Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani mabuku a Mboni za Yehova amasonyeza kuti Paulo anali wadazi?

Kunena zoona, masiku ano palibe anganene mwatchutchutchu mmene Paulo ankaonekera. Choncho zithunzi zimene zimapezeka m’mabuku athu n’zongojambula osati zotengedwa m’zinthu zakale zimene zinafukulidwa pansi.

Koma pali zinthu zingapo zimene zimatithandiza kuzindikira mmene Paulo ankaonekera. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya March 1, 1902, inafotokoza kuti: “Ponena za maonekedwe a Paulo, buku lakuti ‘Acts of Paul and Thecla,’ . . . lomwe linalembedwa cha m’ma 150 A.D limafotokoza bwino kwambiri ndipo zimene limanena n’zodalirika. Limafotokoza kuti Paulo ‘anali wamfupi, sanali wokula thupi, anali ndi dazi, wa timatewe pang’ono, wa thupi lamphamvu ndithu, wa nsidze zokumana pakati komanso wa mphuno yaitali.’”

Buku lina lotanthauzira mawu a zachipembedzo (la mu 1997) linafotokoza kuti buku limene linatchula za Pauloli linkanena zoona.” Buku lakuti The Acts of Paul and Thecla linkadaliridwa ndi anthu ambiri chifukwa mipukutu yokwana 80 yachigiriki ya buku limeneli idakalipo ndipo linatulukanso m’zilankhulo zina. Choncho zimene timajambula m’mabuku athu zimagwirizana ndi zimene anthu ena akale amanena pa nkhani ya maonekedwe a mtumwiyu.

Tizikumbukiranso kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri kuposa maonekedwe a Paulo. Paja ngakhale pa nthawi imene ankachita utumiki wake, anthu ena amene ankatsutsana naye ananena kuti: “Iyeyo akakhala pakati pathu amaoneka wofooka ndipo nkhani zake n’zosagwira mtima.” (2 Akor. 10:10) Koma tisaiwale kuti Paulo anakhala Mkhristu ataonetsedwa zinthu zodabwitsa ndi Yesu. Tiyenera kuganizira zimene Paulo anachita zosonyeza kuti analidi ‘chiwiya cha Khristu chochita kusankhidwa chotengera dzina la Yesu kupita nalo kwa anthu a mitundu ina.’ (Mac. 9:3-5, 15; 22:6-8) Tiziganiziranso mmene mabuku amene iye analemba mouziridwa ndi Yehova angatithandizire.

Paulo sankadzitama chifukwa cha zimene anachita asanakhale Mkhristu ndipo sanafotokoze maonekedwe ake. (Mac. 26:4, 5; Afil. 3:4-6) Koma ananena kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi.” (1 Akor. 15:9) Pa nthawi ina analemba kuti “Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunapatsidwa kwa ine, munthu wochepa pondiyerekeza ndi wochepetsetsa wa oyera onse. Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndilengeze kwa mitundu ina uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu.” (Aef. 3:8) Mfundo zimenezi ndi zofunika kwambiri kuposa maganizo alionse amene anthu angakhale nawo pa nkhani ya maonekedwe a Paulo.