Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 23

Yehova Ali Nanu, Simuli Nokha

Yehova Ali Nanu, Simuli Nokha

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.”​—SAL. 145:18.

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova nthawi zina angamadzione kuti ali okhaokha?

AMBIRIFE nthawi zina timadziona kuti tili tokhatokha. Ena zimenezi zimangowachitikira kwa nthawi yochepa, pomwe kwa ena zimachitika kwa nthawi yaitali. Tikhozanso kumaona kuti tili tokhatokha ngakhale pamene tili ndi anthu ena. Ena amavutika kuti azolowere mpingo wawo watsopano. Ena anakulira m’banja limene anthu ake amakonda kuchitira zinthu pamodzi, choncho amayamba kudziona kuti ali okhaokha akakhala kutali ndi achibale awo. Enanso amamusowa munthu amene amamukonda yemwe anamwalira. Ndipo Akhristu ena, makamaka amene angophunzira kumene choonadi, amayamba kudziona kuti ali okhaokha akamakanidwa kapena kutsutsidwa ndi achibale komanso anzawo omwe si a Mboni.

2. Kodi tikambirana mayankho a mafunso ati?

2 Yehova amadziwa komanso kumvetsa bwino zonse zimene zimatichitikira. Iye amadziwa tikayamba kukhala ndi maganizo odziona ngati tili tokhatokha ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Ndiye kodi Yehova amatithandiza bwanji? Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani tikayamba kukhala ndi maganizo amenewa? Nanga tingathandize bwanji ena mumpingo omwe amadziona ngati ali okhaokha? Tiyeni tione mayankho a mafunso amenewa.

YEHOVA AMADZIWA MMENE TIKUMVERA

Yehova anatumiza mngelo kuti akatsimikizire Eliya kuti sanali yekha (Onani ndime 3)

3. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anakhudzidwa chifukwa cha mmene Eliya ankamvera?

3 Yehova amachita chidwi kwambiri ndi zimene zimachitikira anthu amene amamulambira. Iye ali pafupi ndi aliyense wa ife ndipo amaona tikakhumudwa kapena kufooka ndi zinazake. (Sal. 145:18, 19) Taganizirani mmene anasonyezera kuti anakhudzidwa chifukwa cha mmene mneneri wake Eliya ankamvera. Munthu wokhulupirikayu anakhala ndi moyo pa nthawi imene zinthu sizinali bwino ku Isiraeli. Olambira Yehova ankazunzidwa kwambiri ndipo Eliya anali mdani wamkulu wa anthu amene ankatsutsa Mulungu. (1 Maf. 19:1, 2) N’kuthekanso kuti Eliya ankavutika maganizo chifukwa ankadziona kuti anali mneneri wa Yehova yekhayo amene anatsala. (1 Maf. 19:10) Mulungu anazindikira mwansanga mmene Eliya ankamvera. Choncho anatumiza mngelo kuti akamutsimikizire mneneri wakeyu kuti sanali yekha koma panali Aisiraeli enanso ambiri oopa Mulungu.​—1 Maf. 19:5, 18.

4. Kodi lemba la Maliko 10:29, 30, likusonyeza bwanji kuti Yehova amaganizira atumiki ake omwe sakuthandizidwanso ndi achibale kapena anzawo?

4 Yehova amadziwa kuti tikasankha kumutumikira, ambirife timafunika kusiya zinthu zina. Zimenezi zikuphatikizapo kusiya kuthandizidwa ndi achibale komanso anzathu omwe si a Mboni. Mwina podera nkhawa zimenezi, nthawi ina mtumwi Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani. Kodi tidzapeza chiyani?” (Mat. 19:27) Mokoma mtima Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti adzapeza abale ndi alongo ambiri omwe adzakhale ngati anthu a m’banja lawo. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Ndipo Yehova yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, akulonjeza kuti adzapitiriza kuthandiza aliyense amene wasankha kumutumikira. (Sal. 9:10) Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene mungachite kuti Yehova akuthandizeni kulimbana ndi maganizo odziona ngati muli nokha.

ZIMENE MUNGACHITE NGATI MUKUDZIONA KUTI MULI NOKHANOKHA

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene Yehova amatithandizira?

5 Muziganizira mmene Yehova akukuthandizirani. (Sal. 55:22) Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera. Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Carol, * yemwe anthu a m’banja lake si a Mboni, ananena kuti: “Ndikaganizira mmene Yehova wandithandizira pa mayesero osiyanasiyana ndimaona kuti sindili ndekha. Ndipo zimenezi zimanditsimikizira kuti Yehova adzapitiriza kundithandiza.”

6. Kodi lemba la 1 Petulo 5:9, 10 lingalimbikitse bwanji amene amadziona kuti ali okhaokha?

6 Muziganizira mmene Yehova akuthandizira Akhristu enanso omwe amadziona kuti ali okhaokha. (Werengani 1 Petulo 5:9, 10.) Hiroshi, yemwe kwa zaka zambiri wakhala ali wa Mboni yekhayo m’banja lakwawo anati: “Zimakhala zosavuta kuona kuti aliyense mumpingo akulimbana ndi mavuto enaake. Choncho kudziwa kuti aliyense akuyesetsa kuchita zomwe angathe potumikira Yehova kumalimbikitsa kwambiri ife amene kwathu tilipo tokha m’choonadi.”

