Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova

Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova

‘Chikhulupiriro ndi umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.’—AHEB. 11:1.

NYIMBO: 54, 125

1. Kodi tiyenera kumva bwanji ngati tili ndi chikhulupiriro?

CHIKHULUPIRIRO ndi khalidwe lofunika kwambiri kwa Akhristu. Koma si anthu onse amene amakhala nacho. (2 Ates. 3:2) Yehova amathandiza anthu ake kukhala ndi chikhulupiriro. (Aroma 12:3; Agal. 5:22) Choncho aliyense amene ali ndi chikhulupiriro ayenera kuyamikira.

2, 3. (a) Kodi anthu amene ali ndi chikhulupiriro amapeza madalitso otani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Yehova amagwiritsa ntchito Mwana wake pokoka anthu kuti akhale mabwenzi ake. (Yoh. 6:44, 65) Munthu akamakhulupiririra Yesu amakhala ndi mwayi wokhululukidwa machimo. Izi zingathandize kuti munthuyo akhale bwenzi la Yehova mpaka kalekale. (Aroma 6:23) Kodi pali zilizonse zimene tinachita kuti Yehova atichitire zonsezi? Popeza ndife anthu ochimwa, tinali oyenera kufa basi. (Sal. 103:10) Koma Yehova anaona kuti tingathe kuchita zabwino. Choncho mwa chisomo chake, anatsegula mtima wathu kuti timvetsere uthenga wabwino. Ndiyeno tinayamba kusonyeza kuti timakhulupirira Yesu podziwa kuti zimenezi zingathandize kuti tidzapeze moyo wosatha.—Werengani 1 Yohane 4:9, 10.

3 Koma kodi chikhulupiriro n’chiyani? Kodi chimangotanthauza kudziwa bwino madalitso amene Mulungu watilonjeza? Nanga ifeyo tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro?

TIZISONYEZA KUTI TILI NDI CHIKHULUPIRIRO ‘MUMTIMA MWATHU’

4. N’chifukwa chiyani tingati chikhulupiriro sichimangotanthauza kudziwa bwino madalitso amene Mulungu watilonjeza?

4 Chikhulupiriro sichimangotanthauza kudziwa bwino madalitso amene Mulungu watilonjeza. Chikhulupiriro chimapangitsa kuti munthu azichita zinthu zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kukhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu zotipulumutsa kumatipangitsa kuti tiziuza ena uthenga wabwino. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Ngati ukulengeza kwa anthu mawu amene ali m’kamwa mwakowo, akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.”—Aroma 10:9, 10; 2 Akor. 4:13.

5. Kodi chikhulupiriro n’chofunika bwanji, nanga tingatani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba? Perekani chitsanzo.

5 Kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko la tsopano, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro. Tiyeneranso kuonetsetsa kuti chikhulupiriro chathucho n’cholimba. Chikhulupiriro tingachiyerekezere ndi maluwa. Kuti maluwa azikula bwino, timayenera kuwathirira nthawi zonse. Kupanda kutero angafote kenako n’kufa. N’chimodzimodzinso ndi chikhulupiriro. Kupanda kuchisamalira chikhoza kufooka mpaka kutha. Choncho nthawi zonse tiyenera kuonetsetsa kuti chikhulupiriro chathu ndi “cholimba” komanso “chikukula.”—Tito 2:2; 2 Ates. 1:3; Luka 22:32; Aheb. 3:12.

KODI BAIBULO LIMATI CHIKHULUPIRIRO N’CHIYANI?

6. Kodi lemba la Aheberi 11:1 limafotokoza bwanji tanthauzo la chikhulupiriro?

6 Baibulo limafotokoza tanthauzo la chikhulupiriro pa Aheberi 11:1. (Werengani.) Limati chikhulupiriro ndi: (1) “Chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” Izi ndi zinthu zimene Mulungu walonjeza koma panopa sizinachitike. Mwachitsanzo, walonjeza kuti adzathetsa zoipa zonse n’kubweretsa dziko latsopano. (2) “Umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Palembali mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “umboni wooneka” akutanthauza “umboni wokhutiritsa” wa zinthu zoti sitingathe kuziona, koma zilipo. Mwachitsanzo, timakhulupirira zoti kuli Yehova Mulungu, Yesu Khristu, angelo komanso Ufumu wakumwamba. (Aheb. 11:3) Ndiyeno kodi tingasonyeze bwanji kuti timayembekezera komanso kukhulupirira zinthu zosaoneka zomwe zafotokozedwa m’Mawu a Mulungu? Zochita ndi zolankhula zathu ndi zimene zingasonyeze.

