Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingapeze Bwanji Ufulu Weniweni?

Kodi Tingapeze Bwanji Ufulu Weniweni?

“Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”—YOH. 8:36.

NYIMBO: 54, 36

1, 2. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti anthu akuyesetsa kuti apeze ufulu? (b) Kodi zotsatira za kumenyera ufulu zimakhala zotani?

MASIKU ANO, anthu ambiri amakonda kulankhula za ufulu komanso kuthetsa tsankho. Anthu m’mayiko ambiri amafuna ufulu chifukwa choti amaponderezedwa, amasalidwa komanso ali pa umphawi. Pomwe ena amafuna kuti akhale ndi ufulu wolankhula, wosankha zochita komanso wochita zimene akufuna. Aliyense amafuna kuti azichita zimene akufuna basi.

2 Koma kodi anthu amatani pofuna kupeza ufulu umenewu? Ambiri amakonda kuukira boma, kupanga zionetsero kapena kuyambitsa mabungwe omenyera ufulu. Koma kodi zimene amachitazi zimathandizadi? Ayi. M’malomwake zimangoyambitsa mavuto ndipo ena amaphedwa poyesa kumenyera ufulu. Zonsezi zikungotsimikizira mfundo imene Solomo analemba m’Baibulo yakuti: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”​—Mlal. 8:9.

3. Kodi tingatani kuti tikhale osangalala?

3 Yakobo anatchula mfundo yofunika imene ingathandize munthu kukhala wosangalala komanso waufulu. Iye analemba kuti: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita.” (Yak. 1:25) Yehova ndi amene anatipatsa lamulo langwiro ndipo amadziwa chimene chingathandize munthu kuti akhale pa ufulu komanso wosangalala. Atalenga anthu oyambirira, anawapatsa chilichonse chimene ankafunikira kuti asangalale ndipo chinthu china chimene anawapatsa ndi ufulu.

NTHAWI IMENE ANTHU ANALI PA UFULU WENIWENI

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Adamu ndi Hava anali pa ufulu? (Onani chithunzi choyambirira.)

4 Tikawerenga Genesis chaputala 1 ndi 2 titha kuoneratu kuti Adamu ndi Hava anali ndi ufulu umene anthu amaulakalaka masiku ano. Iwo ankakhala moyo wa mwanaalirenji, sankaopa chilichonse ndipo palibe amene ankawapondereza. Sankadera nkhawa za mavuto monga njala, kusowa ntchito, matenda kapena imfa. (Gen. 1:27-29; 2:8, 9, 15) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iwo anali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna? Tiyeni tikambirane mfundo imeneyi.

5. Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganiza, kodi chimafunika n’chiyani kuti anthu akhale ndi ufulu?

5 Anthu ambiri masiku ano amaganiza kuti munthu akakhala pa ufulu, ndiye kuti ayenera kuchita chilichonse chimene akufuna mosaganizira kuti zotsatira zake zidzakhala zotani. Koma buku lina linanena kuti ufulu umatanthauza “kutha kusankha zochita n’kukwaniritsa zimene wasankhazo.” (The World Book Encyclopedia) Koma bukuli linapitiriza kuti: “Mogwirizana ndi malamulo, anthu amakhala pa ufulu ngati atsogoleri awo sakuwapatsa mfundo zopanikiza kapena zopondereza.” Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu aliyense m’dziko angakhale ndi ufulu wochita zinazake, komabe pamafunikanso malamulo omuletsa kuchita zinthu zina ndi cholinga choti ufulu wakewo usasokoneze ufulu wa anthu ena. Komano funso n’kumati: Kodi ndi ndani amene ali ndi ufulu wopereka malamulo achilungamo, oyenera komanso osapanikiza anthu?

6. (a) N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wopanda malire? (b) Kodi ufulu umene anthu angakhale nawo ndi wotani? Perekani chifukwa.

