Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 30

Pitirizani Kuyenda m’Choonadi

Pitirizani Kuyenda m’Choonadi

“Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”​—3 YOH. 4.

NYIMBO NA. 54 “Njira Ndi Iyi”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi 3 Yohane 3, 4, n’chiyani chimatipangitsa kukhala osangalala?

TANGOGANIZANI mmene mtumwi Yohane anasangalalira pamene anamva zoti anthu amene anawathandiza kuphunzira choonadi akupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika. Akhristuwa ankakumana ndi mavuto ambiri ndipo Yohane ankayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chawo ndipo ankawaona ngati ana ake. Mofanana ndi Yohane, ifenso timasangalala tikaona ana athu kapena anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akudzipereka kwa Yehova n’kumapitiriza kumutumikira.​—Werengani 3 Yohane 3, 4.

2. Kodi cholinga cha makalata amene Yohane analemba chinali chiyani?

2 M’chaka cha 98 C.E., Yohane ayenera ankakhala mumzinda wa Efeso kapena pafupi ndi mzindawu. Zikuoneka kuti anapita kukakhala kumeneku atatulutsidwa m’ndende pachilumba cha Patimo. Pa nthawi imeneyo, mzimu wa Yehova unamuthandiza kulemba makalata atatu. Cholinga cha makalatawa chinali kulimbikitsa Akhristu okhulupirika kuti apitirize kukhulupirira Yesu komanso asasiye kuyenda m’choonadi.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Pa nthawiyo, Yohane anali mtumwi yekhayo amene anatsala ndipo ankada nkhawa kwambiri ndi aphunzitsi onyenga omwe ankasokoneza mipingo. * (1 Yoh. 2:18, 19, 26) Anthu ampatukowa ankanena kuti amadziwa Mulungu koma sankatsatira malamulo ake. Tsopano tiyeni tione malangizo amene Yohane anapereka ndipo kenako tipeza mayankho a mafunso atatu awa: Kodi kuyenda m’choonadi kumatanthauza chiyani? N’chiyani chingatilepheretse kuyendabe m’choonadi? Nanga tingatani kuti tizithandiza abale ndi alongo athu kuyendabe m’choonadi?

 

KODI KUYENDA M’CHOONADI KUMATANTHAUZA CHIYANI?

4. Malinga ndi 1 Yohane 2:3-6 ndi 2 Yohane 4, 6, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiziyenda m’choonadi?

4 Kuti tiziyenda m’choonadi, tiyenera kudziwa choonadi chopezeka m’Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu. Komanso tiyenera “kusunga malamulo ake” zomwe zikutanthauza kuwatsatira. (Werengani 1 Yohane 2:3-6; 2 Yohane 4, 6.) Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera Yehova. Choncho chinthu chofunika kwambiri chomwe tingachite kuti tizimvera Yehova ndi kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.​—Yoh. 8:29; 1 Pet. 2:21.

5. Kodi tiyenera kutsimikizira zinthu ziti?

5 Kuti tipitirize kuyenda m’choonadi, tiyenera kutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wachoonadi ndiponso kuti zonse zimene amatiuza m’Mawu ake ndi zoona. Tiyeneranso kutsimikizira kuti Yesu ndi Mesiya amene Mulungu analonjeza. Anthu ambiri masiku ano amakaikira kuti Yesu anadzozedwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. M’kalata yake, Yohane anachenjeza kuti kunali “anthu onyenga ambiri” omwe akanatha kusocheretsa anthu amene ankakaikira choonadi chokhudza Yehova komanso Yesu. (2 Yoh. 7-11) Iye analemba kuti: “Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?” (1 Yoh. 2:22) Choncho kuti tisapusitsidwe, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi tingadziwe bwino Yehova komanso Yesu. (Yoh. 17:3) Ndipo zimenezi ndi zomwe zingatipangitse kutsimikizira kuti tikudziwa choonadi.

N’CHIYANI CHINGATILEPHERETSE KUYENDABE M’CHOONADI?

