Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuphunzitsa Ena N’kofunika Bwanji?

Kodi Kuphunzitsa Ena N’kofunika Bwanji?

“Ndidzakupatsani malangizo abwino.”—MIY. 4:2.

NYIMBO: 93, 96

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza atsopano kuti achite zambiri?

NTCHITO yaikulu imene Yesu ankagwira inali yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Koma iye ankapezanso nthawi yothandiza ena kuti akhale aphunzitsi komanso abusa. (Mat. 10:5-7) Filipo ankalalikira mwakhama koma ankapezanso nthawi yophunzitsa ana ake aakazi kuti azilalikira mogwira mtima. (Mac. 21:8, 9) Nanga bwanji masiku ano? Kodi kuphunzitsa ena n’kofunika bwanji?

2 Masiku ano, pali anthu ambiri amene akufuna kuphunzira Baibulo. Komanso tiyenera kuthandiza ofalitsa osabatizidwa kuti azikonda kuphunzira Baibulo paokha. Tiyenera kuwathandizanso kuti azilalikira ndi kuphunzitsa mwaluso. Kuwonjezera pamenepo, abale amafunika kuwathandiza kuti ayenerere kukhala akulu ndi atumiki othandiza. Choncho tikamapereka “malangizo abwino,” tidzathandiza atsopano kuti achite zambiri m’gulu la Yehova.—Miy. 4:2.

MUZITHANDIZA ATSOPANO KUTI AZIPHUNZIRA MAWU A MULUNGU

3, 4. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti kuphunzira Malemba kungathandize munthu kuti azilalikira mogwira mtima? (b) Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani tisanayambe kulimbikitsa ena kuti aziphunzira Baibulo mwakhama?

3 Kodi kuphunzira Baibulo patokha n’kofunika bwanji? Yankho la funsoli tingalipeze m’mawu amene Paulo analembera Akhristu a ku Kolose. Iye analemba kuti: “Sitinaleke kukupemphererani. Takhala tikupemphanso kuti mukhale odziwa molondola chifuniro [cha Mulungu], ndiponso kuti mukhale ndi nzeru zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu. Tikupemphereranso kuti muziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti muzimukondweretsa pa chilichonse, pamene mukupitiriza kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino, ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.” (Akol. 1:9, 10) Kudziwa Mulungu molondola kukanathandiza Akhristuwo kuti ‘aziyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, n’kumamukondweretsa pa chilichonse.’ Izi zikanawathandiza kuti apitirize “kubala zipatso m’ntchito iliyonse yabwino” makamaka yolalikira uthenga wabwino. Kuti munthu azitumikira bwino Mulungu ayenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira Baibulo payekha. Choncho tizithandiza anthu amene tikuphunzira nawo kudziwa mfundo imeneyi.

4 Koma tisanayambe kuthandiza anthu kuti aziphunzira Baibulo paokha, ifeyo tiyenera kuzindikira ubwino wochita zimenezi. Mwachidule tingoti ifeyo tiyenera kumaphunzira Baibulo mwakhama. Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi munthu akatchula mfundo yosemphana ndi Malemba kapena akafunsa funso lovuta, ndimatha kuyankha pogwiritsa ntchito Baibulo? Nanga ndikawerenga mavuto amene Yesu, Paulo komanso anthu ena anakumana nawo, kodi ndimaona mmene zitsanzo zawo zingandithandizire potumikira Yehova?’ Tonsefe timafunika kuphunzira Mawu a Mulungu kuti tipeze malangizo komanso kuti tidziwe zambiri. Tikamafotokozera anthu ena mfundo zimene tapeza pophunzira, timawalimbikitsa kuti nawonso aziphunzira Baibulo mwakhama.

