Kodi Mumafuna Kukhala Wodziwika kwa Ndani?
“Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—AHEB. 6:10.
1. Kodi anthufe mwachibadwa timafuna chiyani?
KODI mumamva bwanji ngati munthu amene mumamudziwa komanso kumulemekeza waiwala dzina lanu kapena sakukuzindikirani n’komwe? Kunena zoona zimenezi zingakhale zokhumudwitsa. Tikutero chifukwa chakuti mwachibadwa anthufe timafuna kuti tizikondedwa. Timafuna kuti anthu azitizindikira komanso kukumbukira zimene tachita pa moyo wathu.—Num. 11:16; Yobu 31:6.
2, 3. Kodi zingatheke bwanji kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani yofuna kudziwika kapena kuyamikiridwa? (Onani chithunzi choyambirira.)
2 Koma mofanana ndi zinthu zina zimene timafuna mwachibadwa, n’zotheka kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani yofuna kudziwika kapena kuyamikiridwa ndi anthu ena. Popeza si ife angwiro, tingafune kudziwika m’njira yolakwika. Dziko la Satanali limalimbikitsa mtima wofuna kudziwika kwambiri umene umalepheretsa anthu kulemekeza komanso kulambira Atate wathu Yehova Mulungu.—Chiv. 4:11.
Luka 20:46, 47) Koma Yesu anayamikira mkazi wamasiye amene anapereka tindalama tochepa ngakhale kuti anthu ena sanadziwe n’komwe. (Luka 21:1-4) Apa zikuonekeratu kuti maganizo a Yesu pa nkhani yodziwika anali osiyana kwambiri ndi a anthu ena. Nkhaniyi itithandiza kukhala ndi maganizo a Yehova pa nkhani yofuna kukhala wodziwikayi.
3 Munthawi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo ena anali ndi maganizo olakwika pa nkhani yofuna kukhala odziwika. Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Chenjerani ndi alembi. Iwo amakonda kuyendayenda atavala mikanjo. Amakonda kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala m’mipando yakutsogolo [kapena kuti yabwino] m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.” Kenako ananena kuti: “Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.” (KUDZIWIDWA NDI WOLAMULIRA WA CHILENGEDWE CHONSE
4. Kodi tili ndi mwayi waukulu wodziwidwa ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi mwayi waukulu?
4 Anthu ambiri m’dzikoli amafuna kuti akhale odziwika kwa ena pa nkhani ya maphunziro, zamalonda komanso zosangalatsa. Koma ifeyo timaona kuti pali munthu wofunika kwambiri amene timafuna kuti atidziwe. Pa nkhaniyi, Paulo anafotokoza kuti: “Tsopano pamene mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziwidwa ndi Mulungu, mukubwereranso bwanji ku mfundo zachibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake, n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?” (Agal. 4:9) Ndi mwayitu waukulu ‘kudziwidwa ndi Mulungu,’ yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Iye amatidziwa, amatikonda komanso amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova ndiye kuti takwaniritsa cholinga chimene anatilengera.—Mlal. 12:13, 14.
5. Kodi tingatani kuti Mulungu atidziwe?
5 Mose anali ndi mwayi wodziwidwa ndi Mulungu. Iye atapempha Yehova kuti amuthandize kudziwa bwino njira zake, anamuyankha kuti: “Ndidzachita izinso zimene wanena, chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.” (Eks. 33:12-17) Ifenso tingapeze madalitso ambiri ngati Yehova atatidziwa bwino. Koma kodi tingatani kuti tikhale odziwika kwa Yehova? Tiyenera kumukonda komanso kudzipereka kwa iye.—Werengani 1 Akorinto 8:3.
6, 7. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?
6 Koma tiyenera kuyesetsa kuti tipitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Tikufunika kutsatira malangizo amene Paulo analembera Akhristu a ku Galatiya akuti azipewa kukhala akapolo a “mfundo zachibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake” za m’dzikoli monga kufuna kudziwika kwa anthu. (Agal. 4:9) Akhristu akalewo anali atafika podziwidwa ndi Mulungu. Koma Paulo ananena kuti Akhristuwa anayamba ‘kubwereranso’ ku zinthu zopanda pake. Zinali ngati akuwauza kuti: “Inu mwasintha zambiri kuti mufike pamenepa, ndiye n’chifukwa chiyani mukubwereranso ku zinthu zopusa komanso zopanda phindu zomwe munazisiya?”
