Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingatani Kuti Tizichita Zambiri M’gulu la Yehova?

Kodi Tingatani Kuti Tizichita Zambiri M’gulu la Yehova?

“Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa.”—1 TIM. 4:13.

NYIMBO: 45, 70

1, 2. (a) Kodi lemba la Yesaya 60:22 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano? (b) Kodi pakufunika anthu oti achite zinthu ziti m’gulu la Yehova?

BAIBULO linalosera kuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.” (Yes. 60:22) Mawu amenewa akukwaniritsidwa masiku otsiriza ano. Tikutero chifukwa chakuti m’chaka chautumiki cha 2015, padziko lonse panali ofalitsa okwana 8,220,105. Koma munthu aliyense ayenera kuganizira mawu omaliza a m’vesili. Paja Atate wathu wakumwamba ananena kuti: “Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.” Panopa zili ngati tili m’galimoto yomwe yayamba kuthamanga kwambiri chifukwa ntchito yolalikira ikuchitika mwamsanga kwabasi. Kodi inuyo panokha mukuchita zotani? Kodi mukuchita zonse zimene mungathe pa ntchito yolalikira? Abale ndi alongo ambiri akuyamba upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Komanso ambiri akusamukira m’madera amene kukufunika ofalitsa ambiri.

2 Izi zili apo, pakufunikabe anthu ambiri oti athandize m’gulu la Yehova. Tikutero chifukwa chakuti chaka chilichonse, mipingo pafupifupi 2,000 ikukhazikitsidwa. Izi zikutanthauza kuti ngati mumpingo uliwonse mutati muzikhala akulu 5, ndiye kuti chaka chilichonse pangafunike atumiki othandiza 10,000 oti akhale akulu. Ndiye kutinso pakufunika abale masauzande ambiri oti akhale atumiki othandiza. Koma kaya ndinu m’bale kapena mlongo, pali zinthu zambiri zimene mungachite “mu ntchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.

KODI MUNTHU ANGATANI KUTI AYENERERE UDINDO KOMANSO AZICHITA ZAMBIRI?

3, 4. Kodi inuyo mungatani kuti muzichita zambiri m’gulu la Yehova?

3 Werengani 1 Timoteyo 3:1. Mawu akuti ‘kuyesetsa’ omwe ali palembali, amatanthauza kunyanyamphira kuti ufikire chinthu chimene chili patali. Paulo anagwiritsa ntchito mawuwa pofuna kusonyeza kuti pamafunika khama kuti munthu ayenerere udindo komanso kuti azichita zambiri m’gulu la Yehova. Tiyerekeze kuti m’bale wina akuganizira zimene angachite mumpingo wawo. Iye si mtumiki wothandiza ndipo akuzindikira kuti choyamba ayenera kuyesetsa kuti akhale ndi makhalidwe achikhristu. Kenako akuyesetsa kuti akhale mtumiki wothandiza. Patapita nthawi akuyesetsanso kuti akhale mkulu. Nthawi zonse amayesetsa kukwaniritsa zofunika kuti akhale pa udindo umene akufunawo.

4 N’chimodzimodzinso ndi abale komanso alongo amene akufuna kukhala apainiya, kukatumikira pa Beteli komanso kugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Iwo ayenera kuyesetsa kuti akwaniritse zolinga zawozi. M’nkhaniyi tiona kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa tonsefe kuti tiziyesetsa kuchita zambiri m’gulu la Yehova.

YESETSANI KUTI MUZICHITA ZAMBIRI

5. Kodi achinyamata angagwiritse ntchito bwanji mphamvu zawo potumikira Yehova?

5 Achinyamata ali ndi mphamvu ndipo angathe kuchita zambiri potumikira Yehova. (Werengani Miyambo 20:29.) Achinyamata ena amene akutumikira pa Beteli amagwira ntchito yosindikiza ndi kukonza Mabaibulo komanso mabuku athu. Pamene enanso amathandiza pa ntchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu. Pakachitika ngozi zadzidzidzi, achinyamata ena amathandizana ndi abale ndi alongo aluso pogwira ntchito yothandiza anthu amene akuvutika. Ndiponso apainiya ambiri achinyamata amadzipereka kuphunzira zilankhulo zina n’kumalalikira anthu a zilankhulozo.

