Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 32

Tiziyenda Modzichepetsa ndi Mulungu

Tiziyenda Modzichepetsa ndi Mulungu

“Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”​MIKA 6:8.

NYIMBO NA. 31 Yendani ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani n’zomveka kunena kuti Yehova ndi wodzichepetsa?

KODI n’zomveka kunena kuti Yehova ndi wodzichepetsa? Inde. Wolemba masalimo Davide, analemba kuti: “Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso, ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (2 Sam. 22:36; Sal. 18:35) N’kutheka kuti Davide ankaganizira za tsiku limene mneneri Samueli anabwera kunyumba kwa bambo ake kuti adzadzoze munthu yemwe adzakhale mfumu ya Isiraeli. Davide anali wamng’ono kwambiri pa ana aamuna a m’banjalo koma Yehova anamusankha kuti ndi amene adzalowe m’malo mwa Mfumu Sauli.​—1 Sam. 16:1, 10-13.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Davide anagwirizana ndi zimene wolemba masalimo wina ananena zokhudza Yehova. Wamasalimoyu anati: “Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi. Amakweza munthu wosauka . . . kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka.” (Sal. 113:6-8) Munkhaniyi tiphunzira zinthu zofunika zokhudza kudzichepetsa poona mmene Yehova anasonyezera khalidweli. Kenako tikambirana zimene tingaphunzire kuchokera kwa Mfumu Sauli, mneneri Danieli komanso Yesu pankhani ya kudzichepetsa.

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI PA CHITSANZO CHA YEHOVA?

3. Kodi Yehova amachita bwanji zinthu ndi anthu ochimwafe, nanga zimenezi zikusonyeza chiyani?

3 Yehova amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa akamachita zinthu ndi anthu ochimwa amene amamulambira. Si kuti iye amangovomereza kuti tizimulambira, koma amationanso ngati anzake. (Sal. 25:14) Kuti tikhale naye pa ubwenzi, Yehova anapereka Mwana wake nsembe kuti machimo athu azikhululukidwa. Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima.

4. Kodi Yehova anatipatsa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

4 Tiyeni tionenso njira ina imene Yehova amasonyezera kuti ndi wodzichepetsa. Popeza iye ndi Mlengi, akanatha kutilenga m’njira yoti tisamasankhe zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu. Koma sanatero. Iye anatilenga m’chifaniziro chake komanso anatipatsa ufulu wosankha. Yehova amafuna kuti tizimutumikira chifukwa chomukonda ndiponso chifukwa choti tikudziwa ubwino womumvera. (Deut. 10:12; Yes. 48:17, 18) Timayamikira kuti Yehova ndi wodzichepetsa kwambiri.

Yesu ali kumwamba, kumbuyo kwake kuli olamulira anzake omwe akuyang’ana angelo ambirimbiri. Angelo ena akupita padziko lapansi kuti akagwire ntchito imene apatsidwa. Yehova amapereka zochita kwa onse amene akusonyezedwa pachithunzichi (Onani ndime 5)

5. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kuti tikhale odzichepetsa? (Onani chithunzi chapachikuto.)

5 Yehova amatiphunzitsa kukhala odzichepetsa akamachita nafe zinthu. Iye ndi wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse. Ndiye ngakhale kuti safunikira malangizo kuchokera kwa aliyense, amamvetsera maganizo a anthu ena. Mwachitsanzo, Yehova analola kuti Mwana wake amuthandize pamene ankalenga zinthu zonse. (Miy. 8:27-30; Akol. 1:15, 16) Komanso ngakhale kuti iye ndi Wamphamvuyonse, amapereka mphamvu kwa ena. Mwachitsanzo, iye anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake ndipo adzaperekanso mphamvu zina kwa anthu okwana 144,000 amene adzalamulire ndi Yesu. (Luka 12:32) N’zosakayikitsa kuti Yehova anaphunzitsa Yesu kuti adzakhale Mfumu komanso mkulu wa ansembe. (Aheb. 5:8, 9) Amaphunzitsanso anthu amene adzalamulire ndi Yesu ndipo amawalola kuti akwaniritse maudindo awo popanda kulamulira zimene akuchita. M’malomwake, amawadalira kuti achita chifuniro chake.​—Chiv. 5:10.