6. N’chiyani chingachititse Akhristu achinyamata kusiya kuyenda m’choonadi?

6 Akhristu onse ayenera kusamala kuti asasocheretsedwe ndi nzeru za anthu a m’dzikoli. (1 Yoh. 2:26) Makamaka Akhristu achinyamata ayenera kusamala kwambiri ndi msampha umenewu. Mlongo wina wazaka 25 dzina lake Alexia * wa ku France anati: “Ndili kusukulu ndinaphunzira nzeru zosiyanasiyana za anthu kuphatikizapo zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kukayikira choonadi. Nthawi zina ndinkaona kuti zimene tinkaphunzira ndi zoona. Koma ndinaona kuti si bwino kunyalanyaza zimene Baibulo limaphunzitsa n’kumangokhulupirira chilichonse chimene aphunzitsi amatiuza.” Alexia anaphunzira buku lina lomwe limafotokoza kuti zinthu zinachita kulengedwa. * Atangoliwerenga kwa milungu ingapo, anasiya kukaikira. Iye anati: “Ndinaona kuti m’Baibulo ndi mmene muli choonadi. Ndipo ndinazindikira kuti kutsatira mfundo zake n’kumene kungandithandize kukhala wosangalala.”

7. Kodi tiyenera kupewa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Akhristu onse, kaya ndi achinyamata kapena achikulire, ayenera kupewa moyo wachiphamaso. Mtumwi Yohane ananena kuti sizingatheke kuti tiziyenda m’choonadi kwinaku tikuchita makhalidwe oipa. (1 Yoh. 1:6) Ngati tikufuna kuti Yehova azisangalala nafe, tizikumbukira kuti iye amaona chilichonse chimene timachita. Ngakhale tibisire anthu zimene timachita mseri, Yehova amakhala akutiona.​—Aheb. 4:13.

8. Kodi tiyenera kupewa chiyani?

8 Tiyenera kupewa maganizo a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya tchimo. Mtumwi Yohane analemba kuti, “Tikanena kuti: ‘Tilibe uchimo,’ ndiye kuti tikudzinamiza.” (1 Yoh. 1:8) Munthawi ya Yohane, ampatuko ankanena kuti munthu akhoza kumachita machimo mwadala n’kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu. Nafenso tikukhala pakati pa anthu omwe ali ndi maganizo ngati amenewa. Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Mulungu, koma sagwirizana ndi zimene Yehova amanena pa nkhani ya tchimo, makamaka nkhani ya kugonana. Pali zinthu zina zomwe anthu amachita pa nkhaniyi zimene Yehova amati ndi zoipa. Koma anthuwa amaona kuti palibe vuto kuchita zimenezo ngati ukufuna.

Achinyamata, muzifufuza kuti mudziwe chifukwa chake Yehova amanena kuti khalidwe linalake ndi labwino kapena loipa. Mukatero mungathe kufotokozera ena chifukwa chake simuchita nawo makhalidwe oipa (Onani ndime 9) *

9. Kodi achinyamata amapindula bwanji akamayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo?

9 Kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya kugonana ndi kovuta kwambiri makamaka kwa Akhristu achinyamata. Tikutero chifukwa nthawi zambiri anzawo a kusukulu kapena kuntchito amawakopa kuti aziyendera maganizo awo. Izi ndi zomwe zinachitikira wachinyamata wina dzina lake Aleksandar. Iye anati: “Atsikana ena a kusukulu kwathu ankandinyengerera kuti ndigonane nawo. Ankanena kuti popeza ndilibe chibwenzi, ndiye kuti ndimagonana ndi amuna anzanga.” Ngati nanunso mumakumana ndi mayesero ngati amenewa, muzikumbukira kuti mukamatsatira zimene Baibulo limanena mumakhala ndi mbiri yabwino, mumakhala athanzi, simudziimba mlandu komanso mumakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mukamayesetsa kupewa mayesero, zimakhala zosavuta kuti muzichita zoyenera. Muzikumbukiranso kuti Satana ndi amene amachititsa kuti anthu a m’dzikoli azikhala ndi maganizo olakwika okhudza kugonana. Choncho mukamayesetsa kukana mayesero, mumakhala ‘mukugonjetsa woipayo.’​—1 Yoh. 2:14.

