Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 49

Buku la Levitiko Limatiphunzitsa Mmene Tingachitire Zinthu ndi Ena

Buku la Levitiko Limatiphunzitsa Mmene Tingachitire Zinthu ndi Ena

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”​—LEV. 19:18.

NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi munkhani yapita ija tinakambirana chiyani, nanga tiphunzira chiyani munkhaniyi?

MUNKHANI yapita ija, tinakambirana malangizo ena othandiza opezeka mu Levitiko chaputala 19. Mwachitsanzo, monga tinaonera pavesi 3, Yehova analamula Aisiraeli kuti azilemekeza makolo awo. Tinakambirana mmene tingagwiritsire ntchito malangizo amenewa kuti tizisamalira makolo powagulira zinthu zofunika, kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Pavesi lomweli, anthu a Mulungu anakumbutsidwa kufunika kosunga Sabata. Tinaona kuti ngakhale kuti masiku ano sitikakamizidwa kusunga Sabata, mfundo zake zingatithandize kuti tiziyesetsa kupeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti tikufunitsitsa kukhala oyera, mogwirizana ndi mfundo ya pa Levitiko 19:2 komanso 1 Petulo 1:15.

2 Munkhaniyi, tipitiriza kukambirana Levitiko chaputala 19. Kodi mfundo zamuchaputalachi zingatiphunzitse chiyani pa nkhani yosonyeza kuti timaganizira anthu amene ali ndi mavuto ena pathupi lawo, kuchita zinthu moona mtima pa nkhani ya bizinezi komanso kukonda anzathu? Tikufuna kukhala oyera ngati mmene Mulungu alili, choncho tiyeni tione zimene tingaphunzire.

KUGANIZIRA ANTHU AMENE ALI NDI MAVUTO ENA PATHUPI LAWO

Kodi lemba la Levitiko 19:14, limatilimbikitsa kuti tiziwaona bwanji anthu amene ali ndi vuto losamva kapena losaona? (Onani ndime 3-5) *

3-4. Mogwirizana ndi Levitiko 19:14, kodi Aisiraeli ankafunika kuchita bwanji zinthu ndi anthu omwe ali ndi vuto losamva komanso osaona?

3 Werengani Levitiko 19:14. Yehova ankayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu moganizira anthu omwe ali ndi mavuto pathupi lawo. Mwachitsanzo, Aisiraeli sankayenera kutemberera munthu amene ali ndi vuto losamva. Kutemberera kumeneku kunkaphatikizapo kumuopseza kapena kulankhula mawu omufunira zoipa. Kumenekutu kunali kumuchitira zinthu zoipa kwambiri munthu ameneyu. Iye sakanamva zinthu zomwe zanenedwa zokhudza iyeyo ndipo sakanatha kudziteteza.

4 Kuwonjezera pamenepo, muvesi 14 timaphunzira kuti atumiki a Mulungu sankafunika ‘kuikira munthu wakhungu chinthu chopunthwitsa.’ Ponena za anthu omwe ali ndi mavuto ena pathupi lawo, buku lina linanena kuti: “Kalelo ku Middle East, nthawi zina anthu amenewa ankachitidwa zachipongwe.” Munthu ankatha kuika chinthu patsogolo pa munthu wosaona n’cholinga choti akapunthwa azimuseka. Izitu zinali nkhanza. Choncho popereka lamulo limeneli, Yehova anathandiza anthu ake kuti azichitira chifundo anthu amene ali ndi mavuto ena.

5. Kodi tingasonyeze bwanji chifundo kwa anthu amene ali ndi mavuto pathupi lawo?

5 Yesu ankasonyeza chifundo kwa anthu omwe anali ndi mavuto pathupi lawo. Takumbukirani uthenga umene anatumiza kwa Yohane M’batizi. Iye anati: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa, ogontha akumva, [ndipo] akufa akuukitsidwa.” Poona zozizwitsa zimene Yesu ankachita, “anthu onse . . . anatamanda Mulungu.” (Luka 7:20-22; 18:43) Akhristu amasangalala kutsanzira Yesu pochitira chifundo anthu omwe ali ndi mavuto pathupi lawo. Choncho timayesetsa kuwakomera mtima, kuwaganizira komanso kuwachitira zinthu moleza mtima. N’zoona kuti Yehova sanatipatse mphamvu yochita zozizwitsa. Koma tili ndi mwayi wouza anthu osaona mwakuthupi komanso mwauzimu uthenga wabwino wonena za dziko latsopano, mmene anthu adzakhala athanzi komanso adzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Luka 4:18) Uthenga wabwino umenewu, ukuthandiza kale anthu ambiri kuti azitamanda Mulungu.

