Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 50

“Iwe Udzakhala Ndi Ine M’Paradaiso”

“Iwe Udzakhala Ndi Ine M’Paradaiso”

“Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”​—LUKA 23:43.

NYIMBO NA. 145 Mulungu Watilonjeza Paradaiso

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Atatsala pang’ono kufa, kodi Yesu anauza chiyani wachifwamba yemwe anali pambali pake? (Luka 23:39-43)

 YESU ndi achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi ankamva ululu woopsa pomwe moyo wawo unkachoka pang’onopang’ono. (Luka 23:32, 33) Achifwambawa ankamunyoza Yesu, choncho n’zodziwikiratu kuti sanali ophunzira ake. (Mat. 27:44; Maliko 15:32) Koma mmodzi wa iwo anasintha maganizo. Iye anati: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Yesu anayankha kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Werengani Luka 23:39-43.) Palibe umboni wosonyeza kuti wachifwambayu anavomera zokhudza uthenga wa “Ufumu wa kumwamba” womwe Yesu ankalalikira. Ndipo iye sanauze munthuyu kuti adzalowa mu Ufumuwu kumwamba. (Mat. 4:17) Yesu ankanena za Paradaiso wapadzikoli m’tsogolo. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kodi tinganene chiyani zokhudza wachifwamba yemwe analankhula ndi Yesu komanso zomwe ankadziwa? (Onani ndime 2-3)

2. N’chiyani chikusonyeza kuti wachifwamba amene analapayu anali Myuda?

2 N’kutheka kuti wachifwamba amene analapayu anali Myuda. Iye anauza wachifwamba mnzake kuti: “Kodi iwe suopa Mulungu eti, poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu?” (Luka 23:40) Ayuda ankalambira Mulungu mmodzi pomwe anthu a mitundu ina ankalambira milungu yambiri. (Eks. 20:2, 3; 1 Akor. 8:5, 6) Zikanakhala kuti wachifwambayu sanali Myuda, funso limene akanafunsa likanakhala lakuti, “Kodi iwe suopa milungu eti?” Kuwonjezera pamenepo Yesu sanatumidwe kwa anthu a mitundu ina koma “kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” (Mat. 15:24) Mulungu anali atadziwitsa Aisiraeli kuti adzaukitsa anthu amene anamwalira. Wachifwambayu ayenera kuti ankadziwa zimenezi, ndipo mawu ake akusonyeza kuti ankayembekezera kuti Yehova adzaukitsa Yesu kuti alamulire mu Ufumu wa Mulungu. N’zoonekeratu kuti munthuyu nayenso ankakhulupirira kuti Mulungu adzamuukitsa.

3. Kodi n’kutheka kuti wachifwamba yemwe analapayu ankaganizira za chiyani Yesu atatchula za Paradaiso? Fotokozani. (Genesis 2:15)

3 Monga Myuda, wachifwamba amene analapayu ayenera kuti ankadziwa zokhudza Adamu ndi Hava komanso Paradaiso yemwe Yehova anawaikamo. Choncho iye ayenera kuti ankakhulupirira kuti Paradaiso yemwe Yesu anatchula adzakhala munda wokongola padziko lapansi pompano.​—Werengani Genesis 2:15.

4. Kodi mawu omwe Yesu anauza wachifwamba ayenera kutichititsa kuganizira chiyani?

4 Mawu amene Yesu anauza wachifwambayu ayenera kutichititsa kuganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Ndipotu tingaphunzirepo kanthu zokhudza Paradaiso pa ulamuliro wa Mfumu Solomo womwe unali wamtendere. Tingayembekezere Yesu yemwe ndi woposa Solomo kuti adzagwira ntchito ndi olamulira anzake kukonza dzikoli kuti likhale malo abwino kwambiri. (Mat. 12:42) N’zomveka kuti a “nkhosa zina” angakhale ofunitsitsa kudziwa zomwe akuyenera kuchita kuti adzakhale ndi moyo mpaka kalekale m’Paradaiso.​—Yoh. 10:16.

KODI MOYO UDZAKHALA WOTANI M’PARADAISO?

5. Kodi mukuyembekezera kuti moyo udzakhala wotani m’Paradaiso?

5 Kodi m’maganizo mwanu mumabwera zotani mukamaganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso? N’kutheka kuti mumaganizira za malo okongola ofanana ndi munda wa Edeni. (Gen. 2:7-9) Mwina mumakumbukira ulosi wa Mika wokhudza anthu a Mulungu wonena kuti “aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu.” (Mika 4:3, 4) Mwina mumakumbukiranso zimene Baibulo limanena zakuti kudzakhala zakudya zambiri. (Sal. 72:16; Yes. 65:21, 22) Choncho mungamadziyerekezere muli m’munda wokongola, patebulo pali zakudya zambiri zokoma. Mungamayerekezerenso mukumva kafungo kabwino ka zomera ndi maluwa ndiponso kuseka kwa achibale ndi anzanu kuphatikizaponso oukitsidwa akucheza mosangalala limodzi. Zonsezitu si maloto chabe. Mosakayikira zidzachitikadi padzikoli. Komabe m’Paradaiso tizidzagwiranso ntchito yosangalatsa.

