Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Kulira Kwa Lipenga

Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Kulira Kwa Lipenga

TIMAKHULUPIRIRA kuti Yehova akutsogolera anthu ake komanso kuwathandiza kuti akhalebe naye pa ubwenzi “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1) Koma aliyense amafunika kusankha yekha kuti azimvera Yehova. Zimenezi tingaziyerekezere ndi mmene zinalili ndi Aisiraeli m’chipululu. Iwo ankafunika kuchitapo kanthu akamva kulira kwa lipenga.

Yehova anauza Mose kuti apange malipenga awiri asiliva oti azigwiritsa ntchito “poitanitsa msonkhano ndi posamutsa msasa.” (Num. 10:2) Ansembe ankaliza malipengawo mosiyanasiyana pofuna kudziwitsa anthu zimene akufunika kuchita. (Num. 10:3-8) Masiku ano, anthu a Mulungu amalandira malangizo m’njira zosiyanasiyana. Munkhaniyi, tikambirana njira zitatu zimene timalandirira malangizo zomwe zikufanana ndi mmene Aisiraeli ankalandirira malangizo. Njira zitatuzi ndi kudzera m’misonkhano ikuluikulu, masukulu a akulu komanso pamene malangizo okhudza mipingo yonse asintha.

MISONKHANO IKULUIKULU

Yehova akafuna kuti “khamu lonse” la Aisiraeli lisonkhane kum’mawa kwa khomo la chihema, ansembe ankaliza malipenga onse awiri. (Num. 10:3) Ndiyeno mafuko onse amene ankakhala mozungulira mbali zonse zachihemacho ankamva kulira kwa malipengawo. Amene ankakhala pafupi, ankatha kufika mwansanga. Pomwe ena omwe ankakhala kutali, zinkawatengera nthawi komanso ankafunika kuchita khama kuti afike. Komabe kaya amakhala kutali kapena pafupi, Yehova ankafuna kuti onse afike n’kukamva malangizo.

Masiku ano sitisonkhananso kuchihema, koma timakhalabe ndi misonkhano kumene anthu a Mulungu amakumana. Misonkhanoyi ndi monga misonkhano yachigawo ndi zochitika zina zapadera komwe timalandira malangizo ofunika. Anthu a Yehova amakhala ndi misonkhano yofanana m’mayiko onse. Choncho anthu amene amabwera kumisonkhanoyi amakhala m’gulu la anthu ambirimbiri osangalala omwe asonkhana. Ena mwa anthuwa amayenda mitunda italiitali kuposa ena. Ngakhale zili choncho, onse amene amapezeka pamisonkhanoyi amaona kuti anachita bwino kuyesetsa kuti apezekepo.

Koma pali anthu ena ambirimbiri omwe amakhala kutali kwambiri moti sangakwanitse kufika pamisonkhanoyi. Kodi nawonso angapindule ndi misonkhanoyi? Inde. Pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, ambiri amatha kupindula ndi misonkhanoyi ndipo amadzimva kuti ali m’gulu la anthu ambirimbiri omwe asonkhana. Mwachitsanzo, pamene woimira likulu anapita kukayendera ofesi ya nthambi ya ku Benin, abale ena a m’tauni ya Arlit, yomwe ili ku Niger, m’chipululu cha Sahara, analumikizidwa kuti amvetsere nawo msonkhano umene anachititsa. Abale, alongo ndi anthu ena achidwi okwana 21 ndi amene anasonkhana. Ngakhale kuti anali kutali ankamva kuti anali limodzi ndi abale ndi alongo okwana 44,131, omwenso anali pamsonkhanowu. M’bale wina analemba kuti: “Tikuthokoza kuchokera pansi pamtima chifukwa chotilumikiza kuti tipindule ndi msonkhanowu. Zatithandiza kudziwa kuti mumatikonda kwambiri.”

MASUKULU A AKULU

Wansembe akaliza lipenga limodzi lokha, ‘akuluakulu amene anali atsogoleri a masauzande a Aisiraeli,’ ndi omwe ankafunika kupita kuchihema. (Num. 10:4) Kumeneko ankapatsidwa malangizo komanso kuphunzitsidwa ndi Mose. Zimenezi zinkawathandiza kuti azikwanitsa udindo wawo wosamalira mafuko omwe ankayang’anira. Ndiye mukanakhala mmodzi mwa atsogoleriwa, kodi simukanayesetsa kuti muzipezekapo ndi kulandira malangizo?

