Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

‘Yehova Watichitira Zinthu Zabwino’

‘Yehova Watichitira Zinthu Zabwino’

INE ndi mkazi wanga dzina lake Danièle tinali titangofika kumene kuhotelo pamene wolandira alendo ananena kuti, “Abwana, mungaimbire foni kupolisi?” Maola ochepa apitawo tinali titangofika kumene m’dziko la Gabon ku West Africa kumene ntchito yathu inali yoletsedwa m’ma 1970.

Danièle, yemwe anali wochangamuka, anandinong’oneza kuti, “Musawaimbire apolisiwo afika kale.” Ndiye kumbuyo kwathu kunafika galimoto ya apolisi. Kenako anatigwira tonse. Popeza Danièle anandichenjeza, ndinali ndi mpata wopereka mapepala ena kwa m’bale wina.

Popita kupolisi ndinkaganizira mwayi umene ndili nawo wokhala ndi mkazi wauzimu komanso wolimba mtima. Aka sikanali koyamba kuti ine ndi Danièle tichitire limodzi zinthu mogwirizana. Mwina ndikufotokozereni zimene zinachititsa kuti tizipita kumayiko amene ntchito yathu inali yoletsedwa.

YEHOVA ANANDITSEGULA MASO

Ndinabadwa mu 1930 kutauni ya Croix, kumpoto kwa France, ndipo makolo anga anali a Katolika. Banja lathu linkachita nawo misa mlungu uliwonse ndipo bambo anga anali ndi udindo kutchalitchiko. Komabe ndili ndi zaka 14, kutchalitchi kunachitika zinthu zina zimene zinandichititsa kuti ndiyambe kukayikira chipembedzochi.

Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, asilikali a ku Germany analowa m’dziko la France. Ndiye wansembe wathu akamalalikira, ankatilimbikitsa kuti tikhale kumbali ya Nazi. Zimene ankanenazi zinkatidabwitsa kwambiri. Pa nthawiyo tinkakonda kumvetsera mozemba nkhani za pa wailesi ya BBC, yomwe inkaulutsa nkhani zochokera kumayiko omwe ankamenyana ndi dziko la Germany. Kenako wansembeyo anasintha mwadzidzidzi n’kukonza mwambo mu September 1944 wosangalala kuti asilikali omenyana ndi dziko la Germany anayamba kupambana. Zimenezi zinandidabwitsanso ndipo ndinasiya kukhulupirira ansembe.

Patangopita nthawi yochepa nkhondo itatha, bambo anga anamwalira. Pa nthawiyo mchemwali wanga wamkulu anali atakwatiwa ndipo ankakhala ku Belgium. Choncho ndinaona kuti ndinali ndi udindo wosamalira mayi anga. Kenako ndinapeza ntchito pa kampani ina. Abwana anga komanso ana awo anali a Katolika odzipereka kwambiri. Ngakhale kuti zinthu zinkandiyendera ku ntchitoko, ndinakumana ndi mayesero.

Mchemwali wanga wamkulu uja anabwera kudzationa mu 1953, ndipo anali atakhala wa Mboni. Iye anagwiritsa ntchito Baibulo lake mwaluso posonyeza kuti tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa zabodza pa nkhani yakuti anthu oipa amapita kumoto, pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi komanso kuti pali chinachake m’thupi mwa munthu chimene sichifa. Poyamba ndinkachita makani kuti sakugwiritsa ntchito Baibulo la Katolika, koma kenako ndinakhulupirira kuti akundiuza zoona. Tsiku lina anandibweretsera magazini akale a Nsanja ya Olonda ndipo ndinkawawerenga kwambiri kuchipinda changa usiku. Ndinazindikira mwamsanga kuti zimene ndinkawerengazo zinali zoona, koma ndinkaopa kuti ndikakhala wa Mboni za Yehova abwana anga andichotsa ntchito.

Ndinapitiriza kuwerenga Baibulo komanso Nsanja ya Olonda kwa miyezi ingapo. Patapita nthawi, ndinapita ku Nyumba ya Ufumu. Ndinakhudzidwa kwambiri ndi chikondi chimene anthu ankasonyezana. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi m’bale wina amene anali wodziwa zambiri. Nditaphunzira kwa miyezi 6, ndinabatizidwa mu September 1954. Kenako mayi anga ndi mchemwali wanga wamng’ono anakhalanso a Mboni ndipo ndinasangalala kwambiri.

