NKHANI YOPHUNZIRA 50
Muzimvera M’busa Wabwino
“Zidzamva mawu anga.”—YOH. 10:16.
NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chiyenera kuti chinachititsa Yesu kuyerekezera otsatira ake ndi nkhosa?
YESU anayerekeza kugwirizana komwe kumakhala pakati pa iyeyo ndi otsatira ake ndi kumene kumakhalapo pakati pa m’busa ndi nkhosa zake. (Yoh. 10:14) Kuyerekezera kumeneku n’koyenera. Tikutero chifukwa nkhosa zimadziwa m’busa wawo ndipo zimamvera mawu ake. Munthu wina wokaona malo anaona zimenezi zikuchitika. Iye anati: “Tinkafuna kujambula nkhosa ndiye tinkaziitana kuti zibwere pafupi. Koma sizinabwere chifukwa sizinkadziwa mawu athu. Koma panabwera kamnyamata kena komwe kanali m’busa wa nkhosazo ndipo katangoziitana nthawi yomweyo zinamutsatira.”
2-3. (a) Kodi otsatira a Yesu amasonyeza bwanji kuti akumvera mawu ake? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi komanso yotsatira?
2 Zimene zinachitikira wokaona maloyu zikutikumbutsa mawu a Yesu onena za nkhosa kapena kuti otsatira ake. Iye anati: “Zidzamva mawu anga.” (Yoh. 10:16) Koma popeza Yesu ali kumwamba, kodi tingamumvere bwanji? Njira yaikulu imene timasonyezera kuti tikumvera mawu a Mbuye wathu ndi kugwiritsa ntchito zimene anaphunzitsa pa moyo wathu.—Mat. 7:24, 25.
3 Munkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana zinthu zina zimene Yesu anaphunzitsa. Monga mmene tionere, Yesu anatiphunzitsa kuti pali zinthu zina zimene tiyenera kusiya kuchita komanso zimene tiyenera kuchita. Choyamba tikambirana zinthu ziwiri zimene m’busa wabwinoyu anatilangiza kuti tiyenera kusiya kuzichita.
“SIYANI KUVUTIKA MUMTIMA”
4. Mogwirizana ndi Luka 12:29, kodi n’chiyani chingachititse kuti ‘tizivutika mumtima’?
4 Werengani Luka 12:29. Yesu analangiza otsatira ake kuti ‘asiye kuvutika mumtima’ poganizira mmene apezere zinthu zofunika. Timadziwa kuti malangizo a Yesu nthawi zonse amakhala anzeru komanso abwino. Timafuna kuti tiziwagwiritsa ntchito. Koma nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Chifukwa chiyani?
5. N’chifukwa chiyani ena angamade nkhawa kuti apeza bwanji zinthu zofunikira pa moyo?
5 Ena akhoza kumada nkhawa kuti apeza bwanji zinthu zofunika monga chakudya, zovala komanso malo okhala. N’kutheka kuti iwo amakhala m’mayiko osauka. Choncho zingakhale zovuta kuti azipeza ndalama zokwanira zosamalira mabanja awo. Mwina munthu yemwe ankapezera zofunika banja lawo anamwalira, zimene zingachititse kuti anthu a m’banjalo azivutika kupeza ndalama zogulira zinthu zofunika. Mwinanso muliri wa COVID-19 wachititsa kuti ena ntchito ziwathere komanso asamapeze ndalama. (Mlal. 9:11) Ngati zoterezi zatichitikira kapena takumana ndi mavuto ena, kodi tingatsatire bwanji malangizo a Yesu oti tisiye kuda nkhawa?
6. Fotokozani zomwe zinachitikira mtumwi Petulo pa nthawi ina.
6 Pa nthawi ina mtumwi Petulo komanso atumwi ena anali m’boti pa Nyanja ya Galileya pomwe panali mphepo yamphamvu, ndipo anaona Yesu akuyenda pamwamba pa madzi. Petulo ananena kuti: “Ambuye, ngati ndinudi, ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” Yesu atamuuza kuti, “bwera,” Petulo anatsika m’ngalawamo “n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu.” Koma taonani zimene zinachitika. “Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha, ndipo atayamba kumira anafuula kuti: ‘Ambuye, ndipulumutseni!’” Yesu anamugwira dzanja n’kumupulumutsa. Onani kuti Petulo anakwanitsa kuyenda pamadzi pa nthawi yonse imene ankayang’ana Mat. 14:24-31.
