NKHANI YOPHUNZIRA 51
Mungathe Kupeza Mtendere pa Nthawi ya Mavuto
“Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.”—YOH. 14:27.
NYIMBO NA. 112 Yehova Ndi Mulungu Wamtendere
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1. Kodi “mtendere wa Mulungu” ndi chiyani, nanga umatithandiza bwanji? (Afilipi 4:6, 7)
PALI mtendere wina umene anthu ambiri m’dzikoli saudziwa. Umenewu ndi “mtendere wa Mulungu,” kapena kuti kukhazikika maganizo kumene timakhala nako chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Atate wathu wakumwamba. Tikakhala ndi mtendere wa Mulungu timadzimva kukhala otetezeka. (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi “Mulungu wamtendere” komanso anthu omwe amamukonda. (1 Ates. 5:23) Tikamadziwa, kukhulupirira komanso kumvera Atate wathu, mtendere wa Mulungu ungachititse kuti mitima yathu ikhale m’malo tikakumana ndi mavuto.
2. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti n’zotheka kupeza mtendere wa Mulungu?
2 Kodi n’zothekadi kukhala ndi mtendere wa Mulungu pa nthawi yamavuto monga ngozi zam’chilengedwe, nkhondo, kuzunzidwa kapenanso kukagwa mliri? Chilichonse mwa zinthu zimenezi chingatichititse mantha. Komatu Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha.” (Yoh. 14:27) N’zosangalatsa kuti abale ndi alongo akutsatira malangizo a Yesuwa. Mothandizidwa ndi Yehova, iwo akwanitsa kupeza mtendere ngakhale pamene akumana ndi mayesero aakulu.
TINGAPEZE MTENDERE PA NTHAWI YA MILIRI
3. Kodi mliri ungachititse bwanji kuti tizisowa mtendere?
3 Zinthu zingathe kusintha mofulumira pa moyo wa anthu pa nthawi ya mliri. Taganizirani zimene zinachitikira anthu ambiri pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Kafukufuku wina anasonyeza kuti kupitirira hafu ya anthu padziko lonse ankavutika kugona pa nthawi ya mliriwu. Mliriwu unachititsa kuti anthu ambiri azikhala ndi nkhawa, azivutika maganizo, azimwa mwauchidakwa ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuchita nkhanza za m’banja komanso kufuna kudzipha. Ngati kumene mumakhala kwagwa mliri, kodi mungatani kuti musamade nkhawa kwambiri ndiponso kuti muzipeza mtendere wa Mulungu?
4. N’chifukwa chiyani kudziwa ulosi wa Yesu wonena za masiku otsiriza kumatipatsa mtendere?
4 Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza kudzakhala miliri, kapena kuti matenda omwe amafalikira kwambiri, “m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:11) Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kukhala ndi mtendere? Sitimadabwa tikaona miliri ikuchitika. Timadziwa kuti zimenezi zikuchitika monga mmene Yesu ananenera. Choncho tili ndi chifukwa chomveka chotsatirira malangizo ake omwe anapereka kwa anthu amene akukhala m’nthawi yamapeto, akuti: “Izitu zisadzakuchititseni mantha.”—Mat. 24:6.
5. (a) Mogwirizana ndi Afilipi 4:8, 9, kodi tingapempherere chiyani pa nthawi ya mliri? (b) Kodi kumvetsera Baibulo lochita kujambulidwa kungatithandize bwanji?
5 Mliri ungachititse kuti tizida nkhawa kwambiri komanso tizipanikizika. Zimenezi ndi zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Desi. b Bambo ake aang’ono, msuweni wake komanso dokotala wake atamwalira ndi matenda a COVID-19, ankaopa kuti mwina akhoza kutenga matendawa komanso kupatsira mayi ake omwe ndi okalamba. Chifukwa cha mliriwu ankaopanso kuti mwina ntchito ingamuthere, choncho ankada nkhawa kuti azipeza bwanji ndalama yogulira chakudya komanso kulipirira nyumba. Nkhawa zimenezi zinkamusokoneza maganizo ndipo zinkachititsa kuti azilephera kugona usiku. Koma Desi anakhalanso ndi mtendere. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kukhazikitsa mtima m’malo komanso kuti aziganizira zinthu zabwino. (Werengani Afilipi 4:8, 9.) Ankamva kuti Yehova “akumulankhula,” akamamvetsera Baibulo lochita kujambulidwa. Iye anati: “Mawu otonthoza a owerengawo ankachititsa kuti ndisamade nkhawa komanso ankandikumbutsa za chifundo cha Yehova.”—Sal. 94:19.
