Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mverani Malangizo Kuti Mukhale Anzeru”

“Mverani Malangizo Kuti Mukhale Anzeru”

“Mverani malangizo kuti mukhale anzeru.”—MIY. 8:32, 33.

NYIMBO: 56, 89

1. Kodi chinthu china chimene chimatithandiza kukhala anzeru n’chiyani, nanga chimachitika n’chiyani munthu akakhala ndi nzeru zimenezi?

YEHOVA ndi wanzeru zopanda malire ndipo amapatsa ena nzeru. Paja lemba la Yakobo 1:5 limanena kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” Chinthu china chimene chimatithandiza kukhala anzeru ndi malangizo amene Yehova amatipatsa. (Miy. 2:10-12) Munthu akakhala ndi nzeru zimenezi amatetezeka ku zinthu zimene zingawononge makhalidwe ake abwino komanso moyo wake wauzimu. Ndipo chitetezo chimenechi n’chimene chimathandiza kuti Mulungu apitirize kutikonda.​—Yuda 21.

2. Kodi n’chiyani chingathandize kuti tiziyamikira malangizo a Yehova?

2 Ngakhale zili choncho, zinthu monga uchimo umene tinabadwa nawo, kumene tinakulira komanso mavuto ena, zimachititsa kuti tizivutika kulandira malangizo kapena kuona malangizowo m’njira yoyenera. Koma tikazindikira kuti Yehova amatipatsa malangizo chifukwa chotikonda timayamikira kwambiri malangizowo. Paja lemba la Miyambo 3:11, 12 limanena kuti: “Mwana wanga, usakane malangizo a Yehova . . . chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda.” Tisamaiwale kuti Yehova amatikonda ndipo amatifunira zabwino zokhazokha. (Werengani Aheberi 12:5-11.) Popeza Yehova amatidziwa bwino, amatipatsa malangizo kapena chilango m’njira yoyenera ndipo sapitirira malire. Tiyeni tikambirane zinthu 4 zokhudza malangizo kapena chilango. Tikambirana za (1) kudziletsa (2) kulera ana (3) kuthandiza anthu mumpingo ndiponso (4) chinthu chopweteka kwambiri kuposa chilango.

MUNTHU WANZERU AMADZILETSA

3. Kodi mwana angaphunzitsidwe bwanji kuti akhale wodziletsa? Perekani chitsanzo.

3 Munthu amene amadziletsa amayesetsa kuti asachite zinthu zolakwika komanso asinthe khalidwe ndi maganizo ake. Koma kudziletsa si khalidwe limene timabadwa nalo. Munthu amachita kuphunzira. Mwachitsanzo, mwana akamaphunzira kukwera njinga, bambo kapena mayi ake amagwirizira njingayo kuti asagwe. Kenako amayamba kumusiya pang’onopang’ono. Mwanayo akafika pozolowera amatha kumusiyiratu kuti aziyenda yekha. N’chimodzimodzi ndi kulera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Ana amafunika kuwathandiza kuti azitha kudziletsa n’cholinga choti akhale anzeru.

4, 5. (a) N’chifukwa chiyani kudziletsa n’kofunika kwambiri povala “umunthu watsopano”? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima ngakhale titakhala ngati ‘tagwa nthawi 7’?

4 Mfundo zimene takambiranazi zimagwiranso ntchito kwa anthu amene aphunzira za Yehova atakula kale. N’zoona kuti amakhala atayamba kudziletsa pa zinthu zina. Komabe mwauzimu tinganene kuti amakhalabe ana. Koma pang’ono ndi pang’ono akhoza kukula n’kumakhala ndi makhalidwe a Khristu. Apa zimakhala ngati akuvala “umunthu watsopano.” (Aef. 4:23, 24) Kuti avale umunthu watsopanowu ayenera kukhala odziletsa. Amafunika kuphunzira “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.”​—Tito 2:12.

5 Vuto lina ndi lakuti tonsefe ndi anthu ochimwa. (Mlal. 7:20) Koma sikuti munthu akangolakwitsa chinachake ndiye kuti basi ndi wokanika pa nkhani yodziletsa. Paja lemba la Miyambo 24:16 limanena kuti: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Ndiye kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asagwe ulesi akalakwitsa zinthu zina? Munthu sangathe kuchita zimenezi payekha koma mzimu wa Mulungu ndi umene ungatithandize. (Werengani Afilipi 4:13.) Ndipo khalidwe lina limene mzimuwo umatithandiza kukhala nalo ndi kudziletsa.

