Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizitsanzira Yehova pa Nkhani Yolimbikitsa Ena

Tizitsanzira Yehova pa Nkhani Yolimbikitsa Ena

“Atamandike Mulungu . . . [amene] amatitonthoza m’masautso athu onse.”​2 AKOR. 1:3, 4.

NYIMBO: 7, 3

1. Tchulani lonjezo lolimbikitsa limene Yehova anapereka anthu atangochimwa mu Edeni.

KUNGOYAMBIRA pamene anthu anachimwa, Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi Mulungu wolimbikitsa. Adamu ndi Hava atangochimwa, Yehova anapereka lonjezo lolimbikitsa kwa ana a Adamu. Anasonyeza kuti zimene zinachitikazo sanali mapeto a zonse. Lonjezo la pa Genesis 3:15 limapatsa anthu chiyembekezo chakuti “njoka yakaleyo,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi, adzawonongedwa pamodzi ndi ntchito zake zonse.​—Chiv. 12:9; 1 Yoh. 3:8.

YEHOVA ANALIMBIKITSA ATUMIKI AKE

2. Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Nowa?

2 Nowa ankakhala m’dziko la anthu osaopa Mulungu ndipo iye yekha ndi banja lake ndi amene ankalambira Yehova. Chiwawa ndi chiwerewere zinali ponseponse moti Nowa akanatha kukhumudwa kwambiri. (Gen. 6:4, 5, 11; Yuda 6) Koma Yehova anamuuza mfundo zimene zinamulimbikitsa kuti achite zonse zimene angathe kuti ‘aziyendabe ndi Mulungu.’ (Gen. 6:9) Anamuuza kuti adzawononga anthu onse oipa ndipo anamuuzanso zoyenera kuchita kuti iye ndi banja lake apulumuke. (Gen. 6:13-18) Apatu Yehova anathandiza kwambiri Nowa ndipo anamulimbikitsa.

3. Kodi Mulungu analimbikitsa bwanji Yoswa? (Onani chithunzi choyambirira.)

3 Nayenso Yoswa anali ndi ntchito yaikulu yothandiza Aisiraeli kuti akhazikike m’Dziko Lolonjezedwa. Kuti zimenezi zitheke, anafunika kugonjetsa asilikali amphamvu a mitundu ya anthu amene ankakhala m’dzikolo. Pali zinthu zambiri zimene zikanachititsa Yoswa kukayikira zoti akwanitsa ntchitoyi. Yehova atadziwa zimenezi anauza Mose kuti alimbikitse Yoswa. Anamuuza kuti: “Uike Yoswa kukhala mtsogoleri ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.” (Deut. 3:28) Yoswa asanayambe ntchito yakeyi, Yehova anamulimbikitsa pomuuza kuti: “Monga ndakulamula kale, ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” (Yos. 1:1, 9) Mawu amenewatu anali olimbikitsa kwambiri.

4, 5. (a) Kodi Yehova analimbikitsa bwanji anthu ake akale? (b) Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Mwana wake?

4 Koma nthawi zina Yehova ankalimbikitsanso anthu ake monga gulu. Ayuda ali ku ukapolo ku Babulo, Mulungu anapereka ulosi wolimbikitsa wakuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Yes. 41:10) Mulungu ankalimbikitsanso Akhristu oyambirira ndipo amachitanso zomwezo masiku ano.​—Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.

5 Ngakhale Yesu analimbikitsidwapo ndi Atate ake. Pa nthawi ya ubatizo wake, anamva mawu ochokera kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:17) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsa Yesu pa nthawi yonse ya utumiki wake wapadziko lapansili.

YESU ANKALIMBIKITSA ANTHU

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti fanizo la matalente ndi lolimbikitsa?

6 Yesu ankatsanzira Atate wake. Fanizo la matalente limene anapereka mu ulosi wake wonena za masiku otsiriza limatilimbikitsa kukhala okhulupirika. Mbuye wa mufanizoli anayamikira akapolo okhulupirika ndi mawu akuti: “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe! Unakhulupirika pa zinthu zochepa. Ndikuika kuti uziyang’anira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.” (Mat. 25:21, 23) Mawu amenewatu ndi olimbikitsa ndipo angatithandize kuti tizitumikira Yehova mokhulupirika.

7. Kodi Yesu analimbikitsa bwanji atumwi ake, makamaka Petulo?

7 Ophunzira a Yesu ankakonda kukangana pa nkhani yoti wamkulu ndi ndani. Koma Yesu anawathandiza moleza mtima kuti azikhala ndi mtima wofuna kutumikira anzawo osati kuwalamulira. (Luka 22:24-26) Petulo anakhumudwitsa Yesu maulendo angapo. (Mat. 16:21-23; 26:31-35, 75) M’malo moganiza kuti Petulo ndi wokanika, Yesu anamulimbikitsa ndipo anamupatsa udindo wokalimbikitsa abale ake.​—Yoh. 21:16.

