Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 30

Muziyamikira Mwayi Wanu Wokhala M’banja la Yehova

Muziyamikira Mwayi Wanu Wokhala M’banja la Yehova

“Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi angelo, kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu.”—SAL. 8:5, mawu a m’munsi.

NYIMBO NA. 123 Muzigonjera Mulungu Mokhulupirika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi mafunso otani amene tingakhale nawo tikaganizira zinthu zonse zimene Yehova analenga?

TIKAGANIZIRA zinthu zonse zimene Yehova analenga, tikhoza kumva ngati mmene anamvera wolemba masalimo Davide, yemwe m’pemphero lake anafunsa kuti: “Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga, ndimaganiza kuti: Munthu ndani kuti muzimuganizira, ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?” (Sal. 8:3, 4) Mofanana ndi Davide, mwina tingamaone kuti ndife aang’ono poyerekeza ndi zinthu zina zimene Mulungu analenga ndipo tingadabwe kuona kuti iye amatiwerengera. Koma monga mmene tionere munkhaniyi, kuwonjezera pa kukonda Adamu ndi Hava, Yehova anawaikanso m’banja lake.

2. Kodi Yehova anali ndi cholinga chotani chokhudza ana ake oyamba padzikoli?

2 Adamu ndi Hava anali ana oyamba a Yehova padzikoli, ndipo iye anali Atate wawo wakumwamba yemwe ankawakonda. Iye ankafuna kuti anthu awiriwo abereke ana. Mulungu anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Gen. 1:28) Choncho iwo ankafunika kuti abereke ana ndiponso kusamalira dzikoli. Akanamvera n’kumachita zimene Mulungu amafuna, Adamu ndi Hava komanso ana awo akanapitiriza kukhala m’banja la Mulungu mpaka kalekale.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Adamu ndi Hava anapatsidwa malo abwino kwambiri m’banja la Yehova?

3 Adamu ndi Hava anali ndi malo abwino kwambiri m’banja la Yehova. Palemba la Salimo 8:5 komanso mawu a m’munsi palembali, pofotokoza mmene Yehova analengera munthu Davide anati: “Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi angelo kenako munamuveka ulemerero ndi ulemu monga chisoti chachifumu.” N’zoona kuti anthu sanapatsidwe mphamvu, nzeru kapena luso ngati angelo. (Sal. 103:20) Komabe munthu ‘anangomuchepetsa pang’ono’ kuyerekeza ndi angelo. Kunena zoona, Yehova anawapatsa makolo athuwo moyo wabwino.

4. Kodi n’chiyani chinachitikira Adamu ndi Hava chifukwa choti sanamvere Yehova, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

 4 N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava sanamvere Yehova ndipo sanapitirize kukhala m’banja lake. Monga mmene tionere munkhaniyi, zimenezi zinachititsa kuti ana awo akumane ndi mavuto aakulu. Koma cholinga cha Yehova sichinasinthe. Iye akufuna kuti anthu omvera adzakhale ana ake mpaka kalekale. Choyamba tiyeni tikambirane mmene Yehova wasonyezera kuti amationa kuti ndife ofunika kwambiri. Kenako tikambirana zimene tingachite panopa posonyeza kuti timafuna kukhala m’banja la Mulungu. Pomaliza, tikambirana madalitso amene ana a Yehova adzasangalale nawo padzikoli mpaka kalekale.

KODI YEHOVA WASONYEZA BWANJI KUTI AMAONA ANTHU KUKHALA OFUNIKA?

Kodi Yehova wasonyeza m’njira ziti kuti amaona kuti ndife ofunika? (Onani ndime 5-11) *

5. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Mulungu chifukwa chotilenga m’chifaniziro chake?

5 Yehova anasonyeza kuti amationa kuti ndife ofunika potilenga m’chifaniziro chake. (Gen. 1:26, 27) Popeza kuti tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, timatha kusonyeza makhalidwe abwino amene iye ali nawo monga chikondi, chifundo, kukhulupirika komanso chilungamo. (Sal. 86:15; 145:17) Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe amenewa, timalemekeza Yehova ndipo timasonyeza kuti timamuyamikira. (1 Pet. 1:14-16) Tikamachita zinthu m’njira imene ingasangalatse Atate wathu wakumwamba, ifenso timakhala osangalala. Komanso chifukwa choti anatilenga m’chifaniziro chake, tingathe kukhala mtundu wa anthu amene iye amafuna kuti akhale m’banja lake.

6. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amaona kuti anthu ndi ofunika kwambiri pamene ankalenga dzikoli?

