Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 15

Tizitsanzira Yesu Kuti Tizikhala ndi Mtendere Wamumtima

Tizitsanzira Yesu Kuti Tizikhala ndi Mtendere Wamumtima

“Mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”​AFIL. 4:7.

NYIMBO NA. 113 Yehova Amatipatsa Mtendere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. N’chifukwa chiyani Yesu ankada nkhawa?

TSIKU loti aphedwa mawa lake, Yesu ankada nkhawa kwambiri. Ankadziwa kuti azunzidwa komanso kuphedwa ndi anthu oipa. Koma zimenezi si zimene zinkamudetsa nkhawa kwambiri. Iye ankakonda kwambiri Atate ake ndipo ankafuna kuwasangalatsa. Ankadziwa kuti akakhalabe wokhulupirika pa mayesero ovutawo adzathandiza kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Yesu ankakondanso anthu ndipo ankadziwa kuti zimene angachite zidzathandiza kuti anthuwo adzapeze moyo wosatha.

2 Koma ngakhale kuti anali ndi nkhawa, Yesu anali ndi mtendere wamumtima. Iye anauza atumwi ake kuti: “Ndikupatsani mtendere wanga.” (Yoh. 14:27) Iye anali ndi “mtendere wa Mulungu” womwe umatanthauza kukhala wodekha chifukwa choti uli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtendere umenewu unathandiza kuti maganizo ndi mtima wa Yesu zikhale m’malo.​—Afil. 4:6, 7.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 N’zoona kuti sitingakumane ndi zinthu zodetsa nkhawa ngati zimene Yesu anakumana nazo. Koma anthu onse amene amatsatira Yesu amakumana ndi mavuto. (Mat. 16:24, 25; Yoh. 15:20) Ndipo nthawi zina tikhoza kuda nkhawa ngati mmene Yesu anachitira. Koma kodi tingatani kuti tisamangokhalira kuda nkhawa mpaka kufika posowa mtendere mumtima? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene Yesu anachita ali padzikoli komanso zimene tingachite pomutsanzira.

YESU ANKAKONDA KUPEMPHERA

Kupemphera kungatithandize kuti tikhale ndi mtendere (Onani ndime 4-7)

4. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 5:17, n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anapemphera kwambiri atatsala pang’ono kuphedwa?

4 Werengani 1 Atesalonika 5:17. Yesu ankakonda kupemphera nthawi yonse imene anali padzikoli. Pa tsiku limene anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake, iye anapempherera mkate ndi vinyo. (1 Akor. 11:23-25) Asanachoke pamalo amene anachitira mwambo wa Pasika, Yesu anapempheranso ndi ophunzira ake. (Yoh. 17:1-26) Atafika kuphiri la Maolivi usiku, iye anapemphera mobwerezabwereza. (Mat. 26:36-39, 42, 44) Ndipo mawu omaliza amene Yesu ananena asanafe analinso pemphero. (Luka 23:46) Choncho tingati iye ankaganizira za Yehova pa chinthu chilichonse chachikulu chimene chinkachitika pa tsikulo.

5. N’chifukwa chiyani atumwi anachita mantha?

5 Chinthu chimodzi chimene chinathandiza Yesu kuti apirire bwinobwino mavuto ake n’chakuti ankapemphera kwa Atate ake. Koma usiku woti aphedwa mawa lake, atumwi ake sanalimbikire kupemphera. Izi zinachititsa kuti achite mantha kwambiri pamene anakumana ndi mayesero aakulu. (Mat. 26:40, 41, 43, 45, 56) Choncho kuti nafenso tikhalebe okhulupirika tikakumana ndi mavuto tiyenera ‘kupemphera kosalekeza.’ Ndiye kodi tingatchule zinthu ziti m’pemphero?

6. Kodi chikhulupiriro chingatithandize bwanji kuti tikhale ndi mtendere mumtima?

6 Tingapemphe Yehova kuti ‘atiwonjezere chikhulupiriro.’ (Luka 17:5; Yoh. 14:1) Anthufe timafunika chikhulupiriro chifukwa chakuti Satana amayesa anthu onse amene amatsanzira Yesu. (Luka 22:31) Kodi chikhulupiriro chingatithandize bwanji kuti tizikhalabe ndi mtendere ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto motsatizanatsatizana? Ngati tachita zonse zimene tingathe, chikhulupiriro chimatithandiza kuti tisiye nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Kukumbukira kuti iye amadziwa njira yabwino yothetsera mavuto kuposa mmene ifeyo tikudziwira kungatithandize kuti tikhale ndi mtendere.​—1 Pet. 5:6, 7.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Robert?