6. Kodi kuphunzira Baibulo panokha komanso misonkhano ya mpingo zingakuthandizeni bwanji?
6 Mosakayikira mliri ungasokoneze pulogalamu yanu yochitira zinthu za tsiku ndi tsiku koma musalole kuti zimenezi zikuchititseni kulephera kuphunzira Baibulo panokha, komanso kupezeka pamisonkhano. Zochitika pa moyo wa anthu ena zopezeka m’mabuku athu komanso m’mavidiyo, zingakukumbutseni kuti abale ndi alongo anu akupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto ngati omwewo. (1 Pet. 5:9) Misonkhano ingakuthandizeni kuti muziganizira kwambiri za zinthu zolimbikitsa za m’Malemba. Zonsezi zingakupatseninso mwayi woti muzilimbikitsa ena komanso muzilimbikitsidwa. (Aroma 1:11, 12) Mukamaganizira mmene Yehova anathandizira atumiki ake omwe ankadwala, ankachita mantha kapena omwe ankadziona kuti ali okhaokha, chikhulupiriro chanu chingalimbe ndipo simungakayikire kuti inunso akuthandizani.
7. Kodi tingaphunzire chiyani kwa mtumwi Yohane?
7 Muziyesetsa kulankhulana ndi abale ndi alongo anu. Mwina mliri ungachititse kuti tizikhala motalikirana ngakhalenso ndi Akhristu anzathu. Pa nthawi ngati imeneyi tingamamve ngati mmene mtumwi Yohane anamvera. Iye ankafuna kuonana ndi Gayo, yemwe anali mnzake komabe ankadziwa kuti kwa kanthawi sizikanatheka kuti aonane naye. (3 Yoh. 13, 14) Komabe anachita zomwe akanakwanitsa ndipo analembera Gayo kalata. Ngati inunso n’zosatheka kuti muonane ndi abale ndi alongo anu mungayese kulankhula nawo kudzera pafoni, vidiyokomfelensi kapena kuwatumizira uthenga. Mukamalankhula ndi Akhristu anzanu mungamamve kuti ndinu otetezeka komanso mudzakhala ndi mtendere. Mukakhala ndi nkhawa kwambiri muzilankhulana ndi akulu omwe angakulimbikitseni mwachikondi.—Yes. 32:1, 2.
TINGAPEZE MTENDERE PA NTHAWI YA NGOZI ZAM’CHILENGEDWE
8. Kodi ngozi zam’chilengedwe zingasokoneze bwanji mtendere wathu?
8 Ngati mwakumana ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi, chivomerezi kapena moto, n’kutheka kuti mungakhale ndi nkhawa kwa nthawi yayitali pambuyo pangoziyo. Ngati munthu amene mumamukonda wamwalira kapena katundu wanu wawonongeka, mungamamve chisoni, mungathedwe nzeru kapenanso kumakhala okwiya. Zimenezi sizitanthauza kuti ndinu munthu wokonda chuma kapenanso wopanda chikhulupiriro. Zimakhala kuti mwakumana ndi mayesero aakulu ndipo ena angamayembekezere kuti muchita zinthu mosaganiza bwino. (Yobu 1:11) Ngakhale kuti mwakumana ndi zinthu zodetsa nkhawa kwambiri choncho mungathe kukhalabe ndi mtendere. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?
9. Kodi zimene Yesu ananena zingatithandize bwanji kukonzekera ngozi zam’chilengedwe?
9 Kumbukirani zimene Yesu analosera. Mosiyana ndi anthu ena m’dzikoli omwe amaganiza kuti ngozi zam’chilengedwezi sizingawachitikire, ifeyo timayembekezera kuti ngozizi zipitirira kuwonjezereka ndipo zingatikhudze. Yesu anauza otsatira ake kuti “zivomezi zamphamvu” ndi ngozi zina zam’chilengedwe zidzachitika mapeto asanafike. (Luka 21:11) Analoseranso kuti kudzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo” ndipo timaonadi zinthu monga kuphwanya malamulo, chiwawa komanso za uchigawenga zikuchitika. (Mat. 24:12) Yesu sananene kuti zinthu zimenezi zidzachitikira anthu okhawo amene Yehova sasangalala nawo. Ndipotu atumiki okhulupirika ambiri a Yehova amakumana ndi ngozi zam’chilengedwe. (Yes. 57:1; 2 Akor. 11:25) Yehova sangatiteteze mozizwitsa ku ngozi zonse zam’chilengedwe, koma angatipatse zonse zomwe tikufunikira kuti mtima wathu ukhale m’malo komanso tikhale ndi mtendere.