ATUMIKI A MULUNGU AKALE ANKALIMBIKITSANA

8. Kodi Hezekiya analimbikitsa bwanji akuluakulu a asilikali komanso Ayuda ena?

8 Ngakhale Yesu asanabwere padzikoli, n’kupereka chitsanzo pa nkhani yolimbikitsa anthu, atumiki a Mulungu ena ankalimbikitsa anzawo. Mwachitsanzo, Asuri ataopseza Ayuda, Hezekiya anasonkhanitsa akuluakulu a asilikali komanso Ayuda ena kuti awalimbikitse. Baibulo limanena kuti “anthuwo anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya.”​—Werengani 2 Mbiri 32:6-8.

9. Kodi buku la Yobu likutiphunzitsa chiyani pa nkhani yolimbikitsana?

9 Pa nthawi imene Yobu anali pa mavuto aakulu anaperekanso chitsanzo chabwino pouza anthu amene anabwera kudzamutonthoza njira yabwino yolimbikitsira anthu. M’malo momulimbikitsa, anzakewo ankangomuimba mlandu. Yobu ananena kuti moyo wa anthuwo ukanakhala ngati moyo wake, iye akanawalimbikitsa ndiponso kuwatonthoza. (Yobu 16:1-5) Kenako Yobuyo analimbikitsidwa ndi Elihu komanso Yehova.​—Yobu 33:24, 25; 36:1, 11; 42:7, 10.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani mwana wamkazi wa Yefita ankafunika kulimbikitsidwa? (b) Kodi ndi anthu ati masiku ano amene amafunikanso kuwalimbikitsa?

10 Munthu wina wakale amene anafunika kulimbikitsidwa anali mwana wamkazi wa Yefita. Yefita asanapite kukamenyana ndi Aamoni, analonjeza kuti ngati angapambane pa nkhondoyo, adzapereka kwa Yehova munthu woyamba kudzamuchingamira. Ndiye zinachitika kuti pamene ankabwerako, woyamba kukamulandira anali mwana wake wamkazi ndipo mwana wake anali yekhayo. Yefita ataona zimenezi zinamupweteka kwambiri. Koma anasunga lonjezo lake ndipo anatumiza mwana wakeyo, yemwe anali namwali, kuti azikatumikira kuchihema cha Mulungu ku Silo kwa moyo wake wonse.​—Ower. 11:30-35.

11 N’zoona kuti zimene zinachitikazi zinamupweteka Yefita, koma nayenso mwana wakeyo ayenera kuti anapwetekedwa mtima. Koma chosangalatsa n’chakuti anavomereza zimene bambo ake analonjeza. (Ower. 11:36, 37) Apa tingati analolera kuti asadzakwatiwe n’kukhala ndi ana ndipo analibe mwayi wopitiriza dzina la banja lake kapena kulandira cholowa. Pamenepa titha kuoneratu kuti iye ankafunika kulimbikitsidwa. Pofotokoza nkhaniyi, Baibulo limati: “Mu Isiraeli munakhala chizolowezi chakuti, chaka ndi chaka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikira mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa chaka.” (Ower. 11:39, 40) Masiku anonso, abale ndi alongo omwe sanalowe m’banja n’cholinga choti ‘akondweretse Ambuye’ ayenera kuyamikiridwa komanso kulimbikitsidwa.​—1 Akor. 7:32-35.

ATUMWI ANKALIMBIKITSA AKHRISTU ANZAWO

12, 13. Kodi Petulo analimbikitsa bwanji abale ake?

12 Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza Petulo kuti: “Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu. Koma ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe. Chotero iwenso, ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.”​—Luka 22:31, 32.

Makalata a atumwi ankalimbikitsa mipingo ndipo ndi olimbikitsabe mpaka pano (Onani ndime 12-17)

13 Petulo anali ngati mzati mumpingo wachikhristu woyambirira. (Agal. 2:9) Kulimba mtima kumene anasonyeza kuyambira pa Pentekosite kunathandiza kwambiri Akhristu ena kuti nawonso alimbe mtima. Chakumapeto kwa utumiki wake padzikoli, anauza Akhristu anzake kuti: “Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kupereka umboni wamphamvu wakuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu.” (1 Pet. 5:12) Makalata amene Petulo analemba analimbikitsa Akhristu kwa zaka zambirimbiri. Mfundo zake n’zolimbikitsanso masiku ano pamene tikuyembekezera kuti malonjezo a Yehova akwaniritsidwe.​—2 Pet. 3:13.

14, 15. Kodi uthenga wa Yohane wakhala ukulimbikitsa bwanji Akhristu kuyambira kalekale?

