Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika

Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika

“Mukhale otsanzira anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza monga cholowa chawo.”—AHEB. 6:12.

NYIMBO: 86, 54

1, 2. Kodi n’chiyani chinachitikira Yefita ndi mwana wake?

PA NTHAWI ina Yefita atapita kunkhondo mwana wake wamkazi ankangoyembekezera kuti bambo akewo abwerako liti. Kenako mwanayo anawaona akubwera ndipo anasangalala kwambiri chifukwa iwo anapambana pa nkhondoyo. Nthawi yomweyo ananyamuka kukawachingamira akuvina. Koma bambo akewo atamuona anayamba kung’amba zovala zawo n’kunena kuti: “Kalanga ine mwana wanga! Wandiweramitsa ndi chisoni.” Kenako Yefita ananena mawu osonyeza kuti tsogolo la mwana wakeyo lisinthiratu. Koma mwanayo anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa anauza bambo akewo kuti atsatire zimene analonjeza Mulungu. Iye ankakhulupirira kuti zonse zimene Yehova anganene ndi zoyenera kwa iyeyo. (Ower. 11:34-37) Zimene anachitazi zinasangalatsa kwambiri Yefita chifukwa anadziwa kuti Yehova awadalitsa.

2 Yefita komanso mwana wake ankakhulupirira kwambiri Yehova ngakhale pa nthawi yovuta. Iwo ankaona kuti chofunika kwambiri ndi kusangalatsa Mulungu.

3. Kodi zimene Yefita ndi mwana wake anachita zingatithandize bwanji?

3 Kukhala ndi chikhulupiriro cholimba si kophweka. Pamafunika “kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro.” (Yuda 3) Yefita ndi mwana wake anakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Tiyeni tikambirane mavuto amene iwo anakumana nawo. Izi zitithandiza kuti nafenso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.

ANAKHALABE OKHULUPIRIKA M’DZIKO LOIPA

4, 5. (a) Kodi Yehova anapereka lamulo liti kwa Aisiraeli pamene ankalowa m’Dziko Lolonjezedwa? (b) Malinga ndi Salimo 106, kodi kusamvera kwa Aisiraeli kunabweretsa mavuto otani?

4 Yefita ndi mwana wake ankaona mavuto amene anabwera chifukwa choti Aisiraeli anasiya Yehova. M’mbuyomo, Aisiraeli anauzidwa kuti awononge anthu onse osalambira Yehova amene ankakhala m’Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 7:1-4) Koma iwo sanachite zimenezi ndipo anayamba kulambira mafano komanso kutengera makhalidwe oipa a Akanani.​—Werengani Salimo 106:34-39.

5 Izi zinakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo anasiya kuwateteza. (Ower. 2:1-3, 11-15; Sal. 106:40-43) Pa nthawiyi, zinali zovuta kuti mabanja oopa Mulungu akhalebe okhulupirika. Koma Baibulo limasonyeza kuti panali anthu ena okhulupirika amene ankasangalatsa Mulungu. Anthu ake ndi monga Elikana, Hana, Samueli ndiponso Yefita ndi mwana wake.—1 Sam. 1:20-28; 2:26.

6. Kodi masiku ano anthu amakonda chiyani, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?

6 Anthu ambiri m’dzikoli amachita zinthu ngati Akanani akale ndipo amakonda chiwerewere komanso chuma. Koma mofanana ndi Aisiraeli, Yehova watipatsa malangizo oti azititeteza. Choncho tiyenera kupewa zinthu zolakwika zimene Aisiraeli ankachita. (1 Akor. 10:6-11) Komanso tiyenera kusamala kuti tisayambe kuchita zinthu ngati Akanani. (Aroma 12:2) Kodi inuyo mukuyesetsa kuchita zimenezi?

ANAKHALABE WOKHULUPIRIKA ATAKUMANA NDI MAVUTO

7. (a) Kodi anthu anamuchitira zotani Yefita? (b) Kodi Yefita anatani?

7 M’masiku a Yefita, kusamvera kwa Aisiraeli kunachititsa kuti akhale akapolo a Afilisiti komanso Aamoni. (Ower. 10:7, 8) Kuwonjezera pamenepa, Yefita ankavutitsidwa ndi anthu amene ankatsogolera Aisiraeli komanso abale ake. Mwachitsanzo, abale ake ena anamuthamangitsa chifukwa choti anali mwana wa mayi wina. Anati sankayenera kulandira cholowa ngati mwana woyamba kubadwa. (Ower. 11:1-3) Yefita sanalole kuti zochita za abale akewa zimusokoneze. Tikutero chifukwa atapemphedwa kuti akathandize abale akewo, anapita mosanyinyirika. (Ower. 11:4-11) Kodi n’chiyani chinathandiza Yefita kuti achite zonsezi bwinobwino?