Yesu. Koma atangoyang’ana mphepo yamkunthoyo, anachita mantha kwambiri komanso kukayikira moti anayamba kumira.—7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Petulo?
7 Tingaphuzirepo kanthu pa zimene zinachitikira Petulo. Pamene iye ankatsika m’ngalawa, n’kuyamba kuyenda pamadzi, sankaganiza kuti angachite mantha ndi mphepoyo n’kuyamba kumira. Ankafuna kuyendabe pamadziwo mpaka atafika kumene kunali Mbuye wake. Koma m’malo moyang’ana Yesu iye anayamba kuchita mantha ndi mphepo yamphamvuyo. N’zoona kuti sitingayende pamadzi, koma chikhulupiriro chathu chikhoza kuyesedwa. Ngati titasiya kuganizira kwambiri za Yehova komanso malonjezo ake, chikhulupiriro chathu chikhoza kuchepa chifukwa cha nkhawa ndipo tingayambe kumira mwauzimu. Ndiye kaya takumana ndi mavuto aakulu bwanji pa moyo wathu, tiyenera kupitiriza kuganizira za Yehova komanso kumudalira kuti atithandiza. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
8. N’chiyani chingatithandize kuti tisamadere nkhawa kwambiri kuti tipeza bwanji zinthu zofunika?
8 Zinthu zingatiyendere bwino ngati titasiya kuda nkhawa n’kumadalira Yehova. Kumbukirani kuti Atate wathu wachikondi Yehova, amatilonjeza kuti adzatipatsa zofunikira pa moyo ngati timaika pamalo oyamba zinthu zokhudza kulambira. (Mat. 6:32, 33) Nthawi zonse amakwaniritsa zomwe analonjezazi. (Deut. 8:4, 15, 16; Sal. 37:25) Ngati Yehova amasamalira mbalame komanso maluwa, sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzapeza bwanji chakudya komanso zovala. (Mat. 6:26-30; Afil. 4:6, 7) Monga mmene chikondi chimachititsira makolo kuti azipezera ana awo zofunikira, chimachititsanso Atate wathu wakumwamba kuti azithandiza anthu ake kupeza zinthu zofunika. Choncho sitikayikira kuti Yehova adzatisamalira.
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira banja lina?
9 Taganizirani chitsanzo cha banja lina chomwe chikusonyeza kuti Yehova angatipatse zomwe tikufunikira. Banjali lomwe likuchita utumiki wa nthawi zonse, linayenda ulendo wa ola limodzi kupita kumalo ena osungirako anthu othawa kwawo. Iwo ankakatenga alongo ena kuti apite nawo kumisonkhano. M’baleyo anafotokoza kuti: “Titamaliza misonkhano, tinaitana alongowo kuti akadye nafe chakudya koma kenako tinazindikira kuti tinalibe chakudya chilichonse.” Ndiye kodi iwo akanatani? M’baleyo anapitiriza kuti: “Titafika kunyumba tinapeza majumbo awiri akuluakulu a zakudya ali pakhomo lathu. Sitikudziwa kuti ndani anasiya zakudyazo pamenepo. Koma timaona kuti Yehova anatisamalira.” Pa nthawi ina galimoto yawo ija inawonongeka. Galimotoyo inkawathandiza pa utumiki wawo, koma analibe ndalama zoti aikonzere. Anaitengera kumalo ena okonzera chapafupi kuti adziwe ndalama zimene zinkafunika kuti ikonzedwe. Ndiye panabwera munthu wina yemwe anafunsa kuti: “Galimotoyi ndi ya ndani?” M’bale uja ananena kuti ndi yake ndipo inkafunika kukonzedwa. Munthu uja anayankha kuti: “Limenelo si vuto. Mkazi wanga akufuna galimoto ya mtundu umenewu. Ndikupatseni ndalama zingati?” M’baleyo anachoka ndi ndalama zokwanira kukagula galimoto ina. Iye anamaliza ndi mawu akuti: “Tsiku limenelo tinasangalala kwambiri. Sikuti zimenezi zinangochitika mwangozi. Tinadziwa kuti Yehova ndi amene akutithandiza.”
10. Kodi lemba la Salimo 37:5, limatilimbikitsa bwanji kuti tisamade nkhawa kwambiri pa nkhani yopeza zimene timafunikira?
10 Tikamamvera m’busa wabwino komanso kusiya kuda nkhawa kwambiri pa nkhani yokhudza mmene tipezere zinthu zofunika, tingatsimikize kuti Yehova adzatisamalira. Salimo 37:5; 1 Pet. 5:7) Taganizirani zochitika zosiyanasiyana zomwe zafotokozedwa mundime 5. Mwina panopa Yehova akugwiritsa ntchito mutu wabanja kapena abwana athu potithandiza kupeza zinthu zofunika. Ngati mutu wabanja sungakwanitsenso kutisamalira, kapena ngati ntchito yatithera, Yehova adzatisamalirabe ndipo sitiyenera kukayikira zimenezi. Tsopano tiyeni tikambirane chinthu chinanso chimene m’busa wabwino amatilangiza kuti tisiye kuchita.
(Werengani“LEKANI KUWERUZA ENA”
11. Mogwirizana ndi Mateyu 7:1, 2, kodi Yesu anatiuza kuti tisiye kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kungakhale kovuta?
11 Werengani Mateyu 7:1, 2. Yesu ankadziwa kuti anthu amene ankamumvetsera si angwiro ndipo nthawi zambiri amakonda kuganizira zimene ena alakwitsa. Onani kuti iye anati: “Lekani kuweruza ena.” Tingayesetse kuti tisamaweruze Akhristu anzathu. Komabe nthawi zina timalephera chifukwa si ife angwiro. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani ngati taona kuti nthawi zina timakonda kuganizira zolakwitsa za ena. Tizimvera Yesu n’kuyesetsa kusiya kuweruza ena.
12-13. Kodi kuganizira kwambiri mmene Yehova ankaonera Mfumu Davide kungatithandize bwanji kuti tisiye kuweruza ena?
12 Kuganizira chitsanzo cha Yehova kungatithandize. Iye amaganizira kwambiri zabwino zimene anthu amachita. Timaona zimenezi tikaganizira mmene anachitira zinthu ndi Mfumu Davide, munthu amene anachita machimo akuluakulu. Mwachitsanzo, iye anachita chigololo ndi Bati-seba komanso anaphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15, 24) Chifukwa cha zimenezi, iye ndi anthu a m’banja lake kuphatikizapo akazi ake ena, anakumana ndi mavuto aakulu. (2 Sam. 12:10, 11) Pa nthawi ina, Davide analephera kudalira Yehova polamula kuti asilikali a Isiraeli awerengedwe, zomwe Yehovayo sanamulamule. Iye ayenera kuti anachita zimenezi chifukwa cha kunyada komanso kudalira gulu la asilikali ake, lomwe linali lalikulu kwambiri. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Aisiraeli pafupifupi 70,000 anafa ndi mliri.—2 Sam. 24:1-4, 10-15.
13 Mukanakhala kuti munkakhala ku Isiraeli pa nthawiyo, kodi mukanamamuona bwanji Davide? Kodi mukanamamuona kuti si woyenera kuti Yehova amuchitire chifundo? Yehova sankaona choncho. M’malomwake, iye ankaganizira zinthu zabwino zimene Davide anachita komanso kuti analapa kuchokera pansi pa mtima. Choncho anamukhululukira machimo akuluakulu amene anachitawa. Yehova ankadziwa kuti Davide ankamukonda ndipo ankafuna kuchita zinthu zoyenera. Kodi sitiyenera kuthokoza kuti Mulungu amaona zabwino mwa ife?—1 Maf. 9:4; 1 Mbiri 29:10, 17.
14. Kodi n’chiyani chimathandiza Akhristu kuti asamaweruze ena?
14 Popeza Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu mosalakwitsa, ifenso sitiyenera kuyembekezera kuti ena azichita zinthu mosalakwitsa. Ndipo tiyenera kumaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene amachita. Nthawi zambiri sizivuta kuona zimene ena amalakwitsa n’kuyamba kuwaweruza. Koma munthu yemwe amatsanzira Yehova amapitirizabe kugwira bwino ntchito ndi ena ngakhale kuti akudziwa zimene anthuwo amalakwitsa. Dayamondi yemwe sanakonzedwe saoneka bwino. Koma munthu wozindikira amadziwa kuti adzaoneka bwino akakonzedwa. Mofanana ndi Yehova ndi Yesu, sitiyenera kuganizira kwambiri zimene anthu amalakwitsa koma zabwino zimene amachita.
