Kodi Mukudziwa?
Kodi zinkachitikadi kuti munthu ankafesa namsongole m’munda umene mnzake wafesamo mbewu?
PALEMBA la Mateyu 13:24-26 Yesu ananena kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake. Koma anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo, n’kuchoka. Tsopano mmerawo utakula ndi kutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekera.” Olemba mbiri ena amakayikira ngati zimene Yesu ananena m’fanizoli zinkachitikadi. Koma mabuku a malamulo a Aroma amasonyeza kuti zoterezi zinkachitika.
Buku lina limati malamulo a Aroma ankati munthu akafesa namsongole m’munda mwa mnzake pofuna kumubwezera zoipa zimene wachita, ndiye kuti wapalamula mlandu. Popeza panali lamulo lokhudza zimenezi, ndiye kuti zoterezi zinkachitika. Katswiri wina wazamalamulo dzina lake Alastair Kerr anafotokoza kuti m’chaka cha 533 C.E., Justinian yemwe anali mfumu ya Aroma, analemba buku lake lina. (Digest) M’bukuli, anafotokozamo mwachidule zokhudza malamulo a Aroma komanso zimene akatswiri ena a zamalamulo ananena kuyambira mu 100 C.E. mpaka 250 C.E. Mwachitsanzo, bukuli linafotokoza kuti mmodzi mwa akatswiriwa dzina lake Ulpian, anatchula za mlandu wina umene unachitika m’zaka za m’ma 100 C.E. Munthu wina anafesa namsongole m’munda mwa mnzake ndipo mbewu zonse zimene zinali m’mundamo zinawonongeka. Bukuli linafotokoza kuti panali malamulo amene anathandiza wolakwiridwayo kulandira chipukuta misozi cha ndalama kuchokera kwa wopalamulayo.
Nkhani imeneyi, inachitika mu Ufumu wa Aroma ndipo ikusonyeza kuti zimene Yesu ananena mu fanizo lake lija, zinkachitikadi.
M’nthawi ya atumwi, kodi Aroma ankapereka ufulu wotani kwa Ayuda amene ankalamulira ku Yudeya?
M’NTHAWI ya atumwi, Aroma ankaika bwanamkubwa woti azilamulira ku Yudeya. Bwanamkubwayo ankakhala ndi asilikali ake ndipo ankatolera misonkho komanso kuonetsetsa kuti kuli bata ndi mtendere. Aroma sankalola kuti anthu ena aziphwanya malamulo awo ndipo ankalanga aliyense woyambitsa chisokonezo. Ngakhale zinali choncho, iwo ankapereka ufulu kwa atsogoleri achiyuda kuti aziweruza milandu ina.
Ayuda amene aphwanya malamulo achiyuda ankaweruzidwa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda. Koma panalinso makhoti ena ang’onoang’ono ndipo Ayuda ambiri ankaweruzidwa m’makhoti amenewa. Aroma sankalowerera milandu yokhudza malamulo a Ayuda. Koma sankalola kuti makhoti a Ayudawo aziweruza munthu kuti aphedwe. Sitefano yekha ndi amene tikudziwa kuti anaweruzidwa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda kenako n’kumuponya miyala mpaka kufa.—Mac. 6:8-15; 7:54-60.
Izi zikusonyeza kuti Khoti Lalikulu la Ayuda linali ndi mphamvu zambiri ndithu. Katswiri wina analemba kuti: “Koma Aroma akakayikira zoti munthu wina akuukira boma, mlandu wake ankaweruza okha.” Chitsanzo ndi zimene zinachitika mu ulamuliro wa Kalaudiyo Lusiya. Iye anamanga mtumwi Paulo, yemwe anali nzika ya Roma, pomuganizira kuti ndi woukira boma.—Mac. 23:26-30.