6. Kodi tingatani kuti tizikonda kuphunzira Mawu a Yehova? (Onani chithunzi choyambirira.)

6 Zinthu zina zimene zingatithandize kuti tizitha kudziletsa ndi kupemphera kuchokera pansi pa mtima, kuphunzira Baibulo ndiponso kuganizira kwambiri zimene tikuphunzira. Koma kodi tingatani ngati kuphunzira Mawu a Mulungu kumativuta? N’kutheka kuti mumaona kuti mulibe mtima wokonda kuphunzira. Koma dziwani kuti Yehova akhoza kukuthandizani ngati mungamulole kuti akuthandizeni. Iye angakuchititseni kuti “muzilakalaka” Mawu ake. (1 Pet. 2:2) Choyamba, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala odziletsa kuti muzipeza mpata wophunzira Mawu ake. Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi zimene mumapempha. Mwachitsanzo, muziphunzira Mawuwo mwina kwa nthawi yochepa chabe. Pakamapita nthawi, mwina kuphunzirako kungayambe kukusangalatsani ndipo simungaone kuti n’kovuta. Mukhoza kufika pomakonda kwambiri kukhala panokha n’kumaphunzira komanso kusinkhasinkha mfundo zamtengo wapatali zochokera kwa Yehova.​—1 Tim. 4:15.

7. Kodi kudziletsa kungatithandize bwanji kuti tikwaniritse zolinga zathu zauzimu?

7 Kudziletsa kungatithandizenso kuti tikwaniritse zolinga zathu zauzimu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene anazindikira kuti wayamba kuchita mphwayi potumikira Mulungu. Pofuna kuthana ndi vutoli, anaganiza zoti ayambe upainiya wokhazikika. Choncho anayamba kudziletsa kuti azipeza mpata woti aziwerenga nkhani zofotokoza za upainiya komanso kuipempherera nkhaniyi. Zimenezi zinamulimbikitsa komanso kumuthandiza kuti akhale wolimba mwauzimu. Kenako anayamba upainiya wothandiza. N’zoona kuti anakumana ndi mavuto ena koma sanasinthe maganizo ake ndipo pamapeto pake anakwanitsa kuyamba upainiya wokhazikika.

MUZILERA ANA ANU M’MALANGIZO A YEHOVA

Ana sabadwa ndi mtima wotha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika koma amafunika kuwaphunzitsa (Onani ndime 8)

8-10. N’chiyani chingathandize makolo achikhristu kuti aphunzitse bwino ana awo n’cholinga choti azitumikira Yehova? Perekani chitsanzo.

8 Makolo achikhristu ali ndi mwayi wamtengo wapatali wolera ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Koma kunena zoona, kuchita zimenezi masiku ano si kophweka. (2 Tim. 3:1-5) Ana sabadwa ndi mtima wotha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika. Iwo amangobadwa ndi chikumbumtima ndipo chimafunika kuphunzitsidwa bwino kuti akhale odziletsa. (Aroma 2:14, 15) Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti mawu amene anamasuliridwa kuti “malangizo” angamasuliridwenso kuti “zothandiza mwana kukula.”

9 Ana amene amapatsidwa malangizo oyenera amaona kuti ndi otetezeka. Amadziwa kuti ufulu wawo uli ndi malire ndipo zimene amachita zingakhale ndi zotsatirapo zake, zabwino kapena zoipa. Choncho ndi bwino kuti makolo achikhristu azidalira malangizo a Yehova. Chinthu china chofunika kuchikumbukira n’chakuti maganizo a anthu komanso njira zolerera ana zimakhala zosiyana malinga ndi chikhalidwe komanso zimasintha pakapita nthawi. Koma malangizo a Yehova amathandiza kuti makolo azidziwa zochita polera ana ndipo sadalira nzeru za anthu.

10 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Nowa. Mulungu anamuuza kuti agwire ntchito yomanga chingalawa yomwe anali asanaigwirepo. Choncho iye ankadalira Yehova ndipo “anachita momwemo,” kutanthauza kuti anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. (Gen. 6:22) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anapanga bwinobwino chingalawacho popanda kulakwitsa kalikonse. Nowa ankasamaliranso bwino banja lake chifukwa chakuti ankadalira nzeru zochokera kwa Mulungu. Nzeru zimenezi zinkamuthandiza kuti aphunzitse bwino ana ake komanso aziwapatsa chitsanzo chabwino ngakhale kuti moyo pa nthawiyo unali wovuta kwambiri.​—Gen. 6:5.

