Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu

Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu

“Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.”2 AKOR. 3:17.

NYIMBO: 49, 73

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu m’masiku a Paulo ankakonda kulankhula za ukapolo ndi ufulu? (b) Kodi Paulo ankathandiza anthu kuyembekezera kuti ufulu weniweni ungachokere kwa ndani?

ANTHU a mu ulamuliro wa Aroma ankadziona kuti ndi otsatira kwambiri malamulo komanso kulimbikitsa chilungamo ndi ufulu. Koma zoona zake n’zakuti Aroma anali ndi mphamvu komanso ulemerero chifukwa cha ntchito zimene akapolo ankagwira. Pa nthawi ina, anthu atatu pa anthu 10 alionse mu ulamuliro wa Aroma anali akapolo. Choncho n’zosakayikitsa kuti anthu ambiri, ngakhalenso Akhristu akumeneko, ankakonda kukamba za ukapolo ndi ufulu.

2 Nkhani ya ufuluyi imatchulidwatchulidwanso m’makalata a Paulo. Ngakhale kuti m’masiku a Paulo anthu ankakonda kumenyera ufulu wawo, cholinga cha Paulo sichinali chimenecho. M’malo modalira kuti olamulira kapena mabungwe adzabweretsa ufulu, Paulo ndi Akhristu anzake ankayesetsa kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu komanso kufunika kwa nsembe ya dipo imene Khristu Yesu anapereka. Apa tingati iye ankathandiza anthu kuti apeze ufulu weniweni. Mwachitsanzo, m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Akhristu a ku Korinto, iye anawauza momveka bwino kuti: “Yehova ndiye Mzimu, ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.”​—2 Akor. 3:17.

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Paulo ananena mawu opezeka pa 2 Akorinto 3:17? (b) Kodi tingapeze bwanji ufulu umene Yehova amapereka?

3 M’kalata yake yopita kwa Akorinto, Paulo ananena za ulemerero wa Mose pa nthawi imene ankachokera kokalankhula ndi mngelo wa Yehova m’phiri la Sinai. Anthu ataona Mose anachita mantha kwambiri moti mpaka Moseyo anaphimba nkhope yake. (Eks. 34:29, 30, 33; 2 Akor. 3:7, 13) Ndiyeno Paulo ananena kuti: “Koma munthu akatembenukira kwa Yehova, chophimbacho chimachotsedwa.” (2 Akor. 3:16) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani?

4 Monga tinanenera mu nkhani yoyamba ija, Yehova yekha, amene analenga zinthu zonse, ndi amene ali ndi ufulu wopanda malire. Choncho m’pake kuti pamene pali Yehova komanso mzimu wake pamakhala ufulu. Ndiyeno kuti ife tipeze ufuluwo, tiyenera ‘kutembenukira kwa Yehovayo’ kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi wabwino. Pa nthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu, sankaona moyenera zinthu zimene Yehova ankawachitira. Tingati anali ndi chophimba m’maganizo ndi mumtima moti ankaona kuti ufulu umene analandira potulutsidwa ku Iguputo unali wongowathandiza kuti azipanga zimene akufuna, osati azisangalatsa Yehova.​—Aheb. 3:8-10.

5. (a) Kodi mzimu wa Yehova umapereka ufulu uti? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti munthu akhoza kukhalabe pa ufulu ngakhale akukumana ndi mavuto enaake monga kumangidwa? (c) Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Ufulu umene munthu amapeza mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu umathandiza m’njira zambiri, osati kungom’masula munthu ku ukapolo weniweni. Mzimu wa Mulungu umathandiza munthu kuti asakhale kapolo wa uchimo, imfa, kulambira konyenga komanso zikhulupiriro zabodza. (Aroma 6:23; 8:2) Kodi umenewu si ufulu weniweni? Munthu akhoza kukhala pa ufulu umenewu ngakhale pamene ali mundende kapena ku ukapolo. (Gen. 39:20-23) Umboni wake ndi zimene zinachitikira M’bale Harold King. Iye anapirira bwinobwino pamene anatsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chake. Kuti mudziwe zimene anakumana nazo mungapite pa JW Broadcasting. (Pitani pamene palembedwa kuti ZOCHITIKA PA MOYO WA ANTHU ENA > KUPIRIRA MAYESERO.) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira ufuluwu? Nanga tingatani kuti tiziugwiritsa ntchito mwanzeru?