6 Yehova anatipatsa malo abwino kwambiri oti tizikhalamo. Zaka zambiri asanalenge munthu woyambirira, iye anali atalenga dziko lapansili kuti anthu adzakhalemo. (Yobu 38:4-6; Yer. 10:12) Popeza kuti ndi wokoma mtima komanso wopatsa, Yehova anaikamo zinthu zambiri zabwino kuti anthu adzasangalale nazo. (Sal. 104:14, 15, 24) Nthawi zina, iye ankaganizira zinthu zimene analenga, ndipo ankaona kuti “zili bwino.” (Gen. 1:10, 12, 31) Yehova anasonyeza kuti amaona anthu kukhala ofunika ‘powapatsa mphamvu’ yoti alamulire zinthu zochititsa chidwi zimene analenga padzikoli. (Sal. 8:6) Cholinga cha Mulungu n’choti anthu angwiro azidzasangalala kusamalira zinthu zokongola zimene iye analengazi mpaka kalekale. Kodi mumamuthokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha zinthu zabwino zimene analonjezazi?

7. Kodi lemba la Yoswa 24:15, limasonyeza bwanji kuti munthu ali ndi ufulu wosankha?

7 Yehova anatipatsa ufulu wosankha. Tingathe kusankha zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu. (Werengani Yoswa 24:15.) Mulungu wathu wachikondi amasangalala tikasankha kumutumikira. (Sal. 84:11; Miy. 27:11) Tikhoza kugwiritsa ntchito ufulu umenewu posankha zochita mwanzeru. Taganizirani chitsanzo cha mmene Yesu anagwiritsira ntchito ufulu wake wosankha.

8. Kodi ndi njira imodzi iti imene Yesu anagwiritsira ntchito bwino ufulu wake wosankha?

8 Tingatengere chitsanzo cha Yesu tikamaika zofuna za ena patsogolo m’malo mwa zofuna zathu. Pa nthawi ina Yesu ndi atumwi ake atatopa kwambiri, anapita kumalo ena kuti akapume. Komabe zimenezi sizinatheke. Khamu la anthu linawatsatira ndipo ankafunitsitsa kuti Yesu awaphunzitse. Koma Yesu sanawakwiyire anthuwo. M’malomwake iye anawamvera chisoni. Ndiye kodi Yesu anatani? Iye “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:30-34) Tikamatsanzira Yesu pogwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu pothandiza ena, timalemekeza Atate wathu wakumwamba. (Mat. 5:14-16) Timamusonyezanso Yehova kuti tikufuna kukhala m’banja lake.

9. Kodi ndi mwayi uti umene makolo apatsidwa?

9 Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi ana, ndipo anawapatsa udindo wophunzitsa anawo kuti azimukonda komanso kumutumikira. Ngati ndinu makolo, kodi mumayamikira mwayi umene Yehova anakupatsaniwu? Angelo sanapatsidwe mwayiwu ngakhale kuti anapatsidwa luso lochita zinthu zambiri. Poganizira mfundo imeneyi, makolo amene akulera ana ayenera kuona kuti umenewu ndi udindo wofunika kwambiri. Makolo apatsidwa udindo wolera ana awo “m’malangizo a Yehova ndikuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4; Deut. 6:5-7; Sal. 127:3) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Yehova limapereka zinthu zothandiza pophunzira Baibulo monga mabuku, mavidiyo, nyimbo komanso zinthu zina kudzera pa webusaiti. N’zoonekeratu kuti Atate wathu wakumwamba komanso Mwana wake amakonda kwambiri ana. (Luka 18:15-17) Makolo akamadalira Yehova n’kumachita zonse zomwe angathe posamalira ana awo, omwe ndi amtengo wapatali, Yehova amasangalala. Ndipo makolo oterewa, amathandiza ana awo kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Yehova mpaka kalekale.

10-11. Kodi n’chiyani chimene Yehova wachita pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake?

10 Yehova anapereka Mwana wake wokondedwa n’cholinga choti anthufe tikhalenso m’banja lake. Monga momwe taonera  mundime 4, Adamu ndi Hava sanapitirize kukhala m’banja la Yehova, ndipo zimenezi zinakhudzanso ana awo. (Aroma 5:12) Mwadala Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, choncho m’pomveka kuti iye anawachotsa m’banja lake. Koma bwanji ponena za ana awo? Mwachikondi Yehova anakonza zoti adzatenge ana omvera a Adamu n’kuwaikanso m’banja lake. Iye anachita zimenezi pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake wokondedwa, Yesu Khristu. (Yoh. 3:16; Aroma 5:19) Chifukwa cha nsembe imeneyi anthu okwana 144,000 okhulupirika amaonedwa ngati ana a Mulungu.​—Aroma 8:15-17; Chiv. 14:1.