KUCHITA ZINTHU MOONA MTIMA PA NKHANI ZAMALONDA

6. Kodi zimene zili mu Levitiko chaputala 19, zimatithandiza bwanji kumvetsa zomwe zili m’Malamulo Khumi?

6 Mavesi ena mu Levitiko chaputala 19, amafotokoza mowonjezereka zimene zili m’Malamulo Khumi. Mwachitsanzo, lamulo la 8, limangonena kuti: “Usabe.” (Eks. 20:15) Anthu ena anganene kuti, ngati munthu atamapewa kutenga zinthu zomwe si zake ndiye kuti akutsatira lamulo limeneli. Komatu munthuyo akhoza kukhala kuti akuba m’njira zina.

7. Kodi zikanatheka bwanji kuti wamalonda aphwanye lamulo la 8, lokhudza kuba?

7 Wochita malonda angamaone kuti sanabe chifukwa choti sanatenge zinthu zomwe si zake. Koma bwanji pa nkhani ya mmene amachitira bizinezi yake? Palemba la Levitiko 19:35, 36, Yehova ananena kuti: “Musamachite chinyengo poyeza utali wa chinthu, kulemera kwa chinthu kapena poyeza zinthu zamadzi. Muzikhala ndi masikelo olondola, miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.” Wamalonda yemwe ankagwiritsa ntchito masikelo kapena zoyezera zina zachinyengo n’cholinga choti apusitse anthu omwe akuchita nawo malonda, ankakhala kuti akuwabera. Mavesi enanso a mu Levitiko chaputala 19, amatithandiza kumvetsa bwino zimenezi.

Kodi mfundo ya pa Levitiko 19:11-13, ingathandize bwanji Mkhristu kudzifufuza pa mmene amachitira zinthu pa bizinezi yake? (Onani ndime 8-10) *

8. Kodi mfundo za pa Levitiko 19:11-13, zikanathandiza bwanji Ayuda kutsatira lamulo la 8, nanga ifeyo zingatithandize bwanji?

8 Werengani Levitiko 19:11-13. Mawu oyamba pa Levitiko 19:11 amati: “Musabe.” Vesi 13, likusonyeza kugwirizana pakati pa kuba ndi kuchita bizinezi mwachinyengo ponena kuti: “Usabere mnzako mwachinyengo.” Choncho kuchita malonda mwachinyengo n’kogwirizana ndi kuba komanso uchifwamba. Ngakhale kuti lamulo la 8, limanena za kuba, mfundo za mu Levitiko zikanathandiza Ayuda kuona mmene angagwiritsire ntchito lamuloli. N’zofunika kuti tiziganizira mmene Yehova amaonera chinyengo komanso kuba. Tingadzifunse kuti: ‘Mogwirizana ndi Levitiko 19:11-13, kodi pali mbali zina pa moyo wanga zimene ndiyenera kukonza? Kodi ndikufunika kusintha mmene ndimachitira zinthu pa nkhani ya bizinezi komanso ntchito?’

9. Kodi lamulo la pa Levitiko 19:13, linkateteza bwanji ogwira ntchito?

9 Palinso mfundo ina yokhudza kuchita zinthu moona mtima imene Mkhristu yemwe walemba ntchito munthu wina ayenera kuiganizira. Lemba la Levitiko 19:13, limamaliza ndi mawu akuti: “Malipiro a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikira m’mawa.” Munthawi ya Aisiraeli, anthu omwe alembedwa ganyu yakumunda ankapatsidwa malipiro pakutha pa tsiku. Kusapatsa waganyu malipiro ake kukanachititsa kuti iye alephere kupezera chakudya banja lake pa tsikulo. Yehova anafotokoza kuti: ‘Iye ndi wovutika ndipo akuyembekezera malipiro akewo.’​—Deut. 24:14, 15; Mat. 20:8.

10. Kodi tikuphunzira mfundo iti pa Levitiko 19:13?

10 Masiku ano, ogwira ntchito ambiri amapatsidwa malipiro awo kamodzi kapena kawiri pamwezi, osati tsiku lililonse. Komabe, mfundo ya pa Levitiko 19:13, imagwirabe ntchito. Mabwana ena amapondereza antchito awo powapatsa malipiro ochepa kwambiri. Iwo amadziwa kuti antchitowo palibe chomwe angachite koma kupitirizabe kugwira ntchitoyo ngakhale kuti amalandira malipiro ochepa. Akamachita zimenezi, zimakhala ngati malipiro a waganyu ‘akugona m’nyumba mwawo.’ Mkhristu yemwe amalemba ena ntchito, ayenera kuonetsetsa kuti akuwachitira zinthu mwachilungamo. Tiyeni tionenso zina zomwe tingaphunzire mu Levitiko 19.

