Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda

Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda

“Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.”​—AHEB. 12:6.

NYIMBO: 123, 86

1. Kodi mawu amene anamasuliridwa m’Baibulo kuti chilango angatanthauzenso zinthu ziti?

KODI mumaganizira za chiyani mukamva mawu akuti “chilango”? Mawu amene anamasuliridwa kuti “chilango” m’malemba ena, angamasuliridwenso kuti “malangizo.” Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito limodzi ndi mawu ngati kudziwa zinthu, nzeru, chikondi kapena moyo. (Miy. 1:2-7; 4:11-13) Mulungu amatipatsa chilango kapena malangizo chifukwa chotikonda komanso n’cholinga choti tidzapeze moyo wosatha. (Aheb. 12:6) Ngakhale kuti amatipatsa chilango, sachita zimenezi mwankhanza. Mawu amene anamasuliridwa kuti chilango kapena malangizo nthawi zambiri amanena za kuphunzitsa munthu, ngati mmene makolo amaphunzitsira mwana amene amamukonda.

2, 3. Kodi malangizo ndi chilango zimathandiza bwanji pophunzitsa? (Onani chithunzi choyambirira.)

2 Tiyerekeze kuti mnyamata wamng’ono akusewera mpira m’nyumba. Ndiye mayi ake akumuuza kuti: “Iwe, usamasewere mpira m’nyumba, uswatu zinthu.” Koma akupitiriza kusewera ndipo kenako akuswa mphika wa maluwa. Kodi mayi akewo angatani? Mwina angamupatse malangizo komanso chilango. Pomupatsa malangizo, angamuuze chifukwa chake zimene wachitazo zili zolakwika. Angamuthandize kuona ubwino womvera makolo ake komanso kumufotokozera kuti malamulo amene amapereka ndi othandiza. Kenako angamupatse chilango kuti asadzayambirenso. Mwachitsanzo, akhoza kumulanda mpirawo n’kudzamupatsa m’tsogolo. Zimenezi zingathandize mwanayo kuzindikira kuti kusamvera ndi koipa.

3 Akhristufe tili ngati ana a m’nyumba ya Mulungu. (1 Tim. 3:15) Choncho timazindikira kuti Yehova ali ndi ufulu wotipatsa malamulo komanso chilango tikapanda kumvera malamulowo. Ndipotu tikakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zathu, chilango chake chingatithandize kwambiri kuzindikira kufunika komumvera. (Agal. 6:7) Mulungu amatikonda kwambiri ndipo safuna kuti tizikumana ndi mavuto.​—1 Pet. 5:6, 7.

4. (a) Kodi Yehova amatidalitsa tikamaphunzitsa bwanji? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Tikamapereka malangizo ochokera m’Malemba tingathandize mwana wathu kapena munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kuti akhale wotsatira wa Khristu. Mawu a Mulungu ndi ofunika kwambiri pophunzitsa anthu ndipo amathandiza munthu “kulangiza m’chilungamo.” Baibulo lingathandize mwana kapena munthu amene timaphunzira naye kumvetsa komanso ‘kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamulira.’ (2 Tim. 3:16; Mat. 28:19, 20) Tikamaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito Baibulo, Yehova amatidalitsa ndipo zimathandiza ophunzirawo kuti nawonso aziphunzitsa anthu ena. (Werengani Tito 2:11-14.) Tsopano tiyeni tikambirane mafunso ofunika atatu awa: (1) Kodi Mulungu amasonyeza bwanji chikondi popereka chilango kapena malangizo? (2) Kodi tingaphunzire chiyani kwa anthu amene Mulungu anawapatsa chilango? (3) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova ndi Mwana wake popereka malangizo kapena chilango?

MULUNGU AMAPEREKA CHILANGO MWACHIKONDI

5. Kodi Yehova amasonyeza bwanji chikondi akamatipatsa chilango kapena malangizo?

5 Yehova amatiphunzitsa, kutilangiza komanso kupereka chilango n’cholinga choti tipitirize kukhala naye pa ubwenzi komanso kuti tidzalandire moyo wosatha. Amachita zonsezi chifukwa chakuti amatikonda. (1 Yoh. 4:16) Koma satinyoza kapena kutisambula moti n’kufika podziona ngati achabechabe. (Miy. 12:18) M’malomwake Yehova amatipatsa ulemu, satiphwanyira ufulu wathu ndipo amatithandiza kuti tizimumvera chifukwa choti tili ndi mtima wabwino. Kodi inuyo mukapatsidwa malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu, mabuku athu, kwa makolo kapena akulu, mumaona kuti ndi umboni woti Mulungu amakukondani? Ndipotu tikayamba “kulowera njira yolakwika,” akulu amayesetsa kutithandiza mwachikondi ndiponso mofatsa. Yehova ndi amene amagwiritsa ntchito akuluwo kuti azichita zimenezi posonyeza kuti amatikonda.​—Agal. 6:1.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuletsa munthu kuchita zinthu zina mumpingo kumasonyeza chikondi cha Mulungu?