6 Mfundo imodzi imene tiyenera kuikumbukira pa nkhaniyi ndi yakuti Yehova Mulungu yekha ndi amene ali ndi ufulu wopanda malire. Tikutero chifukwa chakuti iye ndi amene analenga chilichonse ndipo ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. (1 Tim. 1:17; Chiv. 4:11) Taganizirani mawu amene Mfumu Davide anagwiritsa ntchito pofotokoza udindo wapamwamba umene Yehova ali nawo. (Werengani 1 Mbiri 29:11, 12.) Choncho tinganene kuti ufulu umene anthu komanso angelo angakhale nawo umakhala ndi malire ake. Onse ayenera kudziwa kuti Yehova ndi woyenera kuwapatsa mfundo zoti aziyendera ndipo mfundo zake ndi zachilungamo, zothandiza komanso zosapanikiza. Ndipo izi n’zimene Yehova anachita ndi anthu oyambirira.

7. Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene anthu amazichita mwachibadwa?

7 Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wambiri, panali mfundo zina zimene ankafunika kuyendera. Ndipo zina ndi zoti ankazitsatira mwachibadwa. Mwachitsanzo, ankafunika kupuma, kudya, kugona komanso kuchita zinthu zina kuti akhalebe ndi moyo. Ndipo akamachita zinthu zimenezi sankaona kuti akuphwanyiridwa ufulu. Zili choncho chifukwa chakuti Yehova anakonza zinthu m’njira yakuti anthuwo akamachita zinthu za tsiku ndi tsiku ngati zimenezi azisangalala. (Sal. 104:14, 15; Mlal. 3:12, 13) Tonsefe timasangalala tikamapuma mpweya wabwino, kudya chakudya chimene timachikonda komanso kugona bwino. Tikamachita zimenezi sitimva kuti tikupanikizika kapena kuphwanyiridwa ufulu. Adamu ndi Hava ayenera kuti ankamva choncho.

8. Kodi Yehova anapereka lamulo liti kwa anthu oyambirira, nanga cholinga chake chinali chotani?

8 Yehova analamulanso Adamu ndi Hava kuti adzaze dziko lapansi komanso kuliyang’anira. (Gen. 1:28) Kodi lamulo limeneli linali lowaphwanyira ufulu? Ayi. Mulungu analipereka n’cholinga choti anthuwo athandize nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu choti dziko lonse likhale paradaiso wodzaza ndi anthu angwiro. (Yes. 45:18) Koma masiku ano ngati anthu ena asankha kusakhala pa banja kapena kusakhala ndi ana, sakuchita zotsutsana ndi cholinga cha Mulungu. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amasankha kukhala pabanja komanso kulera ana. Amachita zimenezi ngakhale kuti munthu amakumana ndi mavuto ena akalowa m’banja kapena akakhala ndi ana. (1 Akor. 7:36-38) Izitu n’zomveka chifukwa chakuti mwachibadwa anthu amasangalala akamachita zimenezi. (Sal. 127:3) Adamu ndi Hava anali ndi mwayi wokhala m’banja n’kumasangalala ndi ana awo mpaka muyaya.

KODI ANTHU ANATAYA BWANJI UFULU WENIWENI?

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti lamulo la pa Genesis 2:17 linali lachilungamo, lothandiza komanso losapondereza?

9 Yehova anapatsanso Adamu ndi Hava lamulo lina ndipo anafotokoza chilango chimene angalandire ngati ataphwanya lamulolo. Anawauza kuti: “Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:17) Kodi lamulo limeneli linali lopanda chilungamo, losayenera komanso lopanikiza? Kodi tingati Mulungu ankaphwanyira Adamu ndi Hava ufulu wawo? Ayi. Akatswiri ambiri a Baibulo amanena kuti lamulo limeneli linali lomveka bwino komanso losavuta kulitsatira. Mwachitsanzo, katswiri wina anati: “Lamulo limene Mulungu anapereka pa [Genesis 2:16, 17] linali lothandiza kuzindikira kuti Mulungu yekha ndi amene amadziwa zinthu zabwino zimene zingathandize . . . anthu komanso zinthu zoipa zimene zingawabweretsere mavuto. Kuti anthu azisangalala ndi zinthu zabwinozo ayenera kukhulupirira Mulungu komanso kumumvera. Koma akapanda kumumvera, Mulunguyo amawasiya kuti azisankha okha zoyenera . . . ndi zosayenera.” Komatu udindo wosankha zimenezi ndi waukulu kwambiri moti anthu paokha sangaukwanitse.

