Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 35

Muziona Kuti Anthu Ena Ndi Ofunika Mumpingo

Muziona Kuti Anthu Ena Ndi Ofunika Mumpingo

“Diso silingauze dzanja kuti: ‘Ndilibe nawe ntchito,’ kapenanso, mutu sungauze mapazi kuti: ‘Ndilibe nanu ntchito.’”​—1 AKOR. 12:21.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova wapereka chiyani kwa atumiki ake okhulupirika?

MWACHIKONDI Yehova amapereka zochita zosiyanasiyana kwa atumiki ake okhulupirika mumpingo. Ngakhale zili choncho, tonsefe ndi amtengo wapatali ndipo timadalirana. Zimene mtumwi Paulo ananena zingatithandize kumvetsa mfundo yofunika imeneyi.

2. Mogwirizana ndi Aefeso 4:16, n’chifukwa chiyani tiyenera kumaona kuti Akhristu anzathu ndi ofunika komanso kumagwira nawo ntchito limodzi?

2 Mogwirizana ndi zimene zanenedwa mulemba limene pachokera nkhaniyi, mtumwi Paulo anasonyeza kuti mtumiki wa Yehova aliyense sayenera kumaona mnzake kuti ndi wosafunika, zomwe zingakhale ngati akumuuza kuti: “Ndilibe nawe ntchito.” (1 Akor. 12:21) Kuti mumpingo mukhale mtendere, tiyenera kumaona Akhristu anzathu kuti ndi ofunika n’kumagwira nawo ntchito limodzi. (Werengani Aefeso 4:16.) Tikamachita zinthu mogwirizana, zinthu zimayenda bwino mumpingo komanso timakondana kwambiri.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere kuti timalemekeza Akhristu anzathu mumpingo? Munkhaniyi, tiona zimene akulu angachite posonyeza kuti amalekeza akulu anzawo. Kenako, tikambirana mmene tonsefe tingasonyezere kuti timaona abale ndi alongo athu omwe sali pabanja kuti ndi ofunika. Pomaliza, tiona mmene tingasonyezere kuti timakonda anthu omwe amavutika kulankhula chinenero chathu.

MUZILEMEKEZA AKULU ANZANU

4. Kodi ndi malangizo otani opezeka pa Aroma 12:10, amene akulu ayenera kumawatsatira?

4 Akulu onse mumpingo amaikidwa ndi mzimu wa Yehova. Komabe, aliyense amakhala ndi mphatso komanso luso losiyana ndi la mnzake. (1 Akor. 12:17, 18) Akulu amene atumikira kwa nthawi yaitali angakhale kuti akudziwa zambiri kusiyana ndi amene angoikidwa kumene. Ena sangakwanitse kuchita zambiri chifukwa ndi achikulire kapena amadwaladwala. Koma ngakhale zili choncho, palibe mkulu amene ayenera kumaona anzake kuti ndi osafunika, zomwe zingakhale ngati akuwauza kuti: “Ndilibe nanu ntchito.” M’malomwake, mkulu aliyense ayenera kutsatira malangizo amene Paulo analemba pa Aroma 12:10.​—Werengani.

Akulu amasonyeza kuti amalemekeza akulu anzawo ngati amawamvetsera mwatcheru akamalankhula (Onani ndime 5-6)

5. Kodi akulu angasonyeze bwanji kuti amalemekeza akulu anzawo, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika?

5 Akulu amasonyeza kuti amalemekeza akulu anzawo ngati amawamvetsera mwatcheru akamalankhula. Zimenezi ndi zofunika kwambiri makamaka akakumana n’kumakambirana nkhani zokhudza mpingo. Tikutero chifukwa Nsanja ya Olonda ya October 1, 1988, inanena kuti: “Akulu ayenera kuzindikira kuti Khristu angagwiritse ntchito mzimu woyera pothandiza mkulu aliyense kunena mfundo ya m’Baibulo yomwe ingakhale yothandiza kwambiri posankha zoyenera kuchita. (Mac. 15:6-15) Palibe mkulu winawake amene mzimu woyera ungagwire ntchito kwambiri pa iye kuposa anzake.”

6. Kodi akulu angatani kuti azichita zinthu mogwirizana, nanga zimenezi zingathandize bwanji mpingo?

6 Mkulu amene amalemekeza akulu anzake safuna kuti nthawi zonse azingokhala woyambirira kulankhula akamakambirana nkhani inayake. Iye amapewa kulankhula kwambiri ndiponso saona kuti maganizo ake ndi ofunika kuposa a ena. M’malomwake amafotokoza maganizo ake modzichepetsa. Amamvetsera mwatcheru ena akamapereka maganizo awo. Komanso chofunika kwambiri, amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba ndiponso kutsatira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Akulu akamachita zinthu mwachikondi komanso mwaulemu akakhala pamisonkhano yawo, mzimu woyera umagwira ntchito bwino ndipo umawathandiza kusankha zinthu zomwe zingathandize kuti mpingo uziyenda bwino.​—Yak. 3:17, 18.

