Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi ndi mfundo yotani yomwe ikupezeka mulamulo la pa Levitiko 19:16, lomwe limati “Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako,” nanga tikuphunzira chiyani pa lamulo limeneli?
Yehova anauza Aisiraeli kuti akhale anthu oyera. Pofuna kuwathandiza kuti achite zimenezi, iye anawauza kuti: “Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumachita miseche. Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako. Ine ndine Yehova.”—Lev. 19:2, 16.
Mawu akuti “usachite kanthu kalikonse” kapena kuti usalimbane, amafotokoza bwino tanthauzo la mawu ena a Chiheberi. Koma kodi mawuwa amatanthauza chiyani? Buku lina la Chiyuda, pofotokoza za buku la Levitiko, limanena kuti: “Mbali ya vesili ndi yovuta kuimasulira . . . chifukwa ndi zovuta kudziwa tanthauzo lenileni la mawu a Chiheberiwa. Mawuwa angamasuliridwenso kuti ‘kusaima pachinachake, pambali pake kapena pafupi nacho.’”
Akatswiri ena amaphunziro amaganiza kuti mawuwa akugwirizana ndi amuvesi 15 omwe amati: “Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka, ndiponso musamakondere munthu wolemera. Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.” (Lev. 19:15) Ngati ndi choncho, lamulo la muvesi 16 lakuti usalimbane ndi mnzako likanatanthauza kuti anthu a Mulungu sankayenera kuchitira zoipa anzawo pa nkhani za milandu, bizinezi, zam’banja kapenanso kuchita zinthu mwachinyengo n’cholinga chofuna kupeza phindu. N’zoona kuti sitiyenera kuchita zinthu zimenezi, koma pali njira yabwino imene ingatithandize kumvetsa mawu amuvesi 16.
Taganizirani mawu omwe ali koyambirira kwa vesili. Mulungu analamula anthu ake kuti asamayendeyende n’kumanena miseche. Kumbukirani kuti miseche ndi yoipa kwambiri kuposa kungonenera munthu wina zoipa pang’ono chabe, ngakhale kuti kuchita zimenezi kungayambitsenso mavuto. (Miy. 10:19; Mlal. 10:12-14; 1 Tim. 5:11-15; Yak. 3:6) Munthu wamiseche amanena zinthu zoipa kapena zabodza zokhudza munthu wina n’cholinga chofuna kumuipitsira mbiri. Iye angathe kupereka umboni wabodza wokhudza munthu wina, ngakhale kuti kuchita zimenezi kungachititse kuti munthuyo aphedwe. Kumbukirani kuti anthu amiseche anapereka umboni wabodza wokhudza Naboti, zomwe zinachititsa kuti aponyedwe miyala. (1 Maf. 21:8-13) Ndiye monga taonera mumbali yachiwiri ya lemba la Levitiko 19:16, munthu wamiseche akhoza kuchita kanthu kalikonse kuti aphetse mnzake.
Komanso munthu akhoza kunenera mnzake miseche chifukwa choti amadana naye. Pa 1 Yohane 3:15, timawerenga kuti: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu sadzalandira moyo wosatha.” N’chifukwa chake Mulungu atanena mawu omwe ali muvesi 16, anapitiriza muvesi lotsatira kuti: “Usadane ndi m’bale wako mumtima mwako.”—Lev. 19:17.
Choncho lamulo lochititsa chidwi la pa Levitiko 19:16, lili ndi malangizo amphamvu kwa Akhristu. Sitiyenera kukhala ndi maganizo oipa okhudza munthu aliyense kapena kumunenera miseche. Mwachidule, ngati ‘tingachite kanthu kalikonse’ kapena kuti kulimbana ndi winawake chifukwa choti sitimukonda kapena tikumuchitira nsanje, zingasonyeze kuti timadana naye. Akhristu ayenera kupeweratu kuchita zimenezi.—Mat. 12:36, 37.