Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wolungama adzakondwera mwa Yehova”

“Wolungama adzakondwera mwa Yehova”

MLONGO wina dzina lake Diana, yemwe ali ndi zaka zoposa 80, mwamuna wake anamwalira. Mwamunayo anali ndi matenda a mu ubongo ndipo ankakhala kunyumba yosamalira okalamba kwa zaka zingapo asanamwalire. Ana ake awiri anamwaliranso ndipo iyeyo anapezeka ndi khansa ya m’mawere. Koma abale ndi alongo amumpingo wake akamuona ku Nyumba ya Ufumu kapena mu utumiki amaona kuti ndi munthu wansangala.

M’bale wina dzina lake John anakhala woyang’anira woyendayenda kwa zaka zoposa 43. Iye ankaukonda kwambiri utumiki wakewu. Koma wachibale wake atayamba kudwala iye anasiya utumikiwu kuti azikamusamalira. Panopa John akutumikira mumpingo wina. Anthu omudziwa akakumana naye pamisonkhano ikuluikulu amaona kuti sanasinthe ngakhale pang’ono. Iye amakhalabe wosangalala.

Kodi n’chiyani chimathandiza Diana ndi John kuti azikhala osangalala? Kodi zingatheke bwanji kuti anthu amene akukumana ndi mavuto aakulu azisangalala? Nanga zingatheke bwanji kuti munthu amene utumiki wake unatha azisangalalabe? Baibulo limatithandiza kuyankha mafunso amenewa chifukwa limati: “Wolungama adzakondwera mwa Yehova.” (Sal. 64:10) Kuti timvetse mfundo imeneyi tiyeni tikambirane zimene zimathandiza munthu kukhala wosangalala komanso zimene sizimuthandiza kukhala wosangalala.

CHISANGALALO CHOSAKHALITSA

Muyenera kuti mukudziwa zinthu zina zimene zimachititsa kuti munthu azisangalala. Mwachitsanzo, anthu amasangalala akamalowa m’banja, akakhala ndi mwana kapena akalandira utumiki watsopano. M’pake kuti zinthu zimenezi zimakhala zosangalatsa chifukwa Yehova ndi amene anaziyambitsa. Iye anakonza zoti anthu azikwatirana, azibereka komanso kuti azipatsidwa utumiki wosiyanasiyana.​—Gen. 2:18, 22; Sal. 127:3; 1 Tim. 3:1.

Koma nthawi zina chisangalalo chimenechi chimakhala chosakhalitsa. Mwachitsanzo, mwamuna kapena mkazi akhoza kuchita chigololo kapena kumwalira. (Ezek. 24:18; Hos. 3:1) Ana ena samvera makolo awo kapena Mulungu ndipo nthawi zina amachotsedwa mumpingo. Mwachitsanzo, ana a Samueli sanatumikire Yehova mokhulupirika. Komanso Davide analakwitsa zinthu kenako n’kukumana ndi mavuto m’banja mwake. (1 Sam. 8:1-3; 2 Sam. 12:11) Zinthu ngati zimenezi zimachititsa munthu kuti akhale wosasangalala.

Nawonso utumiki ukhoza kutha chifukwa cha matenda, udindo wa m’banja kapena kusintha kwa zinthu m’gulu la Yehova. Anthu ambiri amene izi zawachitikira amanena kuti utumiki wawo unkawasangalatsa ndipo amausowa.

Apa zikuonekeratu kuti chisangalalo chimene zinthu zimenezi zimabweretsa chikhoza kukhala cha nthawi yochepa. Ndiye kodi n’zotheka kukhalabe wosangalala ngakhale zinthu zitasintha? Inde. Tikutero chifukwa Samueli, Davide komanso anthu ena anakhalabe osangalala ngakhale pamene ankakumana ndi mayesero.

CHISANGALALO CHOKHALITSA

Yesu ankasangalala kwambiri. Paja Baibulo limanena kuti asanabwere padzikoli ankakhala “wosangalala pamaso [pa Yehova] nthawi zonse.” (Miy. 8:30) Koma atabwera padzikoli ankakumana ndi mavuto akuluakulu. Ngakhale zinali choncho, iye ankasangalala akamachita zimene Atate ake amafuna. (Yoh. 4:34) Nanga bwanji pa nthawi imene ankaphedwa? Baibulo limanena kuti: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo.” (Aheb. 12:2) Choncho tingachite bwino kukambirana mfundo ziwiri zokhudza chisangalalo chenicheni zimene Yesu anatchula.

Tsiku lina, ophunzira 70 anabwera akusangalala pochokera kokalalikira. Iwo ankasangalala chifukwa choti anachita zinthu zodabwitsa monga kutulutsa ziwanda. Koma Yesu anawauza kuti: “Musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:1-9, 17, 20) Apa ankatanthauza kuti kusangalatsa Yehova n’kofunika kwambiri ndipo kumabweretsa chimwemwe chambiri kuposa utumiki wina uliwonse wapadera.