11 Kuwonjezera pamenepo, anthu mamiliyoni ambiri omwe ndi okhulupirika amamvera ndiponso kuchita zimene Mulungu amafuna. Iwo ali ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Mulungu pambuyo pa mayesero omaliza, zikadzatha zaka 1,000. (Sal. 25:14; Aroma 8:20, 21) Chifukwa cha chiyembekezo chimenechi, ngakhale panopa anthu amenewa amatchula Yehova yemwe ndi Mlengi wawo kuti “Atate.” (Mat. 6:9) Komanso anthu amene adzaukitsidwe, adzapatsidwa mwayi woti aphunzire zimene Yehova amafuna kuti iwo azichita. Ndipo amene adzasankhe kumvera, nawonso adzapatsidwa mwayi woti akhale m’banja lake.

12. Kodi tsopano tikambirana funso liti?

12 Monga mmene taonera, Yehova wachita kale zambiri posonyeza kuti amaona kuti anthu ndi ofunika. Iye watenga kale odzozedwa kuti akhale ana ake ndipo wapereka chiyembekezo kwa a “khamu lalikulu” choti adzakhale ana ake m’dziko latsopano. (Chiv. 7:9) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani panopa kuti tisonyeze kuti tikufuna kudzakhala m’banja la Yehova mpaka kalekale?

TIZIMUSONYEZA YEHOVA KUTI TIKUFUNA KUDZAKHALA M’BANJA LAKE

13. Kodi tingatani kuti tikhale m’banja la Mulungu? (Maliko 12:30)

13 Tizisonyeza kuti timakonda Yehova pomutumikira ndi mtima wathu wonse. (Werengani Maliko 12:30.) Pali mphatso zambiri zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima. Ndipo imodzi mwa mphatsozi ndi mwayi woti tizimulambira. Timasonyeza kuti timakonda Yehova ‘tikamasunga malamulo ake.’ (1 Yoh. 5:3) Polankhula m’malo mwa Atate wake, Yesu anatilamula kuti tizithandiza anthu kukhala ophunzira ake komanso kuwabatiza. (Mat. 28:19) Iye anatilamulanso kuti tizikondana. (Yoh. 13:35) Yehova adzalandira onse omvera m’banja lake lapadziko lonse la anthu amene amamulambira.​—Sal. 15:1, 2.

14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda ena? (Mateyu 9:36-38; Aroma 12:10)

14 Tizikonda anthu ena. Chikondi ndi khalidwe lalikulu la Yehova. (1 Yoh. 4:8) Iye anasonyeza kuti amatikonda tisanamudziwe n’komwe. (1 Yoh. 4:9, 10) Timamutsanzira tikamakonda anthu ena. (Aef. 5:1) Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda anthu ndi kuwathandiza kudziwa za Yehova nthawi idakalipo. (Werengani Mateyu 9:36-38.) Tikamachita zimenezi, timakhala tikuwapatsa mwayi woti akhale ndi chiyembekezo chodzakhala m’banja la Mulungu. Munthu akabatizidwa, tiyenera kupitiriza kumusonyeza chikondi komanso kumulemekeza. (1 Yoh. 4:20, 21) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Njira ina imene tingachitire zimenezi, ndikusonyeza kuti sitikukayikira zolinga zake. Mwachitsanzo, ngati sitinamvetse chifukwa chake wachitira zinazake sitingafulumire kuganiza kuti wachita zimenezo ndi zolinga zoipa. M’malomwake, tidzalemekeza m’bale wathuyo n’kumamuona kuti ndi wotiposa.​—Werengani Aroma 12:10; Afil. 2:3.

15. Kodi ndi ndani amene tiyenera kuwakomera mtima komanso kuwachitira chifundo?

15 Tizichitira chifundo komanso kukomera mtima anthu onse. Ngati tikufuna kupitiriza kukhala m’banja la Yehova, tiyenera kumagwiritsa ntchito zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu pa moyo wathu. Mwachitsanzo, Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenera kumachitira chifundo komanso kukomera mtima anthu onse kuphatikizapo adani athu. (Luka 6:32-36) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Ngati zili choncho, tiyenera kuphunzira kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu ngati Yesu. Tikamayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomvera Yehova komanso kutsanzira Yesu, timasonyeza Atate wathu wakumwamba kuti tikufuna kukhala m’banja lake mpaka kalekale.

16. Kodi tingateteze bwanji mbiri yabwino ya banja la Yehova?

16 Tiziteteza mbiri yabwino ya banja la Yehova. M’banja si zachilendo kuona mwana akutengera chitsanzo cha mkulu wake. Ngati mwana wamkuluyo amagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake, angakhale chitsanzo chabwino kwambiri kwa mng’ono wakeyo. Koma akamachita zoipa, mng’ono wakeyo angatengerenso zimenezo. Zimenezi ndi zomwe zingachitikenso m’banja la Yehova. Ngati Mkhristu yemwe anali wokhulupirika wayamba kukhala ndi maganizo a mpatuko kapena wasankha kumachita zoipa, Akhristu ena angayambe kumutsanzira. Anthu amene amachita zimenezi amaipitsa mbiri ya banja la Yehova. (1 Ates. 4:3-8) Choncho sitiyenera kutsanzira anthu oipa ndipo tisamalole chilichonse kutilekanitsa ndi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi.

