Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 48

“Mukhale Oyera”

“Mukhale Oyera”

“Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse.”​—1 PET. 1:15.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda Ndi Mtima Wosagawanika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi malangizo ati amene mtumwi Petulo anapereka kwa Akhristu anzake, nanga n’chifukwa chiyani angaoneke ngati osatheka kuwatsatira?

KAYA tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tingapindule ndi malangizo amene mtumwi Petulo anapereka kwa Akhristu odzozedwa a munthawi yake. Petulo analemba kuti: “Khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse, chifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Pet. 1:15, 16) Mawu amenewa akusonyeza kuti ndi zotheka kutsanzira Yehova yemwe ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yokhala oyera. Tingathe ndipo tiyenera kukhala oyera m’zochita zathu. Zimenezi zingaoneke ngati zosatheka chifukwa si ife angwiro. Ngakhale Petulo nayenso analakwitsapo zinthu zina, koma chitsanzo chake chimasonyeza kuti tingathe ‘kukhala oyera.’

2. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

2 Munkhaniyi tikambirana mafunso otsatirawa: Kodi kukhala oyera n’kutani? Kodi Baibulo limatiphunzitsa chiyani za Yehova pa nkhani yokhala oyera? Kodi tingatani kuti tikhale oyera m’zochita zathu? Nanga pali kugwirizana kotani pakati pa kukhala oyera ndi ubwenzi wathu ndi Yehova?

KODI KUKHALA OYERA N’KUTANI?

3. Kodi anthu ambiri amaganiza kuti kukhala oyera n’kutani, koma kodi tingapeze kuti mfundo zolondola pa nkhaniyi?

3 Anthu ambiri akaganizira za munthu amene ndi woyera, amaona kuti ndi munthu amene amavala zovala zachipembedzo yemwe nthawi zonse nkhope yake sisekerera. Koma zimenezi si zolondola. Baibulo limati Yehova yemwe ndi woyera ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Ndipo munthu amene amamulambira amatchulidwa kuti ndi “wodala” kapena kuti wosangalala. (Sal. 144:15) Yesu anadzudzula anthu amene ankavala zovala zapadera n’kumadzionetsera kwa anthu kuti ndi olungama. (Mat. 6:1; Maliko 12:38) Monga Akhristu, mmene timaonera nkhani yokhala oyera, zimagwirizana ndi zimene timaphunzira m’Baibulo. Ndife otsimikiza kuti Mulungu wathu yemwe ndi wachikondi komanso woyera, sangatipatse malamulo omwe ndi zosatheka kuti tiwatsatire. Choncho Yehova akamatiuza kuti “mukhale oyera,” timakhulupirira kuti n’zotheka kutsatira lamuloli. Komabe tisanakhale oyera m’zochita zathu, tiyenera kumvetsa kuti kodi kukhala oyera n’kutani.

4. Kodi mawu akuti “kukhala oyera” kapena “chiyero” amatanthauza chiyani?

4 Kodi kukhala woyera n’kutani? M’Baibulo mawu akuti “kukhala woyera” kapena “chiyero,” nthawi zambiri amanena za kukhala wosaipitsidwa kapena wopatulika m’makhalidwe komanso pa nkhani zachipembedzo. Mawu amenewa anganenenso za zinthu kapena munthu amene wapatulidwa kuti atumikire Mulungu. Tingaonedwe kuti ndife oyera ngati tili ndi makhalidwe abwino, timalambira Yehova movomerezeka komanso ngati tili pa ubwenzi wabwino ndi iye. Timasowa chonena tikaganizira mfundo yakuti tingathe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova yemwe ndi woyera komanso tikaganizira zimene Baibulo limanena zokhudza chiyero chake.

“WOYERA, WOYERA, WOYERA NDIYE YEHOVA”

5. Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova kuchokera kwa angelo okhulupirika?

