Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Akhristu odzozedwa?

Tiyenera kutsanzira chikhulupiriro chawo. Komabe, sitiyenera kuchita nawo chidwi kwambiri. Tizipewa ‘kutamanda anthu ena.’ (Yuda 16) Tizipewanso kuwafunsa mafunso okhudza chiyembekezo chawo.​—w20.01, tsamba 29.

N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamakayikire kuti Yehova amakuwerengerani?

Baibulo limasonyeza kuti Iye anakuonani ngakhale musanabadwe. Komanso amamvetsera mapemphero anu. Amadziwa zimene zili mumtima mwanu komanso zimene mukuganiza, ndipo amakhudzidwa ndi zimene mumachita. (1 Mbiri 28:9; Miy. 27:11) Yehova wakukokani kuti mubwere kwa Iye.​—w20.02, tsamba 12.

Kodi ndi panthawi iti pamene tiyenera kulankhula, nanga ndi panthawi iti pamene tiyenera kukhala chete?

Timalankhula tikamauza ena mosangalala za Yehova. Timalankhulanso tikaona kuti zimene munthu wina akuchita zingamubweretsere mavuto. Akulu amalankhula akamaperekanso malangizo othandiza ngati pakufunika kutero. Sitimalankhula anthu akamatifunsa za ntchito yathu m’dziko limene muli bani. Komanso sitilankhula tikamapewa kuulula nkhani zomwe ndi zachinsinsi.​—w20.03, tsamba 20-21.

Kodi dzombe lotchulidwa mu Yoweli chaputala 2 limasiyana bwanji ndi dzombe lotchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 9?

Pa Yoweli 2:20-29 Yehova anati adzachotsa dzombe ndipo adzabwezeretsa zonse zimene dzombelo lawononga. Pambuyo pake Yehova anati adzapereka mzimu wake. Pa Chivumbulutso 9:1-11 amafotokoza za dzombe limene ndi atumiki a Yehova a masiku ano, omwe akulengeza kuti Mulungu adzaweruza dziko loipali. Uthengawu umachititsa kuti anthu a m’dzikoli asamasangalale nawo.​—w20.04, tsamba 3-6.

Kodi mfumu ya kumpoto ndi ndani masiku ano?

Dziko la Russia komanso mayiko ogwirizana nalo. Iwo akhala akuukira anthu a Mulungu poletsa ntchito yolalikira komanso kuzunza abale ndi alongo ambiri amene amakhala m’mayikowa. Mfumu ya kumpotoyi yakhala ikulimbana ndi mfumu ya kum’mwera.​—w20.05, tsamba 13.

Kodi makhalidwe amene ‘mzimu woyera umatulutsa’ ndi 9 okhawa amene amatchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23?

Ayi. Mzimu woyera umatithandiza kukhalanso ndi makhalidwe ena abwino, monga chilungamo. (Aef. 5:8, 9)​—w20.06, tsamba 17.

Kodi ndi ngozi inanso iti imene ingakhalepo tikamaika zinthu zokhudza ifeyo pa intaneti?

Zimene mumaika pa intaneti zingapangitse ena kuyamba kuona kuti ndinu onyada, osati odzichepetsa.​—w20.07, tsamba 6-7.

Kodi Akhristu angaphunzire chiyani kwa asodzi aluso?

Asodzi aluso amagwira ntchito yawo panthawi komanso pamalo amene nsomba zimapezeka. Amadziwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zoyenerera. Komanso amagwira ntchito molimba mtima, ngakhale pamene nyengo yasintha. Ifenso tiyenera kumachita zimenezi muutumiki wathu.​—w20.09, tsamba 5.

Kodi ndi njira zinanso ziti zimene tingathandizire ophunzira Baibulo kuti azikonda Yehova?

Tiziwalimbikitsa kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kuganizira mmene angagwiritsire ntchito mfundo zimene aphunzira. Tiziwaphunzitsanso kupemphera.​—w20.11, tsamba 4.

Kodi mawu a pa 1 Akorinto 15:22 akuti, “Momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo,” amanena za ndani?

Mtumwi Paulo sankatanthauza kuti wina aliyense amene anamwalira adzaukitsidwa. Apa iye ankanena za Akhristu odzozedwa amene “anayeretsedwa mwa Khristu Yesu.” (1 Akor. 1:2; 15:18)​—w20.12, tsamba 5-6.

Kodi odzozedwa adzatani ‘akadzasandulika, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza’?​—1 Akor. 15:51-53.

Iwo limodzi ndi Khristu adzakusa mitundu ya anthu ndi ndodo yachitsulo. (Chiv. 2:26, 27)​—w20.12, tsamba 12-13.