Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”

“Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”

“Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.”—YAK. 1:4.

NYIMBO: 135, 139

1, 2. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Gidiyoni ndi asilikali ake 300 anachita? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Mogwirizana ndi lemba la Luka 21:19, n’chifukwa chiyani tiyenera kupirira?

NKHONDO ya pakati pa Aisiraeli ndi Amidiyani inali itafika poipa kwambiri. Asilikali achiisiraeli omwe ankatsogoleredwa ndi Gidiyoni anathamangitsa adani awowo usiku wonse kwa mtunda wamakilomita pafupifupi 32. Baibulo limati: “Kenako, Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja, ali otopa.” Komabe Gidiyoni ndi asilikali akewo anali asanapambane nkhondoyo chifukwa adani okwana 15,000 anali adakalipo. Aisiraeli anali ataponderezedwa ndi a Midiyani kwa zaka zambiri ndipo ankadziwa kuti iyi sinali nthawi yoti asiye kumenya nkhondo. Choncho, anapitirizabe ‘kuthamangitsa’ a Midiyani mpaka kuwagonjetsa.—Ower. 7:22; 8:4, 10, 28.

2 Masiku ano nafenso tikumenya nkhondo yovuta kwambiri. Tikulimbana ndi Satana, dziko loipali komanso matupi athu ochimwawa. Ambirife tamenya nkhondoyi kwa zaka zambiri ndipo Yehova wakhala akutithandiza. Komabe nthawi zina tingaone kuti tatopa kumenyana ndi adani athu ndiponso kuyembekezera mapeto a dziko loipali. Komatu tiyenera kupitirizabe chifukwa nkhondoyi idakalipo. Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza ano tidzakumana ndi mayesero ndi mavuto ambiri. Koma ananenanso kuti tikhoza kupambana ngati titapirira. (Werengani Luka 21:19.) Kodi kupirira n’kutani? Nanga n’chiyani chingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto? Kodi tingaphunzire chiyani kwa anthu akale amene anapirira? Nanga kodi tingalole bwanji kuti “kupirira kumalize kugwira ntchito yake”?—Yak. 1:4.

KODI KUPIRIRA N’KUTANI?

3. Kodi kupirira n’kutani?

3 M’Baibulo, mawu akuti kupirira amatanthauza zambiri. Mawuwa amatanthauza zimene timaganiza komanso zimene timachita tikakumana ndi mavuto. Munthu wopirira amakhala wolimba mtima, wokhulupirika komanso woleza mtima. Buku lina linati kupirira “n’kukhala ndi mtima wosagonja ukakumana ndi mavuto chifukwa chakuti uli ndi chikhulupiriro cholimba. Khalidweli limathandiza munthu kukhalabe wolimba pamene akukumana ndi mavuto. Munthu wopirira saganizira kwambiri za mavuto amene akukumana nawo koma amaganizira za madalitso amene angapeze akapirira mavutowo.”

4. N’chifukwa chiyani tingati chikondi ndi chimene chimathandiza Akhristu kuti azipirira?

4 Akhristufe timapirira chifukwa cha chikondi. (Werengani 1 Akorinto 13:4, 7.) Popeza timakonda Yehova, timapirira mavuto onse amene timakumana nawo pochita chifuniro chake. (Luka 22:41, 42) Abale ndi alongo athu akatilakwira chifukwa choti si angwiro, timapirira chifukwa choti timawakonda. (1 Pet. 4:8) Komanso kukonda mwamuna kapena mkazi wathu kumatithandiza kuti tizipirira ‘masautso’ alionse amene tingakumane nawo m’banja. Kumatithandizanso kuti tiziyesetsa kulimbitsa banja lathu.—1 Akor. 7:28.

KODI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI KUPIRIRA?

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi amene angatithandize kwambiri kupirira?

5 Muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. Malemba amati Yehova ‘amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amatitonthoza.’ (Aroma 15:5) Iye amadziwa chibadwa chathu komanso zimene tikukumana nazo ndipo amamvetsa mmene tikumvera. Amadziwanso bwino zinthu zimene zingatithandize. Paja Baibulo limanena kuti: “Anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Sal. 145:19) Koma kodi Mulungu amayankha bwanji tikamupempha kuti atipatse mphamvu?