6-8. (a) Kodi m’bale wina anatani kuti azichita zambiri potumikira Yehova ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi munthu ‘angalawe bwanji n’kuona kuti Yehova ndi wabwino’?

6 Inunso mukudziwa kuti kutumikira Mulungu ndi mtima wathu wonse n’kofunika. Koma kodi mungatani ngati nthawi zina mumamva ngati mmene ankamvera m’bale wina dzina lake Aaron? Ngakhale kuti anabadwira m’banja la Mboni, ananena kuti: “Ndinkaona kuti kusonkhana komanso kulalikira n’kotopetsa kwambiri.” Iye ankafuna kuti azisangalala potumikira Mulungu koma ankangoona kuti sizikutheka. Kodi Aaron anatani?

7 Iye anayamba kupemphera pafupipafupi, kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kukonzekera misonkhano komanso kuyankha akafika pa misonkhanopo. Aaron atayamba kukonda kwambiri Yehova, anayambanso kuchita zambiri pomutumikira. Kungoyambira nthawi imeneyo, iye wakhala akuchita upainiya, kuthandiza pakagwa ngozi zadzidzidzi komanso kulalikira kudziko lina. Panopa, Aaron akutumikira pa Beteli ndipo ndi mkulu. Kodi amamva bwanji akaganizira zimene wachita? Aaron anati: “‘Ndalawa ndipo ndaona kuti Yehova ndi wabwino.’ Iye wandidalitsa kwambiri moti ndikuona kuti ndiyenera kumuthokoza. N’chifukwa chake ndikuyesetsa kuchita zambiri pomutumikira ndipo akundidalitsabe.”

8 Wamasalimo anaimba kuti: “Ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.” (Werengani Salimo 34:8-10.) Yehova sagwiritsa mwala anthu amene amamutumikira mwakhama. Tikamayesetsa kuchita zonse zimene tingathe, timakhala ngati ‘tikulawa n’kuona kuti iye ndi wabwino.’ Kunena zoona, tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse timasangalala kwambiri.

MUSAFOOKE KAPENA KUTAYA MTIMA

9, 10. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ‘oleza mtima’?

9 Pa nthawi imene mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zanu, muzikhala ‘oleza mtima.’ (Mika 7:7) Tikutero chifukwa nthawi zina mungafunike kuyembekezera kaye kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino kapena kuti mukhale pa udindo winawake. Komabe muyenera kukumbukira kuti nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake. Iye analonjeza Abulahamu kuti adzakhala ndi mwana, komabe Abulahamu anayenera kuyembekezera. (Aheb. 6:12-15) Ngakhale kuti panadutsa zaka zambiri, Abulahamu sanataye mtima ndipo Yehova anakwaniritsadi lonjezo lake pamene Abulahamuyo anabereka Isaki.—Gen. 15:3, 4; 21:5.

10 Kuyembekezera n’kovuta. (Miy. 13:12) Ndipo munthu akamangoganizira zokhumudwitsa, akhoza kutaya mtima. Choncho ndi bwino kuti pa nthawi imene mukuyembekezerayo, muziyesetsa kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene mungachite.

11. Kodi ndi makhalidwe ati amene tiyenera kuyesetsa kukhala nawo, ndipo ndi ofunika bwanji?

11 Yesetsani kukhala ndi makhalidwe abwino. Tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kusinkhasinkha, timakhala anzeru, oganiza bwino komanso ozindikira. Timadziwanso zambiri ndipo timasankha zochita mwanzeru. Makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri kwa oyang’anira mumpingo. (Miy. 1:1-4; Tito 1:7-9) Komanso tikamawerenga mabuku athu, timadziwa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita pa nkhani zokhudza zosangalatsa, zovala, kudzikongoletsa, kugwiritsa ntchito ndalama komanso kukhala bwino ndi anthu. Tikamagwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’Baibulo, tingathe kusankha zinthu zimene Yehova amasangalala nazo.