Masiku ano, akulu sali ngati “atsogoleri a masauzande a Aisiraeli” aja ndipo sachita ufumu pankhosa za Mulungu zimene amazisamalira. (1 Pet. 5:1-3) Koma iwo amachita zonse zomwe angathe poweta nkhosazi. Choncho akaitanidwa kuti akalandire maphunziro owonjezereka, monga ku Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, amayesetsa kupita. Pamaphunzirowa, akulu amalandira malangizo owathandiza kuti azigwira bwino ntchito zamumpingo. Zimenezi zimathandiza kuti akuluwo komanso anthu onse mumpingo akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Choncho aliyense, ngakhale amene sanalandire nawo maphunzirowa amapindula.

PAKAKHALA KUSINTHA

Nthawi zina ansembe achiisiraeli ankaliza lipenga lomwe linkamveka mosinthasintha. Izi zinkatanthauza kuti Yehova akufuna anthu onse anyamuke. (Num. 10:5, 6) Anthuwa akamanyamuka ankachita zinthu mwadongosolo kwambiri. Komabe kuchita zimenezi sikunali kophweka. Nthawi zina Aisiraeli ena ankanyinyirika kusamukira malo ena. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi?

N’kutheka kuti Aisiraeli ena ankaona kuti lipengalo lalira mwansanga komanso panthawi imene samayembekezera. Nthawi zina mtambo umene unkawatsogolera unkatha “kukhalapo kuchokera madzulo kufika m’mawa.” Pomwe nthawi zina unkatha kukhala “masiku awiri, mwezi, kapena masiku ambiri” asanasamuke. (Num. 9:21, 22) Ndiye kodi anthuwa anasamuka maulendo angati? Chaputala 33 cha buku la Numeri chimasonyeza kuti Aisiraeli anakhala malo okwana 40.

Nthawi zina, ena ankapeza malo a mthunzi wabwino. Kupeza malo abwino oterowo mu “chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,” kunali kosangalatsa. (Deut. 1:19) Choncho kusamuka kunkachititsa ena kuganiza kuti sangakapezenso malo ena abwino.

Ponyamuka, mafuko ena ankafunika kudikira moleza mtima mpaka nthawi yawo yoti anyamuke ifike. Mafuko onse ankamva kulira kwa lipenga, koma sankanyamuka onse nthawi imodzi. Lipengalo likalira koyamba, mafuko a m’misasa yakum’mawa, omwe anali fuko la Yuda, Isakara ndi Zebuloni ndi omwe ankayamba kunyamuka. (Num. 2:3-7; 10:5, 6) Amenewa akanyamuka, ansembe ankalizanso lipenga kachiwiri podziwitsa mafuko atatu a m’misasa yakum’mwera kuti anyamuke. Ansembewa ankachita zimenezi mpaka mafuko onse atanyamuka.

N’kutheka kuti nanunso zinakuvutanipo kuvomereza zinthu zina zitasintha m’gulu la Yehova. Mwina munkaona kuti zinthu zambirimbiri zasintha m’njira imene simunkayembekezera. Kapenanso munkasangalala ndi mmene zinthu zinalili poyamba ndipo simunkafuna zitasintha. Kaya chifukwacho chinali chotani, koma muyenera kuti zinakuvutani kukhala oleza mtima ndipo zinakutengerani nthawi kuti muzolowere zinthu zatsopanozo. Komabe tikamayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizowo tidzaona kuti kusinthako n’kwabwino ndipo Yehova adzasangalala nafe.

M’nthawi ya Mose, Yehova anatsogolera anthu mamiliyoni, amuna, akazi ndi ana kuti adutse m’chipululu. Akanapanda kuwasamalira komanso kuwapatsa malangizo, anthuwa sakanapulumuka. Masiku anonso, timatetezeka mwauzimu chifukwa Yehova akutitsogolera. Iye amatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino komanso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Choncho, tiyeni titsimikize mtima kuti tizitsatira malangizo ngati mmene Aisiraeli okhulupirika ankachitira akamva kulira kosiyanasiyana kwa lipenga.