6. Kodi Yehova amapereka bwanji “njira yopulumukira?”

6 Werengani 1 Akorinto 10:13. Tikapempha Yehova kuti atithandize kupirira mayesero, iye ‘amapereka njira yopulumukira.’ Kodi ndiye kuti Yehova amachotsa mayesero athuwo? Nthawi zina amachotsadi. Koma nthawi zambiri amangotithandiza kuti ‘tithe kuwapirira.’ Yehova amatipatsa mphamvu kuti ‘tithe kupirira zinthu zonse, tikhale oleza mtima ndiponso tikhale achimwemwe.’ (Akol. 1:11) Popeza amadziwa zinthu zimene sitingakwanitse, sangalole kuti vuto likule kwambiri mpaka kufika poti sitingathe kukhalabe okhulupirika.

7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu kumathandiza kuti tipirire?

7 Muziphunzira Mawu a Mulungu kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Munthu amene akufuna kukwera phiri la Everest, lomwe ndi lalitali kwambiri padziko lonse, amafunika mphamvu zambiri. Choncho kuti akweredi amafunika kudya chakudya chambiri chopatsa mphamvu. Kuti ifenso tithe kupirira mayesero amene timakumana nawo tiyenera kuphunzira kwambiri Mawu a Mulungu. Timafunika kudziletsa zinthu zina n’cholinga choti tipeze nthawi yowerenga, kuphunzira komanso kusonkhana. Tikamachita zimenezi timapeza “chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.”—Yoh. 6:27.

8, 9. (a) Malinga ndi lemba la Yobu 2:4 ndi 5, kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikakumana ndi mayesero? (b) Mukakumana ndi mayesero, kodi muyenera kuyerekezera kuti mukuona ndani?

8 Muzikumbukira kuti kukhala okhulupirika n’kofunika kwambiri. Tikakumana ndi mayesero tiyenera kukumbukira kuti zimene tingachite zingasonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova kapena ayi. Zimene tingachitezo zimasonyezanso ngati timaonadi kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Kumbukirani kuti Satana ananyoza Yehova ponena kuti: “Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” Paja ponena za Yobu iye anauza Yehova kuti: “Tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!” (Yobu 2:4, 5) Ponena zimenezi, Satana ankatanthauza kuti palibe munthu amene amatumikira Yehova chifukwa chomukonda. Maganizo amenewa adakali nawobe mpaka pano. Tikutero chifukwa chakuti patapita zaka zambiri, iye anathamangitsidwa kumwamba ndipo pa nthawiyo n’kuti akupitirizabe kuneneza atumiki a Mulungu okhulupirika “usana ndi usiku.” (Chiv. 12:10) Choncho Satana amaonabe kuti anthufe sitingakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati titakumana ndi mavuto. Amafunitsitsa kutiona titasiya kumvera Yehova ndiponso kumutumikira.

9 Choncho mukakumana ndi mavuto muziyerekezera kuti mukuona magulu awiri. Mbali ina kuli Satana ndi ziwanda zake ndipo akunena kuti mavutowo akakupanikizani musiya kutumikira Yehova. Mbali ina kuli Yehova, Yesu, angelo ndiponso odzozedwa amene anaukitsidwa ndipo onse akukuchemererani. Iwo akusangalala chifukwa choti tsiku lililonse mukuyesetsa kupirira ndipo mukusonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ndiyeno mukumva Yehovayo akukuuzani kuti: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.

10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikakumana ndi mavuto?

10 Muziganizira madalitso amene mudzalandire mukapirira. Tiyerekezere kuti mukuoloka mtsinje waukulu ndipo mwafika pakati pa mtsinjewo. Mukayang’ana kutsogolo mukuona kuti padakali mtunda wautali kuti mukafike kutsidya. Koma simukubwerera m’mbuyo chifukwa muli ndi chikhulupiriro kuti mukapitiriza kuoloka, mufika kumtunda. Mavuto amene timakumana nawo angafanane ndi zimenezi. Yesu atakumana ndi mavuto anamvanso chimodzimodzi. Iye ananyozedwa komanso anamva ululu kwambiri atakhomeredwa pamtengo. Koma kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Baibulo limati iye ankaona “chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake.” (Aheb. 12:2, 3) Ankaganizira madalitso amene adzapeze akapirira. Ankaona kuti kupirira kwake kuthandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe komanso kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. Ankadziwanso kuti mavutowo ndi akanthawi koma madalitso amene adzapeze ndi amuyaya. Masiku ano nafenso tingakumane ndi mavuto aakulu koma tizikumbukira kuti mavutowa ndi akanthawi.