5 Yehova ndi woyera pa chilichonse. Timadziwa zimenezi chifukwa cha zimene ananena aserafi, amene ndi angelo ake omwe amakhala pafupi ndi mpando wake wachifumu. Pa nthawi ina, aserafi ena analengeza kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.” (Yes. 6:3) Ndipotu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu wawo yemwe ndi woyera, angelo amafunika kuti nawonso akhale oyera, ndipo ndi mmene alilidi. N’chifukwa chake pamalo amene papezeka mngelo wa Yehova kuti apereke uthenga padzikoli pankakhalanso poyera. Izi ndi zimene zinachitika Mose ataima pafupi ndi chitsamba chaminga choyaka moto.​—Eks. 3:2-5; Yos. 5:15.

Mawu akuti “Chiyero n’cha Yehova” ankalembedwa pa kachitsulo kagolide komwe kankakhala panduwira ya mkulu wa ansembe (Onani ndime 6-7)

6-7. (a) Mogwirizana ndi Ekisodo 15:1, 11, kodi Mose anatsindika bwanji kuti Mulungu ndi woyera? (b) Kodi n’chiyani chinkakumbutsa Aisiraeli kuti Mulungu ndi woyera? (Onani chithunzi chapachikuto.)

6 Atatsogolera Aisiraeli kuwoloka Nyanja Yofiira, Mose anawatsimikizira kuti Mulungu wawo Yehova ndi woyera. (Werengani Ekisodo 15:1, 11.) Makhalidwe a anthu omwe ankalambira milungu ya ku Iguputo ankasonyeza kuti iwo sanali oyera. Ndi mmenenso zinalili ndi anthu amene ankalambira milungu ya ku Kanani. Kulambira kwawo kunkaphatikizapo kupereka ana nsembe komanso kugonana konyansa. (Lev. 18:3, 4, 21-24; Deut. 18:9, 10) Mosiyana ndi zimenezi, Yehova sakanalola kuti anthu amene amamulambira, azichita zinthu zimene zingawaipitse. Iye ndi woyera kwambiri. Zimenezi zinaonekera bwino pa zimene zinalembedwa pakachitsulo kagolide komwe mkulu wa ansembe ankavala pamphumi. Pakachitsulopo analembapo mochita kugoba kuti, “Chiyero n’cha Yehova.”​—Eks. 28:36-38.

7 Mawu amene analembedwa pakachitsuloko ankatsimikizira aliyense wowaona kuti Yehova ndi woyeradi. Nanga bwanji Aisiraeli omwe sakanatha kuona kachitsuloka chifukwa choti sakanatha kukumana ndi mkulu wa ansembe? Kodi ndiye kuti uthengawo sakanaumva? Ayi. Ku Isiraeli, aliyense ankamva uthengawu Chilamulo chikamawerengedwa pamaso pa amuna, akazi komanso ana. (Deut. 31:9-12) Mukanakhalapo pa nthawiyo, bwenzi mukumva mawu akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu. . . . Muzikhala oyera, chifukwa ine ndine woyera.” “Mukhale oyera kwa ine, chifukwa ine Yehova ndine woyera.”​—Lev. 11:44, 45; 20:7, 26.

8. Kodi tikuphunzira chiyani pa Levitiko 19:2 ndi 1 Petulo 1:14-16?

8 Tiyeni tione zimene zinalembedwa pa Levitiko 19:2, zomwe zinkawerengedwa kwa onse. Yehova anauza Mose kuti: “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.’” N’kutheka kuti Petulo ananena mawu a palembali pomwe analimbikitsa Akhristu kuti “mukhale oyera.” (Werengani 1 Petulo 1:14-16.) N’zoona kuti panopa sititsatira Chilamulo cha Mose. Komabe zimene Petulo analemba zikutsimikizira zimene timaphunzira pa Levitiko 19:2, kuti Yehova ndi woyera ndipo onse omwe amamukonda ayenera kuyesetsa kuti akhale oyera. Tonsefe timafunika kuchita zimenezi, kaya tili ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba kapena chodzakhala m’Paradaiso padzikoli.​—1 Pet. 1:4; 2 Pet. 3:13.