Tidzagwira ntchito yofunika yophunzitsa oukitsidwa (Onani ndime 6)

6. Kodi tidzagwira ntchito yotani m’Paradaiso? (Onani chithunzi.)

6 Yehova anatilenga kuti tizisangalala tikamagwira ntchito. (Mlal. 2:24) Tidzatanganidwa ndi kugwira ntchito makamaka pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Anthu omwe adzapulumuke chisautso chachikulu komanso omwe adzaukitsidwe adzafunika zovala, zakudya ndiponso malo okhala. Kuti zofunika zimenezi zipezeke padzakhala ntchito yambiri yosangalatsa. Mofanana ndi Adamu ndi Hava omwe ankafunika kulima munda wawo, tidzakhala ndi mwayi wokonza dzikoli kuti likhale Paradaiso. Taganiziraninso mmene zidzakhalire zosangalatsa kuphunzitsa anthu mamiliyoni amene adzaukitsidwe omwe adzakhale akudziwa zochepa zokhudza Yehova ndi zolinga zake. Zidzakhalanso zosangalatsa kuthandiza anthu okhulupirika omwe anakhalako Yesu asanabwere padzikoli kuti adziwe zambiri.

7. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Tingakhale otsimikiza kuti moyo wa m’Paradaiso udzakhala wamtendere, sitizidzasowa chilichonse komanso zinthu zizidzachitika mwadongosolo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova watipatsa kale chithunzi cha mmene moyo udzakhalire mu Ufumu wa Mwana wake. Timaona zimenezi tikaganizira nkhani ya ulamuliro wa Mfumu Solomo.

ULAMULIRO WA MFUMU SOLOMO UMASONYEZA MMENE ZIDZAKHALIRE M’PARADAISO

8. Kodi mawu opezeka pa Salimo 37:10, 11, 29, omwe Mfumu Davide inalemba anakwaniritsidwa bwanji? (Onani nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” yomwe ili m’magaziniyi.)

8 Mfumu Davide inauziridwa kulemba mmene moyo udzakhalire, mfumu yanzeru ndi yokhulupirika ikadzayamba kulamulira. (Werengani Salimo 37:10, 11, 29.) Nthawi zambiri timawerengera ena Salimo 37:11 tikamanena za Paradaiso amene akubwerayo. Tili ndi zifukwa zabwino zochitira zimenezi chifukwa Yesu anatchulanso mawu a palembali pa ulaliki wake wa paphiri, posonyeza kuti zimenezi zidzakwaniritsidwanso m’tsogolo. (Mat. 5:5) Koma mawu a Davidewa anasonyezanso mmene moyo udzakhalire pa nthawi ya ufumu wa Solomo. Pa nthawi imene Solomo ankalamulira ku Isiraeli, anthu a Mulungu ankasangalala ndi mtendere ndipo sankasowa chilichonse m’dziko “loyenda mkaka ndi uchi.” Mulungu anati: “Mukapitiriza kutsatira malangizo anga . . . , ndidzakupatsani mtendere m’dzikolo, moti mudzagona pansi popanda wokuopsani.” (Lev. 20:24; 26:3, 6) Malonjezo amenewo anakwaniritsidwa mu ulamuliro wa Solomo. (1 Mbiri 22:9; 29:26-28) Ndipo Yehova analonjeza kuti anthu oipa “sadzakhalakonso.” (Sal. 37:10) Choncho mawu opezeka pa Salimo 37:10, 11, 29, anakwaniritsidwapo m’mbuyomo ndipo adzakwaniritsidwanso m’tsogolo.

9. Kodi mfumukazi ya ku Seba inanena zotani zokhudza ulamuliro wa Mfumu Solomo?

9 Mfumukazi ya ku Seba inamva kuti anthu a ku Aisiraeli ankasangalala ndi mtendere komanso moyo wabwino mu ulamuliro wa Mfumu Solomo. Mfumukaziyo inayenda ulendo wautali kuchoka kwawo kupita ku Yerusalemu kuti ikadzionere yokha. (1 Maf. 10:1) Itayendera ufumu wa Solomo, mfumukaziyi inati: “Ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe. . . . Odala anthu anu, odala atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.” (1 Maf. 10:6-8) Komatu mmene zinthu zinalili mu ufumu wa Solomo, zinkangosonyeza zimene Yehova adzachitire anthu mu ulamuliro wa Mwana wake Yesu.

