Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

“Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti . . . alemekeze Atate wanu.”​—MAT. 5:16.

NYIMBO: 77, 59

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatithandiza kukhala osangalala?

TIMASANGALALA tikamamva mmene anthu a Yehova akuchulukira. Mwachitsanzo, chaka chatha, tinachititsa maphunziro a Baibulo oposa 10,000,000. Izi zikusonyeza kuti atumiki a Mulungu akuonetsadi kuwala kwawo. Ndipo panali anthu achidwi mamiliyoni ambiri amene anapezeka pa Chikumbutso. Iwo anakhala ndi mwayi wophunzira mmene Mulungu anasonyezera chikondi popereka nsembe ya Yesu.​—1 Yoh. 4:9.

2, 3. (a) Kodi n’chiyani chimene sichitilepheretsa ‘kuwala monga zounikira’? (b) Malinga ndi mawu a Yesu a pa Mateyu 5:14-16, kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Anthu a Yehova padziko lonse amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana. Koma izi sizimatilepheretsa kuti tizilambira Atate wathu, Yehova, mogwirizana. (Chiv. 7:9) Ngakhale kuti timalankhula zilankhulo zosiyana komanso timakhala kosiyana, tonsefe tikhoza kuwala “monga zounikira m’dzikoli.”​—Afil. 2:15.

3 Zinthu monga kukula kwa gulu lathu, mgwirizano umene tili nawo komanso kukhalabe maso kwathu, zimathandiza kuti Yehova alemekezeke. Munkhaniyi, tikambirana mmene tingaonetsere kuwala kwathu m’mbali zimenezi.​—Werengani Mateyu 5:14-16.

TIZITHANDIZA ENA KUTI AYAMBE KULAMBIRA YEHOVA

4, 5. (a) Kuwonjezera pa kulalikira, kodi tingaonetsenso bwanji kuwala kwathu? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tikamakhala aubwenzi mu utumiki? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1925, munali nkhani ya mutu wakuti “Kuwala Mumdima” ndipo inanena kuti: “Palibe amene angakhale wokhulupirika kwa Ambuye m’masiku otsalawa . . . pokhapokha ngati akuyesetsa kuonetsa kuwala kwake.” Nkhaniyo inapitiriza kuti: “Munthu angaonetse kuwalaku akamauza ena uthenga wabwino komanso akamayenda m’njira za kuwalako.” Izi zikusonyeza kuti njira imodzi imene timaonetsera kuwala kwathu ndi kulalikira uthenga wabwino komanso kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20) Koma timalemekezanso Yehova tikakhala ndi khalidwe labwino. Paja anthu amene timawalalikira kapena kukumana nawo mu utumiki amaona zochita zathu. Tikamamwetulira komanso kupereka moni mwansangala timathandiza anthu kuti akhale ndi maganizo oyenera okhudza ifeyo komanso Mulungu amene timamulambira.

5 Paja Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo.” (Mat. 10:12) M’dera limene Yesu ndi ophunzira ake ankalalikira, anthu ankakonda kuitanira anthu achilendo m’nyumba zawo. Koma zimenezi sizichitikachitika m’madera ambiri masiku ano. Komabe tikakhala aubwenzi tikhoza kuthandiza munthu amene tamupeza kuti asakhale ndi maganizo olakwika. Nthawi zambiri, kumwetulira kumathandiza kuti muyambe kukambirana naye. Zimenezi zimathandizanso tikamalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu m’malo opezeka anthu ambiri. Tikamalalikira m’malo ngati amenewa, anthu amachita chidwi akaona kuti tikumwetulira komanso kuwapatsa moni mwansangala. Zimenezi zikhoza kuwathandiza kuti afike n’kutenga mabuku. Zikhoza kuthandizanso kuti muyambe kukambirana nawo.

6. Kodi achikulire ena anatani kuti azichitabe zambiri mu utumiki?

6 Banja lina la ku England panopa sililalikira kwambiri kunyumba ndi nyumba chifukwa cha mavuto auchikulire. Choncho anaganiza kuti azionetsa kuwala kwawo ali kunyumba kwawo. Iwo amangoika mabuku patebulo pa nthawi imene makolo amabwera kudzatenga ana awo pasukulu yapafupi. Ambiri amachita chidwi ndipo amakonda kutenga buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa komanso timabuku tina. Mlongo wina amene akuchita upainiya mumpingo wawo anapita kukalalikira nawo. Mtima waubwenzi wa mlongoyo komanso khama la achikulirewo zinathandiza kuti bambo wina ayambe kuphunzira Baibulo.

7. Kodi mungathandize bwanji anthu amene asamukira m’dera lanu?

7 Masiku ano, anthu ambiri amathawa kwawo n’kusamukira m’mayiko ena. Kodi mungathandize bwanji anthu oterewa kuti adziwe Yehova komanso cholinga chake? Mwina mungayambe ndi kuphunzira moni wa chilankhulo cha anthu amene asamukira m’dera lanu. Pulogalamu ya JW Language ikhoza kukuthandizani pa nkhaniyi. Mwinanso mungaphunzire mawu ena amene angathandize kuti muyambe kucheza nawo. Kenako mungawasonyeze mavidiyo ndi mabuku achilankhulo chawo pa jw.org.​—Deut. 10:19.

