Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndakhala Ndikulimbikitsidwa pa Mavuto Anga Onse

Ndakhala Ndikulimbikitsidwa pa Mavuto Anga Onse

Ndinabadwa pa 9 November 1929, mumzinda wakalekale wotchedwa Sukkur. Mzindawu uli m’mbali mwa mtsinje wa Indus ku Pakistan. Pa nthawi imeneyi, mmishonale wina wa ku England anapatsa makolo anga mabuku a mitundu yowala. Mabuku amenewa anandithandiza kuti ndisinthe moyo wanga n’kukhala wa Mboni za Yehova.

ANTHU ankanena kuti mabukuwa anali a utawaleza chifukwa cha mitundu yake. M’mabukuwa ndinapezamo zithunzi zokongola zimene zinkachititsa kuti ndiziganizira kwambiri nkhani zake. Izi zinathandiza kuti ndikhale ndi mtima wokonda kuphunzira nkhani za m’Baibulo kuyambira ndili wamng’ono.

Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itayamba kufalikira ku India, zinthu zinayamba kusokonekera pa moyo wanga. Makolo anga anapatukana kenako banja lawo linatha. Ndinkaganiza kuti zingatheke bwanji kuti anthu awiri amene ndinkawakonda kwambiri asiyane. Zinandisokoneza maganizo kwambiri moti ndinkamva ngati ndine munthu wonyanyalidwa. M’banjali mwana ndinali ndekha ndipo ndinkaona kuti sindikulimbikitsidwa kapena kuthandizidwa mokwanira.

Ine ndi mayi anga tinkakhala mumzinda wa Karachi. Tsiku lina, Fred Hardaker, yemwe anali dokotala wachikulire komanso wa Mboni za Yehova, anafika kunyumba kwathu. Mmishonale amene anapereka mabuku kwa makolo anga uja, analinso wa Mboni za Yehova. M’bale Hardaker anapempha mayi anga kuti aziphunzira nawo Baibulo. Mayi angawo anakana koma anamuuza kuti mwina ineyo ndingakonde. Mlungu wotsatira, ndinayamba kuphunzira ndi M’bale Hardaker.

Patangopita milungu yochepa, ndinayamba kupita nawo kumisonkhano yomwe inkachitikira kuchipatala cha m’baleyu. A Mboni achikulire pafupifupi 12 ankasonkhana kumeneko ndipo ankandilimbikitsa komanso kundisamalira ngati mwana wawo. Ndikukumbukira kuti ankakonda kukhala nane limodzi ndipo akafuna kuti ticheze ankawerama kuti tizionana m’maso. Ankangokhala ngati anzanga enieni ndipo zimenezi n’zimene ndinkafunikira pa nthawiyo.

Tsiku lina M’bale Hardaker anandipempha kuti ndipite nawo kukalalikira. Anandiphunzitsa kugwiritsa ntchito galamafoni kuti anthu azimvetsera nkhani za m’Baibulo zimene tinkayenda nazo. Uthenga wa munkhani zina unkakhala wosapita m’mbali moti anthu ena sankazikonda. Koma ndinkasangalala kwambiri polalikira. Ndinkakonda kwambiri mfundo za m’Baibulo ndipo ndinkafunitsitsa kuuza anthu ena.

Pamene asilikali a ku Japan ankalowa m’dziko la India, akuluakulu a boma la Britain anayamba kupanikiza a Mboni za Yehova. Ndipo nkhani imeneyi inandikhudza mu July 1943. Ahedi apasukulu yathu, omwe anali a mpingo wa Anglican, anandichotsa sukulu ponena kuti ndine mwana woipa. Anauza mayi anga kuti ndikusokoneza anzanga chifukwa choti ndikuphunzira ndi a Mboni za Yehova. Mayi anga anakhumudwa kwambiri moti anandiuza kuti ndisiyiretu kuphunzira ndi a Mboni. Kenako ananditumiza kutauni ya Peshawar kuti ndizikakhala ndi bambo anga. Tauniyi inali chakumpoto pa mtunda wa makilomita 1,370 kuchokera kumene tinkakhala. Popeza ndinasiya kuphunzira Baibulo komanso kucheza ndi abale, ndinafooka mwauzimu.

NDINAKONZA UBWENZI WANGA NDI YEHOVA

Mu 1947, ndinabwerera ku Karachi kuti ndikafufuze ntchito. Ndili kumeneko ndinapita kuchipatala cha M’bale Hardaker ndipo anandilandira ndi manja awiri.

Poyamba ankaganiza kuti ndikudwala ndipo anandifunsa kuti, “Chavuta n’chiyani?”

Ndinamuyankha kuti, “Sindikudwala m’thupi koma ndikudwala mwauzimu. Ndikufuna kuyambiranso kuphunzira Baibulo.”

Iye anafunsa kuti, “Ukufuna kuyamba liti?”

Ndinayankha kuti, “Panopa ngati zingatheke.”