10. Kodi lemba la 1 Yohane 1:9 lingatithandize bwanji kuti tizitumikira Yehova ndi chikumbumtima choyera?

10 Timadziwa kuti Yehova ndi amene angatiuze ngati khalidwe linalake lili tchimo kapena ayi. Ndipo timayesetsa kuti tisamachite machimo. Koma tikachimwa, timapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti atikhululukire. (Werengani 1 Yohane 1:9.) Ndipo tikachita tchimo lalikulu, timapempha akulu kuti atithandize. Yehova anapatsa akuluwa udindo woti azitisamalira. (Yak. 5:14-16) Komabe ngati tinakonza zinthu, sitiyenera kumadziimba mlandu chifukwa cha machimo omwe tinachita kalekale. Tikutero chifukwa Atate wathu wachikondi anapereka Mwana wake nsembe kuti azitikhululukira machimo athu. Choncho tisamakaikire zimene amatiuza kuti adzatikhululukira ngati talapadi kuchokera mumtima. Apatu tinganene kuti palibe chomwe chingatilepheretse kumatumikira Yehova ndi chikumbumtima choyera.​—1 Yoh. 2:1, 2, 12; 3:19, 20.

11. Kodi tingadziteteze bwanji ku ziphunzitso zimene zikhoza kuwononga chikhulupiriro chathu?

11 Tiyenera kupewa ziphunzitso za anthu ampatuko. Kungochokera pamene mpingo wa Chikhristu unayamba, Satana wakhala akugwiritsa ntchito ampatuko kuti azichititsa atumiki okhulupirika a Yehova kukayikira kuti zimene amakhulupirira ndi zoona. Choncho n’zofunika kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa zoona ndi zabodza. * Adani athu akhoza kugwiritsa ntchito intaneti kapena malo ena ochezera a pa intaneti n’cholinga choti atichititse kusiya kukhulupirira Yehova komanso kukonda abale ndi alongo athu. Musamaiwale kuti Satana ndi amene amafalitsa mabodza amenewa ndipo sitiyenera kuwakhulupirira.​—1 Yoh. 4:1, 6; Chiv. 12:9.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu pa mfundo za choonadi zimene tinaphunzira?

12 Kuti Satana asafooketse chikhulupiriro chathu, tiyenera kumakhulupirira Yesu komanso kuzindikira udindo umene ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Tiyeneranso kumakhulupirira kwambiri anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito potsogolera gulu lake. (Mat. 24:45-47) Chikhulupiriro chathu chingalimbe kwambiri tikamaphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Tikamatero, chikhulupiriro chathu chingafanane ndi mtengo umene mizu yake yalowa pansi kwambiri. Paulo anatchula mfundo yofanana ndi imeneyi m’kalata yake yopita kumpingo wa Akolose. Iye anati: “Popeza mwalandira Khristu Yesu Ambuye wathu, yendanibe mogwirizana naye. Khalanibe ozikika mozama mwa iye, ndipo monga mmene munaphunzitsidwira, pitirizani kukula pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.” (Akol. 2:6, 7) Tikamayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu, Satana komanso anthu ake sangatilepheretse kuyendabe m’choonadi.​—2 Yoh. 8, 9.

13. Kodi tiziyembekezera chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

13 Akhristufe tiyenera kumayembekezera kuti dzikoli likhoza kudana nafe. (1 Yoh. 3:13) Yohane ananena kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Pamene mapeto akuyandikira, Satana ndi wokwiya kwambiri. (Chiv. 12:12) Choncho akumagwiritsa ntchito njira zosaonekera monga kukonda chiwerewere kapena mabodza a ampatuko. Nthawi zinanso angachititse kuti anthu azitizunza kwambiri. Satana akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa ndipo akuyesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti alepheretse ntchito yathu yolalikira kapena kuwononga chikhulupiriro chathu. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti ntchito yathu ndi yoletsedwa m’mayiko ena. Ngakhale zili choncho, abale ndi alongo athu a m’mayiko amenewa akupitirizabe kupirira. Abalewa akusonyeza kuti palibe chimene Satana angachite kuti atilepheretse kukhala okhulupirika kwa Yehova.

TIZITHANDIZANA KUTI TIZIYENDABE M’CHOONADI

14. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe tingathandizire abale ndi alongo athu kukhalabe m’choonadi?

14 Kuti tithandize abale ndi alongo athu kukhalabe m’choonadi, tiyenera kumawasonyeza chifundo. (1 Yoh. 3:10, 11, 16-18) Tiyenera kumakondana osati pamtendere pokha, komanso pamavuto. Mwachitsanzo, kodi mukudziwa m’bale kapena mlongo amene waferedwa ndipo akufunika kutonthozedwa komanso kuthandizidwa m’njira zina? Kapena mwamva zoti okhulupirira anzanu akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe ndipo akufunika kuwamangiranso Nyumba za Ufumu komanso nyumba zawo? Timasonyeza chifundo ndiponso kuti timakonda kwambiri abale athu ndi zochita zathu, osati ndi zolankhula zathu zokha.