8, 9. (a) Kodi msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu umatithandiza bwanji? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti aziyankha bwino kumisonkhano?

8 Chifukwa chotikonda, Yehova watipatsa msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu kuti uzitithandiza kulalikira mogwira mtima. Zimene timaphunzira pamisonkhano imeneyi zimatithandiza kuti tisamadzikayikire pochita maulendo obwereza kapena pophunzitsa anthu Baibulo.

9 Anthu amene amabwera kumisonkhano yathu amachita chidwi kumva mayankho amene ana amapereka. Makolo angachite bwino kuthandiza ana kuti azipereka ndemanga m’mawu awoawo. Anthu ena anayamba kuphunzira choonadi chifukwa chomva ana akuyankha mwachidule koma kuchokera mumtima.​—1 Akor. 14:25.

TIZILIMBIKITSA MGWIRIZANO

10. Kodi kulambira kwa pabanja kungathandize bwanji kuti anthu a m’banja azigwirizana?

10 Timaonetsanso kuwala kwathu tikamalimbikitsa mgwirizano m’banja ndi mumpingo. Njira ina imene makolo angalimbikitsire mgwirizanowu ndi kuchita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Makolo ambiri amaonera JW Broadcasting pa kulambira kwawo kwa pabanja mwezi uliwonse. Mukaonera pulogalamuyi, mungachite bwino kukambirana mfundo zimene mungagwiritse ntchito. Ndi bwino kukumbukira kuti mfundo zimene zingathandize mwana wamng’ono zingakhale zosiyana ndi zimene zingathandize wachinyamata. Choncho popanga kulambira kwa pabanja, muyenera kukambirana mfundo zimene mwaphunzira m’njira yoti zizithandiza aliyense m’banjamo.​—Sal. 148:12, 13.

Kucheza ndi achikulire n’kolimbikitsa kwambiri (Onani ndime 11)

11-13. Kodi tonsefe tingalimbikitse bwanji mgwirizano mumpingo komanso kuthandiza anthu ena kuti azionetsa kuwala kwawo?

11 Kodi achinyamata angalimbikitse bwanji mgwirizano mumpingo komanso kuthandiza anthu ena kuti azionetsa kuwala kwawo? Ngati ndinu wachinyamata, mungachite bwino kumacheza ndi achikulire. Mukhoza kuwapempha mwaulemu kuti afotokoze zinthu zimene akumana nazo potumikira Yehova. Zimenezi zingalimbikitse achikulirewo komanso inuyo kuti muzionetsa kwambiri kuwala kwanu. Tonsefe tiyeneranso kulandira bwino anthu amene abwera kudzasonkhana nafe ku Nyumba ya Ufumu. Tikamachita zimenezi timalimbikitsa mgwirizano komanso tikhoza kuthandiza anthuwo kuti ayambe kuonetsa kuwala kwawo. Tingalandire anthu powapatsa moni tikumwetulira komanso kuwathandiza kuti apeze malo okhala. Tingawathandizenso kuti adziwane ndi anthu ena n’cholinga choti azimasuka.

12 Munthu amene wapemphedwa kuti achititse msonkhano wokonzekera utumiki angathandizenso kwambiri abale ndi alongo achikulire. Angawapatse gawo lomwe angakwanitse kukalalikira. Nthawi zina pangafunike kuwagawa ndi munthu wamphamvuko amene angamawathandize poyenda. Angachitenso bwino kuganizira anthu amene sangakwanitse kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. Abalewa akamachita zinthu moganizira anthu, kaya achinyamata kapena achikulire, angawathandize kuti azilalikira uthenga wabwino mwakhama.​—Lev. 19:32.

13 Wolemba masalimo ananena kuti: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” (Werengani Salimo 133:1, 2.) Aisiraeli akamalambira Yehova limodzi ankalimbikitsana. Ankamva ngati adzola mafuta amene ankagwiritsa ntchito podzoza munthu omwe ankanunkhira bwino komanso kukhazika mtima m’malo. Tiyeni tiziyesetsa kulimbikitsa mgwirizano pakati pa abale ndi alongo athu. Ngati mumachita kale zimenezi mukuchita bwino kwambiri. Koma mwina mukhoza ‘kufutukula mtima wanu’ powonjezera zimene mukuchitazo.​—2 Akor. 6:11-13.