7 Kodi zimenezi zingatichitikirenso masiku ano? Inde. Titangodziwa Yehova, mwina tinachita ngati Paulo ndipo tinasiya zinthu zimene zikanatichititsa kukhala odziwika m’dziko la Satanali. (Werengani Afilipi 3:7, 8.) N’kutheka kuti tinakana mwayi wopita kuyunivesite, wokwezedwa kuntchito kapena wopanga ndalama zambiri m’dzikoli. Mwina tili ndi luso loimba kapena la masewera enaake lomwe likanatichititsa kukhala odziwika ndiponso olemera koma sitinalole kuti tipite nazo patali. (Aheb. 11:24-27) Kungakhale kupanda nzeru kuganiza kuti tinataya mwayi posiya zinthu ngati zimenezi. Maganizo amenewa akhoza kuchititsa munthu kuti abwerere ku zinthu zimene anaziona kale kuti “n’zosathandiza ndiponso zopanda pake.”
TSIMIKIZANI MUMTIMA MWANU
8. N’chiyani chingatithandize kuti titsimikize mumtima mwathu zokhala odziwika kwa Yehova?
8 Ndiye kodi tingatani kuti titsimikize mumtima mwathu zokhala odziwika kwa Mulungu osati m’dzikoli? Kuti tichite zimenezi, tiyenera kukumbukira mfundo ziwiri zofunika kwambiri. Yoyamba ndi yakuti nthawi zonse Yehova amadalitsa anthu amene amamutumikira mokhulupirika. (Werengani Aheberi 6:10; 11:6) Iye amaona kuti mtumiki wake aliyense ndi wamtengo wapatali, ndipo kwa iye sichingakhale chilungamo kuiwala anthu okhulupirika. Nthawi zonse “Yehova amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Baibulo limanena kuti iye “amadziwa njira za olungama” ndipo amadziwanso kuwapulumutsa akakhala pa mayesero.—Sal. 1:6; 2 Pet. 2:9.
9. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amakonda anthu ake?
9 Yehova wakhala akusonyeza kuti amakonda anthu ake m’njira zodabwitsa kwambiri. (2 Mbiri 20:20, 29) Tangoganizani mmene anapulumutsira anthu ake pa Nyanja Yofiira pamene Farao ndi asilikali ake ankawathamangira. (Eks. 14:21-30; Sal. 106:9-11) Nkhani imeneyi inali yodabwitsa kwambiri moti anthu a m’deralo ankaikambabe patapita zaka 40. (Yos. 2:9-11) Kuganizira mmene Yehova wasonyezera chikondi komanso mphamvu munjira zimenezi kungatilimbikitse pamene tikuyembekezera kuukiridwa ndi Gogi wakudziko la Magogi. (Ezek. 38:8-12) Pa nthawi imeneyo tidzaona kuti tinachita bwino kwambiri kukhala odziwika kwa Mulungu osati m’dzikoli.
10. Kodi mfundo yachiwiri yofunika kuikumbukira ndi iti?
10 Mfundo yachiwiri yofunika kuikumbukira ndi yakuti: Yehova amadalitsa anthu amene akuwadziwa m’njira imene anthuwo sankayembekezera. Malemba amasonyeza kuti anthu amene amachita zabwino n’cholinga choti angoonedwa ndi anthu sadzadalitsidwa ndi Yehova ngakhale pang’ono. Zili choncho chifukwa amakhala atalandiriratu mphoto yawo yonse kuchokera kwa anthu. (Werengani Mateyu 6:1-5.) Koma Yesu ananena kuti Atate ake amayang’ana zinthu zamseri n’kuona anthu amene zochita zawo zabwino sizionekera kwa anthu ena. Iye amaona zinthu zimene anthu oterewa akuchita n’kuwadalitsa moyenerera. Ndipo nthawi zina Yehova akhoza kutidalitsa m’njira zimene sitinkayembekezera. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.