MUZILEMEKEZA AKHRISTU AMENE SALI PABANJA

7. Kodi Yesu ankaona bwanji anthu omwe sali pabanja?

7 Masiku ano m’mipingo muli anthu amene ali ndi mabanja komanso abale ndi alongo ena omwe sali pabanja. Ndiye kodi tiyenera kumawaona bwanji anthu amene sali pabanja? Tizitengera chitsanzo cha Yesu pankhani ya mmene ankaonera anthuwa. Pamene Yesu anali padzikoli, sanakwatire. Iye anagwiritsa ntchito nthawi yake yonse pochita utumiki wake. Yesu sananene kuti kukhala pabanja kapena ayi ndi kofunika kuti munthu akhale Mkhristu. Komabe ananena kuti Akhristu ena amasankha kuti asakhale pabanja. (Mat. 19:11, 12) Yesu ankalemekeza anthu amene sanali pabanja ndipo sankawaona kuti ndi otsika kapena akusowa zinazake.

8. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 7:7-9, kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuganizira chiyani?

8 Mofanana ndi Yesu, mtumwi Paulo anakhala wosakwatira pa nthawi yonse ya utumiki wake. Ngakhale zili choncho, iye sankaphunzitsa kuti n’kulakwa kuti Akhristu azikwatira. Paulo ankadziwa kuti munthu ayenera kusankha yekha kukhala pabanja kapena ayi. Komabe iye analimbikitsa Akhristu kuganizira ngati angathe kutumikira Yehova asali pabanja. (Werengani 1 Akorinto 7:7-9.) Mwachionekere, Paulo sankaona Akhristu omwe sali pabanja ngati otsika. N’chifukwa chake iye anasankha Timoteyo, yemwe anali wosakwatira, kuti azisamalira maudindo aakulu m’gulu la Yehova. * (Afil. 2:19-22) Choncho, zingakhale zolakwika kuganiza kuti m’bale ndi woyenerera potengera kuti ndi wokwatira kapena ndi wosakwatira.​—1 Akor. 7:32-35, 38.

9. Kodi tinganene zotani pa nkhani ya kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja?

9 Yesu kapena Paulo sanaphunzitse kuti Akhristu ayenera kukhala pabanja kapena ayi. Ndiye tinganene zotani pa nkhani ya kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja? Nsanja ya Olonda ya October 1, 2012 inapereka yankho labwino la funsoli. Inati: “Kunena zoona, zonsezi [kukhala pabanja komanso kusakhala pabanja] ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. . . . Yehova saona kuti kusakhala pabanja ndi chinthu chochititsa manyazi kapena chomvetsa chisoni.” Choncho, tiyenera kulemekeza abale ndi alongo amumpingo mwathu omwe sali pabanja.

Kodi tiyenera kupewa chiyani kuti tisonyeze kuti timalemekeza abale ndi alongo omwe sali pabanja? (Onani ndime 10)

10. Kodi tingapewe zinthu ziti kuti tisakhumudwitse anthu omwe sali pabanja?

10 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza mmene abale ndi alongo athu omwe sali pabanja amamvera? Tizikumbukira kuti Akhristu ena anasankha kusakhala pabanja. Ena amafuna atakhala pabanja koma sanapeze munthu woyenera kukwatirana naye. Pamene enanso, mkazi kapena mwamuna wawo anamwalira. Mulimonse mmene zingakhalire, kodi n’koyenera kuti Akhristu azifunsa abale ndi alongo amenewa chifukwa chimene sali pabanja kapena kuyesa kuwathandiza kupeza munthu woti akwatirane naye? N’kutheka kuti ena mwa Akhristuwa angapemphe kuti ena awathandize kupeza wokwatirana naye. Koma ngati sanapemphe thandizo, kodi Akhristuwa angamve bwanji ngati wina atayesa kuwapezera munthu woti akwatirane naye? (1 Ates. 4:11; 1 Tim. 5:13) Tiyeni tione zimene abale ndi alongo ena okhulupirika omwe sali pabanja ananena.

11-12. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani kuti tisakhumudwitse anthu amene sali pabanja?

11 Woyang’anira dera wina, yemwe amachita bwino utumiki wake, amaona kuti kusakhala pabanja kwamubweretsera madalitso ambiri. Koma ananena kuti zimakhala zosalimbikitsa abale ndi alongo ena akamamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simuli pabanja?” M’bale wina wosakwatira yemwe akutumikira pa ofesi ya nthambi, ananena kuti: “Nthawi zina abale ndi alongo amandipangitsa kumva kuti anthu omwe sali pabanja ndi omvetsa chisoni. Zimenezi zingachititse munthu kuona kuti kusakhala pabanja ndi vuto osati mphatso.”