TINKADALIRA YEHOVA POCHITA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE

N’zomvetsa chisoni kuti mayi anga anamwalira patangotsala milungu ingapo kuti msonkhano wamayiko wa mu 1958 uyambe. Msonkhanowu unachitikira ku New York ndipo ndinali ndi mwayi wopezekako. Nditabwerera kwathu panalibenso munthu wina amene ndinkayenera kumusamalira. Choncho ndinasiya ntchito n’kuyamba kuchita upainiya. Pa nthawi imeneyi, ndinafunsira mlongo wina dzina lake Danièle Delie, yemwe anali mpainiya wodzipereka, ndipo tinakwatirana mu May 1959.

Danièle ankachita upainiya kudera lakumidzi ku Brittany komwe kunali kutali kwambiri ndi kwawo. Iye ankafunika kulimba mtima kuti azilalikira kudera la a Katolika ambiri komanso kuti aziyenda pa njinga kukalalikira kumadera akutali. Mofanana ndi ine, Danièle ankaona kuti tinkayenera kulalikira mwamsanga chifukwa tinkaona kuti mapeto ali pafupi kwambiri. (Mat. 25:13) Iye anali ndi mtima wodzipereka kwambiri ndipo zimenezi zinatithandiza kupitiriza utumiki wa nthawi zonse.

Patangopita masiku ochepa titakwatirana, tinapatsidwa utumiki woyang’anira dera. Tinayesetsa kuti tizikhala moyo wosalira zambiri. Mpingo woyamba umene tinachezera unali ndi ofalitsa 14 ndipo abalewo sakanakwanitsa kutilandira kunyumba zawo. Choncho tinkagona papulatifomu m’Nyumba ya Ufumu. Sikuti tinkagona bwino kwenikweni koma zinkathandiza misana yathu.

Tinkayenda pa kagalimoto kathu kakang’ono poyendera mipingo

Ngakhale kuti tinkatanganidwa kwambiri, Danièle anazolowera utumiki watsopanowu. Nthawi zambiri pankachitika misonkhano ya akulu yadzidzidzi. Choncho iye ankayenera kundidikira m’kagalimoto kathu mpaka nditamaliza misonkhanoyo, koma sankadandaula. Tinachita utumiki woyang’anira dera kwa zaka ziwiri zokha koma tinaphunzira kuti anthu a pa banja ayenera kumakambirana momasuka komanso kuchita zinthu mogwirizana.​—Mlal. 4:9.

TINAPATSIDWA UTUMIKI WATSOPANO

Mu 1962, tinaitanidwa kuti tikalowe nawo kalasi ya nambala 37 ya Sukulu ya Giliyadi ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Kalasiyi inatenga miyezi 10. M’kalasiyo munali ophunzira 100 koma panali mabanja 13 okha. Choncho ndinaona kuti unali mwayi waukulu kulowa sukuluyi limodzi ndi mkazi wanga. Ndimakumbukirabe kuti tinali ndi mwayi wocheza ndi abale olimba mwauzimu monga Frederick Franz, Ulysses Glass ndi Alexander H. Macmillan.

Tinasangalala kwambiri kupita limodzi ku Sukulu ya Giliyadi

Pa nthawi yomwe tinali kusukuluyi, ankatiphunzitsa kuti tizichita chidwi ndi zinthu. Masiku ena Loweruka masana tikaweruka, tinkapita kukaona zinthu mumzinda wa New York. Tinkadziwa kuti Lolemba tikalemba mayeso okhudza zimene tinaona. Nthawi zambiri tinkakhala titatopa tikamabwerera kunyumba Loweruka madzulo. Komabe munthu wa pa Beteli amene ankatisonyeza zinthu ankatifunsa mafunso okhudza zimene taona potithandiza kuti tikhoze bwino mayesowo. Loweruka lina tinayendayenda masana onse mumzindawo ndipo tinapita kumalo enaake kumene tinaphunzira kusiyana pakati pa miyala ina imene imayenda m’mlengalenga. Kumyuziyamu ina tinaphunzira kusiyana pakati pa ng’ona ndi nyama ina yofanana nayo. Titabwerera ku Beteli, munthu amene ankatisonyeza zinthu uja anatifunsa kuti, “Kodi miyala yoyenda m’mlengalenga ija imasiyana bwanji?” Ndiye Danièle atatopa anangomuyankha kuti, “Ina imakhala ndi mano aatali.”