8, 9. (a) Kodi ndi mfundo ziti za m’Chilamulo zimene zinamuthandiza Yefita? (b) Kodi Yefita ankaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani?

8 N’zoona kuti Yefita anali msilikali wamphamvu, koma ankaphunziranso zimene Mulungu anachitira anthu ake. Iye ankadziwa bwino mbiri ya Aisiraeli ndipo ankazindikira zinthu zoyenera ndi zosayenera pamaso pa Yehova. (Ower. 11:12-27) Yefita akamasankha zochita ankatsatira mfundo za m’Chilamulo. Ankadziwa kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikondana osati kusungirana zifukwa. Chilamulo chinkanena kuti munthu ayenera kuthandiza anzake ngakhalenso anthu amene amadana naye.​—Werengani Ekisodo 23:5; Levitiko 19:17, 18.

9 Yefita ayenera kuti ankaganizira chitsanzo cha anthu ngati Yosefe. Paja Yosefe anathandiza abale ake ngakhale kuti ‘ankadana naye.’ (Gen. 37:4; 45:4, 5) Kuganizira zimenezi kunathandiza Yefita kuti achite zinthu zosangalatsa Yehova. Zimene abale ake anamuchitira ziyenera kuti zinamuwawa kwambiri, komabe sizinamulepheretse kutumikira Yehova komanso anthu ake. (Ower. 11:9) Iye ankaona kuti kumenya nkhondo poyeretsa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri kusiyana ndi kulimbana ndi abale akewo. Ankafunitsitsa kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwa iyeyo komanso kwa anthu ena.—Aheb. 11:32, 33.

10. Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji pamene ena atilakwira?

10 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yefita anachita? Mwina pali Mkhristu wina amene anakulakwirani kapena kukukhumudwitsani. Ngati ndi choncho, musalole kuti nkhani imeneyo ikulepheretseni kusonkhana kapena kutumikira Yehova limodzi ndi mpingo. Potengera chitsanzo cha Yefita, tizitsatira mfundo za Yehova n’kumachitabe zabwino ngakhale titakumana ndi mavuto.—Aroma 12:20, 21; Akol. 3:13.

MUNTHU WODZIPEREKA AMASONYEZA KUTI ALI NDI CHIKHULUPIRIRO

11, 12. Kodi Yefita analonjeza chiyani kwa Yehova, nanga zimene analonjezazo zinkatanthauza chiyani?

11 Yefita ankadziwa kuti akufunika thandizo la Yehova kuti apulumutse Aisiraeli m’manja mwa Aamoni. Iye analonjeza Yehova kuti: ‘Ndidzapereka aliyense amene adzatuluke m’nyumba yanga kudzandichingamira pamene ndikubwera mwamtendere kuchokera kwa ana a Amoni. Ndidzam’pereka monga nsembe yopsereza.’ (Ower. 11:30, 31) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani?

12 Yehova amadana ndi kupha anthu n’cholinga choti aperekedwe nsembe. Choncho Yefita sankafuna kupha aliyense n’kumupereka nsembe. (Deut. 18:9, 10) Aisiraeli analamulidwa kuti azipereka nyama yathunthu ngati nsembe yopsereza. Choncho Yefita ankatanthauza kuti munthu amene adzamuchingamireyo adzatumikira pachihema cha Yehova kwa moyo wake wonse. Yehova anamva pemphero la Yefita ndipo anamuthandiza kugonjetsa adani ake onse. (Ower. 11:32, 33) Koma kodi Yefita akanapereka ndani kuti akhale ngati “nsembe yopsereza”?

13, 14. Kodi mawu a pa Oweruza 11:35 akusonyeza bwanji kuti Yefita anali ndi chikhulupiriro cholimba?

13 M’ndime yoyamba ija tanena kuti pamene Yefita ankabwera, mwana wake wamkazi ndi amene anamuchingamira. Apa tsopano zinthu zinavuta chifukwa mwana wake anali yekhayo. Ndiye kodi Yefita anatani? Kodi anaperekadi mwana wakeyu kuti akatumikire pachihema moyo wake wonse?