11. Kodi chitsanzo cha makolo n’chofunika bwanji kwa ana?

11 Ngati ndinu makolo, kodi mungatani kuti muzichita zonse zimene Mulungu wakulamulani? Chofunika ndi kutsatira malangizo ake. Malangizo olerera ana mungawapeze m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Mukatero ana anu adzakuthokozani kwambiri. M’bale wina analemba kuti: “Ndimathokoza kwambiri makolo anga chifukwa anandilera bwino. Iwo ankachita zonse zimene angathe kuti andifike pamtima. Kunena zoona, iwowo ndi amene andithandiza kuti ndikule bwino mwauzimu.” Koma ana ena amasiya Yehova ngakhale kuti makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa bwino. Makolo a ana oterewa sayenera kudziimba mlandu chifukwa anachita zonse zimene akanatha. Chofunika n’kukhala ndi chiyembekezo choti tsiku lina mwana wolowererayo adzabwerera kwa Yehova.

12, 13. (a) Kodi makolo angasonyeze bwanji kuti amamvera Yehova ngati mwana wawo wachotsedwa? (b) Kodi kumvera Yehova kunathandiza bwanji makolo ena?

12 Chikhulupiriro cha makolo ena chimayesedwa mwana wawo akachotsedwa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene mwana wake wamkazi anachotsedwa n’kuchoka pakhomo. Mlongoyu anati: “Ndinkayesetsa kufufuza zifukwa m’mabuku athu zondichititsa kuti ndizichezabe ndi mwana wanga komanso chidzukulu changa. Koma mwamuna wanga anandithandiza mokoma mtima kuzindikira kuti pa nthawiyo mwana wathu sanalinso m’manja mwathu choncho tisadzilowetse m’mavuto.”

13 Patapita zaka zingapo, mwana wawoyo anabwezeretsedwa. Mlongoyu anati: “Panopa amandiimbira foni kapena kundilembera meseji tsiku lililonse. Makolofe amatilemekeza kwambiri chifukwa choti tinayesetsa kumvera Mulungu. Kunena zoona timagwirizana kwambiri.” Ngati mwana wanu wachotsedwa, kodi ‘mudzakhulupirira Yehova ndi mtima wanu wonse n’kumapewa kudalira luso lanu lomvetsa zinthu?’ (Miy. 3:5, 6) Tisamaiwale kuti Yehova amapereka malangizo komanso chilango mwachikondi komanso mwanzeru. Tizikumbukiranso kuti iye anapereka Mwana wake kuti afere anthu onse kuphatikizapo mwana wanuyo. Iye safuna kuti aliyense awonongedwe. (Werengani 2 Petulo 3:9.) Choncho musamakayikire malangizo komanso chilango chake. Muzimvera Yehova ngakhale pamene kuchita zimenezi n’kopweteka kwambiri. Tiyeni tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo a Yehova osati motsutsana nawo.

MALANGIZO AMENE TIMALANDIRA MUMPINGO

14. Kodi malangizo amene Yehova amapereka kudzera mwa kapolo wokhulupirika amatithandiza bwanji?

14 Yehova analonjeza kuti azisamalira, kuteteza komanso kulangiza mpingo wachikhristu. Iye amachita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, anapereka mpingo m’manja mwa Mwana wake ndipo Mwana wakeyo anaika kapolo wokhulupirika kuti azipereka chakudya pa nthawi yoyenera. (Luka 12:42) Chakudyachi chimaperekedwa m’njira zosiyanasiyana ndipo n’chothandiza kwambiri. Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi kangati pamene nkhani imene inakambidwa kapena imene inatuluka m’magazini inandithandiza kuti ndisinthe maganizo kapena khalidwe langa?’ Ngati munamvera n’kusintha muyenera kusangalala kwambiri. Umenewu ndi umboni woti mukulola Yehova kuti azikuumbani komanso kukulangizani kuti zinthu zikuyendereni bwino.​—Miy. 2:1-5.

15, 16. (a) Kodi tingatani kuti tizipindula ndi “mphatso za amuna” mumpingo? (b) Kodi tingathandize bwanji akulu kuti azigwira ntchito yawo mosangalala?