14 Nayenso mtumwi Yohane anali mzati mumpingo wachikhristu woyambirira. Uthenga wabwino wonena za Yesu umene analemba unalimbikitsanso Akhristu kwa zaka zambiri ndipo umatilimbikitsanso masiku ano. Mwachitsanzo, mfundo imene Yesu ananena yoti chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu enieni imapezeka mu uthenga wake wokha.​—Werengani Yohane 13:34, 35.

15 Makalata atatu amene Yohane analemba alinso ndi mfundo zachoonadi zolimbikitsa. Mwachitsanzo, ngati tikudziimba mlandu pa machimo amene tinachita, timalimbikitsidwa kwambiri tikawerenga mawu ake akuti “magazi a Yesu . . . akutiyeretsa ku uchimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Ndipo ngati mtima wathu ukupitiriza kutitsutsa, umakhala m’malo ndipo timayamba kumva bwino tikawerenga mawu akuti: “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (1 Yoh. 3:20) Pajanso Yohane yekha ndi amene analemba kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8, 16) Kalata yake yachiwiri ndi yachitatu imayamikira Akhristu amene amapitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’​—2 Yoh. 4; 3 Yoh. 3, 4.

16, 17. Kodi mtumwi Paulo analimbikitsa bwanji Akhristu oyambirira?

16 Mtumwi wina amene anachita zambiri polimbikitsa Akhristu anzake anali Paulo. Zikuoneka kuti Chikhristu chitangoyamba kumene, atumwi ambiri ankakhala ku Yerusalemu ndipo n’kumene kunali bungwe lolamulira. (Mac. 8:14; 15:2) Akhristu a ku Yudeya ankalalikira za Khristu kwa anthu amene ankakhulupirira mfundo yakuti kuli Mulungu mmodzi, yomwe Ayuda ankaphunzitsa. Koma mzimu woyera unathandiza mtumwi Paulo kuti akalalikire kwa anthu a m’madera olamulidwa ndi Agiriki ndi Aroma, omwe ankakhulupirira milungu yambirimbiri.​—Agal. 2:7-9; 1 Tim. 2:7.

17 Paulo anayenda m’madera ambiri a anthu a mitundu ina n’kumakhazikitsa mipingo moti anafika ku Greece, ku Italy komanso kudziko limene panopa limatchedwa Turkey. Akhristu atsopano m’maderawa ankazunzidwa ndi anthu akwawo ndipo ankafunika kulimbikitsidwa. (1 Ates. 2:14) Cha mu 50 C.E., Paulo analembera Akhristu atsopano ku Tesalonika kuti: “Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu. Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro, ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra.” (1 Ates. 1:2, 3) Iye anawauzanso kuti azilimbikitsana. Anati: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.”​—1 Ates. 5:11.

BUNGWE LOLAMULIRA LIMALIMBIKITSA AKHRISTU

18. Kodi bungwe lolamulira linalimbikitsa bwanji Filipo?

18 M’nthawi ya atumwi, bungwe lolamulira linkalimbikitsa oyang’anira komanso Akhristu ena onse. Mwachitsanzo, pamene Filipo ankalalikira za Khristu kwa Asamariya, abale a m’bungwe lolamulira anamuthandiza kwambiri. Anatumiza Petulo ndi Yohane kuti apite kukapempherera Akhristu atsopano kuti alandire mzimu woyera. (Mac. 8:5, 14-17) Filipo komanso Akhristu atsopanowo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona zimene bungwe lolamulira linachitazo.

19. Kodi Akhristu oyambirira anamva bwanji atalandira kalata yochokera ku bungwe lolamulira?

19 Kenako panabuka nkhani yakuti kodi Akhristu omwe si Ayuda ayenera kutsatira Chilamulo cha Mose n’kumadulidwa? (Mac. 15:1, 2) Mothandizidwa ndi mzimu woyera komanso mfundo za m’Malemba, abale anaona kuti si bwino kuchita zimenezo ndipo analemba makalata opita kumipingo ofotokoza nkhaniyi. Ndiyeno bungwelo linatuma anthu kuti akapereke makalatawo m’mipingo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Baibulo limati: “Ataiwerenga, anakondwera chifukwa cha mawu olimbikitsawo.”​—Mac. 15:27-32.

20. (a) Kodi Bungwe Lolamulira limalimbikitsa bwanji Akhristu masiku ano? (b) Kodi tidzakambirana funso liti munkhani yotsatira?

20 Masiku anonso, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limalimbikitsa atumiki a pa Beteli, atumiki apadera ena komanso abale ndi alongo padziko lonse. Mofanana ndi nthawi ya atumwi, abale ndi alongo amasangalala kwambiri akalimbikitsidwa chonchi. Mu 2015, Bungwe Lolamulira linatulutsanso kabuku kakuti Bwererani kwa Yehova, komwe kalimbikitsa anthu ambiri padziko lonse. Koma kodi ndi oyang’anira okha amene ayenera kutsanzira Yehova pa nkhani yolimbikitsa ena? Munkhani yotsatira tidzakambirana yankho la funso limeneli.