15. Mogwirizana ndi 1 Yohane 4:7, 8, kodi tiyenera kuchita chiyani?

15 Tikamakondana timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi. (Werengani 1 Yohane 4:7, 8.) Njira ina yomwe timasonyezera chikondi ndi kukhululukira ena. Mwachitsanzo, munthu wina angatikhumudwitse, kenako n’kupepesa. Zikatere, tingasonyeze chikondi ngati tingamukhululukire n’kuiwala nkhaniyo. (Akol. 3:13) M’bale wina dzina lake Aldo anakumana ndi mayesero amenewa pamene anamva m’bale wina yemwe ankamulemekeza kwambiri akunena zoipa zokhudza anthu amtundu wake. Aldo anati: “Nthawi zonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndisayambe kudana ndi m’baleyo.” Koma Aldo anachitanso zinthu zina. Anaganiza zopempha m’baleyo kuti ayendere limodzi mu utumiki. Pa nthawi imeneyi, Aldo anafotokoza mmene anamvera chifukwa cha zimene m’baleyo analankhula. Iye anati: “M’baleyo atamva mmene ndinamvera, anapepesa. Mmene ankalankhulira, zinkasonyezeratu kuti anazindikira kuti sanachite bwino. Pamene tinkasiyana, tinali titakhululukirana ndipo tinayambiranso kugwirizana kwambiri.”

16-17. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

16 Mtumwi Yohane ankaganizira komanso kuwafunira zabwino abale ake. Zimenezi zimaonekera m’malangizo amene analemba m’makalata ake atatu ouziridwa. N’zosangalatsa kudziwa kuti nawonso amuna ndi akazi omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba ndi achikondi komanso oganizira ena ngati Yohane.​—1 Yoh. 2:27.

17 Tiyeni tiyesetse kugwiritsa ntchito malangizo amene takambiranawa. Tiyeni titsimikize mtima kuti tisasiye kuyenda m’choonadi pomvera Yehova pa zilizonse zomwe timachita. Nthawi zonse tiziphunzira Mawu ake n’kumawakhulupirira komanso tizikhulupirira Yesu. Tizipewa nzeru za anthu a m’dzikoli ndiponso ziphunzitso za anthu ampatuko. Tisamakhale moyo wachiphamaso komanso tisamakopeke ndi anthu amene angatinyengerere kuti tichite zoipa. Tizitsatira mfundo zabwino za Yehova. Komanso tiyeni tizithandiza abale athu kuti akhalebe olimba pokhululukira amene atilakwira komanso kuthandiza anthu amene ali pamavuto. Tikatero, tingapitirizebe kuyenda m’choonadi ngakhale zitakhala kuti tikukumana ndi mavuto.

NYIMBO NA. 49 Tizikondweretsa Mtima wa Yehova

^ ndime 5 Tikukhala m’dziko lomwe wolamulira wake ndi Satana yemwe ndi tate wake wa bodza. Choncho nthawi zambiri zimativuta kuti tiziyendabe m’choonadi. Nawonso Akhristu a munthawi ya atumwi ankakumana ndi vuto lomweli. Pofuna kuwathandiza komanso kutithandiza ifeyo, Yehova anauzira mtumwi Yohane kulemba makalata atatu. Mfundo za m’makalatawa zitithandiza kudziwa zinthu zimene zingachititse kuti tisiye kuyenda m’choonadi komanso zomwe tingachite kuti tisagonje.

^ ndime 6 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 6 Bukuli ndi la mutu wakuti, Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? ndipo limafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova.

^ ndime 11 Onani nkhani yakuti, “Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?” mu Nsanja ya Olonda ya August 2018.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo wachitsikana ali kusukulu ndipo akungokhalira kumva komanso kuona zinthu zomwe zimachititsa anthu kuona kuti palibe vuto kugonana amuna kapena akazi okhaokha. (M’zikhalidwe zina, anthu amagwiritsa ntchito zibangili komanso zinthu zina zokhala ndi mitundu ya utawaleza yomwe imaimira mchitidwewu.) Kenako akufufuza zambiri zokhudza nkhaniyi kuti alimbitse chikhulupiro chake. Izi zikumuthandiza kuchita zinthu mwanzeru..