Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Mwa chilamulo, ine ndinafa ku chilamulo?”​—Agal. 2:19.

Paulo analemba kuti: “Mwa chilamulo, ine ndinafa ku chilamulo, moti sindingachitsatirenso, kuti ndikhale wamoyo kwa Mulungu.”​—Agal. 2: 19.

Paulo analemba zimenezi mogwirizana ndi mfundo yaikulu imene ankafotokozera mipingo ya ku Galatiya, chigawo chomwe chinali pansi pa ulamuliro wa Roma. Akhristu ena kumeneko ankasokonezedwa ndi aphunzitsi a bodza. Aphunzitsiwa ankanena kuti munthu angadzapulumuke pokhapokha ngati akutsatira Chilamulo cha Mose, makamaka pa nkhani ya mdulidwe. Koma Paulo ankadziwa kuti Mulungu sankafunanso kuti anthu omwe amamulambira azichita mdulidwe. Iye anapereka umboni wamphamvu potsutsa zomwe aphunzitsi abodzawa ankaphunzitsa, ndipo anathandiza abale kuti azikhulupirira kwambiri nsembe ya dipo ya Yesu Khristu.​—Agal. 2:4; 5:2.

Baibulo limanena momveka bwino kuti munthu akafa sadziwa kapena kukhudzidwa ndi chilichonse chomwe chikuchitika. (Mlal. 9:5) Choncho pamene Paulo anati: “Ndinafa ku chilamulo,” ankatanthauza kuti sankafunikanso kutsatira Chilamulo cha Mose. M’malomwake, Paulo anali wotsimikiza kuti chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo, iye ‘anakhala wamoyo kwa Mulungu.’

Zinthu zinasintha chonchi kwa Paulo “mwa chilamulo.” Kodi tikutanthauza chiyani pamenepa? Iye anali atangofotokoza kumene kuti “munthu amayesedwa wolungama mwa kukhulupirira Khristu Yesu, osati chifukwa cha ntchito za chilamulo.” (Agal. 2:16) Komabe Chilamulo chinakwaniritsa zinthu zina zofunika kwambiri. Paulo anafotokozera Agalatiya kuti: “Anachiwonjezerapo kuti machimo aonekere, mpaka amene ali mbewuyo atafika, amene anapatsidwa lonjezolo.” (Agal. 3:19) Kunena zoona, Chilamulo chinasonyeza bwino kuti anthu omwe si angwiro sangathe kuchitsatira bwinobwino, ndipo ankafunika nsembe yomaliza yangwiro. Choncho Chilamulo chinathandiza anthu kudziwa kuti “mbewuyo” ndi Khristu. Ngati munthu akanakhulupirira Yesu Khristu, Mulungu akanamuona munthuyo kuti ndi wolungama. (Agal. 3:24) Paulo anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa kudzera mu Chilamulo, iye anavomereza komanso kukhulupirira Yesu. Choncho apa Paulo ‘anafa ku chilamulo’ ndipo anakhala “wamoyo kwa Mulungu.” Chilamulo chinalibenso mphamvu pa iye, koma Mulungu.

Paulo anafotokozanso zofanana ndi zimenezi m’kalata yake yomwe analembera Akhristu a ku Roma. Iye anati: “Abale anga, thupi la Khristu linakupangani kukhala akufa ku Chilamulo . . . Tamasulidwa ku Chilamulo, chifukwa tafa ku chilamulo chimene chinali kutimanga chija.” (Aroma 7: 4, 6) Palembali komanso pa Agalatiya 2:19, Paulo sankanena zokhudza kufa chifukwa cholephera kutsatira Chilamulo. M’malomwake iye ankanena zokhudza kumasulidwa. Choncho Chilamulo chinalibenso mphamvu pa iyeyo komanso anthu ena omwe anali ngati iyeyo. Iwo anamasulidwa chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu.