Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 33

Kuukitsidwa Kwa Akufa Kumasonyeza Kuti Yehova Ndi Mulungu Wachikondi, Wanzeru Komanso Woleza Mtima

Kuukitsidwa Kwa Akufa Kumasonyeza Kuti Yehova Ndi Mulungu Wachikondi, Wanzeru Komanso Woleza Mtima

“Kudzakhala kuuka.”​—MAC. 24:15.

NYIMBO NA. 151 Iye Adzaitana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani Yehova analenga zamoyo?

PA NTHAWI ina, Yehova anali yekhayekha koma zimenezi sizinkachititsa kuti asamasangalale. Tikutero chifukwa iye safunikira kukhala ndi winawake kuti azisangalala. Komabe Mulungu ankafuna kuti enanso akhale ndi moyo n’kumasangalala. Choncho chifukwa cha chikondi chake, iye anayamba kugwira ntchito yolenga.​—Sal. 36:9; 1 Yoh. 4:19.

2. Kodi Yesu ndi angelo anamva bwanji pamene Yehova analenga zinthu zina?

2 Choyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno limodzi ndi Mwana wakeyo, analenga “zinthu zina zonse” kuphatikizapo angelo. (Akol. 1:16) Yesu ankasangalala kugwira ntchito ndi Atate wake. (Miy. 8:30) Angelo nawonso anasangalala. Iwo analipo ndipo anaona pamene Yehova ndi mmisiri wake Yesu, ankalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi angelowo anasonyeza bwanji kuti anasangalala? Iwo “anayamba kufuula ndi chisangalalo” pamene dziko lapansi linalengedwa ndipo n’zosakayikitsa kuti anapitirizabe kusangalala ndi zinthu zonse zimene Yehova analenga, kuphatikizapo anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zimene Yehova analengazi zimasonyeza kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru.​—Sal. 104:24; Aroma 1:20.

3. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 15:21, 22, kodi nsembe ya Yesu inatheketsa chiyani?

3 Yehova ankafuna kuti anthu azikhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko lokongola limene analenga. Koma Adamu ndi Hava atachimwira Atate wawo wachikondiyu, sakanakhalanso ndi moyo wosatha ndipo iwo limodzi ndi ana awo ankayenera kufa. (Aroma 5:12) Ndiye kodi Yehova anachita chiyani? Nthawi yomweyo, anafotokoza zimene adzachite kuti apulumutse anthu. (Gen. 3:15) Yehova anakonza zoti adzapereke Mwana wake nsembe kuti ana a Adamu ndi Hava adzawomboledwe ku uchimo ndi imfa. Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti zikhale zotheka kuti aliyense amene wasankha kumutumikira adzapeze moyo wosatha.​—Yoh. 3:16; Aroma 6:23; werengani 1 Akorinto 15:21, 22.

4. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

4 Timakhala ndi mafunso ambiri okhudza lonjezo la Mulungu lakuti adzaukitsa anthu amene anamwalira. Mwachitsanzo, tingafunse kuti, kodi kuukitsidwa kwa akufa kudzachitika bwanji? Kodi tidzatha kuwazindikira anthu amene adzaukitsidwewo? Kodi kuukitsidwa kwa akufa kudzatithandiza bwanji kukhala osangalala? Nanga kodi kuukitsidwa kwa akufa kumatiphunzitsa chiyani za chikondi, nzeru komanso kuleza mtima kwa Yehova? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa.

KODI KUUKITSIDWA KWA AKUFA KUDZACHITIKA BWANJI?

5. N’chifukwa chiyani sitingayembekezere kuti anthu onse adzaukitsidwa nthawi imodzi?

5 Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake kuukitsa anthu amene anamwalira, koma sitingayembekezere kuti onse adzaukitsidwa nthawi imodzi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa ngati anthu onse ataukitsidwa nthawi imodzi, ndiye kuti chiwerengero cha anthu chingachuluke kwambiri pa nthawi imodzi ndipo izi zingachititse kuti pakhale chisokonezo. Komatu paja Yehova sangachite zinthu zachisokonezo. Iye amadziwa kuti zinthu zimafunika kuchitika mwadongosolo kuti anthu azikhala mwamtendere. (1 Akor. 14:33) Yehova Mulungu anasonyeza nzeru komanso kuleza mtima pamene ankagwira ntchito ndi Yesu pokonza dzikoli pang’onopang’ono asanalenge anthu. Nayenso Yesu adzasonyeza makhalidwe amenewa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Iye adzagwira ntchito limodzi ndi anthu opulumuka pa Aramagedo poonetsetsa kuti pakhale nyumba, chakudya, zovala ndi zinthu zina zimene anthu oukitsidwawo angadzafunikire.

Anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo azidzaphunzitsa anthu oukitsidwa za Ufumu wa Mulungu komanso zimene Yehova amafuna (Onani ndime 6) *

6. Mogwirizana ndi Machitidwe 24:15, kodi ndi anthu enanso ati omwe Yehova adzawaukitse?

6 Njira yofunika kwambiri imene anthu opulumuka Aramagedo adzathandizire anthu oukitsidwa ndi kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu komanso zimene Yehova amafuna. Izi zili choncho chifukwa ambiri mwa anthuwo adzakhala omwe Baibulo limawatchula kuti “osalungama.” (Werengani Machitidwe 24:15.) Anthuwa adzafunika kusintha zinthu zambiri pa moyo wawo kuti adzapindule ndi nsembe ya Yesu n’kukhala ndi moyo wosatha. Idzakhalatu ntchito yaikulu kuphunzitsa anthu ambirimbiri omwe sakudziwa chilichonse chokhudza Yehova. Kodi aliyense azidzakhala ndi mphunzitsi wakewake ngati mmene zimakhalira ndi maphunziro a Baibulo masiku ano? Kodi anthuwa adzaikidwa m’mipingo n’kuphunzitsidwa kuti nawonso azidzaphunzitsa anthu ena omwe adzaukitsidwe pambuyo pawo? Tingoyembekezera kuti tidzaone pa nthawiyo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti pofika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yes. 11:9) Mosakayikira tidzakhala ndi ntchito yambiri yosangalatsa m’zaka 1,000 zimenezi.

7. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu adzafunike kukhala achifundo pophunzitsa anthu amene adzaukitsidwe?

7 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, anthu onse a Yehova adzafunika kupitirizabe kusintha zinthu pa moyo wawo kuti Yehova azidzasangalala nawo. Choncho onse azidzachitira chifundo anthu amene adzaukitsidwe, powathandiza kuti alimbane ndi makhalidwe oipa n’kumatsatira mfundo za Yehova. (1 Pet. 3:8) Anthu oukitsidwawo adzaona kuti anthu a Yehova ndi odzichepetsa komanso akuyesetsa kusintha kuti azikondweretsa Yehova ndipo nawonso adzakhala ofunitsitsa kuti azimulambira.​—Afil. 2:12.

KODI TIDZATHA KUWAZINDIKIRA ANTHU AMENE ADZAUKITSIDWEWO?

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu omwe azidzalandira abale awo oukitsidwa azidzatha kuwazindikira?

8 Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kunena kuti anthu omwe azidzalandira abale awo azidzatha kuwazindikira. Mwachitsanzo, tikaona zimene Yehova anachita poukitsa anthu ena m’mbuyomu, tingayembekezere kuti adzalenganso anthu amene anamwalirawo m’njira yoti azidzaoneka, kulankhula komanso kuganiza ngati mmene ankachitira asanamwalire. Kumbukirani kuti Yesu anayerekezera imfa ndi tulo ndipo kuukitsidwa anakuyerekezera ndi kudzutsidwa kutulo. (Mat. 9:18, 24; Yoh. 11:11-13) Munthu amene anali mtulo akadzuka, amaoneka komanso kulankhula mofanana ndi mmene amachitira asanagone ndiponso amakumbukira zonse zimene amaganiza asanakagone. Chitsanzo pankhaniyi ndi Lazaro. Iye anali atamwalira kwa masiku 4 ndipo thupi lake linali litayamba kuwola. Koma Yesu atamuukitsa, azichemwali ake anamuzindikira ndipo mosakayikira iyenso anawakumbukira.​—Yoh. 11:38-44; 12:1, 2.

