Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 50

“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”

“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”

“Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”​—1 AKOR. 15:55.

NYIMBO NA. 141 Moyo Ndi Wodabwitsa

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera kukhala ndi chidwi ndi nkhani ya kuukitsidwa kwa anthu amene adzapite kumwamba?

ANTHU ambiri amene akutumikira Yehova panopa akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale. Koma Akhristu ochepa omwe anadzozedwa ndi Yehova akuyembekezera kudzaukitsidwa n’kupita kumwamba. Akhristu odzozedwawa amafunitsitsa kudziwa kuti moyo wawo udzakhala wotani kumwamba. Koma kodi n’chifukwa chiyani amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi amafunikiranso kudziwa zimenezi? Monga mmene tionere, kuukitsidwa kwa anthu opita kumwamba kudzabweretsanso madalitso kwa anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale. Choncho kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi, tiyenera kukhala ndi chidwi ndi kuukitsidwa kwa anthu amene adzapite kumwamba.

2 M’nthawi ya atumwi, Mulungu anathandiza ophunzira ena a Yesu kuti alembe zokhudza anthu amene akuyembekezera kupita kumwamba. Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Tsopano ndife ana a Mulungu, koma padakali pano sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani. Tikudziwa kuti akadzaonekera, tidzakhala ngati iyeyo.” (1 Yoh. 3:2) Choncho Akhristu odzozedwa, sakudziwa kuti adzakhala otani akadzaukitsidwa kuti akakhale kumwamba ndi matupi auzimu. Komabe iwo akadzalandira mphoto yawo adzatha kumuona Yehova. Baibulo silimatifotokozera zonse zokhudza kuukitsidwa kwa anthu omwe adzapite kumwamba. Koma mtumwi Paulo anatifotokozera zina zokhudza nkhani imeneyi. Odzozedwa adzakhala ndi Khristu akamadzathetsa “maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.” Zimenezi zikuphatikizaponso kuthetsa imfa “monga mdani womalizira.” Pamapeto pake Yesu adzaika zinthu zonse kuphatikizapo iyeyo ndi amene adzalamulire naye limodzi, pansi pa Yehova. (1 Akor. 15:24-28) Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. *

3. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 15:30-32, kodi zimene Paulo ankakhulupirira zoti akufa adzaukitsidwa zinamuthandiza bwanji?

3 Paulo anakwanitsa kupirira mavuto osiyanasiyana chifukwa choti ankakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa. (Werengani 1 Akorinto 15:30-32.) Iye anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Tsiku ndi tsiku ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa.” Paulo analembanso kuti: “Ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso.” N’kutheka kuti iye ankanena zomenyana ndi zilombo zenizeni m’bwalo la masewera ku Efeso. (2 Akor. 1:8; 4:10; 11:23) Kapenanso ankanena za Ayuda ndi anthu ena ankhanza amene anali ngati “zilombo zakutchire.” (Mac. 19:26-34; 1 Akor. 16:9) Kaya ankanena za chiyani, Paulo anakumana ndi mavuto aakulu komabe ankakhulupirira kuti m’tsogolo adzakhala ndi moyo wosangalala.​—2 Akor. 4:16-18.

Banja lina lomwe limakhala m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa, likupitirizabe kuchita zinthu zonse zokhudza kulambira ndipo akukhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa zinthu zabwino zomwe analonjeza (Onani ndime 4)

4. Kodi Akhristu amalimbikitsidwa bwanji masiku ano chifukwa choyembekezera kuti akufa adzauka? (Onani chithunzi chapachikuto.)

4 Tikukhala mu nthawi yoopsa. Abale athu ena achitiridwa zinthu zankhanza. Ena akukhala m’madera omwe mukuchitika nkhondo ndipo amaona kuti ndi osatetezeka. Pamene m’mayiko ena anthu a Yehova alibe ufulu wolalikira koma amamutumikirabe ngakhale kuti akudziwa kuti akhoza kumangidwa kapena kuphedwa. Abale ndi alongo onsewa akupitirizabe kulambira Yehova ndipo ndi zitsanzo zabwino kwambiri kwa ife. Iwo sachita mantha chifukwa akudziwa kuti ngakhale atafa panopa, Yehova akulonjeza kuti adzawapatsa zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo.