Tinaphunzira Baibulo madzulowo ndipo zinali zosangalatsa kwambiri. Ndinkamva bwino kwambiri kukhalanso limodzi ndi anthu a Yehova. Mayi anga anayesetsa kundiletsa kucheza ndi a Mboni koma ulendowu ndinali nditatsimikiza kuti ndiyambe kutumikira Yehova. Pa 31 August 1947, ndinabatizidwa posonyeza kuti ndinadzipereka kwa Yehova. Pasanapite nthawi yaitali ndinayamba kuchita upainiya wokhazikika ndili ndi zaka 17.

NDINKASANGALALA KUCHITA UPAINIYA

Ndinayamba upainiya ku Quetta, kumene asilikali ena a Britain ankakhala pa nthawi ya nkhondo. Mu 1947, dziko la India linagawidwa kukhala India ndi Pakistan. * Izi zinachititsa kuti anthu azilimbana kwambiri pa nkhani zachipembedzo ndipo ambiri anathawa kwawo. Anthu amene anathawa kwawo anakwana pafupifupi 14 miliyoni. Asilamu amene ankakhala ku India anapita ku Pakistan pomwe anthu achipembedzo chachihindu ndi chachisiki amene anali ku Pakistan anasamukira ku India. Pa nthawi imene anthu ankasamukayi, ndinakwera sitima ku Karachi kupita ku Quetta. Sitimayi inali yodzaza kwambiri ndi anthu moti ndinakhala mopanikizika kwambiri.

Ndili pa msonkhano wadera ku India mu 1948

Nditafika ku Quetta, ndinakumana ndi M’bale George Singh yemwe ankachita upainiya wapadera ndipo anali ndi zaka za m’ma 20. M’baleyu anandipatsa njinga yoti ndiziyendera m’dera lamapiri la kumeneko. Nthawi zambiri ndinkalalikira ndekhandekha. Pamene inkatha miyezi 6 ndinali ndi maphunziro a Baibulo 17 ndipo ena anafika pobatizidwa. Mmodzi mwa anthuwa anali mkulu wa asilikali dzina lake Sadiq Masih ndipo iye ndi George anandithandiza kumasulira mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’Chiurdu, chomwe ndi chilankhulo chachikulu cha ku Pakistan. Patapita nthawi, Sadiq anakhala wa Mboni ndipo ankalalikira uthenga wabwino mwakhama.

Ndinakwera sitima yotchedwa Queen Elizabeth popita ku Sukulu ya Giliyadi

Kenako ndinabwerera ku Karachi ndipo ndinkatumikira ndi amishonale awiri amene anali atangofika kumene kuchokera ku Sukulu ya Giliyadi. Amishonalewo anali Henry Finch ndi Harry Forrest ndipo anandiphunzitsa zambiri. Nthawi ina, ine ndi M’bale Finch tinapita kukalalikira chakumpoto kwa Pakistan. Titafika pafupi ndi phiri lina tinapeza anthu olankhula Chiurdu omwe ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo. Patangopita zaka ziwiri, ndinapita ku Sukulu ya Giliyadi ndipo pobwerera ndinakhala woyang’anira dera wogwirizira ku Pakistan komweko. Ndinkakhala kunyumba ya amishonale ku Lahore limodzi ndi amishonale ena atatu.

ZIMENE ZINANDITHANDIZA NDITALANDIRA MALANGIZO AMPHAMVU

Koma mu 1954 panachitika zinthu zomvetsa chisoni. Amishonalewo anayambana ndipo zinachititsa kuti ofesi ya nthambi iwasinthe utumiki. Inenso ndinali m’gulu lokanganalo moti anandipatsa malangizo amphamvu kwambiri. Zinandikhudza kwambiri moti ndinkangodziona kuti ndine wolephera. Choncho ndinabwerera ku Karachi, kenako ndinapita ku London m’dziko la England kuti ndikakonzenso ubwenzi wanga ndi Yehova.

Nditafika ku London ndinkasonkhana mumpingo womwe unali ndi abale ambiri a ku Beteli. Pa nthawiyo M’bale Pryce Hughes yemwe anali mtumiki wa nthambi ankandithandiza kwambiri. Tsiku lina anandiuza kuti m’mbuyomo nayenso anapatsidwa malangizo amphamvu ndi M’bale Joseph F. Rutherford, yemwe ankayang’anira ntchito yapadziko lonse. Ananena kuti pamene iye ankayesa kudziikira kumbuyo, M’bale Rutherford anamudzudzula kwambiri. Ndinadabwa kuona M’bale Hughes akumwetulira poganizira zimene zinachitikazo. Ananena kuti poyamba anakhumudwa koma kenako anazindikira kuti inali njira imene Yehova anamusonyezera chikondi. (Aheb. 12:6) Zimene ananenazi zinandilimbikitsa kwambiri ndipo zinandithandiza kuti ndiyambenso kutumikira Mulungu mosangalala.

Pa nthawi imeneyi, mayi anga anabweranso ku London ndipo anayamba kuphunzitsidwa Baibulo ndi M’bale John E. Barr amene anadzakhala m’Bungwe Lolamulira. Phunziroli linkayenda bwino kwambiri moti anabatizidwa mu 1957. Kenako ndinamva kuti bambo anga asanamwalire nawonso ankaphunzira ndi a Mboni za Yehova.