MULUNGU ANASONYEZA KUTI ANKADZIWA MARIYA
11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankadziwa bwino Mariya?
11 Nthawi yoti Yesu abadwe padzikoli itakwana, Yehova anasankha Mariya kuti akhale mayi wa mwana wapaderayu. Mariya anali namwali wodzichepetsa ndipo ankakhala mumzinda wa Nazareti. Mzindawu unali wosatchuka ndipo unali kutali ndi Yerusalemu komanso kachisi wake wokongola. (Werengani Luka 1:26-33.) Ndiye n’chifukwa chiyani Mulungu anasankha Mariya? Mngelo Gabirieli anauza Mariyayo kuti “Mulungu wakukomera mtima.” Ndipo zimene Mariya analankhula kwa Elizabeti zimasonyeza kuti ankadziwa bwino Mulungu komanso kumukonda. (Luka 1:46-55) Apa zikuonekeratu kuti Yehova ankaona kukhulupirika kwa Mariya ndipo anamudalitsa m’njira imene sankaiganizira.
12, 13. Kodi Mulungu analemekeza bwanji Yesu pa nthawi imene anabadwa komanso patapita masiku 40?
12 Yesu atabadwa, Yehova sanaulule nkhaniyi kwa anthu otchuka kapena olamulira a ku Yerusalemu ndi ku Betelehemu. M’malomwake anatumiza angelo kuti akauze abusa amene ankagona kubusa n’kumayang’anira nkhosa. (Luka 2:8-14) Abusawa atamva zimenezi anapita kukaona mwanayo. (Luka 2:15-17) Mariya ndi Yosefe ayenera kuti anadabwa kwambiri kuona kuti Yesu akulemekezedwa m’njira imeneyi. Koma zimene Satana anachita zinali zosiyana kwambiri ndi zimene Yehova anachita. Satana atatumiza okhulupirira nyenyezi kuti akaone Yesu ndi makolo ake, anthu onse ku Yerusalemu anamva za kubadwa kwa Yesu ndipo zinayambitsa mavuto aakulu. (Mat. 2:3) Kudziwika kwa nkhaniyi kunachititsa kuti ana osalakwa ambirimbiri aphedwe.—Mat. 2:16.
13 Patapita masiku 40 kuchokera pamene Yesu anabadwa, nthawi inafika yoti Mariya akapereke nsembe kwa Yehova kukachisi wa ku Yerusalemu. Ulendo wochokera ku Betelehemu kupita ku Yerusalemu unali wa makilomita pafupifupi 9. (Luka 2:22-24) Pamene Yosefe ndi Mariya ankapita, mwina Mariyayo ankadzifunsa kuti: ‘Kodi wansembe amene tikamupeze adzanena chilichonse chokhudza udindo umene Yesu adzakhale nawo m’tsogolo?’ Anthu ena ananenadi zinthu zokhudza Yesu koma osati amene Mariya ankayembekezera. Yehova anagwiritsa ntchito munthu “wolungama ndi woopa Mulungu” dzina lake Simiyoni komanso mneneri wamkazi wazaka 84 dzina lake Anna. Anthu awiriwa anamuzindikira Yesu ndipo anafotokoza kuti mwanayo adzakhala Mesiya wolonjezedwa kapena kuti Khristu.—Luka 2:25-38.
14. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Mariya?
14 Nanga bwanji za Mariya? Kodi Yehova anamuyamikira chifukwa cha kulera komanso kusamalira mokhulupirika Yesu ali mwana? Inde. Mulungu anachititsa kuti zimene Mariya anachita komanso kulankhula zilembedwe m’Baibulo. Zikuoneka kuti Mariya analibe mwayi woyenda ndi Yesu pa zaka zitatu ndi hafu zimene anachita utumiki wake padzikoli. Mwina anafunika kukhalabe ku Nazareti pambuyo poti mwamuna wake wamwalira. Koma ngakhale kuti analibe mwayi woona zinthu zambiri zimene Yesu anachita, iye analipo pamene Yesu ankaphedwa. (Yoh. 19:26) Pamene tsiku la Pentekosite linkayandikira, Mariya anali limodzi ndi ophunzira a Yesu ku Yerusalemu. (Mac. 1:13, 14) Zikuonekanso kuti iye anali m’gulu la anthu amene anadzozedwa ndi mzimu woyera. Ngati zinalidi choncho ndiye kuti anali ndi mwayi wokakhala ndi Yesu kumwamba kwamuyaya. Apatu Yehova anasonyeza kuti ankayamikira kwambiri zimene Mariya anachita.