5. Kodi ndi maganizo oopsa ati amene angatipangitse kuti tisiye kukhulupirira kuti akufa adzauka?

5 Paulo anachenjeza abale ake kuti apewe maganizo oopsa omwe anthu ena anali nawo, akuti: “Ngati akufa sadzauka, ‘tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’” Ndipotu anthu ena anali ndi maganizo amenewa ngakhale nthawi ya Paulo isanafike. N’kutheka kuti iye ananena mawu opezeka pa Yesaya 22:13, amene akufotokoza maganizo omwe Aisiraeli anali nawo. M’malo molimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu, iwo ankakonda zinthu zosangalatsa. Tinganene kuti Aisiraeliwo anali ndi maganizo akuti, ‘Tisangalaliretu ndi moyo panopa chifukwa tikhoza kufa nthawi iliyonse.’ Maganizo amenewa ndi ofalanso masiku ano. Koma Baibulo limafotokoza zinthu zoipa zimene zinachitikira mtundu wa Isiraeli chifukwa cha maganizo olakwika omwe anali nawowa.​—2 Mbiri 36:15-20.

6. Kodi kukhulupirira kuti akufa adzauka kumatithandiza bwanji kusankha bwino ocheza nawo?

6 Tikudziwa kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira ndipo zimenezi ziyenera kutithandiza kusankha bwino anthu ocheza nawo. Abale a ku Korinto ankafunika kupewa kucheza ndi anthu amene ankatsutsa zoti akufa adzauka. Pamenepa phunziro kwa ife ndi lakuti: Tikamacheza kwambiri ndi anthu amene saganizira zam’tsogolo koma amangoganizira zinthu zosangalatsa, angatisokoneze. Ngati Mkhristu weniweni atamacheza ndi anthu amenewa, angayambe kutengera maganizo ndi makhalidwe oipa. Ndipotu anthu amenewa angamuchititse kuti ayambe kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. N’chifukwa chake Paulo akutilimbikitsa kuti: “Dzukani ku tulo tanu kuti mukhale olungama ndipo musamachite tchimo.”​—1 Akor. 15:33, 34.

KODI ADZAUKA NDI THUPI LOTANI?

7. Malinga ndi 1 Akorinto 15:35-38, kodi anthu ena ayenera kuti anali ndi funso lotani pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa?

7 Werengani 1 Akorinto 15:35-38. Munthu yemwe akufuna kuti ena azikayikira zoti akufa adzaukitsidwa angafunse kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa motani?” Tingachite bwino kuganizira yankho limene Paulo anapereka chifukwa anthu ambiri masiku ano, amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Koma kodi Baibulo limati chiyani?

Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha njere ndi mbewu, Paulo anasonyeza kuti Mulungu adzapereka matupi oyenerera kwa anthu omwe adzaukitsidwe (Onani ndime 8)

8. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe chikutithandiza kumvetsa kuukitsidwa kwa anthu amene amapita kumwamba?

8 Munthu akamwalira, thupi lake limawola. Koma amene analenga chilengedwe chonsechi, angathe kuukitsa munthu ameneyo n’kumupatsa thupi loyenerera. (Gen. 1:1; 2:7) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo posonyeza kuti Mulungu sadzafunika kuukitsa munthu ndi thupi limene anali nalo poyamba. Taganizirani za njere kapena “mbewu chabe”. Njere ikadzalidwa munthaka imamera n’kukhala mbewu. Mbewu imene yamerayo imakhala yosiyana kwambiri ndi njere imene tinadzala ija. Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi posonyeza kuti Mlengi angapereke “thupi monga mwa kufuna kwake.”