14 Apanso Yefita anagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kuti adziwe zoyenera kuchita. Mwina anakumbukira lemba la Ekisodo 23:19. Lembali limati tiyenera kupereka kwa Yehova zinthu zabwino koposa. Komanso Chilamulo chinkati: “Munthu akalonjeza kwa Yehova, . . . asalephere kukwaniritsa mawu ake. Achite malinga ndi mawu onse otuluka pakamwa pake.” (Num. 30:2) Mofanana ndi Hana amene anakhalaponso m’nthawi yake, Yefita ankafunika kuchita zimene analonjeza ngakhale kuti zinali zovuta kwa iye komanso mwana wakeyo. Paja Yefita analibe mwana wina. Choncho ankayembekezera kuti mwana wakeyu ndi amene adzatenge dzina lake komanso kulandira cholowa cha banja lawo. (Ower. 11:34) Ngakhale zinali choncho, Yefita ananena kuti: “Ndatsegula pakamwa panga pamaso pa Yehova, ndipo sindingathe kubweza mawu anga.” (Ower. 11:35) Yehova anasangalala kwambiri ndi zimene Yefita anachita ndipo anamudalitsa. Kodi nanunso mungathe kuchita zimene Yefita anachitazi?

15. Kodi ambirife tinalonjeza chiyani kwa Mulungu, nanga tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika?

15 Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tinamulonjeza kuti tizichita zonse zimene akufuna. Tinkadziwa kuti tiyenera kudzimana zinthu zina kuti tikwanitse kuchita zimenezi. Ngakhale zili choncho, nthawi zina zimakhala zovuta ngati tapemphedwa kuchita zinthu zimene sitinkaganiza kuti tingachite. Komabe tikamalolera timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova. Ndipotu zotsatira zake zimakhala zabwino chifukwa Yehova amatidalitsa kwambiri. (Mal. 3:10) Tsopano tiyeni tikambirane chitsanzo cha mwana wa Yefita.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro ngati cha Yefita ndi mwana wake? (Onani ndime 16 ndi 17)

16. Kodi mwana wa Yefita anatani atadziwa kuti bambo ake analonjeza kuti iyeyo azikatumikira pachihema? (Onani chithunzi patsamba 5.)

16 Lonjezo la Yefita linali losiyana ndi la Hana. Hana anapereka Samueli kuti azikatumikira pachihema monga Mnaziri. (1 Sam. 1:11) Anaziri ankatha kukwatira komanso kukhala ndi ana. Koma mwana wa Yefita sakanakwatiwa kapena kukhala ndi ana chifukwa anali ngati “nsembe yopsereza.” (Ower. 11:37-40) Sizinali zophweka kuti mwana wa Yefita alolere zimene bambo ake analonjeza kwa Mulungu. Popeza bambo ake anali mtsogoleri wa Isiraeli komanso wodziwa kumenya nkhondo, mtsikanayu akanatha kukwatiwa ndi mwamuna wabwino kwambiri. Koma m’malomwake, anayenera kukhala wantchito wamba n’kumatumikira pachihema. Kodi mwana wa Yefitayu anatani? Iye anasonyeza kuti ankaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika ndipo anati: “Bambo, ngati mwatsegula pakamwa panu pamaso pa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” (Ower. 11:36) Mtsikanayu analolera kuti asakwatiwe ndiponso kuti asakhale ndi ana n’cholinga choti azitumikira Yehova. Kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji?

17. (a) Kodi tingatsanzire bwanji chikhulupiriro cha Yefita ndi mwana wake? (b) Kodi lemba la Aheberi 6:10-12, likutilimbikitsa bwanji kukhala odzipereka?

17 Masiku anonso, abale ndi alongo achinyamata amalolera kuti asalowe m’banja kapena asakhale ndi ana kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Palinso achikulire ena amene amadzipereka kwambiri. Amalolera kusiya ana ndi zidzukulu kuti agwire ntchito zomangamanga, alowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu kapena akalalikire kudera lina. Pa nthawi yoitanira anthu ku Chikumbutso abale ndi alongo enanso amayesetsa kuti akhale ndi nthawi yambiri yogawira nawo timapepala. Yehova amasangalala akamaona zonsezi ndipo sadzaiwala ntchito yawo komanso chikondi chimene amachisonyeza. (Werengani Aheberi 6:10-12.) Kodi nanunso mukhoza kuwonjezera zimene mumachita potumikira Yehova?

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO

18, 19. Kodi Yefita ndi mwana wake anachita chiyani, nanga tingawatsanzire bwanji?

18 Yefita anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake koma ankasankha zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova. Iye sankatengera zochita za anthu ena ndipo anakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti anthu ena ankamuchitira zoipa. Popeza Yefita ndi mwana wake anadzipereka kwambiri potumikira Yehova, anadalitsidwa kwambiri. Iwo ankatsatira mfundo za Yehova pa nthawi imene anthu ambiri ankazinyalanyaza.

19 Baibulo limatilimbikitsa kuti tizitsanzira “anthu amene, mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza.” (Aheb. 6:12) Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira Yefita ndi mwana wake. Tikatero tidzaona umboni wakuti Yehova amadalitsa anthu okhulupirika.