9. N’chifukwa chiyani anthu oukitsidwa sadzafikira kukhala angwiro?

9 Yehova analonjeza kuti mu ulamuliro wa Khristu, palibe amene adzanene kuti: “Ndikudwala.” (Yes. 33:24; Aroma 6:7) Choncho Yehova akamadzaukitsa anthuwa adzawalengera matupi athanzi. Koma si kuti iwo adzangofikira kukhala angwiro. Zitakhala choncho, ndiye kuti achibale komanso anzawo sangadzawazindikire. Zikuoneka kuti anthu onse azidzasintha pang’onopang’ono mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, mpaka kukhala angwiro. Ndipo pamapeto pa zaka 1,000 zimenezi, Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake. Pa nthawiyi Ufumuwu udzakhala utakwaniritsa cholinga chake kuphatikizapo kuthandiza anthu onse kuti akhale angwiro.​—1 Akor. 15:24-28; Chiv. 20:1-3.

KODI KUUKITSIDWA KWA AKUFA KUDZATITHANDIZA BWANJI KUKHALA OSANGALALA?

10. Kodi mudzamva bwanji achibale ndi anzanu akadzaukitsidwa?

10 Taganizirani mmene mudzasangalalire kulandiranso achibale ndi anzanu amene anamwalira. Mwina muzidzangosekerera kapenanso kugwetsa misozi yachisangalalo. N’kuthekanso kuti muzidzayimba nyimbo zotamanda Yehova. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zidzakuthandizani kukonda kwambiri Atate wanu wachikondi komanso Mwana wake, omwe adzaukitse anthu amene anamwalira.

11. Mogwirizana ndi mawu a Yesu a pa Yohane 5:28, 29, kodi n’chiyani chidzachitikire anthu omwe adzamvere Mulungu?

11 Taganiziraninso mmene anthu oukitsidwawo adzasangalalire pamene azidzayesetsa kuvula umunthu wawo wakale kuti azimvera Mulungu. Anthu omwe adzasinthe zinthu pa moyo wawo, adzaloledwa kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Koma Yehova sadzalola kuti anthu omwe akukana kusintha akhalebe m’Paradaiso n’kumasokoneza mtendere.​—Yes. 65:20; werengani Yohane 5:28, 29.

12. Kodi Yehova adzadalitsa bwanji anthu onse padziko lapansi?

12 Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, anthu adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Miyambo 10:22, omwe amati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” Mothandizidwa ndi mzimu woyera, anthu a Mulungu adzakhala olemera mwauzimu kutanthauza kuti adzayamba kufanana kwambiri ndi Khristu ndipo pamapeto pake adzakhala angwiro. (Yoh. 13:15-17; Aef. 4:23, 24) Komanso tsiku lililonse thanzi lawo lizidzawonjezereka ndipo adzakhala anthu abwino. Moyo udzakhalatu wosangalatsa kwambiri. (Yobu 33:25) Koma kodi kuganizira za kuukitsidwa kwa akufa kungatithandize bwanji panopa?

TIZIYAMIKIRA CHIKONDI CHA YEHOVA

13. Kodi lemba la Salimo 139:1-4, limasonyeza bwanji kuti Yehova amatidziwa bwino kwambiri, nanga adzasonyeza bwanji zimenezi poukitsa akufa?

13 Monga taonera kale, Yehova akamadzaukitsa anthu adzabwezeretsa zonse zokhudza anthuwo, monga zimene ankadziwa komanso makhalidwe awo. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amatikonda kwambiri moti amadziwa komanso amakumbukira zimene timaganiza, kulankhula, kuchita ndiponso mmene timamvera. Choncho sangavutike kutiukitsa monga mmene tinalili tisanamwalire. Nayenso Mfumu Davide ankadziwa kuti Yehova amadziwa bwino munthu aliyense payekha. (Werengani Salimo 139:1-4.) Kodi timamva bwanji tikaganizira kuti Yehova amatidziwa bwino kwambiri?