9. Kodi lemba la 1 Akorinto 15:39-41, limanena kuti matupi amasiyana bwanji?

9 Werengani 1 Akorinto 15:39-41. Palembali Paulo anafotokoza kuti Mulungu analenga matupi osiyanasiyana. Mwachitsanzo, matupi a ng’ombe, mbalame ndi nsomba, onse ndi osiyana. Ananenanso kuti kumwamba timaona kuti dzuwa ndi losiyana ndi mwezi. Iye anati: “Ulemerero wa nyenyezi ina, umasiyana ndi ulemerero wa inzake.” Zimenezi n’zoona, ngakhale kuti ndi maso athu sitingathe kuona kusiyana kumeneku. Asayansi amanena kuti pali nyenyezi zosiyanasiyana. Zina ndi zazikulu, zina zazing’ono, zina zofiira, zina zoyera ndipo zina ndi zayelo ngati dzuwa. Paulo ananenanso kuti “Palinso matupi akumwamba, ndi matupi apadziko lapansi.” Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa? Iye ankatanthauza kuti padzikoli tili ndi matupi a nyama koma kumwamba kuli matupi auzimu ngati amene angelo ali nawo.

10. Kodi anthu amene amaukitsidwa kuti apite kumwamba amakhala ndi matupi otani?

10 Onani zimene Paulo kenako ananena. Iye anati: “Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa. Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka.” Tikudziwa kuti munthu akafa, thupi lake limawola ndipo amabwerera kufumbi. (Gen. 3:19) Ndiye akutanthauza chiyani akamanena kuti “limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka”? Apa Paulo sankanena za anthu amene amaukitsidwa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi, ngati amene Eliya, Elisa komanso Yesu anawaukitsa. Iye ankanena za munthu amene amaukitsidwa ndi “thupi lauzimu” lomwe lingathe kukakhala kumwamba.​—1 Akor. 15:42-44.

11-12. Kodi Yesu anaukitsidwa ndi thupi lotani, nanga Akhristu odzozedwa amaukitsidwa ndi matupi otani?

11 Yesu ali padziko lapansili, anali ndi thupi lanyama koma ataukitsidwa anakhala “mzimu wopatsa moyo” ndipo anabwerera kumwamba. Mofanana ndi Yesu, Akhristu odzozedwa amaukitsidwa ndi matupi amene angathe kukakhala kumwamba. Paulo ananena kuti: “Monga tilili m’chifaniziro cha wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’chifaniziro cha wakumwambayo.”​—1 Akor. 15:45-49.

12 Tiyenera kukumbukira kuti Yesu sanaukitsidwe ndi thupi lanyama. Chakumapeto kwa nkhani yakeyi, Paulo anafotokoza chifukwa chake. Iye anati: “Mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu” kumwamba. (1 Akor. 15:50) Atumwi komanso Akhristu odzozedwa saukitsidwa n’kupita kumwamba ndi matupi a nyama ndi magazi omwe angathe kuwola. Koma kodi anayamba kuukitsidwa liti? Pa nthawiyo, Paulo ananena kuti kuukitsidwa kumeneku kudzachitika m’tsogolo osati nthawi yomweyo akangomwalira. Pamene Paulo ankalemba buku la 1 Akorinto, ophunzira ena anali ‘atagona mu imfa.’ Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Yakobo. (Mac. 12:1, 2) Pambuyo pake, atumwi ndi odzozedwa enanso “anagona mu imfa.”​—1 Akor. 15:6.

IMFA IDZAGONJETSEDWA

13. Kodi n’chiyani chidzachitike “pa nthawi ya kukhalapo” kwa Khristu?

13 Yesu komanso Paulo ananeneratu za nthawi yofunika, yomwe ndi nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristuyi pakuchitika nkhondo, zivomezi, miliri ndi zinthu zina zoipa zimene zikuchitika padziko lonse. Kuyambira mu 1914, takhala tikuona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulowu. Koma pali mbali inanso yofunika yosonyeza kukhalapo kwa Khristu. Yesu ananena kuti uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira, udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:3, 7-14) Paulo ananena kuti “pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye” m’pamenenso Akhristu odzozedwa amene ‘akugona mu imfa,’ adzaukitsidwe.​—1 Ates. 4:14-16; 1 Akor. 15:23.