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odalirika?

12 Muzisonyeza kuti ndinu odalirika. Kaya ndife abale kapena alongo tiziyesetsa kugwira bwino ntchito iliyonse imene tapatsidwa. Popeza Nehemiya anali bwanamkubwa, anayenera kusankha anthu oti akhale m’maudindo osiyanasiyana. Ndiye kodi anasankha ndani? Anasankha anthu oopa Mulungu, okhulupirika komanso odalirika. (Neh. 7:2; 13:12, 13) Masiku anonso, “chofunika kwa woyang’anira ndicho kukhala wokhulupirika.” (1 Akor. 4:2) Tizikumbukiranso kuti munthu akamayesetsa kuchita zabwino, sizibisika.—Werengani 1 Timoteyo 5:25.

13. Kodi tingatsanzire bwanji Yosefe, anthu ena akatichitira zinthu zopanda chilungamo?

13 Muzilola kuti Yehova akuthandizeni kukhala munthu wabwino. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati anthu ena akuchitirani zinthu zopanda chilungamo? Mwina mungaganize zoikoka nkhaniyo n’cholinga choti chilungamo chioneke. Koma nthawi zambiri zimenezi zimangowonjezera mavuto. Abale ake a Yosefe anamuchitira zinthu zopanda chilungamo koma iye sanawasungire chakukhosi. Patapita nthawi, Yosefe ananamiziridwa mlandu ndipo anaikidwa m’ndende. Komabe iye analola kuti Yehova azimutsogolera pa nthawi yovutayi. Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Mawu a Yehova anamuyenga” kapena kuti anamuthandiza kukhala munthu wabwino. (Sal. 105:19) Mayesero akewo atatha, Yosefe anali woyenera kupatsidwa udindo wapadera. (Gen. 41:37-44; 45:4-8) Nanunso mukakumana ndi mavuto, muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru, muzilankhula komanso kuchita zinthu mofatsa ndiponso muzidalira Yehova kuti akupatseni mphamvu. Mukamachita zimenezi, Yehova adzakuthandizani.—Werengani 1 Petulo 5:10.

MUZIYESETSA KUCHITA ZAMBIRI MU UTUMIKI

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani ‘nthawi zonse tiyenera kusamala’ ndi zimene timaphunzitsa? (b) Kodi inuyo mungatani kuti muzitha kulalikira anthu onse? (Onani chithunzi patsamba 20 komanso bokosi lakuti, “ Kodi Mungayese Njira Zina Zolalikirira?”)

14 Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa. Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:13, 16) Pa nthawiyi Timoteyo ankadziwa kale kulalikira. Komabe kuti azilalikira mogwira mtima, anafunika kuti ‘nthawi zonse azisamala’ ndi zimene ankaphunzitsa. Sankafunika kuganiza kuti anthu azimvetserabe ngakhale atangomagwiritsa ntchito njira zimene anazolowera. Kuti apitirize kuwafika anthu pamtima, anayenera kukhala wokonzeka kusintha kuti ulaliki wake ugwirizane ndi munthu amene akumulalikira. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi.

15 Ofalitsa ena akamalalikira kunyumba ndi nyumba, sapeza anthu pakhomo. M’madera ena zimavuta kufika m’nyumba zina kapena kulowa m’mipanda. Ngati zoterezi zimachitikanso m’gawo lanu, mungachite bwino kupeza njira zina zolalikirira.

16. Kodi tingatani kuti tizilalikira m’malo opezeka anthu ambiri?

16 Kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri kungathandize kuti anthu osiyanasiyana amve uthenga wabwino. Abale ndi alongo amene ayesapo njirayi aona kuti ndi yothandizadi. Iwo amalalikira pamalo okwerera sitima ndi mabasi, m’misika, m’mapaki komanso malo ena. Mungathe kuyamba kulankhula ndi munthu potchula nkhani yomwe yamveka pa wailesi kapena pa TV, poyamikira ana ake kapena pomufunsa funso lokhudza ntchito yake. Kenako mungatchule mfundo ya m’Malemba n’kumufunsa maganizo ake. Zimene munthuyo angayankhe zingathandize kuti mukambirane mfundo zambiri za m’Baibulo.