17. Kodi tiyenera kupewa kukhala ndi maganizo ati, nanga n’chifukwa chiyani?

17 Tizidalira Yehova osati chuma. Yehova amalonjeza kuti adzatipatsa chakudya, zovala ndi pogona ngati timaika Ufumu wake pamalo oyamba komanso ngati timachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. (Sal. 55:22; Mat. 6:33) Chifukwa cha zimenezi, timapewa kuganiza kuti chuma komanso zinthu za m’dzikoli zingatithandize kukhala otetezeka kapenanso osangalala. Timadziwa kuti chimene chingatithandize kupeza mtendere weniweni wamumtima, ndi kuchita zimene Yehova amafuna basi. (Afil. 4:6, 7) Ngakhale kuti tingakwanitse kugula zinthu zambiri, tiyenera kuganizira ngati tingakhale ndi nthawi komanso mphamvu zogwiritsa ntchito zinthuzo komanso kuzisamalira. Kodi timakonda kwambiri zinthu zimene tili nazo? Tizikumbukira kuti Mulungu watipatsa ntchito yoti tizigwira m’banja lake. Zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kulola kusokonezedwa ndi chilichonse. Sitingafune ngakhale pang’ono kukhala ngati wachinyamata wina, yemwe anakana mwayi wotumikira Yehova komanso kukhala m’gulu la ana ake chifukwa cha zinthu zochepa zimene anapeza m’dzikoli.​—Maliko 10:17-22.

ZIMENE ANA A YEHOVA ADZASANGALALE NAZO MPAKA KALEKALE

18. Kodi ndi madalitso ati amene anthu omvera adzasangalale nawo mpaka kalekale?

18 Anthu omvera adzasangalala ndi mwayi waukulu wolambira komanso kukonda Yehova mpaka kalekale. Anthu amene adzakhale padzikoli adzasangalala kugwira ntchito yosamalira dziko lokongolali, lomwe Yehova anawakonzera kuti azikhalamo. Posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzakonza zinthu zonse padzikoli kuti zikhalenso bwino. Yesu adzathetsa mavuto onse amene anayamba chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anasankha kuchoka m’banja la Mulungu. Yehova adzaukitsa anthu mamiliyoni n’kuwapatsa mwayi woti akhale ndi moyo wosatha komanso wathanzi m’dziko limene adzalikonze kukhala paradaiso. (Luka 23:42, 43) Anthu amene amalambira Yehova akadzakhala angwiro, aliyense azidzasonyeza “ulemerero ndi ulemu” umene Davide analemba.​—Sal. 8:5.

19. Kodi tiyenera kumakumbukira chiyani?

19 Ngati muli m’gulu la a “khamu lalikulu,” mukuyembekezera zinthu zabwino kwambiri. Mulungu amakukondani ndipo akufuna kuti mukhale m’banja lake. Choncho muzichita zonse zimene mungathe kuti azisangalala nanu. Tsiku lililonse muzikumbukira komanso kuganizira malonjezo a Yehova. Muziyamikira mwayi umene muli nawo wolambira Atate wathu wakumwamba, ndipo muzisangalala ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzamutamanda mpaka kalekale.

NYIMBO NA. 107 Tsanzirani Chikondi cha Mulungu

^ ndime 5 Kuti zinthu ziziyenda bwino m’banja, aliyense afunika kudziwa zimene ayenera kuchita komanso kumagwirizana ndi onse m’banjamo. Mwamuna ayenera kumatsogolera mwachikondi banja lake, mkazi wake amafunika kumuthandiza ndipo ana ayeneranso kumamvera makolo awo n’kumachita zinthu mogwirizana nawo. Zimenezi ndi zimene zimachitikanso m’banja la Yehova. Mulungu ali ndi cholinga chabwino chokhudza anthufe ndipo tikamachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chimenecho, tidzakhala m’banja la Yehova la anthu amene amamulambira mpaka kalekale.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chifukwa choti analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, mwamuna ndi mkazi wake amakondana ndiponso amakonda ana awo. Banjali limakondanso Yehova. Iwo akusonyeza kuyamikira mwayi wokhala ndi ana pothandiza anawo kuti azikonda komanso kutumikira Yehova. Makolowa akugwiritsa ntchito vidiyo pofotokozera ana awo chifukwa chake Yehova anapereka Yesu monga dipo. Akuphunzitsanso anawo kuti m’Paradaiso akubwerayo, tizidzasamalira dzikoli komanso nyama mpaka kalekale.