Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Mogwirizana ndi Salimo 61:8, kodi Davide ankakokomeza kapena ankanena zosatheka pomwe analemba kuti adzatamanda Mulungu “mpaka muyaya”?

Ayi. Zimene Davide analemba ndi zenizeni komanso zolondola.

Taganizirani zimene analemba pavesili komanso mavesi ena. Iye anati: “Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka muyaya, kuti ndikwaniritse malonjezo anga tsiku ndi tsiku.” “Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.” “Ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.”​—Sal. 61:8; 86:12; 145:1, 2.

Davide sankakokomeza n’kumaganiza kuti mwina sangafe. Ankadziwa kuti Yehova ananena kuti uchimo udzachititsa kuti anthu azifa ndipo iye anavomereza kuti anali wochimwa. (Gen. 3:3, 17-19; Sal. 51:4, 5) Ankadziwanso kuti anthu okhulupirika monga Abulahamu, Isaki ndi Yakobo anali atafa ndipo iyenso n’kupita kwa nthawi adzafa. (Sal. 37:25; 39:4) Koma mawu ake a pa Salimo 61:8 amasonyeza kuti anali wofunitsitsa komanso wotsimikiza kutamanda Mulungu mpaka kalekale, kutanthauza kuti kwa nthawi yonse yomwe angakhale ndi moyo.​—2 Sam. 7:12.

Zina zomwe Davide analemba zinkakhudza zomwe zinachitika pa moyo wake monga mmene timaonera m’timawu tapamwamba pa Salimo 18, 51 ndi 52. Mu Salimo 23, iye anamufotokoza Yehova monga m’busa yemwe amatsogolera, kutsitsimula komanso kuteteza. Davide nayenso anali m’busa wotero. Ndipo ankafuna kutumikira Mulungu ‘masiku onse a moyo wake.’​—Sal. 23:6.

Tisaiwalenso kuti Yehova ndi amene anauzira Davide kuti adziwe zoyenera kulemba. Zimene analemba zikuphatikizapo maulosi a zomwe zinali kudzachitika m’tsogolo. Mwachitsanzo, mu Salimo 110, Davide anena za nthawi imene Mbuye wake ‘adzakhale kudzanja lamanja’ la Mulungu kumwamba kuti alandire mphamvu. Mphamvu zochitira chiyani? Zogonjetsera adani a Mulungu komanso ‘kupereka chiweruzo pakati pa anthu a mitundu ina’ padzikoli. Davide anali kholo la Mesiya, yemwe anali kudzalamulira ali kumwamba komanso amene adzakhale “wansembe mpaka kalekale.” (Sal. 110:1-6) Yesu anatsimikizira kuti ulosi wa pa Salimo 110 unkanena za iyeyo ndiponso kuti udzakwaniritsidwa m’tsogolo.​—Mat. 22:41-45.

Inde, Davide anauziridwa kulemba zomwe zinali kudzachitika munthawi yake komanso m’tsogolo, pamene adzaukitsidwe n’kukhala ndi mwayi wotamanda Yehova mpaka kalekale. Zimenezi zikutithandiza kuona kuti zimene zili pa Salimo 37:10, 11, 29 zikufotokoza zinthu zomwe zinachitika pa nthawiyo ku Isiraeli komanso zimene zidzachitike m’tsogolo padziko lonse pamene Mulungu adzakwaniritse malonjezo ake.​—Onani ndime 8 munkhani yakuti, “Iwe Udzakhala Ndi Ine M’Paradaiso” yomwe ili m’magaziniyi.

Choncho Salimo 61:8 ndi mavesi ena ofanana nalo akusonyeza kuti Davide ankafuna kulemekeza Yehova mpaka nthawi yomwe adzamwalire. Akufotokozanso zimene Davide adzachite m’tsogolo pamene Yehova adzamuukitse kuti akhalenso ndi moyo.