15 Khristu anaperekanso “mphatso za amuna” omwe ndi akulu amene amaweta nkhosa za Mulungu. (Aef. 4:8, 11-13) Kodi tingatani kuti mphatso zimenezi zizitithandiza? Choyamba, tiyenera kutsanzira chikhulupiriro komanso chitsanzo chabwino cha akuluwo. Njira ina ndi kutsatira malangizo amene amatipatsa. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Tizikumbukira kuti akulu amatikonda ndipo amafuna kuti tizikula mwauzimu. Mwachitsanzo, akaona kuti tayamba kuphonya misonkhano kapena sitikuchitanso zinthu mwakhama amatithandiza mwamsanga. Iwo amamvetsera mavuto athu, kutilimbikitsa ndi malemba oyenerera komanso kutipatsa malangizo othandiza. Kodi inuyo mumaona kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova amakukondani?

16 Tisaiwale kuti sizikhala zophweka kuti akulu abwere kudzatipatsa malangizo. Mwachitsanzo, mukuganiza kuti Natani anamva bwanji pamene Mfumu Davide ankabisa tchimo lake ndipo Nataniyo ankafunika kukamulangiza? (2 Sam. 12:1-14) Nayenso Paulo anafunika kulimba mtima kwambiri kuti adzudzule mtumwi Petulo pa nthawi imene anachita zinthu zokondera Ayuda. (Agal. 2:11-14) Ndiye kodi tingatani kuti tiziwapeputsira akulu ntchito yawo mumpingo? Tiyenera kukhala odzichepetsa, omasuka komanso oyamikira. Tiziona kuti thandizo lililonse limene angatipatse likuchokera kwa Yehova. Tikamatero zinthu zidzatiyendera bwino komanso tidzathandiza kuti akuluwo azigwira ntchito yawo mosangalala.

17. Kodi mlongo wina anathandizidwa bwanji ndi akulu?

17 Mlongo wina ankavutika kukonda Yehova chifukwa cha zimene zinamuchitikira pa moyo wake. Mlongoyu anati: “Mavuto amene ndinakumana nawo akayamba kubwera m’mutumu, ndinkadziwa kuti ndiyenera kulankhula ndi akulu. Iwo sankandinyoza kapena kundidzudzula, koma ankandilimbikitsa kwambiri. Misonkhano ikatha, mkulu wina ankabwera n’kundifunsa mmene zinthu zilili. Mavuto amene ndinakumana nawo pa moyo ankandichititsa kuti ndizikayikira zoti Mulungu angandikonde. Koma nthawi ndi nthawi, Yehova ankagwiritsa ntchito abale ndi alongo komanso akulu kuti anditsimikizire zoti amandikonda. Ndimapemphera kuti zivute zitani ndisadzasiye Yehova.”

CHINTHU CHOPWETEKA KWAMBIRI KUPOSA CHILANGO

18, 19. Kodi chinthu chopweteka kwambiri kuposa mmene amapwetekera malangizo n’chiyani? Perekani chitsanzo.

18 N’zoona kuti chilango chimapweteka, koma pali chinthu china chopweteka kwambiri kuposa chilango. Chinthu chake ndi mavuto amene amabwera chifukwa chosamvera malangizo. (Aheb. 12:11) Kuti timvetse mfundoyi, tiyeni tikambirane chitsanzo cha Kaini ndi Mfumu Zedekiya. Kaini atakwiya n’kumafuna kupha m’bale wake, Yehova anamulangiza kuti: “N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji? Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Kaini sanamvere malangizowa moti uchimo unamugonjetsa. Ndipo zotsatira zake zinali zopweteka kwambiri kuposa mmene anamupwetekera malangizo amene Yehova anamupatsa.​—Gen. 4:11, 12.

19 Mfumu Zedekiya analamulira pa nthawi imene zinthu sizinali bwino mu Yerusalemu. Mneneri Yeremiya anachenjeza Zedekiya mobwerezabwereza kuti asinthe koma sanamvere. Zotsatira zake zinalinso zopweteka kwambiri. (Yer. 52:8-11) Yehova safuna kuti ifeyo tikumane ndi zinthu zopweteka ngati zimenezi.​—Werengani Yesaya 48:17, 18.

20. Kodi anthu amene amamvera malangizo zidzawayendera bwanji, nanga amene samvera zidzawathera bwanji?

20 M’dzikoli anthu ambiri ali ndi mtima wosafuna kulangizidwa komanso kudziletsa. Koma tsiku lina mtima wopusawu udzawabweretsera mavuto aakulu. (Miy. 1:24-31) Choncho tiyeni ifeyo ‘tizimvera malangizo kuti tikhale anzeru.’ Tizitsatira lemba la Miyambo 4:13 lomwe limati: “Gwira malangizo, usawataye. Uwasunge bwino chifukwa iwo ndiwo moyo wako.”