Timatsanzira Yehova tikamaphunzitsa ena komanso kuwapatsa zochita (Onani ndime 6-7) *

6-7. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Atate wathu wakumwamba pankhani yopereka zochita kwa ena?

6 Ngati Atate wathu wakumwamba yemwe safunikira kuthandizidwa ndi aliyense amapereka zochita kwa anthu ena, kuli bwanji ifeyo? Nafenso tiyenera kulola anthu ena kuti azichita zinthu zina. Mwachitsanzo, kodi ndinu mutu wa banja kapena ndinu mkulu mumpingo? Muzitsanzira Yehova popereka zochita kwa ena ndipo mukatero muzipewa kulamulira mmene akuchitira zinthuzo. Mukamatsanzira Yehova, ntchito zambiri zidzayenda bwino komanso mungaphunzitse ena ndi kuwathandiza kuti asamaope kugwira ntchito zina. (Yes. 41:10) Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene anthu amene ali ndi udindo angaphunzire kwa Yehova?

7 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amamvetsera maganizo a angelo. (1 Maf. 22:19-22) Makolo, kodi mungatsanzire bwanji Yehova pankhaniyi? Ngati n’koyenera, muzifunsa ana anu mmene mungachitire zinthu zinazake. Ndiye akapereka maganizo othandiza, muziwatsatira.

8. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuleza mtima pamene ankachita zinthu ndi Abulahamu ndi Sara?

8 Yehova amasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa pokhala woleza mtima. Mwachitsanzo, amaleza mtima atumiki ake akamakayikira zimene wasankha kuchita. Iye anamvetsera pamene Abulahamu ankafotokoza kuti sakanachita bwino kuwononga mzinda wa Sodomu ndi Gomora. (Gen. 18:22-33) Kumbukiraninso mmene Yehova anachitira zinthu ndi Sara, mkazi wa Abulahamu. Sanakhumudwe kapena kukwiya pamene Sara anaseka atamva lonjezo loti adzakhala ndi pakati ngakhale kuti anali wokalamba. (Gen. 18:10-14) M’malomwake Yehova anamulemekeza.

9. Kodi makolo komanso akulu angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yehova?

9 Makolo komanso Akulu, kodi mungaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yehova? Kodi mumatani ngati ana anu kapena anthu ena mumpingo sanagwirizane ndi zimene mwasankha? Kodi nthawi zonse mumangodziikira kumbuyo kuti zosankha zanuzo ndiye zolondola? Kapena mumayesetsa kumvetsera maganizo awo? Zinthu zimayenda bwino m’banja komanso mumpingo ngati anthu amene akutsogolera amatsanzira Yehova. Pofika pano, takambirana mmene chitsanzo cha Yehova chingatithandizire kukhala odzichepetsa. Tsopano tiyeni tikambirane mmene zitsanzo za anthu ena otchulidwa m’Baibulo zingatithandizire pankhaniyi.

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI PA ZITSANZO ZA ANTHU ENA?

10. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji zitsanzo za anthu ena potiphunzitsa?

10 Yehova yemwe ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ amatipatsa zitsanzo zotiphunzitsa kudzera m’Mawu ake. (Yes. 30:20, 21) Timaphunzira zambiri tikamaganizira nkhani za anthu ena otchulidwa m’Baibulo omwe anasonyeza makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo, kuphatikizapo kudzichepetsa. Timaphunziranso zambiri pa zimene zinachitikira anthu ena amene sanasonyeze makhalidwewa.​—Sal. 37:37; 1 Akor. 10:11.

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo choipa cha Sauli?