5. Kodi tingathandize bwanji munthu amene timaphunzira naye kuti aziphunzira Baibulo payekha?

5 Koma mwina mungafunse kuti, ‘Ndingathandize bwanji munthu amene ndimaphunzira naye kuti aziphunzira Baibulo nthawi zonse?’ Poyambira pabwino, n’kumusonyeza mmene angakonzekerere phunziro lake m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungamuuzenso kuti aziwerenga mfundo zakumapeto zomwe zikugwirizana ndi nkhaniyo komanso malemba osagwidwa mawu. Mungamuthandizenso kuti azikonzekera misonkhano n’cholinga choti akathe kuyankhapo. Mukhozanso kumulimbikitsa kuti aziwerenga magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati Laibulale ya Watchtower kapena Laibulale ya pa intaneti ya Watchtower ilipo m’chilankhulo chanu, mungamusonyeze mmene angaigwiritsire ntchito poyankha mafunso a m’Baibulo. Zonsezi zingamuthandize kuti ayambe kuona kuti kuphunzira Mawu a Mulungu payekha n’kosangalatsa.

6. (a) Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azikonda kwambiri kuphunzira Baibulo? (b) Kodi chingachitike n’chiyani ngati wophunzira wayamba kukonda Mawu a Mulungu?

6 Izi sizikutanthauza kuti tizikakamiza munthu amene timaphunzira naye kuti aziwerenga ndi kuphunzira Baibulo payekha. M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zimene gulu latulutsa pomuthandiza kuti azikonda kwambiri Baibulo. Pakapita nthawi wophunzira amene amafunadi kudziwa za Yehova angamve ngati Davide amene anati: “Kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.” (Sal. 73:28) Komanso mzimu wa Yehova ungamuthandize kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova.

MUZIPHUNZITSA ATSOPANO KULALIKIRA NDI KUPHUNZITSA

7. Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji atumwi ake kulalikira uthenga wabwino? (Onani chithunzi patsamba 25.)

7 M’chaputala 10 cha Mateyu timapezamo malangizo amene Yesu anapereka kwa atumwi ake 12. Popereka malangizowo, iye anatchula mwachindunji zoyenera kuchita. [1] Atumwiwo ankamvetsera mwatcheru pamene Yesu ankawaphunzitsa zimene angachite kuti azilalikira mogwira mtima. Kenako anapita limodzi mu utumiki ndipo ankaona mmene Yesu ankaphunzitsira mwaluso. Izi zinawathandiza kuti nawonso azilalikira bwino. (Mat 11:1) Nafenso tingathandize anthu amene timaphunzira nawo kuti aziphunzitsa anthu mogwira mtima. Tiyeni tsopano tikambirane njira ziwiri zimene tingatsatire powaphunzitsa.

8, 9. (a) Kodi Yesu ankalalikira bwanji? (b) Kodi tingathandize bwanji atsopano kuti azikambirana ndi anthu mwaubwenzi ngati Yesu?

8 Azikambirana ndi anthu. Yesu ankakonda kukambirana ndi anthu za Ufumu. Mwachitsanzo, atafika pachitsime cha Yakobo, pafupi ndi mzinda wa Sukari, anakambirana ndi mayi wina mfundo zambiri. (Yoh. 4:5-30) Iye anakambirananso ndi Mateyu Levi yemwe anali wokhometsa misonkho. Baibulo silifotokoza kwambiri zimene anakambirana koma chomwe tikudziwa n’chakuti Mateyuyo anavomera kukhala wophunzira wa Yesu. Ndiyeno atafika kunyumba kwawo, Mateyu ndi anzake anamvetsera kwa nthawi ndithu pamene Yesu ankawaphunzitsa.—Mat. 9:9; Luka 5:27-39.

9 Pa nthawi ina, Natanayeli ankakayikira anthu onse ochokera ku Nazareti. Komabe Yesu anacheza naye bwinobwino ndipo izi zinamuthandiza kuti asinthe maganizo. Iye anafuna kumva zambiri zimene Yesu ankaphunzitsa ngakhale kuti Yesuyo ankachokera ku Nazareti. (Yoh. 1:46-51) Nafenso tiyenera kuthandiza atsopano kuti aziyesetsa kukambirana ndi anthu mwaubwenzi komanso mokoma mtima. [2] Akamachita zimenezi adzasangalala kuona kuti anthu akumvetsera uthenga wawo.