10. Kodi Yesu amaposa Solomo m’njira ziti?

10 Yesu amaposa Solomo m’zinthu zonse. Solomo sanali wangwiro ndipo ankalakwitsa zinthu, zimene zinachititsa kuti anthu a Mulungu akumane ndi mavuto. Koma Yesu ndi Wolamulira wangwiro yemwe salakwitsa zinthu. (Luka 1:32; Aheb. 4:14, 15) Yesu sanagonje pa mayesero ovuta kwambiri amene Satana anamubweretsera. Khristu anasonyeza kuti sangachimwe kapena kuchita chilichonse chimene chingavulaze nzika zake zokhulupirika. Ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala ndi Mfumu ngati imeneyi.

11. Kodi ndi ndani amene adzathandize Yesu kulamulira?

11 Yesu adzagwira ntchito limodzi ndi olamulira anzake okwana 144,000 kuthandiza anthu komanso kukwaniritsa zolinga za Yehova padzikoli. (Chiv. 14:1-3) Olamulira anzakewa adzakhala achifundo chifukwa nawonso anakumanapo ndi mavuto pamene anali padzikoli. Kodi iwo adzakhala ndi udindo wotani?

KODI ODZOZEDWA ADZAKHALA NDI UDINDO WOTANI?

12. Kodi Yehova adzapatsa a 144,000 ntchito yotani?

12 Yesu ndi olamulira anzake adzakhala ndi ntchito yaikulu kuposa imene Solomo anali nayo. Mfumu ya Chiisiraeliyi inkafunika kusamalira anthu mamiliyoni omwe anali m’dziko limodzi lokha. Koma olamulira a Ufumu wa Mulungu adzathandiza anthu mabiliyoni padziko lonse lapansi. Pamenepatu Yehova anapereka mwayi wapadera kwambiri kwa a 144,000.

13. Kodi udindo wa olamulira anzake a Yesu udzaphatikizapo zinthu ziti?

13 Mofanana ndi Yesu, a 144,000 adzatumikira monga mafumu ndi ansembe. (Chiv. 5:10) Potsatira Chilamulo cha Mose, udindo waukulu wa ansembe unali woonetsetsa kuti anthu ali ndi thanzi labwino komanso ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Popeza Chilamulo chinali “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera,” n’zomveka kunena kuti olamulira anzake a Yesu adzathandiza anthu kukhala ndi thanzi labwino komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Aheb. 10:1) Tikungofunika kuyembekezera kuti tidzaone mmene mafumu ndi ansembewa adzathandizire nzika za Ufumu zomwe zidzakhale padziko lapansi. Mulimonse mmene Yehova adzakonzere zinthu, ndife otsimikiza kuti m’Paradaiso akubwerayo, anthu omwe adzakhale padzikoli adzapatsidwa malangizo omwe adzafunikire.​—Chiv. 21:3, 4.

KODI A “NKHOSA ZINA” AYENERA KUCHITA CHIYANI KUTI ADZAKHALE M’PARADAISO?

14. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa a “nkhosa zina” ndi abale ake a Khristu?

14 Yesu anatchula anthu omwe adzalamulire naye limodzi kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Anakambanso za gulu lina lomwe analitchula kuti “nkhosa zina.” Magulu awiri onsewa amapanga gulu limodzi la nkhosa zogwirizana. (Yoh. 10:16) Panopa magulu awiriwa amagwira ntchito limodzi ndipo izi zidzapitirizabe mpaka pamene dzikoli lidzakhale Paradaiso. Pa nthawiyo a “kagulu ka nkhosa” adzakhala ali kumwamba pamene a “nkhosa zina” adzakhala ndi chiyembekezo chodzasangalala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale. Koma pali zimene a “nkhosa zina” ayenera kuchita panopa kuti adzakhale m’Paradaiso.

Ngakhale panopa tingasonyeze kuti tikukonzekera kudzakhala m’Paradaiso akubwerayo (Onani ndime 15) b

15. (a) Kodi a “nkhosa zina” amagwira ntchito bwanji ndi abale ake a Khristu? (b) Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha m’bale yemwe wapita kukagula zinthu? (Onani chithunzi.)

15 Wachifwamba yemwe analapa uja anafa asanakhale ndi mwayi wokwanira wosonyeza kuti ankayamikira Khristu. Mosiyana ndi zimenezi, panopa ifeyo a “nkhosa zina” tili ndi mwayi waukulu wosonyeza kuti tili kumbali ya Yesu. Mwachitsanzo, timasonyeza kuti timamukonda pa zimene timachitira abale ake odzozedwa. Yesu ananena kuti adzaweruza anthu potengera mmene anachitira ndi abale akewa. (Mat. 25:31-40) Tingathandize abale ake a Khristu tikamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:18-20) N’chifukwa chake timafunitsitsa kugwiritsira ntchito bwino zinthu zothandiza pophunzira Baibulo monga buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Ngati simunayambe kuphunzira Baibulo ndi winawake, bwanji osakhala ndi cholinga choti mupemphe anthu ambiri kuti muziphunzira nawo Baibulo?