Tsiku lina Yesu akuphunzitsa mwaluso, mayi wina wachiyuda ananena kuti mayi ake a Yesu ayenera kuti anali osangalala kwambiri. Koma Yesu ananena kuti: “Ayi, m’malomwake, Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” (Luka 11:27, 28) N’zoona kuti kukhala ndi mwana wanzeru n’kosangalatsa koma kukhala pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa chomumvera n’kumene kumasangalatsa kwambiri.

Anthufe timakhala osangalala tikazindikira kuti zochita zathu zikusangalatsa Yehova. Chisangalalo choterechi sichitha ngakhale titakumana ndi mavuto. Ndipo munthu akakhalabe wokhulupirika pa nthawi ya mavuto amamva bwino mumtima mwake. (Aroma 5:3-5) Yehova amaperekanso mzimu wake kwa anthu amene amamudalira ndipo chimwemwe ndi khalidwe lina limene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22) M’pake kuti lemba la Salimo 64:10 limanena kuti: “Wolungama adzakondwera mwa Yehova.”

Kodi n’chiyani chinathandiza John kuti azikhalabe wosangalala?

N’chifukwa chake Diana ndi John, amene tawatchula kumayambiriro aja, amakhalabe osangalala ngakhale kuti akumanapo ndi mavuto akuluakulu. Diana anati: “Ndimadalira kwambiri Yehova ngati mmene mwana amachitira ndi makolo ake.” Kodi n’chiyani chimamuthandiza kuzindikira kuti akusangalatsa Yehova? Iye anati: “Ndimaona kuti Yehova akundidalitsa chifukwa ndimalalikirabe mosangalala.” Nayenso John atasiya utumiki woyendayenda, ankalalikirabe mwakhama. Pofotokoza zimene zinamuthandiza ananena kuti: “Kungoyambira mu 1998 pamene ndinali mlangizi wa Sukulu Yophunzitsa Utumiki, ndakhala ndikuphunzira mwakhama pandekha.” Pofotokoza za iyeyo ndi mkazi wake anati: “Mtima wofuna kutumikira Yehova m’njira iliyonse ndi umene watithandiza kuti tisavutike kwambiri pamene zinthu zasintha. Sitikunong’oneza bondo ngakhale pang’ono.”

Pali anthu ambiri amene aona kuti mawu a pa Salimo 64:10 ndi oona. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi banja lina limene linatumikira pa Beteli ya ku United States kwa zaka zoposa 30. Iwo anapemphedwa kuti apite kukachita upainiya wapadera. Iwo anati: “Zinthu zimene umazikonda kwambiri zikatha sulephera kudandaula koma umangofunika kuvomereza zimene zachitikazo.” Atangofika kugawo lawo latsopano anayamba kulalikira mwakhama ndi mpingo ndipo anati: “Tikamapemphera kwa Yehova tinkatchula zinthu zenizeni zimene tikufuna. Ndiyeno tikaona kuti mapemphero athu akuyankhidwa tinkasangalala komanso kulimbikitsidwa. Pasanapite nthawi yaitali, anthu ena mumpingowo anayambanso upainiya komanso tinapeza maphunziro awiri abwino kwambiri.”

‘TIDZASANGALALA KWAMUYAYA’

N’zoona kuti kukhala osangalala nthawi zonse si kophweka chifukwa nthawi zina timakhumudwa. Koma Yehova amatilimbitsa mtima ndi mawu a pa Salimo 64:10. Ngakhale pamene takhumudwa, sitikayikira zoti tikakhalabe anthu ‘olungama’ pa nthawi yovuta, ‘tidzakondwera mwa Yehova.’ Komanso timayembekezera kuti lonjezo la Mulungu la “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” lidzakwaniritsidwa. Pa nthawi imeneyo uchimo wonse udzatheratu. Anthu a Mulungu onse ‘adzakondwera ndiponso kusangalala kwamuyaya’ chifukwa cha zimene Mulungu adzachite.​—Yes. 65:17, 18.

Zimenezi zikutanthauza kuti tidzakhala angwiro ndipo tsiku lililonse tizidzadzuka tili amphamvu kwambiri. Kaya panopa tikupanikizika ndi mavuto otani, zonsezo zidzaiwalika. Paja Baibulo limati: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” Anzathu amene anamwalira adzaukutsidwanso. Anthu mamiliyoni ambiri ‘adzasangalala kwambiri’ ngati mmene anachitira makolo a mtsikana wazaka 12 yemwe Yesu anamuukitsa. (Maliko 5:42) Pa mapeto pake, munthu aliyense padzikoli adzakhala “wolungama” weniweni ndipo “adzakondwera mwa Yehova” mpaka kalekale.