Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani anthu amene ankatsutsa Yesu ankaona kuti kusamba m’manja ndi nkhani yaikulu?

Yesu ndi ophunzira ake ankatsutsidwa pa nkhani imeneyi komanso nkhani zina. Chilamulo cha Mose chinkafotokoza zinthu zimene zingachititse munthu kukhala wodetsedwa. Zinthu zake zinali monga matenda akukha, matenda akhate komanso kukhudza mtembo wa munthu kapena wa nyama. Chilamulocho chinkafotokozanso zimene munthu angachite kuti ayeretsedwe. Ankafunika kupereka nsembe, kusamba komanso kuwaza madzi kapena magazi.—Levitiko chaputala 11-15; Numeri chaputala 19.

Koma Afarisi ankakokomeza malamulo okhudza nkhani imeneyi. Buku lina linanena kuti iwo anakhazikitsa malamulo ambirimbiri otchula zinthu zimene zingachititse munthu kukhala wodetsedwa komanso kudetsa anzake. Ankanenanso za zipangizo zimene zingadetse anthu komanso miyambo imene ayenera kuchita kuti ayeretsedwe.

Pa nthawi ina anthu amene ankadana ndi Yesu anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira anu satsatira miyambo ya makolo, koma amadya chakudya ndi manja oipitsidwa?” (Maliko 7:5) Apa sikuti ankangonena zosamba m’manja chifukwa cha ukhondo. Koma ankanena za mwambo umene ankachita pothirirana madzi asanayambe kudya. Buku lija linanenanso kuti iwo anakhazikitsa malamulo onena za madzi oyenera, chotungira choyenera, munthu woyenera kukuthirira madziwo komanso kuti munthu azisamba m’manja kufika muti.

Yesu sanavutike poyankha anthuwo. Iye anangowauza kuti: “Yesaya analosera moyenera za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenera kuti, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine [Yehova]. Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’ Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumirira mwambo wa anthu.”—Maliko 7:6-8.