Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 49

Tingakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

Tingakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

“Moyo wosatha adzaupeza.”​—YOH. 17:3.

NYIMBO NA. 147 Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi kuganizira lonjezo la Yehova la moyo wosatha kumatikhudza bwanji?

 YEHOVA akulonjeza kuti anthu omwe amamumvera adzakhala ndi “moyo wosatha.” (Aroma 6:23) Tikamaganizira lonjezoli, timayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani izi: Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri moti palibe chomwe chingatilekanitse ndi iye.

2. Kodi lonjezo la moyo wosatha limatithandiza bwanji?

2 Lonjezo la Mulungu la moyo wosatha limatithandiza kupirira mayesero omwe tikukumana nawo panopa. Ngakhale adani athu atiopseze kuti atipha, sitimasiya kutumikira Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti timadziwa kuti ngati tingafe tili okhulupirika kwa Yehova, iye adzatiukitsa ndipo tidzakhala ndi chiyembekezo choti sitidzafanso. (Yoh. 5:28, 29; 1 Akor. 15:55-58; Aheb. 2:15) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsimikizira kuti n’zotheka kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale? Taganizirani zifukwa zotsatirazi.

YEHOVA ADZAKHALAPO MPAKA KALEKALE

3. N’chifukwa chiyani sitingakayikire kuti Yehova angatithandize kukhala ndi moyo mpaka kalekale? (Salimo 102:12, 24, 27)

3 Timadziwa kuti Yehova angatithandize kukhala ndi moyo mpaka kalekale, chifukwa iye ndi Kasupe wa moyo komanso adzakhalapo mpaka kalekale. (Sal. 36:9) Taonani mavesi angapo a m’Baibulo omwe amatsimikizira kuti Yehova anakhalapo kuyambira kalekale ndipo adzakhalapo mpaka kalekale. Lemba la Salimo 90:2 limanena kuti Yehova ndi Mulungu “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” Lemba la Salimo 102, limatchulanso mfundo yomweyi. (Werengani Salimo 102:12, 24, 27.) Ndipo ponena za Atate wathu wakumwamba, mneneri Habakuku analemba kuti: “Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambira kalekale. Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.”​—Hab. 1:12.

4. Kodi tiyenera kumada nkhawa chifukwa choti sitimvetsa mfundo yoti Yehova wakhala alipo kuyambira kalekale? Fotokozani.

4 Kodi mumavutika kumvetsa mfundo yakuti Yehova wakhala alipo kuyambira “kalekale”? (Yes. 40:28) Anthu ambirinso zimawavuta kumvetsa. Ponena za Mulungu, Elihu anati: “Zaka zake n’zosawerengeka.” (Yobu 36:26) Koma ngati sitikumvetsa chinachake sizitanthauza kuti chinthucho si choona. Mwachitsanzo, ngakhale kuti sitingamvetse zonse zokhudza kuwala, kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuwala kulibeko? Ayi ndithu. Mofanana ndi zimenezi, anthufe sitingathe kumvetsa bwinobwino mfundo yakuti Yehova alibe chiyambi komanso mapeto. Komatu zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu sangakhale ndi moyo mpaka kalekale. Mlengi sangalephere kuchita zinthu chifukwa cha zimene tikumvetsa kapena ayi. (Aroma 11:33-36) Ndipo iye anakhalapo zinthu zina zonse m’chilengedwechi, kuphatikizapo zomwe zimapereka kuwala monga dzuwa, zisanakhalepo. Yehova amatitsimikizira kuti iye “ndi amene anapanga dziko lapansi ndi mphamvu zake.” Iye anakhalako ‘asanayale kumwamba.’ (Yer. 51:15; Mac. 17:24) Kodi ndi chifukwa china chiti chomwe chingatithandize kukhala otsimikiza kuti n’zotheka kukhala ndi moyo mpaka kalekale?

TINALENGEDWA KUTI TIKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE

5. Kodi anthu oyambirira anali ndi chiyembekezo chotani?

5 Yehova analenga zamoyo zina zonse padzikoli kuti zizikhala ndi moyo kwa kanthawi, kupatulapo anthu. Iye anawapatsa chiyembekezo choti asadzafe. Komabe Yehova anachenjeza Adamu kuti: “Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:17) Adamu ndi Hava akanamvera Yehova, sakanafa. Choncho n’zomveka kunena kuti n’kupita kwa nthawi Yehova akanawalola kudya zipatso za “mtengo wa moyo.” Zimenezi zikanatanthauza kuti iye akuwatsimikizira kuti angathe ‘kukhala ndi moyo mpaka kalekale.’ b​—Gen. 3:22.

6-7. (a) N’chiyaninso chimasonyeza kuti anthu sanalengedwe kuti azifa? (b) Kodi inuyo mumafuna kuti mudzachite chiyani m’tsogolo? (Onani zithunzi.)