7. Kodi chitsanzo cha Nowa chingatithandize bwanji kumvetsa tanthauzo la chikhulupiriro? (Onani chithunzi patsamba 26.)

7 Lemba la Aheberi 11:7 limanena za Nowa. Limati: “Atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa kuti banja lake lipulumukiremo.” Nowa anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro pomanga chingalawa. Anthu ayenera kuti ankafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumanga chingalawa chachikulu choncho? Kodi Nowa ankangokhala chete? Kapena kodi ankangowauza kuti sizikuwakhudza? Ayi ndithu. Popeza iye anali ndi chikhulupiriro, ankawalalikira molimba mtima komanso ankawachenjeza za chiweruzo cha Mulungu. Ayenera kuti ankawauza mawu amene Mulungu ananena akuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse, popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. . . . Ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.” Choncho Nowa anasonyezanso kuti anali ndi chikhulupiriro pokhala “mlaliki wa chilungamo.”—Gen. 6:13, 17, 18; 2 Pet. 2:5.

8. Fotokozani zimene Yakobo analemba pa nkhani ya chikhulupiriro.

8 Nayenso Yakobo analemba zokhudza chikhulupiriro m’kalata yake. Iye ayenera kuti analemba zimenezi pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Paulo analemba kalata yake. Mofanana ndi Paulo, nayenso Yakobo anafotokoza kuti munthu wachikhulupiriro chenicheni amachita ntchito zosonyeza chikhulupiriro chakecho. Iye analemba kuti: “Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.” (Yak. 2:18) Yakobo anafotokozanso kuti kungokhulupirira n’kosiyana ndi kuchita ntchito zosonyeza chikhulupiriro. Mwachitsanzo, ziwanda zimakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma sitinganene kuti zili ndi chikhulupiriro chenicheni. Tikutero chifukwa zimachita zinthu zotsutsana ndi Mulungu. (Yak. 2:19, 20) Koma Abulahamu anali ndi chikhulupiriro chenicheni. Ponena za iye, Yakobo anati: “Kodi Abulahamu atate wathu sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka Isaki mwana wake nsembe paguwa? Waonatu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo mwa ntchito zakezo chikhulupiriro chakecho chinakhala changwiro.” Ndiyeno potsindika mfundo yoti chikhulupiriro chiyenera kusonyezedwa ndi ntchito, Yakobo anawonjezera kuti: “Monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa, nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.”—Yak. 2:21-23, 26.

9, 10. Kodi zimene mtumwi Yohane analemba zimatithandiza bwanji kudziwa kufunika kosonyeza chikhulupiriro?

9 Patatha zaka zoposa 30, mtumwi Yohane analemba Uthenga Wabwino komanso makalata ake atatu. Mofanana ndi anthu ena amene analemba Baibulo, nayenso anasonyeza kuti ankamvetsa tanthauzo la chikhulupiriro chenicheni. Akamanena za chikhulupiriro, Yohane ankakonda kugwiritsa ntchito mawu achigiriki amene nthawi zina amamasuliridwa kuti “kukhulupirira” kapena “kusonyeza chikhulupiriro.”

10 Mwachitsanzo, iye anafotokoza kuti: “Wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Choncho munthu wa chikhulupiriro chenicheni amasonyeza kuti amamvera malamulo a Yesu. Ndipotu Yohane ankakonda kugwira mawu a Yesu osonyeza kuti tiyenera kupitirizabe kusonyeza chikhulupiriro.—Yoh. 3:16; 6:29, 40; 11:25, 26; 14:1, 12.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova potithandiza kudziwa choonadi?

11 Yehova amatipatsa mzimu wake woyera ndipo umatithandiza kuti tizimvetsa choonadi komanso tizisonyeza kuti timakhulupirira uthenga wabwino. (Werengani Luka 10:21.) Tiyenera kumamuthokoza kwambiri chifukwa chotikokera kwa iye pogwiritsa ntchito Mwana wake yemwe ndi “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.” (Aheb. 12:2) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira? Tiyenera kupitirizabe kulimbitsa chikhulupiriro chathu popemphera komanso kuphunzira Mawu ake.—Aef. 6:18; 1 Pet. 2:2.

Muzisonyeza chikhulupiriro chanu polalikira paliponse pamene papezeka mpata (Onani ndime 12)

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro?

12 Tiyeni tipitirizebe kusonyeza kuti timakhulupirira malonjezo a Yehova. Tizichita zinthu zimene zingathandize aliyense kuona kuti tili ndi chikhulupiriro. Mwachitsanzo, tizilalikira za Ufumu komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Tipitirizenso kuchitira “onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10) Komanso popeza sitifuna kuti chilichonse chisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova, tiziyesetsa ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.’—Akol. 3:5, 8-10.

