Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini a chaka chino a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi tidzapeza madalitso otani tikamapeza nthawi yolankhula, kumvetsera komanso kuganizira za Yehova?

Tikhoza kumasankha zochita mwanzeru, kukhala aphunzitsi abwino komanso chikhulupiriro chathu chidzalimba kwambiri.​—w22.01, tsamba 30-31.

Kodi tidzapindula bwanji chifukwa chokhulupirira Yehova komanso anthu omwe wawapatsa udindo wotisamalira?

Panopa ndi nthawi yoti tiphunzire kukhulupirira mmene Mulungu amachitira zinthu osati kumakayikira malangizo a gulu komanso zimene akulu amasankha. Chisautso chachikulu chikadzayamba, tidzakhala okonzeka kumvera ngakhale titapatsidwa malangizo ooneka ngati osamveka kapenanso achilendo.​—w22.02, tsamba 4-6.

Kodi mngelo ankatanthauza chiyani pamene ananena za “chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja la [Bwanamkubwa] Zerubabele”? (Zek. 4:8-10)

Masomphenyawa ankatsimikizira anthu a Mulungu kuti ngakhale kuti kachisi ankamangidwayo sankaoneka wogometsa, adzamalizidwa ndipo adzakhala wogwirizana ndi zimene Yehova amafuna.​—w22.03, tsamba 16-17.

Kodi tingakhale bwanji “chitsanzo . . . m’kalankhulidwe”? (1 Tim. 4:12)

Tizilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu mu utumiki, tiziimba ndi mtima wonse, tizipereka ndemanga pafupipafupi pamisonkhano, tizilankhula zoona ndiponso zimene zingalimbikitse ena komanso tizipewa kulankhula mawu achipongwe.​—w22.04, tsamba 6-9.

N’chifukwa chiyani maonekedwe a zilombo 4 (maulamuliro) zotchulidwa mu Danieli chaputala 7 akupezeka pa chilombo chimodzi chofotokozedwa pa Chivumbulutso 13:1, 2?

Chilombo cha pa Chivumbulutso 13 sichikuimira ulamuliro winawake umodzi, monga wa Roma. M’malomwake chikuimira maulamuliro onse omwe akhala akulamulira anthu.​—w22.05, tsamba 9.

Kodi njira yaikulu yomwe tingasonyezere kuti timakhulupirira kuti Mulungu adzachita chilungamo ndi iti?

Munthu wina akatikhumudwitsa kapena kutiIakwira, timayesetsa kuti tisamukwiyire komanso tisamusungire chakukhosi ndipo timasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Iye adzachotsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha uchimo.​—w22.06, tsamba 10-11.

Kodi m’bale yemwe akupereka pemphero pamisonkhano ayenera kukumbukira chiyani?

Pemphero si njira yoperekera malangizo kapena zilengezo. Choncho sayenera kunena “mawu ambirimbiri,” makamaka m’pemphero la kumayambiriro kwa misonkhano. (Mat. 6:7)​—w22.07, tsamba 24-25.

Kodi anthu “amene anali kuchita zoipa” “adzauka kuti aweruzidwe” m’njira yotani? (Yoh. 5:29)

Iwo sadzaweruzidwa potengera zimene anachita asanamwalire. Koma zikutanthauza kuti Yesu azidzaonetsetsa zimene iwo adzachite pambuyo poti aukitsidwa.​—w22.09, tsamba 18.

Kodi pamsonkhano wa mu September 1922, M’bale J. F. Rutherford anapereka chilengezo chosangalatsa chiti?

Pamsonkhano wa ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., iye analengeza kuti: “Mfumu yayamba kale kulamulira! Ndipo inu ndi atumiki ake olengeza za Ufumuwu. Choncho, lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi Ufumu wake!”​—w22.10, tsamba 3-5.

Kodi mu Yesaya 30, afotokoza njira zitatu ziti zomwe Mulungu amatithandizira kupirira?

Chaputalachi chikusonyeza kuti iye (1) amamvetsera mwatcheru ndi kuyankha mapemphero athu, (2) amatipatsa malangizo, komanso (3) amatipatsa madalitso panopa ndiponso m’tsogolo.​—w22.11, tsamba 9.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a pa Salimo 37:10, 11, 29, anakwaniritsidwapo m’mbuyomu ndipo adzakwaniritsidwanso m’tsogolo?

Mawu a Davidewa choyamba amafotokoza madalitso omwe Aisiraeli ankasangalala nawo, monga zinalili mu ulamuliro wa Solomo. Yesu anatchula mawu a pa vesi 11, posonyeza kuti zimenezi zidzachitikanso m’tsogolo. (Mat. 5:5; Luka 23:43)​—w22.12, tsamba 8-10, 14.