6 N’zochititsa chidwi kuti asayansi ena apeza umboni woti ubongo wathu ukhoza kusunga zinthu zambiri kuposa zimene timadziwa pa nthawi imene timakhala ndi moyo. Mu 2010, magazini ina inanena kuti ubongo wathu uli ndi malo osunga zinthu pafupifupi ma GB 2.5 miliyoni, omwe ndi ofanana ndi maola 3 miliyoni (kuposa zaka 300) a mapulogalamu a pa TV ochita kujambulidwa. (Scientific American Mind) Komatu ubongo wathu ungathe kusunga zinthu zambiri kuposa pamenepa. Zimenezitu zikusonyeza kuti Yehova analenga ubongo wathu kuti uzitha kusunga zinthu zambiri kuposa zimene timasunga pa zaka 70 kapena 80 zimene timakhala ndi moyo.​—Sal. 90:10.

7 Yehova anatilenganso ndi mtima wofunitsitsa kuti tizikhala ndi moyo mpaka kalekale. Ponena za anthu, Baibulo limanena kuti Mulungu “anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlal. 3:11) Ichi ndi chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuti tiziona imfa monga mdani. (1 Akor. 15:26) Tikadwala kwambiri, kodi timangokhala n’kumadikira kuti tife? Ayi. Nthawi zambiri timapita kukaonana ndi dokotala kapenanso kumwa mankhwala kuti tichire. Ndipotu timachita zonse zomwe tingathe kuti tisafe. Komanso munthu yemwe timamukonda akamwalira, kaya wamkulu kapena wamng’ono, timamva kupweteka ndiponso chisoni kwa nthawi yaitali. (Yoh. 11:32, 33) N’zoonekeratu kuti Mlengi wathu wachikondi sakanatilenga kuti tizitha kuphunzira kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa kukhala ndi moyo mpaka kalekale, zikanakhala kuti si cholinga chake kuti anthu azikhala ndi moyo wosatha. Koma tili ndi zifukwa zinanso zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti tingakhale ndi moyo mpaka kalekale. Tiyeni tikambirane zimene Yehova wachitapo m’mbuyomu komanso zimene akuchita panopa posonyeza kuti cholinga chake choyambirira sichinasinthe.

Pokhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha, timasangalala kuganizira zinthu zomwe tidzakwanitse kuchita m’tsogolo (Onani ndime 7) c

CHOLINGA CHA YEHOVA SICHINASINTHE

8. Ponena za cholinga cha Yehova chokhudza anthufe, kodi lemba la Yesaya 55:11 limatitsimikizira chiyani?

8 Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anachimwa ndipo zinachititsa kuti ana awo azifa, Yehova sanasinthe maganizo ake okhudza cholinga chake. (Werengani Yesaya 55:11.) Iye amafunabe kuti anthu okhulupirika adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Tikutero poganizira zimene Yehova wakhala akunena komanso kuchita kuti akwaniritse cholinga chake.

9. Kodi Mulungu akulonjeza chiyani? (Danieli 12:2, 13)

9 Yehova akulonjeza kuti adzaukitsa akufa n’kuwapatsa moyo wosatha. (Mac. 24:15; Tito 1:1, 2) Munthu wokhulupirika Yobu sankakayikira kuti Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa omwe anamwalira. (Yobu 14:14, 15) Mneneri Danieli ankadziwa kuti anthu ali ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa n’kukhala ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. (Sal. 37:29; werengani Danieli 12:2, 13.) Ayuda a munthawi ya Yesu ankadziwanso kuti Yehova angathe kupereka “moyo wosatha” kwa atumiki ake okhulupirika. (Luka 10:25; 18:18) Mobwerezabwereza, Yesu ankalankhula za lonjezoli ndipo iye anaukitsidwa ndi Atate wake.​—Mat. 19:29; 22:31, 32; Luka 18:30; Yoh. 11:25.

Kodi zimene Eliya anachita poukitsa mwana zimatitsimikizira chiyani? (Onani ndime 10)

10. Kodi kuukitsidwa kwa anthu komwe kunachitika m’mbuyomu kumasonyeza chiyani? (Onani chithunzi.)

10 Yehova ndi Wopatsa Moyo ndipo ali ndi mphamvu yobwezeretsa moyo kwa amene anamwalira. Iye anapatsa mphamvu Eliya kuti aukitse mwana wa mkazi wa ku Zarefati. (1 Maf. 17:21-23) Patapita nthawi, mneneri Elisa mothandizidwa ndi Mulungu anaukitsa mwana wa mkazi wa Chisunemu. (2 Maf. 4:18-20, 34-37) Kuukitsidwa kwa anthu amenewa ndi enanso kunasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu yotha kubwezeretsa moyo. Yesu ali padzikoli anasonyeza kuti Atate wake anamupatsa mphamvu zimenezi. (Yoh. 11:23-25, 43, 44) Panopa Yesu ali kumwamba, ndipo anapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” Choncho iye angathe kukwaniritsa lonjezo lakuti “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi chiyembekezo chokhalabe ndi moyo mpaka kalekale.​—Mat. 28:18; Yoh. 5:25-29.