“KHALANI OYERA M’MAKHALIDWE ANU ONSE”

9. Kodi kukambirana mfundo za muchaputala 19 cha Levitiko kutithandiza bwanji?

9 Popeza timafuna kusangalatsa Mulungu yemwe ndi woyera, timafunitsitsa kudziwa zimene tingachite kuti ifenso tikhale oyera. Yehova amatipatsa malangizo omwe angatithandize. Malangizo ena abwino kwambiri timawapeza mu Levitiko chaputala 19. Katswiri wina wa Chiheberi dzina lake Marcus Kalisch analemba kuti: “Chaputala chimenechi chikhoza kukhala chofunika kwambiri m’buku la Levitiko komanso m’mabuku 5 oyambirira a Baibulo.” Tiyeni tione mavesi ena m’chaputalachi omwe ali ndi mfundo zofunika kwambiri zomwe zingatithandize pa moyo wathu. Kumbukirani kuti mfundo za muchaputala 19 zikuyamba ndi mawu akuti, “Mukhale oyera.”

Kodi lamulo lokhudza makolo lomwe lili pa Levitiko 19:3, liyenera kulimbikitsa Akhristu kuganizira chiyani? (Onani ndime 10-12) *

10-11. Kodi mawu oyambirira mu Levitiko 19, amati tiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezo n’kofunika?

10 Pambuyo ponena kuti Aisiraeli akhale oyera, Yehova anawonjezera kuti: “Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake . . . Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”​—Lev. 19:2, 3.

11 N’zoonekeratu kuti n’zofunika kwambiri kutsatira malangizo a Mulungu okhudza kulemekeza makolo athu. Kumbukirani zimene Yesu anayankha munthu wina atamufunsa kuti: “N’chiyani chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?” Zina zomwe Yesu anayankha zinali zoti munthuyo ankafunika kulemekeza bambo ndi mayi ake. (Mat. 19:16-19) Ndipotu Yesu anadzudzula alembi ndi Afarisi chifukwa cholephera kulemekeza makolo awo. Choncho iwo anachititsa “mawu a Mulungu kukhala opanda pake.” (Mat. 15:3-6) “Mawu a Mulungu” amenewo ankaphatikizapo lamulo la nambala 5 pa Malamulo Khumi komanso zimene timawerenga pa Levitiko 19:3. (Eks. 20:12) Apanso kumbukirani kuti malangizo a pa Levitiko 19:3, akuti munthu azilemekeza mayi ndi bambo ake, amabwera pambuyo pa mawu akuti, “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.”

12. Mogwirizana ndi malangizo a pa Levitiko 19:3, kodi tingachite bwino kudzifunsa funso liti?

12 Mogwirizana ndi malangizo a Yehova akuti tizilemekeza makolo athu, tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikuchita bwanji pa nkhani imeneyi?’ Ngati mukuona kuti munkafunika kuchita zambiri m’mbuyomu, mungasankhe kuti muyambe kuchita bwino panopa. Simungathe kusintha kale lanu, koma mungakhale otsimikiza kuti kuyambira panopa muzichita zambiri pothandiza makolo anu. Mungakonze zoti muzikhala ndi nthawi yambiri yocheza nawo. Mwina mungawagulire zinthu, kuwathandiza kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kapenanso kuwalimbikitsa. Kuchita zimenezi ndi kogwirizana ndi zimene lemba la Levitiko 19:3 limanena.

13. (a) Kodi timapeza malangizo enanso ati pa Levitiko 19:3? (b) Kodi masiku ano tingatsanzire bwanji Yesu mogwirizana ndi zomwe zili pa Luka 4:16-18?

13 Lemba la Levitiko 19:3, limatiphunzitsa kanthu kenanso pa nkhani yokhala oyera. Limanena za kusunga Sabata. Akhristu satsatiranso Chilamulo, choncho sitimasunga Sabata. Komabe tingaphunzire zambiri pa zimene Aisiraeli ankachita posunga Sabata komanso mmene kuchita zimenezi kunkawathandizira. Tsiku la Sabata linali nthawi imene ankapuma pa ntchito zimene ankagwira ndipo linkawapatsa mwayi wolambira Yehova. * N’chifukwa chake pa tsikuli, Yesu ankapita ku sunagoge m’tauni yakwawo kukawerenga Mawu a Mulungu. (Eks. 31:12-15; werengani Luka 4:16-18.) Lamulo la Mulungu lopezeka pa Levitiko 19:3 lakuti, “muzisunga masabata anga,” likutiphunzitsa kuti tsiku lililonse tiyenera kumapeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Kodi inuyo mukuona kuti pali zina zimene muyenera kusintha pa nkhani imeneyi? Ngati nthawi zonse mumapeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira, mudzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova zomwe ndi zofunika kwambiri kuti mukhale woyera.

MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

14. Kodi ndi mfundo yofunika iti ya choonadi yomwe yatchulidwa mobwerezabwereza mu Levitiko 19?

14 Chaputala 19 cha buku la Levitiko chimatchula mobwerezabwereza mfundo ya choonadi yofunika yomwe ingatithandize kupitirizabe kukhala oyera. Vesi 4 limamaliza ndi mawu akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Mawuwa kapena ofanana nawo amapezeka nthawi 16 m’chaputalachi. Zimenezi zimatikumbutsa lamulo loyamba lomwe limati: “Ine ndine Yehova Mulungu wako . . . Usakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.” (Eks. 20:2, 3) Mkhristu aliyense amene akufuna kukhala woyera, ayenera kuwonetsetsa kuti palibe chilichonse kapena aliyense yemwe ndi wofunika kwambiri pa moyo wake kuposa ubwenzi wake ndi Mulungu. Ndipo popeza timadziwika kuti ndife Mboni za Yehova, tiyenera kukhala otsimikiza kupewa chilichonse chimene chingachititse kuti dzina lake loyera lidetsedwe.​—Lev. 19:12; Yes. 57:15.

15. Kodi mavesi a mu Levitiko 19 onena za nsembe ayenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

15 Aisiraeli ankasonyeza kuti amavomereza Yehova monga Mulungu wawo akamamvera malamulo amene anawapatsa. Lemba la Levitiko 18:4 limati: “Muzisunga zigamulo zanga ndi kutsatira mfundo zanga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Chaputala 19 chili ndi zina mwa “mfundo” zimene Aisiraeli anapatsidwa. Mwachitsanzo, m’mavesi 5-8, 21, 22, amafotokozamo za nsembe zanyama. Nsembezi zinkayenera kuperekedwa m’njira yakuti ‘zisaipitse chinthu chopatulika cha Yehova.’ Kuwerenga mavesiwa kuyenera kutilimbikitsa kuti tizisangalatsa Yehova komanso kumupatsa nsembe zomutamanda zovomerezeka, monga mmene lemba la Aheberi 13:15 limanenera.

16. Kodi n’chiyani chingatikumbutse kuti pali kusiyana pakati pa anthu amene amatumikira Mulungu ndi omwe samutumikira?

16 Kuti tikhale oyera, tiyenera kukhala osiyana ndi anthu amene satumikira Mulungu. Komatu kuchita zimenezi si kophweka. Nthawi zina anzathu a kusukulu, a kuntchito, achibale ndi ena angatilimbikitse kuchita zinthu zosemphana ndi kulambira kwathu. Zikatero timayenera kusankha zochita pa nkhani yofunikayi. Ndiye n’chiyani chingatithandize kusankha mwanzeru? Taganizirani mfundo yochititsa chidwi yomwe ili pa Levitiko 19:19, lomwe mbali ina limati: “musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.” Lamuloli linkathandiza kuti Aisiraeli azioneka mosiyana ndi anthu a mitundu yoyandikana nawo. Popeza kuti masiku ano sititsatira Chilamulo, sizolakwika kuti Mkhristu avale chovala chopangidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya ulusi. Komabe n’zolakwika kuti tizichita zinthu ngati anthu omwe zikhulupiriro komanso zochita zawo n’zosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, kaya anthuwo ndi anzathu a kusukulu, a kuntchito kapena achibale. N’zoona kuti timakonda achibale athu komanso anthu ena komabe pa nkhani zofunika kwambiri zokhudza moyo, monga atumiki a Yehova timafunitsitsa kukhala osiyana ndi ena. Kumbukirani kuti kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa kukhala oyera kumaphatikizapo kupatulidwa kuti tizitumikira Mulungu.​—2 Akor. 6:14-16; 1 Pet. 4:3, 4.

Kodi ndi mfundo iti imene anthu a Mulungu ankaphunzirapo pa Levitiko 19:23-25, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (Onani ndime 17-18) *

17-18. Kodi tikupeza phunziro lofunika liti pa Levitiko 19:23-25?