TIZIYAMIKIRA UFULU UMENE MULUNGU WATIPATSA

6. Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti sankayamikira ufulu umene Yehova anawapatsa?

6 Munthu amayamikira kwambiri mphatso imene walandira akazindikira kuti ndi yamtengo wapatali. Aisiraeli sankaona kuti kumasulidwa ku ukapolo ku Iguputo ndi mwayi wamtengo wapatali. Pasanapite miyezi yambiri, anayamba kulakalaka zakudya ndi zakumwa zimene anazisiya ku Iguputo ndipo ankadandaula kuti zinthu zimene Yehova akuwapatsa si zabwino. Anafika mpaka pofuna kubwerera ku Iguputo. Tangoganizani, eti ankaona kuti ‘nsomba, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi’ zinali zabwino kuposa ufulu wolambira umene Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, anawapatsa. M’pake kuti Yehova anakwiya nawo kwambiri. (Num. 11:5, 6, 10; 14:3, 4) Kodi tikuphunzirapo chiyani?

7. Kodi Paulo anachita bwanji zinthu mogwirizana ndi malangizo ake a pa 2 Akorinto 6:1, nanga ife tingamutsanzire bwanji?

7 Mtumwi Paulo anauza Akhristu onse kuti asamapeputse ufulu umene Yehova watipatsa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu. (Werengani 2 Akorinto 6:1.) Ndiye taganizirani mmene Paulo zinkamupwetekera mumtima chifukwa choti anali kapolo wa uchimo ndi imfa. Koma iye ananena moyamikira kuti Mulungu adzamumasula “kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” Iye anafotokozera Akhristu anzake mmene izi zingachitikire. Iye anati: “Chilamulo cha mzimu umene umapatsa moyo mwa Khristu Yesu chakumasulani ku chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.” (Aroma 7:24, 25; 8:2) Ifenso tiyenera kutsanzira Paulo ndipo tisamapeputse zimene Mulungu wachita potimasula ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Dipo limatithandiza kuti tizitumikira Mulungu mosangalala tili ndi chikumbumtima chabwino.​—Sal. 40:8.

Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito ufulu wanu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu kapena pongochita zinthu zanuzanu? (Onani ndime 8-10)

8, 9. (a) Kodi mtumwi Petulo anapereka chenjezo liti pa nkhani yogwiritsa ntchito ufulu wathu? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene tingakopeke nazo mosavuta masiku ano?

8 Kuwonjezera pa kuyamikira ufulu wathu, tiyenera kupewa kuugwiritsa ntchito molakwika. Mtumwi Petulo ananena kuti si bwino kugwiritsa ntchito ufuluwu kuti tikwaniritse zimene thupi lathu limalakalaka. (Werengani 1 Petulo 2:16.) Chenjezo limeneli liyenera kutikumbutsa zimene zinachitikira Aisiraeli m’chipululu. Choncho nafenso tiyenera kukhala osamala kwambiri chifukwa n’zosavuta kuti tikodwe mumsamphawu. Satana ndi dziko lakeli amafuna kuti tizikopeka ndi kavalidwe, njira zodzikongoletsera, chakudya, zakumwa, zosangalatsa komanso zinthu zosiyanasiyana. Makampani amatsatsa malonda pogwiritsa ntchito anthu ooneka bwino n’cholinga choti tizilakalaka kukhala ndi zinthu zambiri zosafunika kwenikweni. Choncho n’zosavuta kukopeka n’kuyamba kugwiritsa ntchito ufulu wathu m’njira yolakwika.