6 Koma nthawi zina munthu akhoza kupatsidwa chilango osati kungolangizidwa. Mwachitsanzo, ngati munthu wachita tchimo lalikulu akhoza kuletsedwa kuti asamachite zinthu zina mumpingo. Komabe zinthu ngati zimenezi nazonso zimasonyeza chikondi cha Mulungu. Munthu akaletsedwa kuchita zinthu zina mumpingo, akhoza kuzindikira kufunika kokhala ndi nthawi yambiri yophunzira Baibulo, kusinkhasinkha komanso kupemphera. Zimenezi zingamuthandize kuti akhale wolimba mwauzimu. (Sal. 19:7) Pakapita nthawi, akhoza kuuzidwa kuti ayambirenso kuchita zimene analetsedwazo. Kuchotsa munthu mumpingo kumasonyezanso chikondi cha Yehova chifukwa mpingo umakhala wotetezeka. (1 Akor. 5:6, 7, 11) Mulungu amapereka chilango kwa munthu mogwirizana ndi zimene walakwitsa. Choncho munthu akachotsedwa mumpingo amatha kuzindikira kuti tchimo lake ndi lalikulu kwambiri ndipo akufunika kulapa.​—Mac. 3:19.

CHILANGO CHIMENE YEHOVA ANAMUPATSA CHINAMUTHANDIZA

7. Kodi Sebina anali ndani, nanga anali ndi vuto lotani?

7 Kuti timvetse ubwino wa chilango tiyeni tsopano tikambirane za anthu awiri amene Yehova anawapatsa chilango. Woyamba ndi Sebina, yemwe anakhalapo pa nthawi ya Mfumu Hezekiya, ndipo wachiwiri ndi Graham, yemwe ndi m’bale wamasiku ano. Sebina anali ndi udindo waukulu chifukwa Baibulo limanena kuti anali “kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu” ndipo mfumu yake iyenera kuti inali Hezekiya. (Yes. 22:15) Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anayamba kudzikuza ndipo ankafuna kuti anthu azimutama. Anafika mpaka podzipangira manda apamwamba ochita kugoba komanso ankayenda pa “magaleta ankhondo aulemerero.”​—Yes. 22:16-18.

Anthu amene amadzichepetsa n’kusintha maganizo amadalitsidwa (Onani ndime 8-10)

8. Kodi Yehova anathandiza bwanji Sebina ndipo zotsatira zake zinali zotani?

8 Mulungu ataona kuti Sebina ali ndi mtima wofuna kutamandidwa, ‘anamuchotsa pa udindo wake’ ndipo m’malomwake anaikapo Eliyakimu. (Yes. 22:19-21) Kusinthaku kunachitika pa nthawi imene Mfumu Senakeribu ankafuna kuwononga Yerusalemu. Patapita nthawi, mfumuyi inatuma akuluakulu a boma limodzi ndi asilikali ambiri kuti akaopseze Ayuda komanso akachititse Hezekiya kungonena kuti wagonja. (2 Maf. 18:17-25) Ndiyeno Eliyakimu ndi amene anatumidwa kuti akalankhule ndi anthuwo. Koma anapita ndi anthu ena awiri ndipo mmodzi mwa iwo anali Sebina, yemwe pa nthawiyo anali mlembi. Izitu zikusonyeza kuti Sebina sanakwiye koma anadzichepetsa n’kuvomera udindo wotsikirapo. Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhaniyi? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tikuphunzirapo.

9-11. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Sebina? (b) Kodi zimene Yehova anachitira Sebina zakulimbikitsani bwanji inuyo?

9 Choyamba, Sebina anachotsedwa pa udindo wake. Izi zikutsimikizira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.” (Miy. 16:18) Ngati muli ndi udindo woonekera mumpingo, kodi mudzayesetsa kukhala odzichepetsa? Kodi muzilemekeza Yehova chifukwa cha zabwino zimene muli nazo kapena zimene mwachita? (1 Akor. 4:7) Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.”​—Aroma 12:3.