Tinkasangalala kuyendera abale ndi alongo athu okhulupirika ku Africa

Anatitumiza kunthambi ya ku France ndipo sitinkayembekezera. Tinatumikira kumeneko zaka zoposa 53. Mu 1976, ndinaikidwa kukhala wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi komanso tinapemphedwa kuti tikayendere mayiko ena a ku Africa ndi ku Middle East kumene ntchito yathu inali yoletsedwa. N’chifukwa chake tinapita ku Gabon kumene tinakumana ndi zimene ndinafotokoza kumayambiriro zija. Kunena zoona, nthawi zina ndinkaona ngati sindingakwanitse maudindo ngati amenewa. Koma mkazi wanga ankandithandiza kwambiri kuti ndizigwira bwino ntchito iliyonse imene ndapatsidwa.

Ndikumasulira nkhani ya M’bale Theodore Jaracz pamsonkhano wakuti “Chilungamo Chaumulungu” womwe unachitikira ku Paris mu 1988

TINAKUMANA NDI VUTO LALIKULU

Tinasangalala kwambiri kutumikira ku Beteli. Popeza Danièle anaphunzira Chingelezi kwa miyezi 5 tisanapite ku Giliyadi, anakhala womasulira mabuku waluso. N’zoona kuti tinkasangalala kugwira ntchito pa Beteli koma kuchita zinthu ndi mpingo wathu kunatithandiza kukhala osangalala kwambiri. Ndikukumbukira kuti nthawi ina tinachititsa maphunziro a Baibulo abwino kwambiri moti tinabwerera ku Beteli usiku. Tinali titatopa koma tinkasangalala kwambiri. Kenako Danièle anayamba kudwala ndipo ankalephera kuchita zambiri.

Mu 1993 anamupeza ndi khansa ya m’mawere. Iye anapangidwa opaleshoni ndipo analandira mankhwala amphamvu kwambiri. Koma patapita zaka 15, anamupezanso ndi khansa yoopsa kwambiri. Popeza ankakonda kwambiri ntchito yake yomasulira mabuku, anayambiranso kugwira ntchito atangopezako bwino.

Ngakhale kuti Danièle ankadwala kwambiri, sitinaganizepo zochoka pa Beteli. Koma kudwala kwambiri muli pa Beteli kumavuta, makamaka ngati anthu ena sakudziwa kukula kwa matenda anu. (Miy. 14:13) Ngakhale pamene Danièle anali ndi zaka za m’ma 70, sankaoneka kuti akudwala chifukwa anali wansangala komanso wodzilimbitsa. Iye sankangokhalira kudandaula koma ankakonda kuthandiza anthu ena. Ankadziwa kuti kumvetsera anthu akamamuuza mavuto awo kungawathandize kwambiri. (Miy. 17:17) Sikuti Danièle ankadziona kuti ndi mlangizi kungoti ankayesetsa kuthandiza alongo ena kuti asamaope matenda a khansa.

Tinaphunzira kupirira mavuto athuwo. Danièle anafika poti sankakwanitsanso kugwira ntchito tsiku lonse koma ankayesetsabe kundithandiza m’njira zosiyanasiyana. Iye ankandichitira zinthu zambiri ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndikhale wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi kwa zaka 37. Mwachitsanzo, ankakonza zoti tizidya limodzi kunyumba yathu masana n’cholinga choti tizipuma uku tikucheza.​—Miy. 18:22.