YEHOVA ANALEMEKEZA MWANA WAKE
15. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankayamikira Yesu ali padzikoli?
15 Yesu sankafuna kulemekezedwa ndi atsogoleri achipembedzo kapena andale. Koma ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri Yehova atalankhula kuchokera kumwamba maulendo atatu posonyeza kuti amayamikira mwana wakeyu. Yesu atangobatizidwa mumtsinje wa Yorodano, Yehova ananena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:17) N’kutheka kuti Yohane M’batizi yekha ndi amene anamva mawuwa. Kutatsalanso chaka chimodzi kuti Yesu aphedwe, ophunzira ake atatu anamva Yehova akunena za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” (Mat. 17:5) Yehova analankhulanso ndi Mwana wake kuchokera kumwamba kutatsala masiku ochepa kuti Mwanayo aphedwe.—Yoh. 12:28.
16, 17. Kodi Yehova analemekeza bwanji Yesu m’njira imene sankaiyembekezera?
16 Yesu ankadziwa kuti adzafa imfa yochititsa manyazi ndipo anthu adzamunena kuti ndi wonyoza Mulungu. Ngakhale zinali choncho, iye anapempherabe kuti zinthu zichitike mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu osati chake. (Mat. 26:39, 42) Baibulo limanena kuti iye ‘anapirira mtengo wozunzikirapo ndipo sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira.’ (Aheb. 12:2) Yesu sankafuna kutchuka m’dzikoli koma kusangalatsa Atate ake. Kodi Yehova anamudalitsa bwanji?
17 Yesu ali padzikoli anapempha Atate ake kuti amupatse ulemerero umene anali nawo poyamba kumwamba. (Yoh. 17:5) Palibe umboni wakuti Yesu ankayembekezera zambiri kuposa zimene anali nazo poyamba. Sankayembekezera kuti akapita kumwambako akapatsidwa udindo wapamwamba. Koma kodi Yehova anachita chiyani? Analemekeza Yesu m’njira imene sankayembekezera chifukwa Baibulo limanena kuti anamupatsa “malo apamwamba” komanso anali woyamba kulandira “moyo wosakhoza kufa.” * (Afil. 2:9; 1 Tim. 6:16) Apatu Yehova anasonyeza kuti ankadziwa komanso kuyamikira utumiki umene Yesu anauchita mokhulupirika.
18. N’chiyani chingatithandize kuti tipewe kufuna kukhala odziwika m’dzikoli?
18 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamafune kukhala odziwika m’dzikoli? Tizikumbukira kuti nthawi zonse, Yehova amadalitsa atumiki ake okhulupirika ndipo nthawi zambiri amachita zimenezi m’njira imene sankayembekezera. Panopa palibe amene akudziwa madalitso osayembekezereka amene Yehova adzatipatse m’tsogolomu. Chongofunika panopa n’kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’dzikoli, n’kumakumbukira kuti dzikoli ndi zinthu zonse zimene anthu ake amadziwika nazo zitha posachedwapa. (1 Yoh. 2:17) Koma Atate wathu Yehova ‘si wosalungama woti angaiwale ntchito yathu ndi chikondi chimene timachisonyeza pa dzina lake.’ (Aheb. 6:10) Tizikumbukira nthawi zonse kuti adzatidalitsa mwinanso m’njira imene sitingaiganizire n’komwe panopa.
^ ndime 17 Zikuoneka kuti anamudalitsa m’njira yomwe sankaiyembekezera chifukwa m’Malemba Achiheberi onse nkhani ya “moyo wosakhoza kufa” sinatchulidwe.