17 Mawu akuti, “Ine ndine Yehova Mulungu wanu,” ankayenera kuthandiza Aisiraeli kuti aziona kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ndi wofunika kwambiri. Kodi akanachita bwanji zimenezi? Lemba la Levitiko 19:23-25 limasonyeza mmene akanachitira. (Werengani.) Taganizirani zimene mawuwa akanatanthauza kwa Aisiraeli pambuyo polowa m’Dziko Lolonjezedwa. Munthu akadzala mtengo wa zipatso sankayenera kudya zipatso zake kwa zaka zitatu. M’chaka cha 4, zipatso za mtengowo zinkayenera kuperekedwa kwa Mulungu kumalo opatulika. M’chaka cha 5, ndi pamene mwini wake wa mtengowo ankadya zipatso zake. Lamuloli linkathandiza Aisiraeli kudziwa kuti sankafunika kuika zofuna zawo pamalo oyamba. Yehova ankafuna kuti anthuwo azimudalira kuti iye aziwasamalira ndiponso kuti aziika kumulambira pamalo oyamba. Iye akanaonetsetsa kuti iwo ali ndi chakudya chokwanira. Mulungu ankawalimbikitsa kuti azipereka mphatso zawo mowolowa manja kumalo opatulika komwe ankamulambirira.

18 Lamulo lomwe lili pa Levitiko 19:23-25, limatikumbutsa mawu a Yesu a mu ulaliki wake wa paphiri. Iye anati: “Lekani kudera nkhawa . . . kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani.” Anawonjezeranso kuti: “Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” Choncho Mulungu adzatisamalira ngati mmene amasamalilira mbalame. (Mat. 6:25, 26, 32) Timakhulupirira kuti iye azitipatsa zofunika pa moyo. Komanso mosadzionetsera, timapereka “mphatso zachifundo” kwa amene akufunika thandizo. Timayesetsanso kupereka ndalama zomwe zimathandiza kulipirira zinthu zofunika pa mpingo. Yehova amaona tikamapereka mowolowa manja ndipo adzatidalitsa. (Mat. 6:2-4) Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikumvetsa mfundo zimene tikuphunzira pa Levitiko 19:23-25.

19. Kodi kuganizira mfundo zina za m’buku la Levitiko kwakuthandizani bwanji inuyo?

19 Tangokambirana mavesi ochepa chabe mu Levitiko chaputala 19, ndipo taona njira zina zomwe tingatsanzirire Mulungu wathu woyera. Tikamamutsanzira, timayesetsa ‘kukhala oyera m’makhalidwe athu onse.’ (1 Pet. 1:15) Anthu ena omwe satumikira Yehova akhala akuona makhalidwe athu abwino. Ndipotu ena afika mpaka polemekeza Yehova chifukwa cha zimenezi. (1 Pet. 2:12) Koma palinso zambiri zimene tingaphunzire mu Levitiko chaputala 19. Nkhani yotsatira ifotokoza mavesi ena a muchaputalachi ndipo itithandiza kuona mbali zina za moyo wathu zimene tingafunike ‘kukhala oyera,’ monga mmene Petulo ananenera.

NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

^ ndime 5 Timakonda kwambiri Yehova ndipo timafuna kuti tizimusangalatsa. Iye ndi woyera ndipo amayembekezera kuti anthu amene amamulambira akhalenso oyera. Kodi zimenezi ndi zothekadi kwa anthu ochimwafe? Inde n’zotheka. Kuphunzira mosamala malangizo amene mtumwi Petulo anapereka kwa Akhristu anzake komanso malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, kungatithandize kudziwa zimene tingachite kuti tikhale oyera m’makhalidwe athu onse.

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya Sabata komanso zimene tingaphunzirepo, onani nkhani yakuti, “‘Pali Nthawi’ Yogwira Ntchito ndi Nthawi Yopuma,” mu Nsanja ya Olonda ya December 2019.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Bambo limodzi ndi mkazi komanso mwana wake apita kukaona makolo ake ndipo amayesetsa kulumikizana nawo pafupipafupi.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlimi wa Chiisiraeli akuyang’ana zipatso za mtengo umene anadzala.