15. Kodi kuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu ena kungatithandize bwanji kuti tisamawaweruze?
15 Kuwonjezera pa kuganizira makhalidwe abwino omwe ena ali nawo, n’chiyaninso Luka 21:1-4.
chingatithandize kuti tisamawaweruze? Tiziganizira mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Taganizirani chitsanzo ichi: Tsiku lina Yesu ali kukachisi, anaona mayi wamasiye wosauka akuponya tindalama tiwiri tochepa mphamvu moponyamo zopereka. Iye sanafunse kuti, “N’chifukwa chiyani waponya zochepa choncho?” M’malo moganizira kuchuluka kwa ndalama zimene mayi wamasiyeyo anapereka, Yesu anaganizira zolinga zake komanso mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Ndipo anamuyamikira chifukwa chochita zonse zimene akanatha.—16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Veronica?
16 Tingaone kufunika koganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu ena tikaona zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Veronica. Mumpingo wawo munali mlongo wina yemwe ankalera yekha mwana wake. Veronica anati: “Ndinkaona kuti sankasonkhana komanso kulalikira mokwanira. Choncho ndinkawaweruza chifukwa cha zimenezi. Koma kenako ndinalowa mu utumiki ndi mlongoyo. Iye anandifotokozera mavuto omwe ankakumana nawo chifukwa choti mwana wake anali ndi matenda a mu ubongo. Ankayesetsa kupezera banja lake zofunika komanso kuonetsetsa kuti iye ndi mwana wake ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Nthawi zina chifukwa cha vuto la mwana wakeli, ankafunika kukasonkhana ku mpingo wina.” Veronica anati: “Sindinkadziwa kuti mlongoyu akukumana ndi mavuto ngati amenewa. Panopa ndimamuyamikira
komanso kumulemekeza kwambiri chifukwa cha zimene amachita potumikira Yehova.”17. Kodi lemba la Yakobo 2:8, limatilangiza kuti tizichita chiyani, nanga tingachite bwanji zimenezo?
17 Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira kuti taweruza Mkhristu mnzathu? Tizikumbukira kuti tiyenera kumakonda abale athu. (Werengani Yakobo 2:8.) Komanso tizipempha Yehova mochokera pansi pa mtima kuti atithandize kusiya kuweruza ena. Tingachite zinthu mogwirizana ndi pemphero lathulo, poyesetsa kupeza nthawi yolankhulana ndi munthu yemwe tinamuweruzayo. Zimenezi zingatithandize kuti timudziwe bwino. Tingamupemphe kuti tilowe naye mu utumiki kapena kumuitanira kunyumba kwathu kudzadya naye chakudya. Tikayamba kumudziwa bwino m’bale wathuyo, tingayambe kutsanzira Yehova ndi Yesu poona zabwino mwa munthuyo. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikumvera lamulo la m’busa wabwino loti tisiye kuweruza ena.
18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera mawu a m’busa wabwino?
18 Mofanana ndi nkhosa zomwe zimamvera mawu a m’busa wawo, otsatira a Yesu nawonso amamvera mawu ake. Tikamayesetsa kuti tileke kudera nkhawa mmene tingapezere zinthu zofunika, komanso kuti tisiye kuweruza ena, Yehova ndi Yesu adzadalitsa khama lathulo. Kaya ndife a “kagulu ka nkhosa” kapena a “nkhosa zina”, tiyenera kupitiriza kumvera mawu a m’busa wabwino. (Luka 12:32; Yoh. 10:11, 14, 16) Munkhani yotsatira tidzakambirana zinthu ziwiri zimene Yesu anauza otsatira ake kuti azichita.
NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana
^ ndime 5 Pamene Yesu ananena kuti nkhosa zake zidzamva mawu ake, ankatanthauza kuti ophunzira ake azidzamvera zimene iye anaphunzitsa n’kumazigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Munkhaniyi tikambirana mfundo ziwiri zimene Yesu anaphunzitsa, zomwe ndi kusiya kuda nkhawa kuti tipeza bwanji zofunika komanso kusiya kuweruza ena. Tiona zimene tingachite kuti tizitsatira malangizo akewa.
^ ndime 51 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale ntchito yamuthera, alibe ndalama zothandizira banja lake komanso akufunika kupeza nyumba. Ngati sangasamale akhoza kumangokhalira kuda nkhawa n’kusiya kuika pamalo oyamba zinthu zokhudza kulambira.
^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale wafika mochedwa kumisonkhano. Koma akusonyeza makhalidwe abwino pomwe akulalikira mwamwayi, kuthandiza wachikulire komanso kugwira nawo ntchito yokonza pa Nyumba ya Ufumu.