Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndayesetsa Kuti Ndisagwe Ulesi

Ndayesetsa Kuti Ndisagwe Ulesi

ACHINYAMATA ambiri ku Beteli amakonda kunditchula kuti “Adadi,” “Bambo” kapena “Ankolo.” Zimenezi zimandisangalatsa chifukwa ndili ndi zaka 89. Ndimaona kuti amenewa ndi ena mwa madalitso amene ndapeza chifukwa chotumikira Yehova mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 72. Zimene ndakumana nazo potumikira Mulungu zimandithandiza kuuza achinyamatawa kuchokera pansi pa mtima kuti, ‘Nanunso mudzapeza madalitso ngati simudzagwa ulesi.’​—2 Mbiri 15:7.

MAKOLO KOMANSO AZIBALE ANGA

Makolo anga anasamukira ku Canada kuchokera ku Ukraine. Iwo anakakhala m’tauni ya Rossburn kudera la Manitoba. Mayi anga anabereka anyamata 8 komanso atsikana 8 ndipo panalibe mapasa. Ineyo ndinali wa nambala 14. Bambo ankakonda kwambiri Baibulo ndipo ankatiwerengera Lamlungu lililonse m’mawa. Koma iwo ankaona kuti zipembedzo zimangofuna kupeza ndalama basi ndipo ankakonda kufunsa mwanthabwala kuti, “Kodi ndi ndani ankapatsa Yesu malipiro chifukwa cholalikira ndi kuphunzitsa?”

Azichimwene anga 4 ndi azichemwali anga 4 analowa m’choonadi. Mchemwali wanga dzina lake Rose anachita upainiya mpaka pamene anamwalira. Masiku omalizira a moyo wake iye ankangokhalira kulimbikitsa aliyense kuti azitsatira Mawu a Mulungu ndipo ankanena kuti, “Ndikufuna kuti ndidzakuoneni m’dziko latsopano.” Mchimwene wanga wamkulu dzina lake Ted anali m’busa ndipo ankakonda kwambiri kulalikira zoti anthu oipa adzapita kumoto. Lamlungu lililonse ankalalikira pa wailesi ndipo ankanena kuti anthu oipa onse adzakawotchedwa kwa muyaya kumoto wosazima. Koma kenako anasintha ndipo anayamba kutumikira Yehova mokhulupirika komanso mwakhama kwambiri.

MMENE NDINAYAMBIRA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

Tsiku lina mu June 1944 nditabwera kunyumba kuchokera kusukulu ndinapeza patebulo lathu kabuku kenakake kofotokoza mmene zinthu zidzasinthire m’dzikoli. (The Coming World Regeneration *) Nditayamba kuliwerenga sindinathe kulisiya mpaka ndinalimaliza. Kenako ndinatsimikizira kuti ndiyenera kutumikira Yehova ngati mmene Yesu ankachitira.

Kodi zinatheka bwanji kuti kabukuka kapezeke patebulolo? Mchimwene wanga wina wamkulu dzina lake Steve ananena kuti azibambo awiri anabwera kunyumba kudzagulitsa mabuku. Iye anati: ‘Ndinasankha limeneli chifukwa ndi limene linali lotchipa.’ Azibambowo anabweranso Lamlungu lotsatira. Iwo ananena kuti ndi a Mboni za Yehova ndipo amagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso amene anthu angakhale nawo. Zimenezi zinatisangalatsa chifukwa makolo athu anatiphunzitsa kuti tizilemekeza Mawu a Mulungu. Abalewo anatiuzanso kuti a Mboni adzakhala ndi msonkhano mumzinda wa Winnipeg. Mchemwali wanga dzina lake Elsie ankakhala mumzindawo ndipo ndinaganiza zopita kumsonkhanowo.