12 Mlongo wina wosakwatiwa yemwe amatumikira pa Beteli anati: “Abale ndi alongo ena amaganiza kuti anthu onse omwe sali pabanja amangokhalira kufunafuna munthu woti adzakwatirane naye moti akakhala pagulu amaona kuti ndi mpata woti afunsire kapena kufunsiridwa. Nthawi ina ndinapita kudera lina kukagwira ntchito zina zokhudzana ndi utumiki wanga ndipo linali tsiku lamisonkhano. Mlongo yemwe ndinkakhala naye anandiuza kuti mumpingomo muli abale awiri amsinkhu wanga. Iye ananditsimikizira kuti si kuti akufuna kundipezera mwamuna. Koma titangolowa mu Nyumba ya Ufumu, ananditengera kwa abale awiriwo kuti ndikalankhule nawo. Zinali zochititsa manyazi kwambiri kwa ineyo komanso abalewo.”

13. Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zinalimbikitsa mlongo wina wosakwatiwa?

13 Mlongo winanso wosakwatiwa yemwe amatumikira pa Beteli anati: “Ndimadziwa apainiya ena achikulire omwe sali pabanja. Apainiyawa amachita zinthu moganiza bwino, ali ndi zolinga zauzimu, amakhala ofunitsitsa kuthandiza ena komanso amakhala osangalala. Iwo amathandiza kwambiri kuti mpingo uziyenda bwino. Apainiyawa amaona moyenera nkhani ya banja. Samadziona kuti iwowo ndi apamwamba kuposa ena. Saonanso kuti amamanidwa zinazake chifukwa choti sali pabanja komanso alibe ana.” Zimene mlongoyu ananena zikusonyeza kuti kukhala mumpingo umene aliyense amakulemekeza komanso kukuona kuti ndiwe wofunika n’kosangalatsa kwambiri. Ukamakhala umadziwa kuti abale ndi alongo ako sakumvera chisoni kuti suli pabanja ndipo sakuchitira nsanje. Komanso sachita zinthu ngati alibe nawe ntchito, ndiponso saona kuti ndiwe wapamwamba kuposa iwowo. Umadziwanso kuti amakukonda kwambiri.

14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza anthu omwe sali pabanja?

14 Abale komanso alongo omwe sali pabanja angasangalale kwambiri tikamawaona kuti ndi ofunika chifukwa cha makhalidwe awo abwino. Koma angakhumudwe tikamawamvera chisoni chifukwa choti sali pabanja. Choncho m’malo mochita zimenezi, tiziwayamikira chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Tikamachita zimenezi, abale ndi alongo athu omwe sali pabanja sangamaone ngati tikuwauza kuti: ‘Tilibe nanu ntchito.’ (1 Akor. 12:21) Ndipo angadziwe kuti timawalemekeza komanso timawaona kuti ndi ofunika kwambiri mumpingo.

MUZILEMEKEZA ANTHU OMWE AMAVUTIKA KULANKHULA CHINENERO CHANU

15. Kodi abale ndi alongo ena achita zotani kuti awonjezere utumiki wawo?

15 Zaka zapitazi, ofalitsa ambiri akhala akuphunzira zinenero zina kuti awonjezere utumiki wawo. Kuti achite zimenezi, amafunika kusintha zinthu zina pa moyo wawo. Abale ndi alongowa ankafunika kusiya mpingo wachinenero chawo n’kusamukira mumpingo wachinenero china komanso kumene kukufunika ofalitsa ambiri. (Mac. 16:9) Mkhristu aliyense amasankha yekha kuchita zimenezi n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova. Ngakhale kuti pamatenga zaka kuti adziwe bwino chinenero chatsopanocho, iwo amathandiza kwambiri mpingo umene asamukirawo. Amalimbikitsa mpingo chifukwa cha zimene akudziwa komanso makhalidwe awo abwino. Timaona abale ndi alongo odziperekawa kuti ndi amtengo wapatali.

16. Kodi akulu ayenera kugwiritsa ntchito chiyani kuti aone ngati m’bale akuyenerera kutumikira monga mkulu kapena mtumiki wothandiza?

16 Bungwe la akulu siliyenera kulephera kuvomereza m’bale kuti atumikire monga mkulu kapena mtumiki wothandiza chifukwa choti amavutika kulankhula chinenero champingowo. Akulu ayenera kugwiritsa ntchito Malemba kuti aone ngati m’baleyo akuyenerera kutumikira monga mkulu kapena mtumiki wothandiza, osati potengera mmene amalankhulira chinenerocho.​—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9.