Zimene Adamu ndi Hava anasankha zinabweretsa mavuto aakulu (Onani ndime 9-12)

10. Kodi kukhala ndi ufulu wosankha kumasiyana bwanji ndi kukhala ndi udindo wonena kuti izi n’zabwino izi n’zoipa?

10 Anthu ena akawerenga lamulo limene Mulungu anapatsa Adamu amanena kuti ankamuphera ufulu. Anthu amene amanena zimeneziwa, vuto lawo ndi lakuti satha kusiyanitsa pakati pa ufulu wosankha ndi udindo wonena kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika. Adamu ndi Hava anali ndi ufulu wosankha kumvera Mulungu kapena kusamumvera. Koma Yehova ndi amene anali ndi udindo wonena kuti izi n’zabwino izi n’zoipa ndipo chizindikiro cha udindowu chinali “mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” umene unali m’munda wa Edeni. (Gen. 2:9) Tiyenera kuvomereza kuti pa zinthu zimene timasankha kuchita, sitingadziwe zotsatira zake zonse ndipo sitingatsimikizire kuti zivute zitani ziyenda bwino. N’chifukwa chake timaona anthu akusankha zochita ali ndi zolinga zabwino koma zotsatira zake n’kukhala zomvetsa chisoni komanso zoopsa. (Miy. 14:12) Vuto ndi lakuti anthufe sitingathe kuchita zinthu zina patokha. Lamulo limene Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava linali lowathandiza kuzindikira njira yabwino yogwiritsira ntchito ufulu wawo. N’chifukwa chiyani tikutero, nanga Adamu ndi Hava anatani atapatsidwa lamuloli?

11, 12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Adamu ndi Hava anasankha zinali zoopsa? Perekani chitsanzo.

11 N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyambirira anasankha kusamvera Mulungu. Hava anakopeka pamene Satana anamulonjeza kuti: “Maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” (Gen. 3:5) Kodi zimene Adamu ndi Hava anasankha zinawathandiza kukhala ndi ufulu wambiri? Ayi. Zimene Satana anawalonjeza zija sizinatheke. Nthawi yomweyo anazindikira kuti zotsatira za kuphwanya malamulo a Yehova zimakhala zoopsa. (Gen. 3:16-19) Zili choncho chifukwa chakuti Yehova sanalenge anthu m’njira yoti akhale ndi udindo wosankha kuti zabwino ndi izi zoipa ndi izi.​—Werengani Miyambo 20:24; Yeremiya 10:23.

12 Zimenezi tingaziyerekezere ndi zimene woyendetsa ndege amachita. Kuti akafike kumene akupita ayenera kudutsa m’njira yovomerezeka. Masiku ano, pali zipangizo zothandiza woyendetsa ndege kuti azizindikira komwe akupita komanso kuti azikambirana ndi anthu oyang’anira za mayendedwe a ndege n’cholinga choti akafike bwinobwino. Koma ngati woyendetsayo ataganiza zosiya kutsatira malangizowo n’kudutsa njira imene akufuna, zotsatira zake zingakhale zoopsa kwambiri. Zimene Adamu ndi Hava anachita tingaziyerekezere ndi zimene woyendetsa ndege wamakani angachite. Iwo anakana kutsatira malangizo a Yehova. Ndipo zotsatira zake zinali zoopsa chifukwa zinabweretsa uchimo ndi imfa kwa iwowo komanso kwa ana awo onse. (Aroma 5:12) Mtima wofuna ufulu wambiri unawatayitsa ufulu weniweni umene anapatsidwa.

TINGATANI KUTI TIPEZE UFULU WENIWENI?