KUKHULUPIRIRA MULUNGU N’KOFUNIKA KWAMBIRI

13. Kodi ‘kukhulupirira Mulungu’ n’kofunika bwanji ndipo kwayerekezeredwa ndi chiyani?

13 Baibulo limati: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Baibulo limasonyeza kuti ‘kukhulupirira Mulungu’ ndi mbali ya “maziko” a chikhulupiriro chathu ndipo ndi kofunika kuti munthu akhale Mkhristu weniweni. (Aheb. 6:1) Akhristufe tiyenera “kuwonjezera pa chikhulupiriro” chathu makhalidwe ena ofunika, n’cholinga choti ‘Mulungu apitirize kutikonda.’—Werengani 2 Petulo 1:5-7; Yuda 20, 21.

14, 15. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi n’chofunika kwambiri kuposa chikhulupiriro?

14 Olemba Baibulo anatchula za chikhulupiriro kambirimbiri posonyeza kuti khalidweli ndi lofunika kwambiri. Palibe khalidwe limene linatchulidwa kwambiri kuposa chikhulupiriro. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuposa makhalidwe onse? Ayi.

15 Paulo anayerekezera chikhulupiriro ndi chikondi ndipo analemba kuti: “Ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse choti n’kusuntha nacho mapiri, koma ndilibe chikondi, sindili kanthu.” (1 Akor. 13:2) Komanso Yesu ananena kuti “lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo” ndi loti tizikonda Mulungu. (Mat. 22:35-40) Chikondi chimatithandiza kukhalanso ndi makhalidwe ena abwino monga chikhulupiriro. Baibulo limanena kuti chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse.” Choncho chikondi chimatithandiza kuti tizikhulupirira zonse zimene Mawu a Mulungu amanena.—1 Akor. 13:4, 7.

16, 17. (a) Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya chikhulupiriro ndi chikondi? (b) Kodi khalidwe lalikulu kwambiri pa awiriwa ndi liti, ndipo n’chifukwa chiyani?

16 Komabe makhalidwe awiri onsewa ndi ofunika. Choncho olemba Baibulo ambiri anatchula chikhulupiriro ndi chikondi mobwerezabwereza ndipo nthawi zina ankatchula makhalidwewa pamodzi. Mwachitsanzo, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘avale chodzitetezera pachifuwa chachikhulupiriro ndi chikondi.’ (1 Ates. 5:8) Petulo nayenso analemba kuti: “Ngakhale kuti simunamuonepo, [Yesu] mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Komanso Yakobo anauza Akhristu odzozedwa anzake kuti: “Mulungu anasankha anthu amene ali osauka m’dzikoli kuti akhale olemera m’chikhulupiriro ndi olandira cholowa cha ufumu umene anaulonjeza kwa omukonda, sanatero kodi?” (Yak. 2:5) Nayenso Yohane analemba kuti: “Lamulo [la Mulungu] ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu ndiponso tizikondana.”1 Yoh. 3:23.

17 Ngakhale kuti chikhulupiriro n’chofunika, chidzatha malonjezo a Mulungu akadzakwaniritsidwa. Koma tidzapitirizabe kukonda Mulungu ndi anzathu. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Komabe, tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.”—1 Akor. 13:13.

AKHRISTU AKUSONYEZA KUTI ALI NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA

18, 19. Kodi zinthu zili bwanji masiku ano, nanga ndani ayenera kutamandidwa chifukwa cha zimenezi?

18 Masiku ano anthu a Yehova oposa 8 miliyoni amasonyeza kuti amakhulupirira zoti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Izi zachititsa kuti akhale m’paradaiso wauzimu ndipo amayesetsa kusonyeza makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Zimenezi zikusonyeza kuti kukhala ndi chikhulupiriro komanso chikondi kumathandiza kwambiri.

19 Zonsezi zikutheka chifukwa choti Mulungu amatithandiza. Tingati izi ‘zatchukitsa Yehova, ndipo zidzakhala chizindikiro choti sichidzachotsedwa mpaka kalekale.’ (Yes. 55:13) ‘Tapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro’ ndipo iyi ndi mphatso yamtengo wapatali yomwe Mulungu watipatsa. (Aef. 2:8) Paradaiso wathu wauzimu apitirizabe mpaka padziko lonseli padzakhale anthu angwiro, olungama ndi osangalala n’kumatamanda dzina la Yehova mpaka kalekale. Choncho tiyeni tipitirize kusonyeza kuti timakhulupirira malonjezo a Yehova.