11 Taganizirani zimene zinachitikira Mfumu Sauli. Ali mnyamata, anali wodzichepetsa. Iye ankadziwa malire ake moti nthawi ina anakayikira kuti sakanakwanitsa kukhala ndi udindo waukulu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma patapita nthawi, Sauli anayamba kudzikweza ndipo anachita zinthu zimene sankayenera kuchita. Anayamba kusonyeza khalidweli atangokhala mfumu. Pa nthawi ina, analephera kudikira moleza mtima kuti mneneri Samueli afike. M’malo modalira Yehova kuti athandize anthu ake, Sauli anapereka nsembe ngakhale kuti umenewu sunali udindo wake. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova asiye kumukonda ndipo pamapeto pake ufumu wake unatha. (1 Sam. 13:8-14) Chitsanzochi chikutiphunzitsa kuti tiyenera kupewa kuchita zinthu modzikweza.

12. Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa?

12 Mosiyana ndi chitsanzo choipa cha Sauli, tiyeni tikambirane chitsanzo chabwino cha mneneri Danieli. Iye anakhalabe wodzichepetsa kwa moyo wake wonse ndipo nthawi zonse ankalola kuti Yehova azimutsogolera. Mwachitsanzo, pamene Yehova anamugwiritsa ntchito kumasulira loto la Nebukadinezara, Danieli sananene kuti anakwanitsa kuchita zimenezi ndi nzeru zake. M’malomwake, iye modzichepetsa anapereka ulemelero wonse kwa Yehova. (Dan. 2:26-28) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati abale amasangalala ndi nkhani zathu kapena ngati zinthu zimatiyendera bwino mu utumiki, tizikumbukira kuti ulemerero wonse uyenera kupita kwa Yehova. Tiyenera kuzindikira kuti sitikanakwanitsa kuchita zinthuzo popanda kuthandizidwa ndi Yehova. (Afil. 4:13) Tikamachita zimenezi, timakhala tikutsanziranso Yesu. N’chifukwa chiyani tikutero?

13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu malinga ndi zimene ananena pa Yohane 5:19, 30?

13 Ngakhale kuti Yesu anali Mwana wangwiro wa Mulungu, iye ankadalira kwambiri Yehova. (Werengani Yohane 5:19, 30.) Iye sanayese kulanda udindo wa Atate wake wakumwamba. Lemba la Afilipi 2:6 limatiuza kuti kwa iye “kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.” Monga Mwana wogonjera, Yesu ankadziwa malire ake ndipo ankalemekeza ulamuliro wa Atate wake.

Yesu ankadziwa malire ake (Onani ndime 14)

14. Kodi Yesu anayankha bwanji atapemphedwa zinthu zimene sunali udindo wake kupereka?

14 Taganizirani zimene Yesu anayankha pamene Yakobo ndi Yohane limodzi ndi amayi awo anamupempha zinthu zimene sunali udindo wake kupereka. Mosazengereza iye ananena kuti ndi Atate wake okha amene ayenera kusankha yemwe angakhale kudzanja lake lamanja kapena lamanzere mu Ufumu wake. (Mat. 20:20-23) Pamenepa Yesu anasonyeza kuti ankadziwa malire ake. Iye anali wodzichepetsa ndipo sanachite zinthu zimene Yehova sanamuuze kuti achite. (Yoh. 12:49) Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo chabwino cha Yesu?

Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pankhani ya kudzichepetsa? (Onani ndime 15-16) *

15-16. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo a m’Baibulo opezeka pa 1 Akorinto 4:6?

15 Timatsanzira Yesu tikamatsatira malangizo a m’Baibulo opezeka pa 1 Akorinto 4:6. Lembali limati: “Musapitirire zinthu zolembedwa.” Choncho ena akapempha malangizo, sitiyenera kuwakakamiza kutsatira maganizo athu kapena kungolankhulapo tisanaganizire bwino nkhaniyo. M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo komanso m’mabuku athu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timadziwa malire athu. Timasonyezanso kudzichepetsa tikamatsatira ‘malamulo olungama’ a Wamphamvuyonse.​—Chiv. 15:3, 4.

16 Kuwonjezera pa kulemekeza Yehova, tilinso ndi zifukwa zina zotichititsa kukhala odzichepetsa. Tsopano tiona mmene kudzichepetsa kungatithandizire kuti tizisangalala komanso kuti tizigwirizana ndi anthu ena.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZICHEPETSA N’KOFUNIKA?