11. Kodi dipo limathandiza bwanji kuti tidzakhale ndi moyo mpaka kalekale?

11 N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Mwana wake wokondedwa afe imfa yopweteka? Yesu anafotokoza chifukwa chake pomwe ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Popereka Mwana wake monga dipo lophimba machimo athu, Mulungu anachititsa kuti zikhale zotheka kuti tidzapeze moyo wosatha. (Mat. 20:28) Mtumwi Paulo anafotokoza bwino mfundo yofunikayi yokhudza cholinga cha Mulungu, pomwe analemba kuti: “Imfa inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”​—1 Akor. 15:21, 22.

12. Kodi Ufumu udzathandiza bwanji kuti cholinga cha Yehova chokhudza anthufe chikwaniritsidwe?

12 Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mat. 6:9, 10) Mbali ina ya cholinga cha Mulungu ndi yakuti anthu adzakhale padzikoli mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, Yehova wasankha Mwana wake kuti akhale Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. Mulungu wakhala akusonkhanitsa anthu okwana 144,000 padzikoli kuti adzagwire ntchito ndi Yesu pokwaniritsa cholinga chake.​—Chiv. 5:9, 10.

13. Kodi Yehova akuchita chiyani panopa, nanga ifeyo timathandizapo bwanji?

13 Panopa Yehova akusonkhanitsa a “khamu lalikulu” komanso kuwaphunzitsa kuti akhale nzika za Ufumu wake. (Chiv. 7:9, 10; Yak. 2:8) Ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri m’dzikoli ndi ogawikana chifukwa cha chidani komanso nkhondo, a khamu lalikuluwa amayesetsa kukhala mwamtendere posatengera kuti akuchokera m’mayiko kapena mitundu yosiyana. Mophiphiritsa iwo asula kale malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo. (Mika 4:3) M’malo momenya nawo nkhondo zomwe zimaphetsa anthu ambiri, iwo amathandiza anthu kupeza “moyo weniweniwo” powaphunzitsa zokhudza Mulungu woona komanso zolinga zake. (1 Tim. 6:19) Achibale awo angamawatsutse kapena angamakumane ndi mavuto azachuma chifukwa chokhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, koma Yehova amaonetsetsa kuti iwo ali ndi zonse zimene akufunikira. (Mat. 6:25, 30-33; Luka 18:29, 30) Mfundo zimenezi zimatitsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni komanso kuti udzapitiriza kukwaniritsa cholinga cha Yehova.

TSOGOLO LABWINO KWAMBIRI

14-15. Kodi lonjezo la Yehova lodzathetseratu imfa lidzakwaniritsidwa bwanji?

14 Panopa Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba ndipo adzakwaniritsa malonjezo onse a Yehova. (2 Akor. 1:20) Kuyambira mu 1914, Yesu wakhala akugonjetsa adani ake. (Sal. 110:1, 2) Posachedwapa iye ndi olamulira anzake amaliza kugonjetsa ndipo awononga anthu onse oipa.​—Chiv. 6:2.

15 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo omvera adzathandizidwa kuti akhale angwiro. Pambuyo pa mayesero omaliza, anthu omwe Yehova adzawaweruze kuti ndi olungama “adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:10, 11, 29) N’zosangalatsa kuti “imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”​—1 Akor. 15:26.

16. Kodi chifukwa chachikulu chomwe chiyenera kutichititsa kutumikira Yehova n’chiyani?

16 Monga mmene taonera, chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale n’chochokera m’Mawu a Mulungu. Chiyembekezochi chingatithandize kukhalabe okhulupirika m’masiku otsiriza ovutawa. Koma kuti tizisangalatsa Yehova, tiyenera kumamutumikira osati chabe chifukwa chakuti tikufunitsitsa kudzapeza moyo. Chifukwa chachikulu chokhalirabe okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu ndi chakuti timawakonda kwambiri. (2 Akor. 5:14, 15) Chikondichi chimatilimbikitsa kuti tiziwatsanzira komanso kuuza ena za chiyembekezo chathu. (Aroma 10:13-15) Tikamayesetsa kukhala owolowa manja komanso kupewa kukhala odzikonda timakhala anthu amene Yehova akufuna kuti akhale anzake mpaka kalekale.​—Aheb. 13:16.

17. Kodi aliyense payekha ali ndi udindo wotani? (Mateyu 7:13, 14)

17 Kodi tidzakhala m’gulu la anthu omwe adzapeze moyo wosatha? Yehova watipatsa mwayi umenewu. Zili ndi ife panopa kusankha kuti tipitirize kuyenda pa msewu wa kumoyo. (Werengani Mateyu 7:13, 14.) Kodi zinthu zidzakhala bwanji pa nthawi yomwe tidzakhale ndi moyo mpaka kalekale? Tidzakambirana yankho la funso limeneli munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 141 Moyo Ndi Wodabwitsa

a Kodi mukuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha? Yehova akulonjeza kuti tsiku lina tidzakhala ndi moyo osadanso nkhawa kuti mwina timwalira. Munkhaniyi tikambirana zifukwa zina zomwe zingachititse kuti tizikhulupirira kwambiri kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezoli.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire akuganizira zinthu zina zomwe akufuna kudzachita akadzakhala ndi moyo wosatha.