13, 14. Kodi tingatani kuti tipeze ufulu weniweni?

13 Anthu ambiri amaganiza kuti munthu amasangalala ngati wapatsidwa ufulu wambiri. Koma zoona zake ndi zakuti munthu akakhala ndi ufulu wopanda malire amakhala ngati ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. N’zoona kuti ufulu umathandiza. Koma kodi mukuganiza kuti dzikoli likanafika pati zikanakhala kuti aliyense ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna? Pa nkhani imeneyi, buku limene tatchula kale lija linati: “Malo alionse amakhala ndi malamulo amitundumitundu omwe amathandiza kuti anthu azikhala ndi ufulu wochita zinazake komanso aziletsedwa kuchita zinthu zina.” M’pake kuti bukuli linati pali malamulo amitundumitundu chifukwa kunena zoona kunja kuno anthu alemba mabuku ambirimbiri a malamulo. Amalembanso ntchito maloya ndi oweruza milandu ankhaninkhani n’cholinga choti azithandiza anthu kumvetsa komanso kutsatira malamulowo.

14 Koma Yesu Khristu anatchula njira yosavuta yopezera ufulu weniweni. Iye anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Apa Yesu anasonyeza kuti pali zinthu ziwiri zofunika kuti munthu apeze ufulu weniweni. Choyamba, munthuyo ayenera kutsatira mfundo zachoonadi zimene Yesu ankaphunzitsa. Chachiwiri, ayenera kukhala wophunzira wake. Munthu akachita zimenezi amakhaladi pa ufulu weniweni. Koma kodi ufulu wake umakhala wotani? Yesu anapitiriza kuti: “Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo. . . . Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”​—Yoh. 8:34, 36.

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ufulu umene Yesu analonjeza ndi weniweni?

15 Apa n’zodziwikiratu kuti ufulu umene Yesu ananena kuti ophunzira ake adzaupeza ndi wapamwamba kwambiri kuposa uliwonse umene anthu amamenyera m’dzikoli. Pamene Yesu ananena kuti “ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka,” ankatanthauza kumasuka ku ukapolo wa uchimo womwe ndi woopsa kwambiri. Uchimo sumangotichititsa zoipa koma umatilepheretsanso kuchita zimene tingathe kapena zimene tikudziwa kuti n’zolondola. Zoterezi zikamachitika munthu amakhala pa ukapolo ndipo zotsatira zake zimakhala zakuti amakhala ndi nkhawa, amavutika, amamva ululu kenako n’kufa. (Aroma 6:23) Mtumwi Paulo zinkamuwawa kwambiri akaganizira mmene uchimo unkamuzunzira. (Werengani Aroma 7:21-25.) Tikadzamasuka ku uchimo m’pamene tidzakhale pa ufulu weniweni umene Adamu ndi Hava anali nawo poyamba.

16. Kodi ufulu weniweni tingaupeze bwanji?

16 Mawu a Yesu akuti “mukamasunga mawu anga nthawi zonse” amasonyeza kuti pali zinthu zina zimene tiyenera kutsatira komanso zimene tiyenera kupewa kuti iye atithandize kukhala pa ufulu. Popeza tinadzipereka kwa Mulungu, ndiye kuti tinadzikana tokha n’kusankha moyo wotsatira zimene Yesu ankaphunzitsa. (Mat. 16:24) Malinga ndi zimene Yesu analonjeza, tidzakhala pa ufulu weniweni pa nthawi imene mavuto onse adzatha chifukwa cha dipo limene anapereka.

17. (a) N’chiyani chingathandize munthu kukhala wosangalala? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 Munthu akamatsatira zimene Yesu anaphunzitsa, amakhala wosangalala. Ndipo zotsatira zake n’zakuti posachedwa adzamasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Werengani Aroma 8:1, 2, 20, 21.) Munkhani yotsatira tidzaona zimene tingachite kuti panopa tizigwiritsa ntchito ufulu wathu mwanzeru n’cholinga choti tizilemekeza Yehova Mulungu mpaka kalekale.