17. N’chifukwa chiyani anthu odzichepetsa amakhala osangalala?

17 Kukhala odzichepetsa kumatithandiza kuti tizisangalala. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikamadziwa kuti pali zina zimene sitingakwanitse kuchita, timayamikira anthu ena akatithandiza. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Yesu atachiritsa anthu 10 akhate. Mmodzi yekha ndi amene anabwerera kukamuthokoza chifukwa chomuchiritsa matenda ake oopsawo. Munthuyu anali wodzichepetsa ndipo ankadziwa kuti sakanatha kuchira popanda kuthandizidwa ndi Yesu. Iye anayamikira thandizo lomwe anapatsidwa ndipo analemekeza Mulungu.​—Luka 17:11-19.

18. Mogwirizana ndi Aroma 12:10, kodi kudzichepetsa kumathandiza bwanji kuti tizigwirizana ndi ena?

18 Anthu odzichepetsa amagwirizana ndi ena ndipo savutika kupeza anzawo abwino. Izi zili choncho chifukwa amazindikira kuti anthu ena ali ndi makhalidwe abwino ndipo zimakhala zosavuta kuti awakhulupirire. Anthu odzichepetsa amasangalala anthu ena zikamawayendera bwino ndipo anthuwo akachita zinthu zabwino amawayamikira komanso kuwalemekeza.​—Werengani Aroma 12:10.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa mtima wonyada?

19 Mosiyana ndi zimenezi, anthu onyada zimawavuta kuti ayamikire ena chifukwa amaona kuti iwowo ndi amene ayenera kutamandidwa. Nthawi zambiri iwo amakonda kudziyerekezera ndi ena komanso amalimbikitsa mzimu wampikisano. M’malo mophunzitsa ena kuti azichita zinazake kapena kuwapatsa udindo, anthu onyada amaganiza kuti ayenera kuchita chilichonse okha chifukwa amaona kuti ena sangakwanitse kuchita bwino ngati mmene iwowo amachitira. Nthawi zambiri, munthu wonyada amafuna azioneka kuti ndi wofunika kuposa ena, ndiye ena akamachita bwino kuposa iyeyo amawachitira nsanje. (Agal. 5:26) Anthu oterewa amavutika kupeza anzawo. Ngati tazindikira kuti tayamba kunyada, tiyenera kupempha mochokera pansi pa mtima kuti Yehova atithandize ‘kusintha maganizo athu,’ kuti mtima wonyadawu usatilowerere.​—Aroma 12:2.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa?

20 Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatisonyeza mmene tingakhalire odzichepetsa. Timaona kuti iye ndi wodzichepetsa tikaona mmene amachitira zinthu ndi atumiki ake ndipo timafuna kumutsanzira. Komanso tikufuna kutsanzira zitsanzo zabwino za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe anayenda modzichepetsa ndi Mulungu. Nthawi zonse tiziyesetsa kulemekeza Yehova komanso kumupatsa ulemelero womwe amayenera kulandira. (Chiv. 4:11) Tikatero, nafenso tidzayenda ndi Atate wathu wakumwamba yemwe amakonda anthu odzichepetsa.

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

^ ndime 5 Munthu wodzichepetsa amakhala wachifundo komanso wokoma mtima. Choncho n’zomveka kunena kuti Yehova ndi wodzichepetsa. Monga tionere munkhaniyi, tikhoza kuphunzira kudzichepetsa kuchokera kwa Yehova. Tiphunziranso zambiri pankhaniyi kuchokera m’chitsanzo cha Mfumu Sauli, mneneri Danieli komanso Yesu.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu akuphunzitsa m’bale wachinyamata mmene angasamalirire magawo a mpingo. Kenako akulola kuti m’bale wachinyamatayo azigwira ntchitoyo popanda kulamulira chilichonse chimene akuchita.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akufunsa mkulu ngati n’zoyenera kuti akakhale nawo pa ukwati womwe ukachitikire m’tchalitchi. Mkuluyo sakungofotokoza za m’maganizo mwake koma akumusonyeza mfundo za m’Baibulo.