16. Kodi tikufunika kuchita chiyani kuti tidzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu?

16 Sitikuyenera kuyembekezera mpaka tidzalowe m’Paradaiso kuti tidzayambe kukhala mtundu wa anthu amene Yehova akufuna kuti adzakhalemo. Panopa tiziyesetsa kukhala oona mtima mu zolankhula komanso zochita ndiponso tizikhala ndi makhalidwe abwino. Tiyeneranso kukhala okhulupirika kwa Yehova, mwamuna kapena mkazi wathu komanso Akhristu anzathu. Tikamayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu panopa pomwe tili m’dziko loipali, zidzakhalanso zosavuta kuzitsatira tili m’Paradaiso. Tingayambiretu panopa kukulitsa luso komanso makhalidwe omwe adzafunike pa nthawiyo. Onani nkhani yakuti, “Kodi Ndinu Okonzeka ‘Kudzalandira Dziko Lapansi’?” yomwe ili m’magaziniyi.

17. Kodi tiyenera kumangokhalira kudziimba mlandu chifukwa cha machimo omwe tinachita m’mbuyomu? Fotokozani.

17 Sitikuyenera kumangodziimba mlandu chifukwa cha machimo akuluakulu omwe tinachita m’mbuyomo. N’zoona kuti sitiyenera kumaona nsembe ya dipo ngati chifukwa ‘chomachitira machimo mwadala.’ (Aheb. 10:26-31) Koma tingakhale otsimikiza kuti ngati talapa mochokera pansi pamtima ndipo talandira thandizo lochokera kwa Yehova komanso tasintha khalidwe lathu, iye angatikhululukire ndi mtima wonse. (Yes. 55:7; Mac. 3:19) Kumbukirani mawu amene Yesu anauza Afarisi kuti: “Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mat. 9:13) Choncho nsembe ya dipo ndi yamphamvu kwambiri moti ingaphimbe machimo athu onse.

MUNGATHE KUDZAKHALA M’PARADAISO MPAKA KALEKALE

18. Kodi mungafune kudzakambirana zotani ndi munthu yemwe anapachikidwa ndi Yesu?

18 Kodi mumadziyerekezera muli m’Paradaiso mukucheza ndi wachifwamba yemwe analankhula ndi Yesu uja? N’zosakayikitsa kuti nonse awiri mudzafotokoza mmene mumayamikirira nsembe ya Yesu. Mwina mungadzamufunse kuti akufotokozereni zambiri zokhudza zimene zinachitika m’maola omalizira a moyo wa Yesu padzikoli, komanso mmene anamvera Yesu atayankha pempho lake. N’kutheka kuti iye angadzakufunseni kuti mumufotokozere mmene zinthu zinalili m’masiku otsiriza. Udzakhalatu mwayi waukulu kuphunzira Mawu a Mulungu ndi anthu ngati iyeyu.​—Aef. 4:22-24.

Pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000, m’bale akusangalala kuwonjezera luso lomwe ankafuna kudzakhala nalo (Onani ndime 19)

19. N’chifukwa chiyani moyo m’Paradaiso sudzakhala wotopetsa? (Onani chithunzi chapachikuto.)

19 Moyo m’Paradaiso sudzakhala wotopetsa. Nthawi zonse tizidzakumana ndi anthu abwino komanso kugwira ntchito yosangalatsa. Koposa zonse, tsiku lililonse tizidzadziwa bwino Atate wathu wakumwamba komanso kusangalala ndi zinthu zimene watipatsa. Sitidzamaliza kuphunzira za iye ndipo padzakhala zambiri zoti tiphunzire zokhudza chilengedwe chake. Pamene tidzakhale ndi moyo kwa nthawi yaitali, m’pamenenso tizidzakonda kwambiri Mulungu. Timayamikira kwambiri Yehova ndi Yesu potilonjeza kuti tingadzakhale ndi moyo mpaka kalekale m’Paradaiso.

NYIMBO NA. 22 Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere

a Kodi nthawi zambiri mumaganizira mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso? N’zolimbikitsatu kumachita zimenezi. Tikamaganizira kwambiri zimene Yehova adzatichitire m’tsogolo, m’pamenenso timaphunzitsa anthu ndi mtima wonse zokhudza dziko latsopano. Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri lonjezo la Yesu lokhudza Paradaiso.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale yemwe akuyembekezera kudzagwira nawo ntchito yophunzitsa anthu omwe adzaukitsidwe, wayamba kale kuphunzitsa ena.