Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Mulungu amadziwa mmene timamvera?

Aisiraeli ali akapolo ku Iguputo, Mulungu ankadziwa za mavuto awo komanso ankakhudzidwa ndi mmene ankamvera. (Eks. 3:7; Yes. 63:9) Tinapangidwa m’chifaniziro chake choncho nafenso timatha kumvera ena chisoni. Yehova amatimvera chisoni ngakhale pamene tikuona kuti si ife oyenerera kuti azitikonda.​—wp18.3, tsamba 8-9.

Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zinathandiza bwanji anthu kuti apewe tsankho?

Ayuda ambiri munthawi ya Yesu anali atsankho. Khristu ankalimbikitsa anthu kuti akhale odzichepetsa komanso asamaone kuti mtundu wawo ndi wapamwamba kuposa mitundu ina. Iye ankalimbikitsa otsatira ake kuti azionana ngati abale.​—w18.06, tsamba 9-10.

Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yoti Mulungu analetsa Mose kuti alowe m’Dziko Lolonjezedwa?

Mose anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Deut. 34:10) Chakumapeto kwa zaka 40 zimene Aisiraeli anali m’chipululu, iwo anadandaulanso kachiwiri kuti akusowa madzi. Mulungu anauza Mose kuti alankhule ndi mwala. Koma iye anaumenya mwalawo. N’kutheka kuti Yehova anakwiya chifukwa chakuti Mose sanatsatire malangizo ake, apo ayi chifukwa sanamulemekeze monga wochititsa chozizwitsacho. (Num. 20:6-12) Nkhaniyi ikutiphunzitsa kuti tiyenera kumvera Yehova komanso kumulemekeza.​—w18.07, tsamba 13-14.

Kodi tingalakwitse bwanji tikamaweruza poona maonekedwe?

Tikhoza kuweruza anthu potengera mtundu wawo, chuma chawo kapena msinkhu wawo. Tiyenera kuyesetsa kuona anthu ngati mmene Mulungu, yemwe alibe tsankho, amawaonera. (Mac. 10:34, 35)​—w18.08, tsamba 8-12.

Kodi Akhristu achikulire angathandize bwanji anthu ena?

Mulungu amaonabe kuti Akhristu achikulire amene utumiki wawo wasintha ndi ofunika kwambiri ndipo iwo akhoza kumathandiza anthu ena. Angathandize amuna amene akazi awo ndi a Mboni, kuchititsa maphunziro a Baibulo komanso angamachite zambiri mu utumiki.​—w18.09, tsamba 8-11.

Kodi ndi zinthu ziti zomwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa?

Zinthu zake ndi makadi odziwitsa anthu za webusaiti yathu, timapepala toitanira anthu, timapepala tina tamitundu 8 komanso magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Zinthuzi zikuphatikizanso timabuku tingapo, mabuku awiri amene timaphunzira ndi anthu komanso mavidiyo 4 monga vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?​—w18.10, tsamba 16.

Mogwirizana ndi Miyambo 23:23, kodi Mkhristu ‘angagule’ bwanji choonadi?

Sitigula choonadi ndi ndalama. Koma timagwiritsa ntchito nthawi yathu komanso kuchita khama kuti tichipeze.​—w18.11, tsamba 4.

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Hoseya anachita ndi mkazi wake Gomeri?

Gomeri ankachita chigololo mobwerezabwereza. Koma Hoseya ankamukhululukira ndipo sanamusiye. Ngati mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu angachite dama, Mkhristu wosalakwayo angasankhe kumukhululukira. Mkhristu akayambanso kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wakeyo, ndiye kuti alibenso chifukwa chovomerezeka ndi Malemba kuti athetse banja.​—w18.12, tsamba 13.