7 Pemphero limatithandiza kuti tikhalebe ndi mtendere ngakhale mavuto athu atakhala aakulu kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Robert yemwe ndi mkulu wokhulupirika wazaka za m’ma 80. Iye anati: “Mawu a pa Afilipi 4:6, 7 andithandiza kwambiri kupirira mavuto amene ndakumana nawo pa moyo wanga. Ndakumanapo ndi mavuto azachuma. Pa nthawi ina ndinachotsedwa pa udindo wokhala mkulu.” Kodi n’chiyani chinathandiza M’bale Robert kuti akhalebe ndi mtendere mumtima? M’baleyu anati: “Ndikangoyamba kuda nkhawa kwambiri, ndinkapemphera. Ndipo ndikapemphera mobwerezabwereza komanso mochokera pansi pa mtima m’pamene ndinkakhala ndi mtendere wambiri mumtima.”

YESU ANKALALIKIRA MWAKHAMA

Kulalikira kungatithandize kuti tikhale ndi mtendere (Onani ndime 8-10)

8. Malinga ndi Yohane 8:29, kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kukhala ndi mtendere wamumtima?

8 Werengani Yohane 8:29. Yesu anakhalabe ndi mtendere mumtima pamene ankazunzidwa chifukwa ankadziwa kuti akusangalatsa Atate ake. Iye anakhalabe womvera ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri. Iye ankakonda kwambiri Atate ake ndipo chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake chinali kutumikira Yehova. Yesu asanabwere padzikoli anali “mmisiri waluso” wa Yehova. (Miy. 8:30) Ali padzikoli, iye ankalalikira mwakhama mfundo zokhudza Atate ake. (Mat. 6:9; Yoh. 5:17) Yesu ankasangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi.​—Yoh. 4:34-36.

9. Kodi kugwira mwakhama ntchito yolalikira kungatithandize bwanji kuti tikhale ndi mtendere mumtima?

9 Ifenso tingatsanzire Yesu pomvera Yehova komanso kukhala ndi “zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) ‘Tikamatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira’ timayamba kuona mavuto athu m’njira yoyenera. (Mac. 18:5) Mwachitsanzo, anthu amene timawalalikira nthawi zambiri amakumana ndi zinthu zoipa kuposa ifeyo. Koma akayamba kukonda Yehova komanso kutsatira malangizo ake, amasintha kwambiri n’kukhala osangalala. Ndiye nthawi iliyonse imene taona zimenezi, zimatitsimikizira kuti Yehova adzatisamalira zivute zitani. Kuzindikira mfundo imeneyi n’kumene kumatithandiza kuti tikhale ndi mtendere wamumtima. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene wakhala akudwala matenda a nkhawa ndipo amalimbana ndi maganizo odziona kuti ndi wachabechabe. Iye anati: “Ndikatanganidwa kwambiri ndi utumiki, maganizo anga amakhala m’malo ndipo ndimasangalala. Ndikuganiza kuti zili choncho chifukwa chakuti kulalikirako kumandithandiza kumva kuti Yehova ali nane pafupi.”

10. Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene Brenda ananena?

10 Chitsanzo china ndi cha mlongo wina dzina lake Brenda. Iye ndi mwana wake wamkazi amadwala matenda oopsa kwambiri. Brenda amayenda panjinga ya olumala ndipo amakhala wofooka kwambiri. Iye amalalikira kunyumba ndi nyumba akapeza mphamvu koma nthawi zambiri amangolemba makalata. Iye anati: “Nditangovomereza kuti vuto langali silingathe m’dziko lino koma m’dziko latsopano, ndinayamba kuika maganizo pa utumiki. Ndikamalalikira ndimaiwalako mavuto anga. Ndimayamba kuganizira kwambiri mmene ndingathandizire anthu a m’gawo lathu. Zimandithandizanso kuti ndizikumbukira zimene ndikuyembekezera m’tsogolomu.”

YESU ANKALOLA KUTI ANZAKE AMUTHANDIZE

Anzathu abwino angatithandize kuti tikhale ndi mtendere (Onani ndime 11-15)

11-13. (a) Kodi atumwi ndi anthu ena anasonyeza bwanji kuti anali anzake a Yesu apamtima? (b) Kodi anzake a Yesu anamuthandiza bwanji?

11 Pa utumiki wake wonse padzikoli, Yesu ankathandizidwa ndi atumwi omwe analinso anzake apamtima. Kunena zoona, atumwiwo anakwaniritsa mwambi wakuti: “Pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.” (Miy. 18:24) Yesu ankayamikira kukhala ndi anzake otere. Pa nthawi yonse ya utumiki wake, azichimwene ake sankamukhulupirira. (Yoh. 7:3-5) Pa nthawi ina, achibale ake ankaganiza kuti wapenga. (Maliko 3:21) Koma usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Inu mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga.”​—Luka 22:28.

12 N’zoona kuti nthawi zina atumwiwo ankamukhumudwitsa, koma Yesu sankaganizira kwambiri zimenezo. M’malomwake ankaona kuti iwo amamukhulupirira. (Mat. 26:40; Maliko 10:13, 14; Yoh. 6:66-69) Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anawauza kuti: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” (Yoh. 15:15) Yesu ankalimbikitsidwa kwambiri ndi anzakewa. Iwo ankamuthandiza pa ntchito yolalikira moti zinamuchititsa kusangalala kwambiri.​—Luka 10:17, 21.