10-12. (a) Kodi Yesu ankalimbikitsa bwanji anthu amene ankafuna kumva uthenga wabwino? (b) Kodi tingathandize bwanji atsopano kuti aziphunzitsa mwaluso mu utumiki?

10 Azilimbikitsa anthu amene asonyeza chidwi. Yesu anali ndi nthawi yochepa yoti alalikire padzikoli. Koma ankayesetsa kupeza nthawi yolimbikitsa anthu amene asonyeza chidwi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anaphunzitsa anthu ali m’boti. Kenako anathandiza Petulo kugwira nsomba zambirimbiri m’njira yodabwitsa. Ndiyeno anamuuza kuti: “Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.” Kodi zimene Yesu anachita komanso kulankhula zinathandiza bwanji anthu ena? Petulo ndi anzake atangofika kumtunda, “anasiya chilichonse ndi kumutsatira.”—Luka 5:1-11.

11 Mfarisi wina amene ankaweruza m’Khoti Lalikulu la Ayuda dzina lake Nikodemo, ankafuna kudziwa zimene Yesu ankaphunzitsa. Koma ankaopa zimene anthu ena anganene akamuona akulankhula ndi Yesuyo. Choncho anapita kwa Yesu usiku ndipo iye sanadandaule kuti wamusokoneza. (Yoh. 3:1, 2) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu ankachitazi? Iye ankapeza nthawi yoti alimbitse chikhulupiriro cha anthu ena. Nafenso tiziyesetsa kuchita maulendo obwereza komanso kuphunzitsa anthu.

12 Chinthu china chimene chingathandize atsopano kuti aziphunzitsa Baibulo mwaluso ndi kuyenda nawo mu utumiki. Tiyenera kuwaphunzitsa kuti azithandiza anthu amene asonyeza chidwi ngakhale chochepa. Tiyeneranso kuwatenga popita ku maulendo obwereza kapena ku maphunziro. Tikamatero tidzawathandizanso kuti azikhala oleza mtima mu utumiki komanso kuti asamagwe ulesi mwamsanga.—Agal. 5:22; onani bokosi lakuti, “ Musamafulumire Kugwa Ulesi.”

MUZIPHUNZITSA ATSOPANO KUTI AZITUMIKIRA AKHRISTU ANZAWO

13, 14. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene ankadzipereka kwambiri kuti athandize ena? (b) Kodi tingaphunzitse bwanji atsopano ndi ana kuti azikonda abale ndi alongo awo?

13 Yehova amafuna kuti anthu ake azikondana komanso kuthandizana. (Werengani 1 Petulo 1:22; Luka 22:24-27.) Mwana wa Mulungu ankatumikira anthu ndi mtima wonse ndipo mpaka anawafera. (Mat. 20:28) Komanso Dorika ankachita “ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.” (Mac. 9:36, 39) Panalinso mlongo wina wa ku Roma dzina lake Mariya, amene ‘ankachita ntchito zambiri’ pothandiza anthu a mumpingo wawo. (Aroma 16:6) Ndiye kodi tingaphunzitse bwanji atsopano kuti adziwe ubwino wothandiza abale ndi alongo awo?

Muziphunzitsa atsopano kuti azisonyeza chikondi kwa Akhristu anzawo (Onani ndime 13 ndi 14)

14 Akhristu angatenge atsopano pamene akupita kukaona odwala komanso okalamba. Nthawi zinanso makolo angatenge ana awo pa maulendo oterewa. Akulu angathandizane ndi Akhristu ena poonetsetsa kuti abale ndi alongo achikulire ali ndi chakudya komanso malo okhala abwino. Zonsezi zingathandize kuti ana komanso atsopano aphunzire kuchitira ena chifundo. Akakhala mu utumiki, mkulu amene wayenda ndi wachinyamata angadutse kunyumba kwa a Mboni a m’deralo n’kuwaona mwachidule. Izi zingathandize wachinyamatayo kudziwa kuti akulu amakonda anthu onse a mumpingo wawo.—Aroma 12:10.

15. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuthandiza abale mumpingo?