SITINKADERA NKHAWA ZA TSIKU LOTSATIRA

Danièle sanasiye kukhala ndi maganizo abwino komanso sankataya mtima. Koma kenako anamupezanso ndi khansa kachitatu. Zimenezi zinatikhumudwitsa kwambiri. Chithandizo cha mankhwala chimene ankalandira chinali champhamvu kwambiri moti nthawi zina ankalephera kuyenda. Ndinakhumudwa kwambiri kuona kuti mkazi wanga, yemwe anali katswiri pa ntchito yomasulira mabuku, akuvutika kutchula mawu.

Ngakhale kuti tinakhumudwa kwambiri, tinkapemphera kwa Yehova nthawi zonse. Ndipo sitinkakayikira kuti sangalole kuti tikumane ndi mavuto amene sitingathe kuwapirira. (1 Akor. 10:13) Nthawi zonse tinkayesetsa kuti tiziyamikira mmene Yehova ankatithandizira kudzera m’Mawu ake, ogwira ntchito kuchipatala cha ku Beteli komanso abale ndi alongo ena.

Nthawi zambiri tinkapempha Yehova kuti atithandize kusankha chithandizo cha mankhwala choyenera. Danièle anafika pomakomoka akangolandira chithandizo cha mankhwala. Dokotala amene anakhala akumuthandiza kwa zaka 23 sankadziwa chimene chinkachititsa zimenezi ndipo sanapeze njira ina yomuthandizira. Choncho pa nthawi ina Danièle sankalandira chithandizo cha mankhwala chilichonse. Tinkaona kuti tilibiretu mtengo wogwira ndipo sitinkadziwa kuti zitithera bwanji. Kenako dokotala wina wa matenda a khansa ananena kuti akhoza kumuthandiza. Apa tinaona kuti Yehova watithandiza kuti tithane ndi nkhawa zathu.

Tinkayesetsa kuti tisamadere nkhawa za tsiku lotsatira. Paja Yesu anati: “Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.” (Mat. 6:34) Chinthu china chomwe chinatithandiza ndi kuchitako tinthabwala komanso kupewa kumangodandaula. Mwachitsanzo, pa nthawi imene Danièle sankalandira chithandizo cha mankhwala kwa miyezi iwiri, anandiuza uku akumwetulira kuti, “Panopa ndikumva bwino kuposa m’mbuyo monsemu.” (Miy. 17:22) Ngakhale kuti ankavutika ndi matendawa, iye ankakonda kwambiri kuimba nyimbo za Ufumu zatsopano ndipo ankaimba mochokera pansi pa mtima.

Danièle ankayesetsa kukhala wansangala ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndipirire mavuto amene tinkakumana nawo. Kunena zoona, iye ankandithandiza kwambiri pa zaka zonse 57 zimene tinakhala pa banja. Sankalola kuti ndiziphika ngakhale zinthu zosavuta ngati mazira. Choncho atadwala kwambiri, ndinayenera kuphunzira kutsuka mbale, kuchapa komanso kuphika. Pochita zimenezi, ndinaswa matambula angapo koma ndinkasangalala kuti ndikuyesetsa kumuthandiza. *

NDIMATHOKOZA YEHOVA CHIFUKWA CHONDIKOMERA MTIMA

Ndikuona kuti ndaphunzira zinthu zofunika chifukwa chokumana ndi mavuto monga matenda komanso ukalamba. Choyamba, ndaphunzira kuti sitiyenera kutanganidwa kwambiri moti n’kukanika kupeza nthawi yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wathu. Tiyenera kugwiritsa ntchito nthawi yathu tidakali ndi mphamvu posamalira ndiponso kusangalala ndi anthu amene timawakonda. (Mlal. 9:9) Chachiwiri, sitiyenera kudera nkhawa zinthu zing’onozing’ono chifukwa zingatilepheretse kuzindikira madalitso amene tikulandira tsiku ndi tsiku.​—Miy. 15:15.

Ndikaganizira kuti takhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa nthawi yaitali, ndimaona kuti tadalitsidwa kwambiri ndi Yehova kuposa mmene tinkayembekezera. Ndimakhala ndi maganizo ofanana ndi a wolemba masalimo amene anati: ‘Yehova wandichitira zinthu zabwino.’​—Sal. 116:7.

^ ndime 32 Mlongo Danièle Bockaert anamwalira ali ndi zaka 78 pamene nkhaniyi inkakonzedwa.