Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu a Paulo opezeka pa 1 Akorinto 15:29, akutanthauza kuti Akhristu ena kalelo ankabatizidwa m’malo mwa anthu akufa?

Ayi, tikutero chifukwa chakuti palibe paliponse m’Baibulo kapena m’mabuku a mbiri yakale, pamene pamasonyeza kuti zimenezi zinkachitika.

M’mene ma Baibulo ena amamasulirira lembali zimapangitsa anthu ena kuganiza kuti m’nthawi ya Akhristu oyambirira anthu ena ankabatizidwa m’malo mwa anthu amene anamwalira. Mwachitsanzo, Baibulo lina limati: “Ngati akufa saukitsidwa n’komwe, bwanji nanga anthu akubatizidwa m’malo mwawo?”​—Chipangano Chatsopano M’Chichewa Chalero.

Koma tiyeni tione zimene akatswiri ena awiri a Baibulo ananena. Dr.  Gregory Lockwood, ananena kuti: “Palibe umboni m’Baibulo kapena m’mabuku a mbiri yakale wosonyeza kuti winawake anabatizidwa m’malo mwa munthu amene anamwalira.” Nayenso Pulofesa Gordon D. Fee, analemba kuti: “Palibe umboni wa m’mbiri yakale kapena m’Baibulo wosonyeza kuti ubatizo ngati umenewu unkachitika. Chipangano Chatsopano sichifotokoza chilichonse chokhudza ubatizo umenewu. Komanso palibe umboni wosonyeza kuti Akhristu oyambirira kapena matchalitchi amene anayambika atumwi atamwalira, ankachita ubatizo umenewu.”

Baibulo limanena kuti otsatira a Yesu ankayenera ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake . . . , kuwabatiza . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse’ zimene iye anawalamula. (Mat. 28:19, 20) Choncho, kuti munthu abatizidwe n’kukhala wophunzira wa Yesu ankayenera kuphunzira za Yehova ndi Mwana wake, kuwakhulupirira komanso kuwamvera. Ndiye munthu amene wamwalira ndipo ali m’manda sakanatha kuchita zimenezi komanso Mkhristu wina amene ali moyo, sakanatha kumuchitira zimenezi.​—Mlal. 9:5, 10; Yoh. 4:1; 1 Akor. 1:14-16.

Ndiyeno kodi Paulo ankatanthauza chiyani?

Anthu ena a ku Korinto ankanena kuti akufa sadzaukitsidwa. (1 Akor. 15:12) Paulo anawasonyeza kuti maganizo amenewo anali olakwika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye anafotokoza kuti ‘tsiku ndi tsiku ankakhala pa ngozi yoti akhoza kufa.’ N’zoona kuti anali adakali ndi moyo. Koma ngakhale kuti ankakumana ndi zoopsa, sankakayikira kuti ngati atafa adzaukitsidwa kuti akakhale ndi moyo kumwamba ngati mmene zinakhalira ndi Yesu.​—1 Akor. 15:30-32, 42-44.

Akhristu a ku Korinto ankafunika kuzindikira kuti monga odzozedwa, ankayenera kukumana ndi mayesero tsiku ndi tsiku komanso kufa kenako n’kuukitsidwa. Choncho pamene ‘anabatizidwa n’kukhala mu mgwirizano ndi Khristu Yesu,’ ndiye kuti ‘anabatizidwanso mu imfa yake.’ (Aroma 6:3) Zimenezi zikutanthauza kuti mofanana ndi Yesu, nawonso ankayenera kukumana ndi mayesero kenako n’kufa kuti adzaukitsidwe n’kupita kumwamba.

Patadutsa zaka zoposa ziwiri kuchokera pamene Yesu anabatizidwa, anauza atumwi ake awiri kuti: “Mudzabatizidwadi ndi ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo.” (Maliko 10:38, 39) Apa Yesu sankatanthauza kubatizidwa ndi madzi. Iye ankatanthauza kuti kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kudzachititsa kuti aphedwe. Paulo analemba kuti Akhristu odzozedwa ‘adzavutika naye limodzi kuti akalandire ulemerero limodzi ndi iye.’ (Aroma 8:16, 17; 2 Akor. 4:17) Choncho, nawonso anayenera kufa kuti adzaukitsidwe n’kupita kumwamba.

Malinga ndi zimene takambiranazi mawu a Paulo palembali, tingawamasulire molondola kuti: “Apo ayi, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzatani? Ngati akufa sadzauka, n’chifukwa chiyani anthuwo akubatizidwa kuti akhale akufa?”