KUKONDA ANZATHU MMENE TIMADZIKONDERA

11-12. Kodi Yesu anatsindika mfundo iti potchula mawu a pa Levitiko 19:17, 18?

11 Kuwonjezera pa kusachita zinthu zopweteka ena, Mulungu amayembekezeranso kuti tizichita zina zambiri. Timaona umboni wa zimenezi pa Levitiko 19:17, 18. (Werengani.) Taonani lamulo lomwe likupezeka palembali: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” Mkhristu yemwe amafuna kusangalatsa Mulungu, amayenera kuchita zimenezi.

12 Taganizirani mmene Yesu anatsindikira kufunika kwa lamulo lopezeka pa Levitiko 19:18. Mfarisi wina anamufunsa kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti “lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba” ndi lakuti, uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse ndi maganizo ako onse. Kenako, Yesu anatchula mawu a pa Levitiko 19:18, ponena kuti: “Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Mat. 22:35-40) Pali njira zambiri zosonyezera chikondi kwa ena, komabe tingaphunzirenso zambiri mu Levitiko chaputala 19.

13. Kodi nkhani ya m’Baibulo ya Yosefe imatithandiza bwanji kumvetsa mfundo ya pa Levitiko 19:18?

13 Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda anzathu ndi kutsatira malangizo a pa Levitiko 19:18. Lembali limati: ‘Usabwezere choipa kapena kusunga chakukhosi.’ Ambiri a ife tikudziwa anthu ena omwe anasungira chakukhosi mnzawo wakuntchito, wakusukulu, wachibale kapena munthu wam’banja lawo, mwinanso kwa zaka zambiri. Kumbukirani kuti abale ake a Yosefe, anamusungira chakukhosi, zomwe zinawachititsa kuti achite zinthu zoipa kwambiri. (Gen. 37:2-8, 25-28) Koma Yosefe anachita zinthu mosiyana kwambiri ndi abale akewa. Iye anawasonyeza chifundo pa nthawi imene anali ndi udindo waukulu ngakhale kuti akanatha kuwabwezera. Yosefe sanasunge chakukhosi. M’malomwake, anachita zinthu mogwirizana ndi malangizo a pa Levitiko 19:18.​—Gen. 50:19-21.

14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mfundo za mulamulo la pa Levitiko 19:18, zikugwirabe ntchito masiku ano?

14 Akhristu omwe akufuna kusangalatsa Mulungu ayenera kutengera chitsanzo cha Yosefe, yemwe anakhululukira abale ake m’malo mowasungira chakukhosi kapena kuwabwezera. Zimenezi ndi zogwirizananso ndi pemphero lachitsanzo. Paja Yesu anatilimbikitsa kukhululukira anthu amene atilakwira. (Mat. 6:9, 12) Nayenso mtumwi Paulo anapereka malangizo kwa Akhristu akuti: “Okondedwa, musabwezere choipa.” (Aroma 12:19) Anawalimbikitsanso kuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.” (Akol. 3:13) Mfundo za Yehova sizisintha. Choncho mfundo za mulamulo la pa Levitiko 19:18, zikugwirabe ntchito masiku ano.

Mofanana ndi mmene timapewera kugwiragwira pabala, tingachite bwinonso kusiya kumangoganizira zimene ena anatilakwira. Tiziyesetsa kuiwala zimene anatichitira (Onani ndime 15) *

15. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chingatithandize kudziwa kufunika kosasunga chakukhosi?

15 Kukhumudwa tingakuyerekezere ndi bala. Mabala ena amakhala aang’ono, pomwe ena amakhala aakulu. Mwachitsanzo, potsegula envelopu, mwina pepala lingaticheke pachala. Tingamve kupweteka, koma ululu wake sungatenge nthawi yaitali. Mwinanso pambuyo pa tsiku limodzi kapena awiri, sitingakumbukire pamene tinachekeka paja. Mofanana ndi zimenezi, zina mwa zimene ena atilakwira zingakhale zazing’ono. Mwachitsanzo, mnzathu angalankhule kapena kuchita zinthu mosaganizira ndipo zingatikhumudwitse. Komabe timamukhululukira mosavuta. Ngati tili ndi bala lalikulu, dokotala angafunike kulisoka kapenanso kulimanga ndi bandeji. Koma ngati tingamagwiregwire pabalapo, zingachititse kuti lisapole msanga. N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina munthu akakhumudwa kwambiri ndi zimene ena amuchitira, angamachite zofanana ndi zimenezi. Nthawi ndi nthawi angamaganizire zinthu zoipa zimene munthu wina anamuchitira komanso mmene anakhumudwira. Komatu anthu amene amasunga chakukhosi, amangodzivulaza okha. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a pa Levitiko 19:18.