15 Popeza Yehova amagwiritsa ntchito amuna kuti aziphunzitsa mumpingo, ndi bwino kuti abale aziyesetsa kukhala ndi luso lophunzitsa. Ngati ndinu mkulu, mwina mungamvetsere pamene mtumiki wothandiza akuyeserera nkhani yake. Mutamuthandiza angayambe kuphunzitsa Mawu a Mulungu mogwira mtima.—Neh. 8:8. [3]

16, 17. (a) Kodi Paulo anathandiza bwanji Timoteyo? (b) Kodi akulu angaphunzitse bwanji abale kuti akhale abusa abwino?

16 M’gulu la Yehova mukufunika abale ambiri oti akhale abusa. Anthu amene adzakhale pa udindowu amafunika kuphunzitsidwa. Paulo anatchula mwachidule zoyenera kuchita pophunzitsa anthuwa pamene anauza Timoteyo kuti: “Iwe mwana wanga, pitiriza kupeza mphamvu m’kukoma mtima kwakukulu kumene kuli mwa Khristu Yesu. Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri zokhudza ine, zimenezo uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:1, 2) Timoteyo anaphunzira zambiri chifukwa ankayenda ndi Paulo yemwe anali wachikulire. Kenako nayenso ankagwiritsa ntchito njira zimene anaphunzirazo akamalalikira komanso pochita zinthu zina.—2 Tim. 3:10-12.

17 Sikuti Paulo ankangomusiya Timoteyo kuti aziphunzira yekha zinthu. M’malomwake ankayenda naye n’kumamuphunzitsa. (Mac. 16:1-5) Akulu angatsanzire Paulo pomatenga atumiki othandiza popita ku maulendo aubusa ngati akuona kuti n’zoyenera kutero. Akamachita zimenezi amawathandiza kuti akadzakhala oyang’anira azidzaphunzitsa bwino. Atumikiwo amaphunziranso makhalidwe monga chikhulupiriro, kuleza mtima komanso chikondi. Izi zidzawathandizanso kuti adzakhale abusa abwino a “gulu la nkhosa za Mulungu.”—1 Pet. 5:2.

UBWINO WOPHUNZITSA ENA

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzitsa ena panopa?

18 Panopa pakufunika anthu ambiri oti azithandiza m’gulu la Yehova choncho kuphunzitsa ena n’kofunika kwambiri. Monga tanenera, Yesu ndi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Yehova amafuna kuti anthu ake aziphunzitsidwa n’cholinga choti azichita bwino utumiki wawo. Iye watipatsa mwayi wophunzitsa atsopano kuti azichita zambiri mumpingo. Masiku ano, zinthu m’dzikoli zikuipiraipira komanso pali anthu ambiri amene akufunika kumva uthenga wabwino. Choncho ntchito yophunzitsayi ndi yofunika kwambiri ndipo tiyenera kuigwira panopa.

19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tingakwanitse bwinobwino kuphunzitsa ena?

19 Pamafunika khama komanso nthawi kuti tiphunzitse ena. Koma Yehova ndi Yesu adzatithandiza kuti tigwire bwino ntchitoyi. Tidzasangalala kwambiri kuona anthu amene tawaphunzitsa ‘akugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu.’ (1 Tim. 4:10) Pamene tikuphunzitsa ena, nafenso tiyenera kuyesetsa kuchita zambiri potumikira Yehova.

^ [1] (ndime 7) Mfundo zina zimene Yesu anawauza ndi izi: (1) Azilalikira uthenga woyenera. (2) Azikhutira ndi zimene Mulungu wawapatsa. (3) Azipewa kukangana ndi anthu. (4) Azidalira Mulungu akamatsutsidwa. (5) Asamaope anthu.

^ [2] (ndime 9) M’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, tsamba 62-64, muli mfundo zothandiza kuti tizikambirana ndi anthu mwaubwenzi.

^ [3] (ndime 15) Buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu tsamba 52 mpaka 61 limafotokoza makhalidwe ofunika kuti munthu azitha kulankhula bwino pagulu.