17. Kodi makolo ayenera kuganizira chiyani akasamukira m’dziko lina?

17 Mabanja ena a Chikhristu asamukira kumayiko ena chifukwa cha mavuto omwe ali m’mayiko awo kapena kuti akapeze ntchito. Zikatere, ana awo akamapita kusukulu angaphunzire chinenero cham’dziko lomwe asamukiralo. Makolo nawonso angafunike kuphunzira chinenero cham’dzikolo kuti apeze ntchito. Koma bwanji ngati m’deralo muli mpingo kapena kagulu kachinenero chakwawo? Kodi banjali liyenera kumasonkhana mpingo wachinenero chiti, cham’dzikolo kapena chakwawo?

18. Mogwirizana ndi Agalatiya 6:5, kodi tingasonyeze bwanji kuti tikulemekeza zimene mutu wabanja wasankha?

18 Mutu wabanja uyenera kusankha mpingo umene banja lake lizisonkhana. Komabe, ayenera kusankha zinthu zomwe zingathandizedi banjalo. (Werengani Agalatiya 6:5.) Popeza aliyense ali ndi ufulu wosankha pankhaniyi, tiyenera kulemekeza zimene mutu wabanjalo wasankha. Ngati mutu wabanja wasankha kuti azisonkhana ndi mpingo wathu, tiyenera kuwalandira ndi manja awiri n’kumasonyeza kuti timawakonda.​—Aroma 15:7.

19. Kodi ndi nkhani iti imene mutu wabanja uyenera kuiganizira mosamala?

19 Nthawi zina banja lingamasonkhane mumpingo wachinenero chakwawo. Koma ana am’banjamo angakhale kuti sadziwa bwinobwino chinenerocho. Choncho sangamapindule ndi misonkhano, zomwe zingachititse kuti asakule mwauzimu. Zimenezi zingachitike chifukwa anawo angakhale kuti anazolowera kulankhula chinenero chimene amagwiritsa ntchito kusukulu osati chinenero cha makolo awo. Ngati zili choncho, mutu wabanja uyenera kuganizira nkhaniyi mosamala komanso kupempha nzeru kwa Yehova kuti asankhe zimene zingathandize anawo kukonda kwambiri Yehova ndi anthu ake. Mwina angafunike kuthandiza ana awo kudziwa bwino chinenero chakwawocho. Kapena akhoza kungosamukira kumpingo wa chinenero chimene anawo amachidziwa bwino. Kaya mutu wabanja wasankha zotani, anthu amumpingo umene akusonkhanawo ayenera kumawakonda komanso kumawasonyeza kuti ndi ofunika.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza anthu omwe akuphunzira chinenero chatsopano? (Onani ndime 20)

20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza abale ndi alongo omwe akuphunzira chinenero chatsopano?

20 Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti m’mipingo yambiri mungakhale abale ndi alongo omwe akuyesetsa kuphunzira chinenero chatsopano. Nthawi zina angamavutike kufotokoza maganizo awo. Koma tikamapewa kuganizira kwambiri mmene akuvutikira kulankhula chinenerocho, tingaone kuti amakonda kwambiri Yehova komanso amafuna kumutumikira. Tikamaona makhalidwe awo abwinowa, tingayambe kuwalemekeza komanso kuwaona kuti ndi ofunika kwambiri. Sitikuyenera kumawaona ngati osafunika chifukwa choti amavutika kulankhula chinenero chathu. Kuchita zimenezi kungakhale ngati kuwauza kuti: “Ndilibe nanu ntchito.”

NDIFE AMTENGO WAPATALI KWA YEHOVA

21-22. Kodi tonsefe tili ndi mwayi wotani?

21 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa watipatsa ntchito yofunika kwambiri mumpingo wake. Ndiye zilibe kanthu kuti ndife mwamuna kapena mkazi, tili pabanja kapena ayi, ndife wachikulire kapena wachinyamata, timalankhula bwino chinenero chinachake kapena timavutika nacho, tonsefe ndife amtengo wapatali kwa Yehova komanso kwa abale ndi alongo athu.​—Aroma 12:4, 5; Akol. 3:10, 11.

22 Tiyeni tipitirize kugwiritsa ntchito mfundo zimene taphunzira kuchokera m’chitsanzo cha Paulo chonena za ziwalo zathupi. Zimenezi zingatithandize kuona zomwe tingachite kuti tizilimbikitsa abale ndi alongo athu. Zingatithandizenso kuti tiziwakonda komanso kuwalemekeza.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

^ ndime 5 M’gulu la Yehova muli anthu osiyanasiyana ndipo aliyense amagwiranso ntchito zosiyanasiyana. Nkhaniyi itithandiza kuona kuti aliyense ndi wofunika kwambiri mumpingo.

^ ndime 8 Sitinganene motsimikiza kuti Timoteyo sanakwatire.