Ndinakwera njinga n’kuyenda ulendo wa makilomita pafupifupi 320 wopita ku Winnipeg. Koma ndinaima m’tauni ya Kelwood kumene kunkakhala a Mboni awiri amene anabwera kunyumba kwathu aja. Ndili kumeneko, ndinapita kumisonkhano ndipo ndinadziwa bwino za mpingo. Ndinazindikiranso kuti aliyense, kaya mwamuna, mkazi kapena mwana ayenera kuphunzitsa anthu kunyumba ndi nyumba ngati mmene Yesu ankachitira.

Ku Winnipeg, ndinakumana ndi mchimwene wanga wamkulu dzina lake Jack yemwe anabwera kumsonkhanowu kuchokera kumpoto kwa Ontario. Tsiku loyamba la msonkhanowo m’bale wina analengeza kuti kudzakhala ubatizo. Ine ndi Jack tinaganiza zoti tibatizidwe pamsonkhanowu. Tonsefe tinkafunitsitsa kuti tiyambe upainiya tikangobatizidwa. Jack anayamba upainiyawo titangomaliza msonkhanowo. Popeza ndinali ndi zaka 16 ndinayenera kubwerera kaye kusukulu. Koma chaka chotsatira nanenso ndinayamba upainiya wokhazikika.

NDINAPHUNZIRA ZAMBIRI

Ine ndi m’bale wina dzina lake Stan Nicolson tinayamba kuchita upainiya m’tauni ya Souris kudera la Manitoba. Pasanapite nthawi, ndinazindikira kuti nthawi zina kuchita upainiya n’kovuta. Ndalama zathu zinayamba kutha koma tinangopitiriza upainiyawo. Tsiku lina tinalalikira tsiku lonse koma tinalibe ndalama iliyonse ndipo tinali ndi njala. Titabwerera kunyumba tinadabwa kupeza kuti munthu wina anasiya chakudya chambirimbiri pakhomo lathu. Mpaka pano, sitikudziwa kuti ndi ndani amene anasiya chakudyacho. Koma madzulowo tinadya bwino kwambiri. Kunena zoona tinadalitsidwa chifukwa choti sitinagwe ulesi. Pamene mwezi umenewo unkatha, ndinali nditanenepa kuposa kale lonse.

Patapita miyezi ingapo, tinatumizidwa kutauni ya Gilbert Plains imene inali pa mtunda wa makilomita 240 kumpoto kwa Souris. Pa nthawiyo, mpingo uliwonse unali ndi tchati papulatifomu chimene chinkasonyeza zimene mpingo unkachita mu utumiki mwezi ndi mwezi. Ndiye mwezi wina mpingo wathu unachita zochepa mu utumiki. Choncho ndinakamba nkhani youza abale ndi alongo kuti ayenera kuchita bwino kuposa mmene anachitira mwezi umenewu. Titamaliza misonkhano, mpainiya wina wachikulire amene mwamuna wake sanali wa Mboni anabwera n’kundiuza misozi ikulengeza kuti, “Ndinayesetsa koma sindikanatha kuchita kuposa zimene ndinachitazo.” Kenako inenso ndiyamba kulira ndipo ndinamupepesa chifukwa cha zimene ndinanena.

Mofanana ndi zimene zinandichitikirazi, achinyamata akhama akhoza kulakwitsa zinthu kenako n’kumadzimvera chisoni. Koma ndaona kuti m’malo mogwa ulesi zinthu zoterezi zikakuchitikira, ndi bwino kungophunzirapo kanthu n’kumapitiriza kutumikira Yehova. Tikamapitiriza kumutumikira mokhulupirika timadalitsidwa.

MAVUTO AMENE TINAKUMANA NAWO KU QUEBEC

Ndili ndi zaka 21 zokha ndinali ndi mwayi waukulu wokalowa kalasi ya nambala 14 ya Sukulu ya Giliyadi. Tinamaliza maphunzirowo mu February 1950 ndipo ambirife tinatumizidwa kudera la Quebec ku Canada kumene anthu ambiri amalankhula Chifulenchi. Pa nthawiyo a Mboni ankazunzidwa kwambiri kuderali. Ndinatumizidwa kutauni ya Val-d’Or kumene kunali migodi ya golide. Tsiku lina ine ndi abale ndi alongo ena tinakalalikira kumudzi wina wapafupi wotchedwa Val-Senneville. Wansembe wam’mudziwu anatiuza kuti tichoke mwamsanga ndipo ngati sitichoka atikhaulitsa. Zitatero ndinakamusumira kukhoti ndipo iye analipitsidwa chindapusa. *