“AMENE ANAPIRIRA”

11. Kodi kuganizira zitsanzo za “anthu amene anapirira” kungatithandize bwanji?

11 Tiyenera kukumbukira kuti si ife tokha amene tikukumana ndi mayesero. Paja Petulo analimbikitsa Akhristu amene ankakumana ndi mayesero kuti apirire. Iye anawauza kuti: “Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye, podziwa kuti anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumana ndi masautso ngati omwewo.” (1 Pet. 5:9) Zitsanzo za “amene anapirira” zimatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti nafenso tipirire. Zimatitsimikiziranso kuti nafenso tingathe kupirira ndipo tidzadalitsidwa tikakhalabe okhulupirika. (Yak. 5:11) Tiyeni tsopano tikambirane zitsanzo zingapo. [1]

12. Kodi tikuphunzira chiyani kwa akerubi amene ankalondera munda wa Edeni?

12 Akerubi. Adamu ndi Hava atachimwa, Yehova ‘anaika akerubi kum’mawa kwa munda wa Edeni. Anaikanso lupanga loyaka moto limene linali kuzungulira mosalekeza potchinga njira yopita kumtengo wa moyo.’ [2] (Gen. 3:24) Zimene akerubiwa anachita zingatithandize kuti nafenso tizipirira tikapatsidwa ntchito yovuta potumikira Mulungu. Mulungu sanalenge akerubi kuti azigwira ntchito yolonderayi ndipo sichinali cholinga chake kuti anthu adzachimwe. Koma Adamu ndi Hava atachimwa akerubiwa anagwira ntchitoyi mosanyinyirika. Anachita zimenezi ngakhale kuti anali ndi udindo waukulu kwambiri kumwamba. Iwo anagwira ntchitoyi mokhulupirika mpaka mapeto. N’kutheka kuti anaigwira kwa zaka zoposa 1,600 ndipo inatha pa nthawi ya Chigumula.

13. Kodi n’chiyani chinathandiza Yobu kuti apirire mayesero amene anakumana nawo?

13 Yobu. Zimakhala zowawa kwambiri ngati mnzathu kapena wachibale watilankhula mawu opweteka, ngati tikudwala matenda aakulu kapena ngati munthu amene timamukonda wamwalira. Koma chitsanzo cha Yobu chikhoza kutilimbikitsa zoterezi zikachitika. (Yobu 1:18, 19; 2:7, 9; 19:1-3) Yobu sankadziwa chimene chinayambitsa mavuto ake koma anakhalabe wokhulupirika. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? N’chifukwa chakuti ‘ankaopa Mulungu.’ (Yobu 1:1) Yobu ankafunitsitsa kusangalatsa Yehova zivute zitani. Yehova anamuthandiza ndipo iye ankaganizira zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova anachita pogwiritsa ntchito mzimu woyera. Yobu ankadziwa kuti Yehova adzathetsa mavuto akewo pa nthawi yoyenera. (Yobu 42:1, 2) Ndipo izi n’zimene zinachitikadi. Baibulo limanena kuti: ‘Yehova anathetsa masautso a Yobu ndipo anayamba kum’patsa zonse zimene anali nazo, kuwirikiza kawiri.’ Limanenanso kuti Yobu “anamwalira ali wokalamba ndiponso wokhutira ndi masiku ake.”—Yobu 42:10, 17.