14. Kodi n’chiyani chimachitikira Akhristu odzozedwa omwe akumwalira pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?

14 Panopa Akhristu odzozedwa akamwalira, nthawi yomweyo amaukitsidwa n’kupita kumwamba. Mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 15:51, 52, akutsimikizira zimenezi. Iye anati: “Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza.” Mawu a Paulowa akukwaniritsidwa panopa. Abale a Khristuwa akaukitsidwa, amasangalala kwambiri ndipo ‘amakakhala ndi ambuye nthawi zonse.’​—1 Ates. 4:17.

Anthu amene amasandulika “m’kuphethira kwa diso” adzamenya nkhondo ndi Yesu powononga anthu onse oipa padzikoli (Onani ndime 15)

15. Kodi amene adzasandulike “m’kuphethira kwa diso,” adzagwira ntchito yotani?

15 Baibulo limatiuza ntchito imene anthu amene adzasandulike “m’kuphethira kwa diso,” adzagwire akapita kumwamba. Yesu anawauza kuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo, ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.” (Chiv. 2:26, 27) Iwo adzatsatira Mtsogoleri wawo Yesu ndipo adzakusa mitundu ya anthu ndi ndodo yachitsulo.​—Chiv. 19:11-15.

16. Kodi anthu ambiri adzagonjetsa bwanji imfa?

16 Apa n’zoonekeratu kuti Akhristu odzozedwa adzagonjetsa imfa. (1 Akor. 15:54-57) Akadzaukitsidwa, iwo adzakhala ndi mwayi wogwira nawo ntchito yothetsa kuipa konse padziko lapansi pa nkhondo ya Aramagedo. Akhristu ena mamiliyoni ambiri ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu’ n’kulowa m’dziko latsopano. (Chiv. 7:14) Opulumukawo adzaona kugonjetsedwa kwinanso kwa imfa chifukwa anthu mabiliyoni amene anamwalira adzaukitsidwa. Tangoganizirani mmene tidzasangalalire kuona zinthu zodabwitsa zimenezi zikuchitika. (Mac. 24:15) Onse amene adzakhale okhulupirika kwa Yehova adzagonjetsanso imfa imene tinatengera kwa Adamu. Ndipo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

17. Kodi lemba la 1 Akorinto 15:58, limatilimbikitsa kuchita chiyani panopa?

17 Mkhristu aliyense ayenera kusangalala kwambiri ndi mawu olimbikitsa okhudza kuukitsidwa kwa akufa amene Paulo analembera Akhristu a ku Korinto. Tili ndi zifukwa zabwino zomvera malangizo a Paulo akuti tizichita zonse zimene tingathe “mu ntchito ya Ambuye.” (Werengani 1 Akorinto 15:58.) Tikamayesetsa kugwira nawo ntchitoyi mwakhama, tingayembekezere kudzasangalala ndi moyo m’tsogolo. Moyo umenewu udzakhala wosangalatsa kwambiri kuposa chilichonse chimene tingachiganizire panopa. Umenewu udzakhala umboni wakuti zonse zimene tikuchita mu ntchito ya Ambuye, sizinapite pachabe.

NYIMBO NA. 140 Tidzapeza Moyo Wosatha

^ ndime 5 Mbali yomaliza ya chaputala 15 cha buku la 1 Akorinto ikufotokoza za kuuka kwa akufa, makamaka kokhudza Akhristu odzozedwa. Koma zimene Paulo analemba m’chaputalachi n’zofunikanso kwa a nkhosa zina. Munkhaniyi, tiona mmene kuyembekezera kuti akufa adzauka kuyenera kukhudzira moyo wathu panopa komanso kutithandiza kuti tidzakhale osangalala m’tsogolo.

^ ndime 2Mafunso Ochokera kwa Owerenga” amene ali m’magaziniyi akufotokoza zimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 15:29.