14. Kodi timamva bwanji tikaganizira kuti Yehova amatidziwa bwino kwambiri?

14 Kuganizira mfundo yoti Yehova amatidziwa bwino, kungatithandize kuti tisamadere nkhawa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani kuti Yehova amatikonda kwambiri. Iye amaona kuti munthu aliyense payekha ndi wamtengo wapatali ndipo amachita chidwi ndi zinthu zimene zimatichitikira. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri. Choncho sitiyenera kumadzimva kuti tili tokhatokha. Nthawi zonse Yehova amakhala nafe pafupi ndipo ndi wofunitsitsa kutithandiza.​—2 Mbiri 16:9.

TIZIYAMIKIRA NZERU ZA YEHOVA

15. Kodi chiyembekezo choti akufa adzaukitsidwa chimasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wanzeru?

15 Munthu amene amaopa kufa akhoza kuchita chilichonse ngati wauzidwa kuti akapanda kutero aphedwa. Ndiye anthu amene amatsogoleredwa ndi Satana amaopseza ena kuti awapha pofuna kuwakakamiza kuti aulule anzawo kapena kuti achite zinazake zomwe akudziwa kuti ndi zoipa. Koma kwa atumiki a Yehovafe, njira imeneyi siingatigonjetse. Tikutero chifukwa timadziwa kuti ngati adani athu angatiphe, Yehova adzatiukitsa. (Chiv. 2:10) Timadziwanso kuti palibe chomwe iwo angachite chimene chingatilepheretse kutumikira Yehova. (Aroma 8:35-39) Apatu Yehova anasonyeza kuti ndi wanzeru kwambiri potipatsa chiyembekezo chakuti akufa adzaukitsidwa. Chiyembekezochi chimatithandiza kuti tisamachite mantha adani athu akamatiopseza kuti atipha tikapanda kuchita zimene akufuna. Chimatithandizanso kukhala olimba mtima ndiponso okhulupirika kwa Yehova.

Kodi zimene timasankha zimasonyeza kuti timakhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzatisamalira? (Onani ndime 16) *

16. Kodi muyenera kudzifunsa mafunso ati, nanga mayankho a mafunsowa angakuthandizeni bwanji?

16 Ngati adani a Yehova akukuopsezani kuti akuphani, kodi mudzakhulupirira kuti iye adzakuukitsani? Kodi mungadziwe bwanji ngati mungadzakhulupirire Yehova pa nthawiyo? Njira ina ndi kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimasankha tsiku lililonse zimasonyeza kuti ndimakhulupirira Yehova?’ (Luka 16:10) Funso lina lingakhale lakuti, ‘Kodi mmene ndimachitira zinthu pa moyo wanga ndimasonyeza kuti ndimakhulupirira lonjezo la Yehova loti adzandisamalira ndikamaika zinthu za Ufumu pamalo oyamba?’ (Mat. 6:31-33) Ngati mwayankha kuti “inde” pa mafunso onsewa, ndiye kuti mumakhulupirira Yehova ndipo ndinu okonzeka kulimbana ndi mayesero aliwonse omwe mungadzakumane nawo.​—Miy. 3:5, 6.

TIZIYAMIKIRA KULEZA MTIMA KWA YEHOVA

17. (a) Kodi nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi woleza mtima? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kuleza mtima kwa Yehova?

17 Yehova akudziwa tsiku komanso nthawi imene adzawononge dziko loipali. (Mat. 24:36) Iye apitirizabe kuleza mtima mpaka nthawiyo idzakwane. Yehova amafunitsitsa kuukitsa anthu amene anamwalira koma akuleza mtima. (Yobu 14:14, 15) Akudikira kuti nthawi yoyenera yoti adzawaukitse ifike. (Yoh. 5:28) Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova chifukwa cha kuleza mtima kwake. Tangoganizani: Chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova, anthu ambiri kuphatikizapo ifeyo, tinapeza mwayi woti ‘tilape.’ (2 Pet. 3:9) Yehova amafuna kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Choncho tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira kuleza mtima kwakeko. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingasonyeze kuyamikira tikamayesetsa kufufuza anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha,’ n’kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova komanso kumutumikira. (Mac. 13:48) Tikatero, tidzawathandiza kuti nawonso apindule ndi kuleza mtima kwa Yehova.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima kwa anthu ena?