14. Kodi lemba la 2 Akorinto 1:6 likusonyeza kuti kupirira kwa Paulo kunathandiza bwanji Akhristu anzake?

14 Mtumwi Paulo. Kodi mukuzunzidwa chifukwa chotumikira Mulungu? Kodi ndinu mkulu kapena woyang’anira dera ndipo mukuona kuti muli ndi ntchito yambiri? Chitsanzo cha Paulo chingakuthandizeni. Iye anakumana ndi mavuto aakulu ochokera kwa adani ake komanso ankadera nkhawa kwambiri za abale ndi alongo a m’mipingo yonse. (2 Akor. 11:23-29) Koma Paulo sanafooke ndipo chitsanzo chake chinalimbikitsanso ena. (Werengani 2 Akorinto 1:6.) Ngati inunso mukukumana ndi mavuto enaake, dziwani kuti mukakhalabe okhulupirika mukhoza kulimbikitsa Akhristu anzanu.

KODI MUMALOLA KUTI “KUPIRIRA KUMALIZE KUGWIRA NTCHITO YAKE”?

15, 16. (a) Kodi kupirira kumamaliza kugwira “ntchito” yotani? (b) Kodi tingatani “kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake”? Perekani zitsanzo.

15 Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake.” Kodi kupirira kumamaliza kugwira “ntchito” iti? Kumatithandiza kukhala “okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.” (Yak. 1:4) Mayesero amatithandiza kudziwa mbali zimene sitichita bwino. Koma tikapirira mayeserowo tingati timakhala okwanira mbali zonse. Mwachitsanzo, tikakumana ndi mayesero n’kupirira, timaphunzira kukhala oleza mtima, oyamikira komanso achifundo.

Tikapirira mayesero timaphunzira makhalidwe abwino (Onani ndime 15 ndi 16)

16 Kupirira kumatithandiza kuti tikhale Akhristu okhulupirika. Choncho tikakumana ndi mayesero tisamagonje n’kusiya kutsatira mfundo za m’Baibulo n’cholinga choti mavuto athuwo athe. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mukuyesetsa kuti musamaganizire zinthu zoipa? Simuyenera kugonja. M’malomwake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni kuthana ndi vutolo. Zikatere mumaphunzira kukhala odziletsa kwambiri. Nanga mungatani ngati mukutsutsidwa ndi wachibale wanu amene si wa Mboni? Musagonje ndipo pitirizani kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Zimenezi zingachititse kuti muzidalira kwambiri Yehova. Musaiwale kuti tikamapirira mayesero, Yehova amatidalitsa.—Aroma 5:3-5; Yak. 1:12.

17, 18. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tiyenera kupirira mpaka mapeto. (b) Kodi tisamakayikire za chiyani masiku otsiriza ano?

17 Tiyenera kupirira osati kwa kanthawi chabe, koma mpaka mapeto. Tiyerekeze kuti anthu akwera sitima ndipo ikumira. Kuti munthu apulumuke, ayenera kusambira mpaka kumtunda. Ngati munthu wasambira kwa nthawi yaitali koma n’kutopa atatsala pang’ono kufika pamtunda akhoza kufa mofanana ndi munthu amene anangosambira pang’ono n’kusiya. Mofanana ndi zimenezi, kuti tidzalowe m’dziko latsopano tiyenera kupirira mpaka mapeto. Tiyenera kukhala ndi maganizo amene mtumwi Paulo anali nawo. Kawiri konse iye anati: “Sitikubwerera m’mbuyo.”—2 Akor. 4:1, 16.

18 Tisamakayikire kuti Yehova atithandiza kupirira mpaka mapeto. Paja Paulo ananena kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzera mwa iye amene anatikonda. Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu, msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:37-39) N’zoona kuti nthawi zina timatopa, koma tiyeni tipitirize kupirira mpaka mapeto. Tikatero nafenso tidzakhala ngati Gidiyoni ndi asilikali ake amene anapitirizabe ‘kuthamangitsa adani awo.’—Ower. 8:4.

^ [1] (ndime 11) Kuganizira zitsanzo za anthu amene apirira masiku ano kukhoza kukuthandizaninso. Mwachitsanzo mungawerenge Buku Lapachaka lachingelezi la 1992, 1999, ndi la 2008 komanso kabuku kakuti, Mboni za Yehova M’Malawi kuti mumve za abale athu amene anapirira ku Ethiopia, ku Malawi ndi ku Russia.

^ [2] (ndime 12) Baibulo silitchula kuti akerubi amene ankalondera mundawu analipo angati.