13 Panalinso amuna ndi akazi ena omwe anali anzake a Yesu ndipo ankamuthandiza polalikira komanso m’njira zina. Ena ankamuitanira kunyumba kwawo kuti adzadye. (Luka 10:38-42; Yoh. 12:1, 2) Ena ankayenda naye n’kumamupatsa zinthu. (Luka 8:3) Yesu anali ndi anzake apamtima chifukwa choti nayenso anali waubwenzi. Iye ankawachitira zabwino ndipo sankayembekezera kuti azichita zimene sangakwanitse. Ngakhale kuti anali wangwiro, ankayamikira zimene anzake ankachita pomuthandiza. Kunena zoona, anzakewo anamuthandiza kuti akhale ndi mtendere wamumtima.

14-15. Kodi tingatani kuti tikhale ndi anzathu apamtima, nanga anzathuwo angatithandize bwanji?

14 Anzathu abwino amatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova. Kuti tipeze anzathu abwino, ifenso tiyenera kukhala aubwenzi. (Mat. 7:12) Mwachitsanzo, Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kuthandiza anzathu, makamaka amene akumana ndi mavuto. (Aef. 4:28) Ndiye kodi mumpingo wanu muli munthu amene inuyo mungamuthandize? Kodi mungathandize munthu amene akudwala kwambiri moti sangakwanitse kukagula yekha zinthu? Nanga mungapereke chakudya ku banja lina limene lili pa mavuto azachuma? Ngati mumadziwa kugwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org® ndi pulogalamu ya JW Library®, kodi mungathandize ena kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zinthu zimenezi? Tikamatanganidwa ndi kuthandiza ena timakhala osangalala kwambiri.​—Mac. 20:35.

15 Tikakhala ndi anzathu abwino, akhoza kutithandiza tikakumana ndi mavuto ndipo zimenezi zingachititse kuti tikhale ndi mtendere mumtima. Mofanana ndi Elihu amene anamvetsera Yobu akufotokoza mavuto ake, anzathu akhozanso kumvetsera moleza mtima tikamafotokoza mavuto athu. (Yobu 32:4) N’zoona kuti anzathu sangatisankhire zochita koma ndi bwino kumvetsera malangizo awo ochokera m’Malemba. (Miy. 15:22) Davide atakumana ndi mavuto analola kuthandizidwa ndi anzake. Nafenso sitiyenera kukhala odzikuza moti n’kulephera kulola kuti anzathu atithandize pa mavuto athu. (2 Sam. 17:27-29) Anzathu oterowo ali ngati mphatso yochokera kwa Yehova.​—Yak. 1:17.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHALABE NDI MTENDERE WAMUMTIMA

16. Malinga ndi Afilipi 4:6, 7, kodi tingapeze bwanji mtendere wamumtima? Fotokozani.

16 Werengani Afilipi 4:6, 7N’chifukwa chiyani Yehova amanena kuti tingapeze mtendere wake “mwa Khristu Yesu”? Chifukwa chakuti mtendere wamumtima wosatha tingaupeze pokhapokha ngati timamvetsa komanso kukhulupirira udindo wa Yesu. Mwachitsanzo, dipo la Yesu limathandiza kuti tikhululukidwe machimo. (1 Yoh. 2:12) Zimenezi zimatikhazika mtima pansi kwambiri. Komanso monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo chifukwa cha Satana ndi dziko lakeli. (Yes. 65:17; 1 Yoh. 3:8; Chiv. 21:3, 4) Mfundo imeneyi imatithandiza kukhala ndi chiyembekezo champhamvu. Ngakhale kuti ntchito imene Khristu watipatsa si yophweka, iye walonjeza kuti akhala nafe n’kumatithandiza mpaka mapeto a dzikoli. (Mat. 28:19, 20) Kuzindikira mfundo imeneyi kumatithandiza kuti tizikhala olimba mtima. Ndipo mtima wathu ukakhala m’malo, tikakhala ndi chiyembekezo komanso tikakhala olimba mtima timakhala ndi mtendere wamumtima.

17. (a) Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtendere wamumtima? (b) Malinga ndi Yohane 16:33, kodi anthufe tingathe kuchita chiyani?

17 Koma kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtendere wamumtima ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu? Tiyenera kutsanzira Yesu. Choyamba, tiyenera kupemphera kwambiri. Chachiwiri, tiyenera kumvera Yehova n’kumalalikira mwakhama ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. Ndipo chachitatu, tiyenera kulola kuti anzathu atithandize. Tikatero, mtendere wa Mulungu udzateteza maganizo ndi mitima yathu. Ndipo mofanana ndi Yesu, tingathe kugonjetsa mayesero alionse.​—Werengani Yohane 16:33.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

^ ndime 5 Tonsefe timakumana ndi mavuto amene angatilepheretse kukhala ndi mtendere mumtima. Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene Yesu ankachita zomwe zingatithandize kukhala ndi mtendere ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto aakulu.