Zinthu ngati zimenezi zinkachitikachitika ku Quebec. Zinali choncho chifukwa chakuti derali linali m’manja mwa tchalitchi cha Katolika kwa zaka 300. Atsogoleri a tchalitchichi komanso andale amene ankagwirizana nawo ankazunza kwambiri Mboni za Yehova. Nthawiyo inali yovuta kwambiri ndipo a Mbonife tinali ochepa koma tinayesetsa kuti tisagwe ulesi. Anthu a ku Quebec amene anali ndi mtima wabwino analowa mu choonadi. Ndinali ndi mwayi wophunzira ndi anthu ambiri amene anadzabatizidwa. Panyumba ina ndinkaphunzira ndi banja la anthu 10 ndipo onsewa anayamba kutumikira Yehova. Iwo anali olimba mtima ndipo analimbikitsa anthu ena kuti nawonso achoke m’tchalitchi cha Katolika. Tinapitiriza kulalikira mpaka pamene zinthu zinayamba kuyenda bwino ku Quebec.

TINKAPHUNZITSA ANTHU M’CHILANKHULO CHAWO

Mu 1956, ndinatumizidwa kukatumikira ku Haiti. Amishonale atsopano kumeneko ankavutika kuti aphunzire Chifulenchi koma anthu ambiri ankamvetsera uthenga wathu. Mmishonale wina dzina lake Stanley Boggus ananena kuti, “Tinadabwa kuti anthu ankayesetsa kwambiri kuti atithandize kufotokoza zinthu.” Poyamba, ineyo sindinkavutika chifukwa ndinali nditaphunzira kale Chifulenchi ku Quebec. Koma pasanapite nthawi yaitali, tinazindikira kuti abale ambiri ankangodziwa chilankhulo cha Chikiliyo cha ku Haiti. Choncho kuti amishonalefe tiziwathandiza tinayenera kuphunzira chilankhulocho. Titachiphunzira tinadalitsidwa kwambiri.

Kuti tithandize kwambiri abalewo, tinapempha ngati tingamasulire Nsanja ya Olonda komanso mabuku ena mu Chikiliyo cha ku Haiti ndipo Bungwe Lolamulira linavomereza. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri ayambe kufika kumisonkhano. Mu 1950, ku Haiti kunali ofalitsa 99 okha koma pofika mu 1960 kunali ofalitsa oposa 800. Pa nthawiyo ndinapemphedwa kuti ndipite ku Beteli. Mu 1961, ndinali ndi mwayi wophunzitsa nawo Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Tinaphunzitsa akulu ndiponso apainiya apadera okwana 40. Pamsonkhano wachigawo mu January 1962, tinalimbikitsa abale oyenerera kuti awonjezere utumiki wawo ndipo ena anaikidwa kukhala apainiya apadera. Zimenezi zinachitika pa nthawi yake chifukwa pasanapite nthawi yaitali, a Mboni anayamba kutsutsidwa kwambiri.

Titangomaliza kumene msonkhanowu pa 23 January 1962, ine ndi mmishonale wina dzina lake Andrew D’Amico tinamangidwa tili ku ofesi ya nthambi ndipo magazini onse achifulenchi a Galamukani! ya January 8, 1962 analandidwa. Zinali choncho chifukwa chakuti mu Galamukani! imeneyo analemba kuti manyuzipepala achifulenchi amanena kuti anthu a ku Haiti amachita zamatsenga. Zimenezi sizinasangalatse anthu ena ndipo ananena kuti akunthambife ndi amene tinalemba nkhaniyo. Patangopita milungu ingapo, amishonale ena anathamangitsidwa m’dzikoli. * Koma abale akumeneko amene anaphunzitsidwa bwino anapitiriza ntchito yathu bwinobwino. Ndimasangalala ndi abalewa chifukwa apirira zambiri ndipo chikhulupiriro chawo chalimba. Panopa ali ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika mu Chikiliyo cha ku Haiti. Zaka zam’mbuyomo sakanaganiza n’komwe kuti zimenezi zingatheke.

