’ono. Ndiye tonsefe sitingafune kuchititsa munthu kuti ayambirenso zinthu zimene zingamubweretsere mavuto aakulu. (1 Akor. 6:9, 10) Choncho ngati m’bale wabwera kwathu n’kukana mowa, si bwino kumukakamiza kuti amwe.

13. Kodi Timoteyo analolera kuchita chiyani pofuna kuti asakhumudwitse anthu amene ankafuna kuwalalikira?

13 Chitsanzo chabwino ndi zimene Timoteyo anachita poopa kukhumudwitsa Ayuda amene ankafuna kuwalalikira. Iye atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena atakwanitsa, analolera kuti adulidwe ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri. Maganizo ake anali ofanana ndi a mtumwi Paulo. (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:19-23) Kodi nanunso mungalolere zinthu zinazake n’cholinga choti musakhumudwitse anthu ena?

“TIYESETSE MWAKHAMA KUTI TIKHALE OLIMBA MWAUZIMU”

14, 15. (a) Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti akhale wolimba mwauzimu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusonyeza chikondi kwa anthu ena kumasonyezanso kuti ndife olimba mwauzimu?

14 M’malo mongodziwa “chiphunzitso choyambirira cha Khristu,” Akhristu onse ayenera ‘kuyesetsa mwakhama kuti akhale olimba mwauzimu.’ (Aheb. 6:1) Koma zimenezi sizingachitike pazokha. Tiyenera ‘kuyesetsa mwakhama’ ndipo sitiyenera kusiya. Kuti munthu akhale wolimba mwauzimu, ayenera kuwonjezera zimene amadziwa komanso kuzimvetsa bwino. N’chifukwa chake timakumbutsidwa pafupipafupi kuti tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3) Kodi mumayesetsa kuchita zimenezi? Tikamawerenga Baibulo tsiku lililonse tingayambe kulimvetsa bwino kwambiri komanso kumvetsa malamulo ndi mfundo za Yehova.

15 Lamulo lalikulu kwambiri la Akhristu ndi lonena za chikondi. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Yakobo, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba kuti lamulo lonena za chikondi ndi “lamulo lachifumu.” (Yak. 2:8) Nayenso Paulo ananena kuti: “Chilamulo chimakwaniritsidwa m’chikondi.” (Aroma 13:10) N’zosadabwitsa kuti anthuwa anatsindika za chikondi chifukwa Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Sikuti Mulungu amasonyeza chikondi ndi mawu okha. Paja Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Chikondi cha Mulungu n’chimene chinamulimbikitsa kuti achitepo kanthu. Tikamasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake, Akhristu anzathu komanso anthu ena timasonyeza kuti ndife olimba mwauzimu.​—Mat. 22:37-39.

Tikamaganizira mfundo za Mulungu chikumbumtima chathu chimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru (Onani ndime 16)

16. N’chifukwa chiyani tikamakula mwauzimu, timayamba kuona kuti mfundo za Mulungu n’zofunika kwambiri?

16 Munthu akamakula mwauzimu amayamba kuona kuti mfundo za Mulungu ndi zofunika kwambiri. Zili choncho chifukwa malamulo angathandize pa nkhani imodzi koma mfundo zimathandiza pa nkhani zosiyanasiyana. Munthu akakhala wamng’ono sangamvetse kuopsa kocheza ndi anthu oipa, choncho makolo akhoza kumupatsa malamulo amene angamuteteze pa nkhaniyi. (1 Akor. 15:33) Koma akamakula, amayamba kumvetsa zinthu n’kumaganizira mfundo za m’Baibulo. Choncho amatha kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo. (Werengani 1 Akorinto 13:11; 14:20.) Tikamaganizira mfundo za Mulungu chikumbumtima chathu chimatha kutitsogolera kuti tizisankha zinthu zimene Mulungu angasangalale nazo.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tili ndi zinthu zotithandiza kusankha zochita mwanzeru?

17 Kodi tili ndi zonse zofunika kuti tizisankha zinthu mwanzeru n’kumasangalatsa Yehova? Inde. Tikamagwiritsa ntchito mwanzeru malamulo ndiponso mfundo za m’Mawu a Mulungu tidzakhala ‘oyenerera bwino komanso okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Tim. 3:16, 17) Choncho tiyenera kufufuza mfundo za m’Baibulo n’cholinga choti ‘tizindikire chifuniro cha Yehova.’ (Aef. 5:17) Tiyeneranso kugwiritsa ntchito bwino zinthu zimene gulu lathu latipatsa monga Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, LAIBULALE YA PA INTANETI, Watchtower Library komanso JW Library. Zinthuzi zinapangidwa kuti zizitithandiza kwambiri pophunzira Baibulo patokha kapena ndi banja lathu.

TIMADALITSIDWA CHIKUMBUMTIMA CHATHU CHIKAMAYENDERA MFUNDO ZA M’BAIBULO

18. Kodi munthu amapeza madalitso otani akamatsatira malamulo ndi mfundo za Yehova?

18 Lemba la Salimo 119:97-100 limasonyeza kuti timadalitsidwa kwambiri tikamatsatira malamulo ndi mfundo za Yehova. Lembali limati: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse. Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga, chifukwa ndi anga mpaka kalekale. Ndakhala wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga, chifukwa ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu. Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire, chifukwa ndimasunga malamulo anu.” Nzeru zathu, luso la kuzindikira komanso lomvetsa zinthu zikhoza kuwonjezereka ‘tikamasinkhasinkha’ malamulo ndi mfundo za Mulungu. Tikamachita khama kwambiri pophunzitsa chikumbumtima chathu kuti chiziyendera malamulo ndi mfundo za Yehova, tikhoza kufika “pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.”​—Aef. 4:13.

^ ndime 2 Kampasi ndi kachipangizo kokhala ngati wotchi yamivi. Imakhala ndi muvi umodzi wokha umene nthawi zonse umaloza kumpoto ndipo ngati ikugwira bwino ntchito imathandiza munthu kuti asasochere.