14. Kodi mungatani kuti muzionetsa kuwala kwanu m’dera lanu?

14 Kodi mungawonjezere zimene mumachita poonetsa kuwala kwanu m’dera limene mumakhala? Mawu ndi zochita zanu zingathandize anthu amene mumakhala nawo pafupi kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amene ndimakhala nawo pafupi amandiona bwanji? Kodi pakhomo panga ndi paukhondo? Kodi ndimayesetsa kuthandiza anthu ena? Mukamacheza ndi abale ndi alongo mungachite bwino kuwapempha kufotokoza mmene kukoma mtima kwawo ndi khalidwe lawo labwino zathandizira achibale awo, anthu okhala nawo pafupi, anzawo akuntchito kapena akusukulu. N’kutheka kuti angafotokoze zinthu zosangalatsa kwambiri.​—Aef. 5:9.

TIZIKHALABE MASO

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe maso?

15 Kukumbukira kuti tili m’masiku otsiriza kungatithandize kuti tizionetsa kwambiri kuwala kwathu. Yesu ankauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti: “Khalanibe maso.” (Mat. 24:42; 25:13; 26:41) Ngati titayamba kuona kuti “chisautso chachikulu” chidakali kutali moti sichingabwere tidakali moyo, tikhoza kusiya kulalikira mwakhama. (Mat. 24:21) Zikatero kuwala kwathu kukhoza kuyamba kuchepa mwina mpaka kufika pozimiratu.

16, 17. Kodi mungatani kuti mukhalebe maso?

16 Tonsefe tikufunika kukhalabe maso pamene zinthu zikuipiraipira m’dzikoli. Ndipo tikudziwa kuti mapeto a dzikoli sadzalephera kufika pa nthawi imene Yehova anasankha. (Mat. 24:42-44) Pakali pano tikufunika kukhala oleza mtima komanso kukhalabe maso. Tiziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndiponso tizipemphera nthawi zonse. (1 Pet. 4:7) Tizitengera chitsanzo cha abale ndi alongo amene akhalabe maso kwa nthawi yaitali ndipo akuonetsabe kuwala kwawo. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi m’bale amene anafotokozedwa munkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 18-21, ya mutu wakuti “Ndagwira Chovala cha Myuda kwa Zaka Zoposa 70.”

17 Muzikhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova komanso muzicheza kwambiri ndi abale ndi alongo amene angakulimbikitseni. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale wosangalala komanso musamaone kuti nthawi ikuchedwa. (Aef. 5:16) N’zoona kuti pa zaka 100 zapitazi, abale athu ankachita zambiri pa ntchito ya Yehova. Koma masiku ano Yehova akutithandiza kuchita zochuluka kwambiri. Panopa tikuonetsa kwambiri kuwala kwathu kuposa mmene tinkayembekezera.

Akulu akabwera kudzatichezera timakhala ndi mwayi wopeza nzeru za m’Mawu a Mulungu (Onani ndime 18, 19)

18, 19. Kodi akulu mumpingo angatithandize bwanji kuti tikhalebe maso komanso tizichita khama? Perekani chitsanzo.

18 N’zolimbikitsa kuti Yehova amatilolabe kuti tizimutumikira ngakhale kuti si ife angwiro. Ndi bwino kuti tiziyamikira akulu omwe ndi “mphatso za amuna” zimene Yehova anatipatsa. (Werengani Aefeso 4:8, 11, 12.) Choncho mkulu wina akadzakuyenderani kunyumba kwanu, mudzagwiritse ntchito mwayi umenewo kuti mupindule ndi nzeru komanso malangizo ake.

19 Akulu awiri a ku England anapita kukaona banja lina limene linapempha thandizo. Mkazi wa m’banjalo ankaona kuti mwamuna wake sankatsogolera banjalo pa zinthu zauzimu. Mwamuna wake anavomereza kuti analibe luso lophunzitsa komanso sankapangitsa kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Akuluwo anathandiza banjalo pogwiritsa ntchito chitsanzo cha Yesu. Iye ankasamalira bwino ophunzira ake komanso ankawaganizira. Ndiye akuluwo analimbikitsa mwamunayo kuti azitsanzira Yesu komanso anauza mkazi wake kuti aziyesetsa kukhala woleza mtima. Akuluwo anapatsa banjalo malangizo othandiza kuti azikwanitsa kuchita kulambira kwa pabanja pamodzi ndi ana awo awiri. (Aef. 5:21-29) Patapita nthawi, akuluwo anayamikira mwamunayo chifukwa cha khama limene anasonyeza. Anamulimbikitsa kuti apitirize kuchita khama komanso kudalira mzimu woyera kuti uzimuthandiza kukhala mutu wabwino wa banja lake. Zimene akuluwa anachita zinathandiza kuti banjali lizionetsa kuwala kwawo.

20. Kodi chingachitike n’chiyani mukamaonetsa kuwala kwanu?

20 Wolemba masalimo ananena kuti: “Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njira za Mulungu.” (Sal. 128:1) Mudzasangalala kwambiri mukamaonetsa kuwala kwanu pothandiza anthu kuti azilambira Mulungu, polimbikitsa mgwirizano komanso pokhalabe maso. Anthu adzaona ntchito zanu zabwino ndipo ambiri adzalemekeza Atate wathu.​—Mat. 5:16.