18 Yehova adzapitiriza kuyembekezera moleza mtima kuti tikhale angwiro, mpaka kumapeto kwa zaka 1,000. Kufikira pa nthawiyo, Yehova akhala akutikhululukira machimo athu. Choncho nafenso tiyenera kumutsanzira poyesetsa kumaona makhalidwe abwino a anthu ena n’kumawalezera mtima. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina yemwe mwamuna wake anayamba kudwala matenda ovutika maganizo, moti anasiya kupezeka pamisonkhano. Mlongoyu anati: “Zimenezi zinandipweteka kwambiri. Moyo wathu unasintha mwadzidzidzi ndipo sitikanathanso kuchita zinthu zimene tinkafuna kuchita.” Koma pa nthawi yonseyi, mlongoyu anapitiriza kukhala woleza mtima kwa mwamuna wake. Iye ankadalira Yehova ndipo sanataye mtima. Mofanana ndi Yehova, mlongoyu sankaganizira kwambiri za vutoli koma ankayesetsa kuona zabwino mwa mwamuna wakeyo. Iye anati: “Mwamuna wanga ali ndi makhalidwe abwino ndipo akuyesetsa kuchita zomwe angathe kuti athane ndi vuto lakeli.” N’zofunika kwambiri kuti tizikhala oleza mtima pochita zinthu ndi anthu am’banja kapena amumpingo mwathu, omwe akulimbana ndi mavuto.

19. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

19 Yesu komanso angelo anasangalala dziko lapansi litangolengedwa. Koma taganizirani mmene adzasangalalire akadzaona dziko lonse litadzaza ndi anthu angwiro, omwe amakonda komanso kutumikira Yehova. Taganizirani mmene anthu omwe adzalamulire ndi Khristu adzamvere akadzaona anthu akupindula ndi ntchito yawo padzikoli. (Chiv. 4:4, 9-11; 5:9, 10) Tayerekezerani kuti muli m’dziko limene simudzakhalanso zopweteka zilizonse monga matenda, chisoni ndi imfa. (Chiv. 21:4) Mpaka pa nthawi imeneyo, tiyeni titsimikize mtima kuti tizitsanzira Atate wathu wachikondi, wanzeru komanso woleza mtima. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kuti tizikhalabe osangalala ngakhale tikumane ndi mayesero. (Yak. 1:2-4) Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha lonjezo lake lakuti “kudzakhala kuuka.”​—Mac. 24:15.

NYIMBO NA. 141 Moyo Ndi Wodabwitsa

^ ndime 5 Yehova ndi Atate wachikondi, wanzeru komanso woleza mtima. Makhalidwewa amaonekera bwino tikaganizira mmene analengera zinthu zonse komanso cholinga chake chodzaukitsa anthu amene anamwalira. Munkhaniyi, tikambirana mafunso ena omwe tingakhale nawo okhudza kuukitsidwa kwa akufa ndipo tiona mmene tingasonyezere kuyamikira Yehova chifukwa cha chikondi, nzeru komanso kuleza mtima kwake.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Munthu amene anamwalira zaka zambiri zapitazo, waukitsidwa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. M’bale amene wapulumuka pa Aramagedo, akumuphunzitsa zimene ayenera kuchita kuti apindule ndi nsembe ya Khristu.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akufotokozera bwana wake kuti masiku ena mkati mwa mlungu sazigwira ovataimu. Iye akuuza abwana akewo kuti pa masiku amenewa amachita zinthu zina zokhudza kulambira Yehova. Koma ngati angafunike kwambiri masiku ena, akhoza kugwira ovataimu.