9 Malangizo a Petulowa amagwiranso ntchito posankha zinthu zikuluzikulu monga maphunziro ndi ntchito. Mwachitsanzo, achinyamata amene ali pasukulu amalimbikitsidwa kuti aphunzire kwambiri m’masukulu apamwamba. Iwo amauzidwa kuti maphunziro apamwamba ndi amene angawathandize kuti apezenso ntchito yapamwamba n’kumalandira ndalama zambiri. Ndipo kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene anaphunzira kwambiri amalandira ndalama zambirimbiri tikayerekezera ndi amene sanaphunzire kwambiri. Ndiye poti achinyamatawo amafuna kukhala ndi tsogolo labwino, zimakhala zosavuta kuti akopeke ndi zimenezi. Koma kodi ndi mfundo ziti zimene achinyamatawo limodzi ndi makolo awo ayenera kuziganizira?

10. Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti posankha zochita pa moyo wathu?

10 Anthu ena amaganiza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhani ngati zimenezi malinga ngati chikumbumtima chake chikumulola. Mwina amaona kuti nkhaniyi ikufanana ndi nkhani ya chakudya imene Paulo anauza Akhristu a ku Korinto. Paja ananena kuti: “N’chifukwa chiyani ufulu wanga ukulamulidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina?” (1 Akor. 10:29) N’zoona kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha pa nkhani ya maphunziro ndi ntchito. Koma kumbukirani kuti ufulu umene timapatsidwa uli ndi malire ake ndipo chilichonse chimene timasankha chimakhala ndi zotsatira zake. N’chifukwa chake Paulo anayamba mawu akewa ndi mfundo yakuti: “Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa.” (1 Akor. 10:23) Mfundo imeneyi ingatithandize kuona kuti munthu asanasankhe zochita pa nkhani ngati zimenezi ayenera kuganizira kaye zinthu zina zofunika kwambiri.

TIZIGWIRITSA NTCHITO UFULU WATHU POTUMIKIRA MULUNGU

11. Kodi Mulungu anatimasula n’cholinga chotani?

11 Pamene Petulo ankapereka chenjezo pa nkhani yogwiritsa ntchito ufulu wathu anafotokoza cholinga chimene Mulungu anatimasulira. Iye anati tiyenera kugwiritsa ntchito ufulu wathu “monga akapolo a Mulungu.” Choncho cholinga chachikulu chimene Mulungu anatimasulira ku ukapolo wa uchimo ndi imfa, pogwiritsa ntchito Yesu, n’chakuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse ngati akapolo ake.

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Nowa ndi banja lake ndi chitsanzo chabwino kwa ife?

12 Choncho kuti tisakopeke ndi zinthu za m’dzikoli n’kubwerera ku ukapolo woipa uja, tiyenera kutanganidwa ndi zinthu zauzimu. (Agal. 5:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Nowa ndi banja lake. Iwo ankakhala m’dziko la anthu achiwawa komanso achiwerewere. Koma sanakopeke ndi zimene anthu ankakonda pa nthawiyo. Kodi iwo anakwanitsa bwanji kuchita zimenezi? Iwo ankatanganidwa kwambiri kuchita zimene Mulungu anawauza kuti azichita. Ankamanga chingalawa, kusonkhanitsa chakudya chawo ndi cha zinyama komanso kuchenjeza anthu. Baibulo limanena kuti: “Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Nowa ndi banja lake anapulumuka pamene dziko linkawonongedwa.​—Aheb. 11:7.

13. Kodi ndi ntchito iti imene Yesu anapatsidwa yomwe ifenso tiyenera kuigwira?

13 Ndiye kodi Yehova watilamula kuti tizichita chiyani masiku ano? Popeza timatsanzira Khristu, tonsefe timadziwa ntchito imene tapatsidwa. (Werengani Luka 4:18, 19.) Masiku ano, anthu ambiri achititsidwa khungu ndi mulungu wa nthawi ino ndipo ali mu ukapolo pa nkhani ya chipembedzo, zachuma komanso moyo wa tsiku ndi tsiku. (2 Akor. 4:4) Koma ifeyo tili ndi mwayi wotsanzira Yesu pothandiza anthu kuti adziwe Mulungu n’kuyamba kumulambira mwaufulu. (Mat. 28:19, 20) Ntchito imeneyi si yophweka ndipo pali mavuto ambiri amene tingakumane nawo. M’mayiko ena anthu amadana kwambiri ndi ntchitoyi ndipo amatilusira. Koma funso limene aliyense ayenera kudzifunsa ndi lakuti: ‘Kodi n’zotheka kuti ineyo ndigwiritse ntchito ufulu umene ndili nawo panopa kuti ndizichita zambiri popititsa patsogolo ntchito za Ufumu?’