NTCHITO YA ZOMANGAMANGA KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

Nditatumikira ku Haiti kwa zaka zingapo, ndinapemphedwa kuti ndikakhale mmishonale ku Central African Republic. Ndinakhalanso ndi mwayi wokhala woyang’anira woyendayenda m’dzikoli ndipo kenako ndinakhala woyang’anira nthambi.

Pa nthawiyo, Nyumba za Ufumu zambiri sizinali zabwino kwenikweni. Choncho ndinaphunzira kumweta udzu komanso kufolera madenga. Anthu ambiri odutsa ankadabwa kundiona ndikugwira ntchitoyi movutikira. Koma zinalimbikitsa abale kuti aziyesetsa kuthandiza pomanga komanso kusamalira Nyumba za Ufumu zawo. Atsogoleri achipembedzo ankatinyoza chifukwa matchalitchi awo anali ndi madenga amalata osati audzu. Koma tinangopitiriza kumanga Nyumba za Ufumu zathu zamadenga audzu. Anthuwo anasiya kutinyoza pamene mphepo yamkuntho inachitika mumzinda wa Bangui, womwe ndi likulu la dzikoli. Mphepoyo inakakatula malata a tchalitchi china ndipo malatawo anagwera mumsewu waukulu. Koma madenga audzu a Nyumba za Ufumu zathu sanachoke. Kuti ntchito ya Ufumu iziyang’aniridwa bwinobwino tinamanga ofesi ya nthambi komanso nyumba ya amishonale yatsopano m’miyezi 5 yokha. *

NDINAKWATIRA MKAZI WOKONDA UTUMIKI

Pa tsiku la ukwati wathu

Mu 1976, ntchito yathu inaletsedwa m’dziko la Central African Republic ndipo ndinatumizidwa ku dziko la Chad mumzinda wa N’Djamena. Chosangalatsa n’chakuti m’dzikoli ndinakumana ndi mlongo wa ku Cameroon dzina lake Happy, yemwe anali mpainiya wapadera wakhama kwambiri. Tinakwatirana pa 1 April 1978. Mwezi womwewo, nkhondo yapachiweniweni inayambika ndipo ife limodzi ndi anthu ambiri tinathawira kum’mwera kwa dzikoli. Nkhondoyo itatha tinabwerera kunyumba yathu n’kupeza kuti inkagwiritsidwa ntchito monga likulu la gulu lina la asilikali. Iwo anaba mabuku athu onse, diresi limene Happy anavala pa ukwati wathu komanso mphatso zimene tinapatsidwa. Komabe sitinagwe ulesi. Tinangoyamikira kuti tinali moyo ndipo tinkafunitsitsa kupitiriza utumiki wathu.

Patapita zaka ziwiri, boma la Central African Republic linasiya kuletsa ntchito yathu. Choncho tinabwerera ndipo tinayamba kugwira ntchito yoyendayenda. Tinali ndi minibasi imene tinkagwiritsa ntchito popita kumipingo ndipo tinkagona momwemo. M’basiyo tinali ndi bedi imene tinkaipinda, diramu yamalita 200 imene tinkasungamo madzi, firiji ndiponso chophikira. Maulendo opita kumipingo ankakhala ovuta. Tsiku lina, tinaimitsidwa ndi apolisi m’marodibuloko okwana 117.

Nthawi zina kunkatentha madigiri seshasi 50 ndipo kumisonkhano ikuluikulu tinkavutika kupeza madzi okwanira a ubatizo. Choncho abale ankakumba kumitsinje imene inali youma mpaka atapeza madzi okwanira. Ndipo nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito diramu pobatiza anthu.

