Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Mu nthawi ya Yesu, kodi anthu ankafunika kupereka misonkho iti?

KWA ZAKA zambiri, Aisiraeli ankapereka ndalama zothandizira pa kulambira koona. Koma pofika mu nthawi ya Yesu, Ayuda ankapereka misonkho yambirimbiri zomwe zinkachititsa kuti moyo ukhale wovuta.

Pofuna kuthandizira pa zochitika za pakachisi, Myuda aliyense wamkulu ankafunika kupereka hafu ya sekeli (madalakima awiri). Ndalama imeneyi inkagwiritsidwa ntchito kupezera zofunika popereka nsembe komanso posamalira kachisi amene Herode anamanga. Ayuda ena anafunsa Petulo kuti adziwe maganizo a Yesu pa nkhaniyi. Ndipo Yesu sananene kuti kupereka msonkhowu n’kolakwika. M’malomwake, iye anauza Petulo kumene angakapeze ndalama yoti akapereke msonkhowo.​—Mat. 17:24-27.

Kalero anthu a Mulungu ankafunikanso kupereka msonkho wina, womwe unkaphatikizapo kupereka chakhumi cha zokolola zawo kapena ndalama. (Lev. 27:30-32; Num. 18:26-28) Atsogoleri achipembedzo ankafunanso kuti anthu azipereka chakhumi pa mbewu zilizonse zamasamba ngakhale “timbewu ta minti, dilili ndi chitowe.” Yesu sananene kuti kupereka chakhumi n’kolakwika, m’malomwake iye anadzudzula alembi ndi Afarisi poika malamulo awoawo pa nkhaniyi.​—Mat. 23:23.

Ayuda ankafunikanso kupereka misonkho yambiri kwa Aroma omwe ankawalamulira. Mwachitsanzo, msonkho wina ankapereka ndi anthu amene anali ndi malo. Iwo ankalipira msonkhowu popereka ndalama kapena zinthu. Zikuoneka kuti munthu ankafunika kupereka 20 mpaka 25 peresenti ya zokolola za pamalo ake. Ndiye panalinso msonkho wina wapachaka umene Myuda aliyense ankayenera kupereka. Ndipo inali nkhani yokhudza msonkho umenewu, imene Afarisi anafunsa Yesu. Posonyeza mmene tiyenera kuonera nkhaniyi, iye anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”​—Mat. 22:15-22.

Amalonda ankaperekanso msonkho akamalowa kapena kutuluka m’madera amene munkachitikira zamalonda. Otolera misonkhoyi ankakhala m’madoko, m’maburiji, m’mphambano za misewu kapenanso m’malo olowera m’matauni ngakhale m’misika.

Kunena zoona, nkhani yopereka misonkho inali mtolo waukulu kwambiri kwa anthu amene ankalamuliridwa ndi Aroma. Mogwirizana ndi zimene wolemba mbiri wina wa Chiroma, dzina lake Tacitus ananena, pa nthawi ya ulamuliro wa Tiberiyo, Yesu ali padzikoli, “anthu a ku Siriya ndi a ku Yudeya ataona kuti zikuwavuta, anapempha kuti awachepetsereko misonkho ina.”

Njira imene ankagwiritsa ntchito potolera misonkhoyi ndi imenenso inkachititsa kuti ikhale yokwera. Kuti munthu apatsidwe ntchito imeneyi ankachita kupereka ndalama ndipo amene wapereka zambiri ndi amene ankapatsidwa ntchitoyo. Anthu amenewa ankalemba ntchito anthu ena kuti azitolera misonkhoyo, ndipo otolera misonkhowo ankakweza mitengo n’cholinga choti nawonso azipezapo phindu. Zikuoneka kuti Zakeyu anali ndi antchito omwe ankatolera misonkho. (Luka 19:1, 2) Choncho, m’pomveka kuti anthu ankadana kwambiri ndi anthu otolera misonkhowo