14, 15. Kodi anthu a Mulungu achita zotani pa nkhani yogwira ntchito yolalikira mwakhama? (Onani chithunzi choyambirira.)

14 N’zolimbikitsa kuona kuti anthu ambiri masiku ano azindikira zoti nthawi yotsalayi yafupika ndipo ayamba moyo wosalira zambiri n’cholinga choti azilalikira kwambiri. (1 Akor. 9:19, 23) Ena amalalikira m’gawo lawo, pomwe ena amasamukira kumene kukufunika anthu ambiri olalikira. Malipoti akusonyeza kuti pa zaka 5 zapitazi, chiwerengero cha apainiya chakwera kwambiri moti panopa alipo oposa 1,100,000. Uwutu ndi umboni wakuti anthu akugwiritsa ntchito ufulu wawo kuti azitumikira Yehova.​—Sal. 110:3.

15 Kodi n’chiyani chathandiza abale ndi alongowa kuti azigwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wawo? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane za John ndi Judith amene akhala akutumikira m’mayiko osiyanasiyana kwa zaka 30. Iwo ananena kuti pamene Sukulu ya Utumiki wa Upainiya inayamba mu 1977, anthu ankalimbikitsidwa kusamukira kumene kukufunika anthu ambiri olalikira. Ndiyeno kuti akwanitse kuchita zimenezi, John anasintha ntchito maulendo angapo n’cholinga choti azikhala moyo wosalira zambiri. Iwo atasamukira kudziko lina anazindikira kuti kupemphera kwa Yehova komanso kumudalira kunathandiza kuti athane ndi mavuto amene ankakumana nawo pokhala m’dera losiyana ndi kwawo pa nkhani ya chilankhulo, chikhalidwe komanso nyengo. Kodi iwo amamva bwanji akaganizira zaka zimene atumikira? John anati: “Ndimaona kuti ndinkatanganidwa kwambiri ndi zinthu zabwino kwambiri kuposa chilichonse. Ndinayamba kuona umboni wakuti Yehova alikodi ndipo ali ngati Atate wanga wachikondi. Ndinayamba kumvetsa tanthauzo la mawu a pa Yakobo 4:8 akuti: ‘Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.’ Ndinkamva kuti ndapeza zimene ndinkafunikira pa moyo wanga.”

16. Kodi abale ndi alongo ambiri achita zotani kuti agwiritse ntchito mwanzeru ufulu wawo?

16 Koma abale ndi alongo ena amangokhala ndi mpata wochita utumiki wa nthawi zonse kwa kanthawi kochepa. Ngakhale zili choncho, ambiri amadzipereka kuti agwire nawo ntchito zomangamanga zimene zikuchitika padziko lonse. Mwachitsanzo, pamene likulu linkamangidwa ku Warwick ku New York, abale ndi alongo pafupifupi 27,000 anadzipereka kuti athandize. Ena ankadzipereka kwa milungu iwiri yokha, pomwe ena anakwanitsa chaka kapena kuposerapo. Ambiri ankachita kusiya ntchito zawo n’cholinga choti athandize. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yogwiritsa ntchito ufulu umene Mulungu watipatsa kuti tizimulemekeza.

17. Kodi anthu amene amagwiritsa ntchito mwanzeru ufulu umene Mulungu watipatsa adzadalitsidwa bwanji?

17 Ndife osangalala kwambiri kuti timadziwa Yehova komanso timasangalala ndi ufulu umene timaupeza chifukwa chomulambira. Tiyeni tiziyesetsa kuti zosankha zathu zizisonyeza kuti timayamikira ufuluwu. M’malo mouwononga kapena kuugwiritsa ntchito molakwika, tiyenera kuugwiritsa ntchito potumikira Yehova mmene tingathere. Tikamatero tidzadalitsidwa kwambiri ndipo tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:21.