10 Chachiwiri n’chakuti zimene Mulungu anachitira Sebina sizinkasonyeza kuti Sebinayo ndi wokanika. (Miy. 3:11, 12) Mfundo imeneyi ndi yothandiza kwa anthu amene aimitsidwa pa udindo masiku ano. M’malo mokwiya, ndi bwino kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse pa nthawi imeneyi n’kumaona kuti chilango chimene apatsidwacho ndi umboni wakuti Yehova amawakonda. Tisaiwale kuti Yehova sationa kuti ndife okanika ngati tili ndi mtima wodzichepetsa. (Werengani 1 Petulo 5:6, 7.) Nthawi zina Yehova amaumba anthu powapatsa chilango. Choncho tiyeni tizikhala ngati dongo loumbika m’manja mwake.

11 Chachitatu, zimene Yehova anachitira Sebina n’zothandiza kwa anthu amene ali ndi udindo wopereka chilango monga makolo ndi akulu. Tikutero chifukwa chakuti chilango cha Yehova chimasonyeza kuti amadana ndi zoipa koma pa nthawi imodzimodziyo chimasonyeza kuti amaganizira munthu amene walakwitsa zinthuyo. Choncho ngati ndinu makolo kapena mkulu, muyenera kutsanzira Yehova. Mukamapereka chilango muzisonyeza kuti mumadana ndi zoipa koma mumaona zabwino zimene mwana wanu kapena Mkhristu mnzanu amachita.​—Yuda 22, 23.

12-14. (a) Kodi anthu ena amatani akapatsidwa chilango? (b) Kodi Mawu a Mulungu anathandiza bwanji m’bale wina kusintha mtima umene anali nawo, nanga zotsatira zake zinali zotani?

12 Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena akapatsidwa chilango saona patali. Iwo amangoona kuti chilangocho n’chopweteka ndipo amasiya kukonda Mulungu ndi anthu ake. (Aheb. 3:12, 13) Koma kodi tingati anthu amenewa ndi okanika? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane chitsanzo cha m’bale wina dzina lake Graham. M’baleyu anachotsedwa ndipo patapita nthawi anabwezeretsedwa. Koma kenako anafooka kwambiri mwauzimu. Patapita zaka, m’baleyu anapempha mkulu amene ankacheza naye kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo.

13 Mkuluyo anati: “Vuto la Graham linali kudzikuza. Iye ankadana ndi akulu amene anasamalira nkhani yake pa nthawi imene anachotsedwa. Choncho maulendo angapo amene tinkaphunzira, tinakambirana malemba amene amafotokoza kwambiri za kunyada komanso zotsatira zake. Izi zinathandiza Graham kuti adziwe mmene Yehova ankamuonera. Zotsatira zake zinali zosangalatsa kwambiri. Iye anavomereza kuti mtima wodzikuza komanso wopezera ena zifukwa unali ngati mtanda wa denga umene unkaphimba maso ake ndipo anayamba kusintha kwambiri. Ankapezeka pamisonkhano yonse, kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama komanso kupemphera tsiku lililonse. Anayambanso kusamalira bwino banja lake moti mkazi ndi ana ake anayamba kusangalala.​—Luka 6:41, 42; Yak. 1:23-25.

14 Mkulu uja anati: “Tsiku lina Graham anandiuza mfundo ina imene inandisangalatsa kwambiri. Anati: ‘Ndakhala ndikudziwa choonadi kwa zaka zambiri ndipo ndatumikirapo ngati mpainiya. Koma kunena zoona, panopa m’pamene ndayamba kukonda Yehova.’ Pasanapite nthawi yaitali anapatsidwa mwayi woti aziyendetsa maikofoni m’Nyumba ya Ufumu ndipo anayamikira kwambiri mwayi umenewu. Izi zinandithandiza kudziwa kuti munthu akadzichepetsa pamaso pa Mulungu n’kulandira chilango, madalitso amangovumba ngati mvula.”

TIZITSANZIRA MULUNGU NDI KHRISTU POPEREKA MALANGIZO KAPENA CHILANGO

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kuti tizipereka malangizo abwino?

15 Kuti tikhale aphunzitsi abwino, tiyenera kuyamba ifeyo kuphunzira mwakhama. (1 Tim. 4:15, 16) N’chimodzimodzi ndi nkhani yopereka malangizo. Munthu amene ali ndi udindo wopereka malangizo ayenera kuyamba iyeyo kutsatira malangizo a Yehova ndi mtima wonse. Munthu akakhala wodzichepetsa n’kumamvera Yehova amalemekezedwa ndipo amakhala ndi ufulu wolankhula pophunzitsa ena komanso kuwalangiza. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Yesu.

16. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu pa nkhani yophunzitsa komanso kupereka malangizo?

16 Yesu ankamvera Atate wake ngakhale pamene kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri. (Mat. 26:39) Iye ankaphunzitsa bwino ndiponso ankachita zinthu mwanzeru koma ankaonetsetsa kuti ulemu wonse ukupita kwa Yehova. (Yoh. 5:19, 30) Popeza Yesu anali wodzichepetsa komanso womvera, anthu amaganizo abwino ankamukonda ndipo iye ankawachitira chifundo komanso kuwaphunzitsa mokoma mtima. (Werengani Mateyu 11:29.) Mawu ake okoma mtima ankalimbikitsa kwambiri anthu amene anali ngati bango lophwanyika komanso nyale yomwe yangotsala pang’ono kuzima. (Mat. 12:20) Yesu ankasonyezabe chikondi ndi kukoma mtima ngakhale pamene anthu achita zinthu zopsetsa mtima. Umboni wake ndi zimene anachita pothandiza atumwi ake omwe ankasonyeza mtima wonyada komanso wofuna maudindo.​—Maliko 9:33-37; Luka 22:24-27.

17. Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene angathandize anthu amene akuweta nkhosa za Mulungu?

17 Anthu onse amene ali ndi udindo wopereka malangizo a m’Malemba ayenera kutsanzira Yesu. Akamatero amasonyeza kuti akufunitsitsa kuti Mulungu ndi Mwana wake aziwaumba. Paja mtumwi Petulo analemba kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse. Osati mochita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa. Ndipo m’busa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira mphoto yosafwifwa, yaulemerero.” (1 Pet. 5:2-4) Mwachidule tingati oyang’anira amene amagonjera ulamuliro wa Mulungu ndi Yesu amakhala osangalala komanso amathandiza kwambiri anthu amene akuwayang’anira.​—Yes. 32:1, 2, 17, 18.

18. (a) Kodi Yehova amafuna kuti makolo azitani? (b) Kodi Mulungu amathandiza bwanji makolo kuti azikwaniritsa udindo wawo?

18 Mfundo zimene takambiranazi n’zothandizanso m’banja. Paja mitu ya mabanja imalangizidwa kuti: “Inunso abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Nkhani imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa chakuti lemba la Miyambo 19:18 limanena kuti: “Langa mwana wako padakali chiyembekezo, ndipo usalakelake imfa yake.” Palembali, mawu amene anawamasulira kuti “usalakelake imfa yake” amatanthauza kuti ‘usakhale ndi mlandu pa imfa yake.’ Choncho Yehova amaimba mlandu makolo amene amalephera kulanga mwana wawo. (1 Sam. 3:12-14) Koma Yehova amapereka mphamvu komanso nzeru kwa makolo amene amapemphera kwa iye modzichepetsa, kudalira Mawu ake ndiponso kulola kuti mzimu wake uziwatsogolera.​—Werengani Yakobo 1:5.

TIZIPHUNZIRA KUKHALA MWAMTENDERE MPAKA KALEKALE

19, 20. (a) Kodi munthu amadalitsidwa bwanji akalandira malangizo ochokera kwa Yehova? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

19 Pali madalitso ambiri amene tingapeze tikamatsatira malangizo a Mulungu komanso tikamatsanzira Yehova ndi Yesu popereka malangizo. Ubwino wina ndi wakuti m’mabanja ndi mumpingo mumakhala mtendere. Aliyense amaona kuti ndi wotetezeka komanso amazindikira kuti amakondedwa ndiponso amaonedwa kuti ndi wamtengo wapatali. Komatu uku n’kulawa chabe madalitso amene tidzakhale nawo m’tsogolo. (Sal. 72:7) Malangizo amene Yehova amatipatsa masiku ano amatiphunzitsa mmene tingakhalire mwamtendere mpaka kalekale. Pa nthawiyo tizidzakhala ngati banja logwirizana loyang’aniridwa ndi Atate wachikondi. (Werengani Yesaya 11:9.) Tikakhala ndi maganizo amenewa pa nkhani ya malangizo a Yehova sitidzakayikira mfundo yakuti Mulungu amatilangiza chifukwa chotikonda.

20 Munkhani yotsatira tidzaona mmene malangizo amathandizira m’banja komanso mumpingo. Tidzaona mmene munthu angasonyezere kudziletsa komanso tidzakambirana za chinthu china chopweteka kwambiri kuposa malangizo kapena chilango.