TINATUMIKIRA KUMAYIKO ENANSO A KU AFRICA

Mu 1980 tinatumizidwa ku Nigeria. Kwa zaka ziwiri, tinkathandiza pa ntchito yokonzekera kumanga nthambi yatsopano m’dzikoli. Abale anagula nyumba yansanjika ziwiri yomwe ankafuna kuiphwasula n’kutenga zipangizo zake kukamangira kumalo ena amene tinagula. Tsiku lina ndinapita kukathandiza kugwetsa nyumbayo ndipo ndinakwera pamwamba. Cha m’ma 12 koloko masana ndikutsika, malo amene ndinaponda pokwera anali ataphwasulidwa moti ndinagwa. Zinkaoneka kuti ndavulala kwambiri koma adokotala atandiunika kuchipatala anauza Happy kuti: “Aaa usadandaule. Sanathyoke, wangong’ambika timinofu tina. Apeza bwino ukamatha mlungu umodzi kapena iwiri basi.”

Tikupita kumsonkhano wadera

Mu 1986, tinatumizidwa ku Côte d’Ivoire ndipo tinkagwira ntchito yoyendayenda moti tinkafika mpaka ku Burkina Faso. Pa nthawiyo sindinkadziwa kuti nthawi inayake tidzakhala ku Burkina Faso.

Tinkagona muminibasi yathu pa nthawi imene tinkagwira ntchito yoyendayenda

Ndinachoka ku Canada mu 1956 ndipo ndinabwererako patatha zaka 47 mu 2003. Ine ndi Happy tinkatumikira ku Beteli. Ndife nzika za ku Canada koma mumtima tinkaona kuti kwathu ndi ku Africa.

Ndikuphunzitsa munthu ku Burkina Faso

Mu 2007, ndili ndi zaka 79 anatitumizanso ku Africa. Pa nthawiyi tinapita ku Burkina Faso komwe ndinkatumikira mu Komiti ya Dziko. Kenako ofesi yathu anaisintha kukhala ofesi yomasulira mabuku ndipo inkayang’aniridwa ndi nthambi ya ku Benin. Choncho mu August 2013 tinatumizidwa ku Beteli ya ku Benin.

Ine ndi Happy tili kunthambi ya ku Benin

Ngakhale kuti panopa ndimavutika ndi uchikulire ndimakonda kwambiri utumiki. Pa zaka zitatu zapitazi, akulu komanso mkazi wanga andithandiza kwambiri mu utumiki moti anthu awiri amene ndinkaphunzira nawo anabatizidwa. Anthu ake ndi Gédéon ndi Frégis ndipo akutumikira Yehova mwakhama.

Panopa, ine ndi mkazi wanga tili kunthambi ya ku South Africa kumene banja la Beteli limandisamalira malinga ndi ukalamba wangawu. Pa mayiko amene ndatumikira ku Africa kuno, dziko la South Africa ndi la nambala 7. Mu October 2017, tinadalitsidwanso mwapadera. Tinakhala ndi mwayi wopita kumwambo wotsegulira likulu lathu ku Warwick ku New York. Unalitu mwayi waukulu kwambiri.

Mu Buku Lapachaka la 1994 lachingelezi patsamba 255 muli mawu akuti: “Kwa anthu amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri tikuwauza kuti: ‘Khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.’​—2 Mbiri 15:7.” Ine ndi Happy tikuyesetsa kutsatira malangizo amenewa ndipo timalimbikitsa ena kuti azichitanso zomwezo.

^ ndime 9 Kabukuka kanayamba kufalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1944 koma kanasiya kufalitsidwa.

^ ndime 18 Onani nkhani yakuti “Quebec Priest Convicted for Attack on Jehovah’s Witnesses” mu Galamukani! yachingelezi ya November 8, 1953, tsamba 3-5.

^ ndime 23 Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1994 lachingelezi, tsamba 148-150, limafotokoza zambiri pa nkhaniyi.

^ ndime 26 Onani nkhani yakuti “Building on a Solid Foundation” mu Galamukani! yachingelezi ya May 8, 1966, tsamba 27.