10. N’chifukwa chiyani kukonzekera panopa ngozi zomwe zingachitike kungasonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro? (Miyambo 22:3)
10 Zingakhale zosavuta kuti mtima wathu ukhale m’malo pa nthawi yangozi ngati takonzekereratu pasadakhale. Koma kodi kukonzekera kumasonyeza kuti sitikukhulupirira Yehova? Ayi si choncho. Ndipotu kukonzekerako kumasonyeza kuti timakhulupirira kuti iye adzatisamalira. N’chifukwa chiyani tikutero? Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizikonzekera ngozi zomwe zingachitike. (Werengani Miyambo 22:3.) Kudzera m’nkhani za m’magazini, misonkhano yampingo komanso zilengezo za pa nthawi yake, gulu la Mulungu lakhala likutilimbikitsa mobwerezabwereza kuti tizikonzekera ngozi zosiyanasiyana. c Kodi timakhulupirira Yehova? Ngati ndi choncho tidzatsatira malangizowa panopa, ngozi iliyonse isanachitike.
11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Margaret?
11 Taganizirani zomwe zinachitikira mlongo wina dzina lake Margaret. Iye anauzidwa kuti achoke kunyumba kwawo kutayambika moto m’deralo. Popeza kuti anthu ambiri ankafuna kuthawa pa nthawi imodzi, misewu inatsekeka ndipo magalimoto sankayendanso. Dera lonselo linadzadza ndi utsi wakuda ndipo Margaret anakanika kutuluka m’galimoto yake kwa kanthawi. Komabe iye anapulumuka chifukwa anali atakonzekera. Iye anali ndi mapu m’kachikwama kake omwe anamuthandiza kudziwa njira yoti atulukire m’deralo. Iye anali atadutsapo msewu umenewo m’mbuyomo pokonzekera kuti asadzavutike kudutsamo pa nthawi yangozi. Popeza kuti anali atakonzekera Margaret anapulumuka pangoziyi.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo otithandiza kuti tikhale otetezeka?
12 Pofuna kutiteteza komanso kuti zinthu zichitike mwadongosolo, akuluakulu a boma angatipemphe kuti titsatire malamulo ena ake, tichoke m’deralo kapena tichite zinthu zina. Anthu ena amachedwa kumvera kapena kuchita zinthu mozengereza chifukwa chakuti sakufuna kusiya zinthu zawo. Koma kodi Akhristu amachita bwanji pa nkhaniyi? Baibulo limatiuza kuti: “Chifukwa cha Ambuye, gonjerani dongosolo lililonse lopangidwa ndi anthu: kaya mfumu chifukwa ili ndi udindo waukulu, kapena nduna chifukwa n’zotumidwa ndi mfumuyo.” (1 Pet. 2:13, 14) Gulu la Mulungu limatipatsanso malangizo pofuna kutiteteza. Nthawi zonse timalimbikitsidwa kuti tiyenera kupereka ma adiresi ndi manambala a foni amene tikugwiritsa ntchito panopa kwa akulu n’cholinga choti adzathe kulankhula nafe pakachitika ngozi. Kodi inu munachita kale zimenezi? Mwina tingapatsidwenso malangizo oti tikhale malo otetezeka, tichoke m’deralo komanso okhudza mmene tingalandirire zinthu zofunika pa moyo kapenanso mmene tingathandizire ena. Ngati sitingamvere, tingaike pangozi moyo wathu komanso wa akuluwo. Tizikumbukira kuti amuna okhulupirikawa amatiyang’anira. (Aheb. 13:17) Margaret ananena kuti: “Ndimakhulupirira kwambiri kuti kutsatira malangizo a akulu komanso a gulu, kunapulumutsa moyo wanga.”
13. Kodi n’chiyani chathandiza Akhristu ambiri omwe athawa kwawo kuti azisangalala komanso kukhala ndi mtendere?
13 Abale ndi alongo omwe anathawa kwawo chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe, nkhondo kapena zipolowe amayesetsa kusintha kuti azolowere moyo wawo watsopano ndipo amayambiranso mwamsanga kuchita zinthu zokhudza kulambira. Mofanana ndi Akhristu a mu nthawi ya atumwi omwe anabalalitsidwa chifukwa chozunzidwa, iwo amapitiriza ‘kulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’ (Mac. 8:4) Kulalikira kumawathandiza kuti aziganizira kwambiri za Ufumu osati mavuto awo, zomwe zachititsa kuti apitirizebe kukhala osangalala komanso ndi mtendere.
TINGAPEZE MTENDERE TIKAMAZUNZIDWA
14. Kodi kuzunzidwa kungasokoneze bwanji mtendere wathu?
14 Kuzunzidwa kungachititse kuti tisakhale ndi zinthu zambiri zomwe zimachititsa kuti tikhale ndi mtendere. Timasangalala komanso kukhala okhutira tikamasonkhana momasuka, kulalikira paliponse komanso kuchita zinthu za tsiku ndi tsiku popanda kuchita mantha kuti mwina timangidwa. Ngati tilibenso ufulu wochita zimenezi, tingamade nkhawa posadziwa chimene chitichitikire. Si zachilendo kumva choncho. Komabe tiyenera kukhala osamala. Yesu ananena kuti kuzunzidwa kudzachititsa kuti otsatira ake afooke. (Yoh. 16:1, 2) Ndiye kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala ndi mtendere tikamazunzidwa?
15. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kuzunzidwa? (Yohane 15:20; 16:33)
15 Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) M’bale wina dzina lake Andrei, zinamuvuta kukhulupirira mfundo imeneyi pamene ntchito yathu inaletsedwa m’dziko lawo. Iye ankaganiza kuti: ‘Kuno kuli a Mboni ambirimbiri, ndiye zingatheke bwanji kuti akuluakulu a boma atimange tonsefe?’ M’malo moti kukhala ndi maganizo amenewo kuchititse Andrei kukhala ndi mtendere kunamuchititsa kuti azingokhala ndi nkhawa. Abale ena anangosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova ndipo sankaganiza kuti sangamangidwe. Iwo ankadziwa kuti akhoza kumangidwa koma sankadera nkhawa kwambiri ngati Andrei. Choncho iye anaganiza zotengera chitsanzo chawo ndipo anayamba kudalira kwambiri Mulungu. Posakhalitsa iye anakhalanso ndi mtendere ndipo amasangalala ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo. Ngakhale kuti Yesu anafotokoza kuti tiziyembekezera kuzunzidwa, anatitsimikiziranso kuti tingathe kukhalabe okhulupirika.—Werengani Yohane 15:20; 16:33.
16. Kodi ndi malangizo ati omwe tiyenera kumvera tikamazunzidwa?
16 Ngati akuluakulu a boma atiletsa kuchita zinthu zina kapena aletseratu ntchito yathu, tingalandire malangizo kuchokera ku ofesi ya nthambi komanso kwa akulu. Cholinga cha malangizowo n’kutiteteza kuti tipitirizebe kulandira chakudya chauzimu komanso kugwira ntchito yolalikira mmene tingathere. Tiziyesetsa kuwatsatira ngakhale pamene sitikumvetsa chifukwa chake tapatsidwa malangizowo. (Yak. 3:17) Komanso tisamaulule nkhani zokhudza abale ndi alongo athu kapena mpingo, kwa anthu amene sakufunika kuzidziwa.—Mlal. 3:7.
17. Mofanana ndi atumwi, kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
17 Chimodzi mwa zifukwa zimene zimachititsa kuti Satana azilimbana ndi anthu a Mulungu, ndi chakuti iwo “ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (Chiv. 12:17) Musamalole kuti Satana ndi dziko lakeli akuchititseni mantha. Kulalikira komanso kuphunzitsa anthu ngakhale pamene tikuzunzidwa, kumatipatsa chimwemwe komanso mtendere. M’mbuyomo olamulira a Chiyuda atalamula atumwi kuti asiye kulalikira, amuna okhulupirikawa anasankha kumvera Mulungu. Iwo anapitirizabe kulalikira ndipo zimenezi zinawathandiza kukhala osangalala. (Mac. 5:27-29, 41, 42) N’zoona kuti pamene ntchito yathu yaletsedwa timayenera kulalikira mosamala. (Mat. 10:16) Koma ngati timachita zonse zomwe tingathe, tingapeze mtendere umene umabwera chifukwa chakuti tikusangalatsa Yehova komanso tikugwira ntchito yolengeza uthenga wopulumutsa moyo.
“MULUNGU WAMTENDERE ADZAKHALA NANU”
18. Kodi tizikumbukira chiyani pa nkhani ya kumene tingapeze mtendere weniweni?
18 Musamakayikire kuti ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri mungathe kukhala ndi mtendere. Pa nthawi ngati zimenezi tizikumbukira kuti mtendere umene timafunika ndi mtendere wa Mulungu, umene Yehova yekha ndi amene angatipatse. Muzimudalira pa nthawi ya mliri, ngozi zam’chilengedwe komanso mukamazunzidwa. Tisamasiyane ndi gulu lake. Tiziganizira zinthu zabwino kwambiri zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Tikamatero, ‘Mulungu wamtendere adzakhala nafe.’ (Afil. 4:9) Munkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingathandizire Akhristu anzathu omwe akukumana ndi mavuto kuti akhale ndi mtendere wa Mulungu.
NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa
a Yehova akulonjeza kupereka mtendere kwa anthu amene amamukonda. Kodi mtendere umene Mulungu amaperekawo ndi chiyani, nanga tingaupeze bwanji? Kodi “mtendere wa Mulungu” ungatithandize bwanji ngati kwagwa miliri, kwachitika ngozi zam’chilengedwe kapenanso tikamazunzidwa? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.
b Mayina ena asinthidwa.
c Onani nkhani yakuti, “Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi” mu Galamukani! Na. 5 2017.