17, 18. (a) Kodi mungatani kuti musamaope kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri? (b) Kodi n’chiyani chingakulimbikitseni kutamanda Yehova ngati mmene Davide anachitira?

17 Ngati mumaona kuti kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri n’kovuta, musataye mtima. Mpainiya wina wa mumzinda wa New York, dzina lake Eddie, ankavutikanso kuchita zimenezi. Koma kenako mantha ake anatha. Pofotokoza zimene zinamuthandiza, Eddie anati: “Tikamachita kulambira kwa Pabanja, ine ndi mkazi wanga timayerekezera kuti tili mu utumiki ndipo anthu akutitsutsa kapena akunena maganizo awo pa nkhani zina. Timafunsanso abale ndi alongo ena kuti atipatse nzeru.” Panopa m’baleyu amakonda kwambiri kulalikira anthu m’njira imeneyi.

18 Mukamayesetsa kuwonjezera luso lanu polalikira, anthu amaona. (Werengani 1 Timoteyo 4:15.) Komanso khama lanu likhoza kuthandiza kuti anthu ofatsa ayambe kulambira Yehova. Paja Davide anaimba kuti: “Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse. Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza. Ndidzadzitamandira mwa Yehova. Ofatsa adzamva ndi kukondwera.”—Sal. 34:1, 2.

MUKAMAYESETSA KUCHITA ZAMBIRI MUMALEMEKEZA MULUNGU

19. Kodi n’chiyani chingathandize kuti mtumiki wa Yehova azisangalala ngakhale patakhala mavuto?

19 Davide anaimbanso kuti: “Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova, ndipo okhulupirika anu adzakutamandani. Iwo adzanena za ulemerero wa ufumu wanu. Ndi kulankhula za mphamvu zanu, kuti ana a anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu ndi kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.” (Sal. 145:10-12) Mawu amenewa akufotokoza bwino mmene abale ndi alongo ambiri amamvera. Koma bwanji ngati simutha kuchita zambiri potumikira Yehova chifukwa cha matenda, ukalamba kapena mavuto ena? Muzikumbukira kuti mukamalalikira anthu ena, monga amene akukusamalirani, ndiye kuti mukuchita utumiki wopatulika umene umalemekeza Mulungu. Ngati muli m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chanu, muyenera kuti nthawi zina mumapeza mpata wolalikira ndipo zimenezi zimasangalatsa Yehova. (Miy. 27:11) N’chimodzimodzinso kwa anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti ali m’banja limene wina si Mboni. (1 Pet. 3:1-4) Zimenezi zikusonyeza kuti aliyense angathe kutamanda Yehova komanso kuchita zambiri pomutumikira ngakhale patakhala mavuto.

20, 21. Ngati mumachita zambiri m’gulu la Yehova, kodi zotsatira zake zingakhale zotani?

20 Yehova adzakudalitsani mukamapitiriza kuchita zambiri m’gulu lake. Mwina mungafunikire kusintha zina ndi zina kuti muzikhala ndi nthawi yokwanira yolalikira kwa anthu amene akufuna kumva choonadi. Mukamachita zimenezi modzipereka mudzathandizanso Akhristu anzanu. Mukakhala ndi mtima wodzichepetsa, abale ndi alongo adzayamba kukukondani, kukuyamikirani komanso kukuthandizani.

21 Kaya tatumikira Yehova kwa zaka zambiri kapena kwa miyezi yochepa, tonsefe tingathe kuchita zambiri. Koma kodi Akhristu angathandize bwanji atsopano kuti nawonso azichita zambiri m’gulu la Yehova? Tidzakambirana nkhani imeneyi m’mutu wotsatira.