16. Mogwirizana ndi Levitiko 19:33, 34, kodi Aisiraeli ankayenera kuwaona bwanji alendo, nanga tikuphunzirapo chiyani?

16 Pamene Yehova analamula Aisiraeli kuti azikonda anzawo, sanatanthauze kuti azingokonda anthu a mtundu wawo okha. Iye anawauza kuti azikondanso alendo okhala pakati pawo. Umenewu ndi uthenga womveka bwino womwe uli pa Levitiko 19:33, 34. (Werengani.) Mlendoyo ankayenera kumaonedwa ngati “mbadwa,” ndipo Aisiraeli ankafunika ‘kumamukonda’ ngati mmene amadzikondera okha. Aisiraeli ankayenera kulola alendo komanso osauka kuti azikunkha m’minda yawo. (Lev. 19:9, 10) Mfundo yokhudza kukonda alendo, imagwiranso ntchito kwa Akhristu masiku ano. (Luka 10:30-37) Motani? Pali anthu ambiri omwe anachoka m’mayiko awo kupita mayiko ena ndipo n’kutheka kuti ena amakhala pafupi ndi kumene timakhala. Choncho n’zofunika kuti tizilemekeza amuna, akazi ndi ana amenewa.

CHINTHU CHINANSO CHIMENE TINGAPHUNZIRE MU LEVITIKO 19

17-18. (a) Kodi pa Levitiko 19:2 ndi 1 Petulo 1:15, timalimbikitsidwa kuchita chiyani? (b) Kodi mtumwi Petulo anatilimbikitsa kuti tizigwira ntchito yofunika iti?

17 Pa Levitiko 19:2 komanso 1 Petulo 1:15, Baibulo limalimbikitsa anthu a Mulungu kuti akhale oyera. Mavesi enanso ambiri mu Levitiko chaputala 19, amatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti Yehova azisangalala nafe. Tangokambirana mavesi ochepa chabe, omwe akutchula zinthu zimene tiyenera kuchita komanso zoipa zimene tiyenera kupewa. * Malemba a Chigiriki amasonyeza kuti tiyenera kumatsatira mfundo zimenezi pa moyo wathu. Koma mtumwi Petulo anawonjezeranso kanthu kena.

18 Tikhoza kumachita zambiri polambira Mulungu ndiponso kumachita ntchito zabwino zambiri. Koma Petulo analimbikitsa Akhristu kuchita chinthu china chofunika kwambiri. Iye asanauze Akhristu kuti akhale oyera m’makhalidwe awo onse, anawalimbikitsa kuti: “Konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.” (1 Pet. 1:13, 15) Kodi iye ankanena ntchito yotani? Petulo ananena kuti abale ake a Khristu odzozedwa ‘adzalengeza makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana.’ (1 Pet. 2:9) Ndipotu Akhristu onse masiku ano, ali ndi mwayi wogwira nawo ntchito yofunikayi yomwe imathandiza kwambiri anthu. Monga anthu oyera, tili ndi mwayi waukulu wogwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu nthawi zonse komanso mwakhama. (Maliko 13:10) Tikamayesetsa kutsatira mfundo za mu Levitiko 19, timasonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu ena. Timasonyezanso kuti tikufuna ‘kukhala oyera’ m’makhalidwe athu onse.

NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

^ ndime 5 Akhristu satsatiranso Chilamulo cha Mose, komabe Chilamulochi chimatchula zinthu zina zimene tiyenera kuchita ndiponso zimene tiyenera kupewa. Kuphunzira mfundo zake kungatithandize kuti tizikonda anzathu komanso kusangalatsa Mulungu. Nkhaniyi ifotokoza mfundo zina zothandiza zimene tingaphunzire muchaputala 19 cha buku la Levitiko.

^ ndime 17 Munkhaniyi komanso yapita ija, sitinakambirane mavesi omwe amanena za tsankho, miseche, kudya magazi, kukhulupirira mizimu, kulosera zam’tsogolo komanso khalidwe la chiwerewere.​—Lev. 19:15, 16, 26-29, 31.​—Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga,” yomwe ili m’magaziniyi.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Wa Mboni akuthandiza m’bale amene ali ndi vuto losamva kuti alankhule ndi dokotala.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale yemwe amagwira ntchito yopenta akulipira wantchito wake.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo angaiwale mosavuta ululu wa bala laling’ono. Koma kodi adzasankhanso kuchita chimodzimodzi ndi ululu wa bala lalikulu?