Mu 1958, ndinakwatira mlongo wa ku Denmark amene anabwera kudzakhala ku London ndipo dzina lake ndi Lene. Chaka chotsatira tinakhala ndi mwana wamkazi dzina lake Jane, yemwe ndi woyamba pa ana athu 5. Ndinayambanso kutumikira pa maudindo osiyanasiyana mumpingo wa ku Fulham. Koma kenako Lene anayamba kudwaladwala moti tinafunika kusamukira kudera lotentherapo. Choncho mu 1967, tinasamukira ku Adelaide m’dziko la Australia.

TINAKUMANA NDI ZOMVETSA CHISONI KWAMBIRI

Mumpingo wa ku Adelaide munali Akhristu 12 achikulire omwe anali odzozedwa. Iwo ankatsogolera mwakhama pa ntchito yolalikira ndipo pasanapite nthawi yaitali moyo wathu wauzimu unayamba kuyenda bwino.

Mu 1979, ine ndi Lene tinakhala ndi mwana wa nambala 5 dzina lake Daniel. Mwanayu anabadwa ndi vuto linalake la mu ubongo ndipo madokotala anatiuza kuti sitikhala naye kwa nthawi yaitali. * Mpaka pano zimandivuta kufotokoza mmene zinatipwetekera pa nthawiyo. Tinkayesetsa kumusamalira uku tikusamaliranso ana athu ena 4. Nthawi zina thupi la Daniel linkasintha n’kumaoneka labuluu chifukwa chosowa mpweya wa okosijeni ndipo zikatero tinkapita naye mwamsanga kuchipatala. Vutoli linkayamba chifukwa choti mtima wake unabooka malo awiri. Koma ngakhale kuti anali ndi mavuto amenewa, Daniel anali wanzeru ndiponso wachikondi. Iye ankakondanso kwambiri zinthu zokhudza kulambira. Tikamapemphera tisanayambe kudya, ankakonda kuika manja ake pamodzi, kuvomereza ndi mutu komanso kunena ndi mtima wonse kuti “Ame!” Pambuyo pake ankayamba kudya.

Daniel atakwanitsa zaka 4 anayamba matenda a khansa ya m’magazi. Ine ndi Lene zinatipweteka koopsa komanso tinkangokhala otopa nthawi zonse moti ine zinandisokoneza kwambiri maganizo. Koma zinthu zitafika poipa chonchi, woyang’anira dera wathu dzina lake Neville Bromwich anafika kwathu. Madzulo a tsiku limenelo anatihaga tonse uku misozi ikulengeza ndipo tonse tinalira. Zimene analankhula komanso kuchita zinatilimbikitsa kwambiri. Ananyamuka cha m’ma 1 koloko m’bandakucha ndipo pasanapite nthawi yaitali Daniel anamwalira. Imfa yake inatipweteka koopsa. Koma tinakwanitsa kupirira podziwa kuti ngakhale imfa singasiyanitse Danieli ndi chikondi cha Yehova. (Aroma 8:38, 39) Timalakalaka kwambiri kudzamuona akadzaukitsidwa m’dziko latsopano.​—Yoh. 5:28, 29.

NDIMASANGALALA NDIKAMATHANDIZA ENA

Matenda a sitiroko anandigwirapo kawiri koma ndikutumikirabe ngati mkulu mumpingo. Zimene ndakumana nazo pa moyo wanga zandithandiza kuti ndikhale wokoma mtima komanso wachifundo makamaka kwa anthu amene akukumana ndi mavuto. Sindikonda kuwaweruza. M’malomwake ndimadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene akumana nazo pa moyo wawo zakhudza bwanji maganizo ndi mtima wawo? Nanga ndingasonyeze bwanji kuti ndimawakonda? Kodi ndingawalimbikitse bwanji kuti azitsatira njira za Yehova?’ Ndimakonda kwambiri kuchita maulendo aubusa. Ndikamalimbikitsa anthu ena mwauzimu ndimaona kuti nanenso ndikulimbikitsidwa.

Ndimasangalalabe ndikamachita maulendo aubusa

Ndimamva ngati wolemba masalimo amene ananena kuti: ‘Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, Yehova ananditonthoza n’kuyamba kusangalatsa moyo wanga.’ (Sal. 94:19) Yehova anandilimbikitsa nditakumana ndi mavuto m’banja lathu, ndikutsutsidwa, nditakhumudwa komanso pamene ndinkavutika maganizo. Kunena zoona, Yehova wakhaladi Bambo wanga weniweni.

^ ndime 19 Poyamba dziko la Pakistan linali ndi zigawo ziwiri. Choyamba chinali West Pakistan (panopa ndi Pakistan) ndipo chachiwiri chinali East Pakistan (panopa ndi Bangladesh).

^ ndime 29 Onani nkhani yakuti, “Kulera Ana Obadwa ndi Matenda Ozerezeka” mu Galamukani ya June 2011.