7. Kodi inuyo pemphero limakuthandizani bwanji?

7 Nthawi zonse muzichita zinthu zokhudza kulambira. Zimenezi zikuphatikizapo kumuuza Yehova momasuka mmene mukumvera. (1 Pet. 5:7) Massiel anati: “Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri chimene chinandithandiza kuti ndithe kulimbana ndi maganizo odziona kuti ndili ndekhandekha, ndi kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Mlongo wachitsikanayu atasankha kuti ayambe kutumikira Yehova, ankadziona kuti ali yekhayekha chifukwa chakuti anthu a m’banja lake sankatumikira Yehova. Iye ananenanso kuti: “Ndinkaona kuti Yehova ndi Atate wanga ndipo ndinkapemphera kwa iye tsiku lililonse kambirimbiri, kumufotokozera mmene ndinkamvera.”

Kumvetsera Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo ojambulidwa kungathandize kwambiri anthu amene amadziona kuti ali okhaokha (Onani ndime 8) *

8. Kodi kuwerenga Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama kwakuthandizani bwanji?

8 Muziwerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndipo muziganizira mozama nkhani zimene zimasonyeza kuti Yehova amakukondani. Mlongo wina dzina lake Bianca, yemwe anthu a m’banja lake amalankhula zinthu zomufooketsa anafotokoza kuti: “Kuwerenga komanso kuganizira mozama nkhani za m’Baibulo ndiponso zofotokoza mbiri ya moyo wa atumiki a Yehova, amene anakumana ndi mavuto ngati anga kumandithandiza kwambiri.” Akhristu ena amawerenga Malemba otonthoza monga Salimo 27:10 komanso Yesaya 41:10. Enanso amaona kuti kumvetsera zinthu zojambulidwa kumawathandiza kuti asamadzione kuti ali okhaokha akamakonzekera misonkhano kapena akamawerenga Baibulo.

9. Kodi kupezeka pamisonkhano kumakuthandizani bwanji?

9 Muziyesetsa kuti muzisonkhana nthawi zonse. Mukamachita zimenezi muzilimbikitsidwa ndi mfundo zothandiza komanso mungadziwane ndi abale ndi alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Massiel yemwe tamutchula uja anati: “Ngakhale kuti ndinali wamanyazi, ndinkayesetsa kupezeka pamisonkhano yonse komanso ndinkapereka ndemanga. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti ndili pafupi ndi abale ndi alongo mumpingo.”

10. Kodi kugwirizana ndi Akhristu okhulupirika n’kofunika chifukwa chiyani?

10 Muzigwirizana ndi Akhristu okhulupirika. Muzipeza anzanu mumpingo omwe mungaphunzire zinthu kwa iwo ngakhale mutakhala kuti mukusiyana msinkhu komanso kochokera. Baibulo limatikumbutsa kuti okalamba “amakhala ndi nzeru.” (Yobu 12:12) Achikulire angaphunzirenso zambiri kuchokera kwa achinyamata okhulupirika. Davide anali wamng’ono poyerekezera ndi Yonatani koma zimenezi sizinachititse kuti asakhale mabwenzi. (1 Sam. 18:1) Iwo ankathandizana potumikira Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto aakulu. (1 Sam. 23:16-18) Mlongo wina dzina lake Irina, amene m’banja lawo alipo yekha wa Mboni ananena kuti: “Abale ndi alongo akhoza kukhala ngati makolo athu komanso achibale athu enieni. Yehova akhoza kuwagwiritsa ntchito kuti azitithandiza.”

11. Kodi mungatani kuti muzigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo?

11 Kupeza anzanu atsopano si kophweka makamaka mukakhala kuti ndinu amanyazi. Mlongo wina dzina lake Ratna, yemwe ndi wamanyazi ndipo anaphunzira choonadi ngakhale kuti ankatsutsidwa, anafotokoza kuti: “Ndinkayenera kuvomereza kuti ndinkafunika kuthandizidwa ndi abale ndi alongo mumpingo.” Zikhoza kukhala zovuta kuti mufotokozere munthu wina mmene mukumvera, koma mukamumasukira zingachititse kuti muyambe kugwirizana. Anzanu amafuna kukulimbikitsani komanso kukuthandizani, koma mumafunika kuti muwafotokozere kuti adziwe mmene angakuthandizireni.

12. Kodi kugwira nawo ntchito yolalikira kungakuthandizeni bwanji kupeza anzanu abwino?

12 Njira imodzi imene ingakuthandizeni ndi kulalikira ndi Akhristu ena. Carol yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndapeza anzanga ambiri abwino polalikira ndi alongo ena komanso pogwira nawo ntchito zina m’gulu la Mulungu. Pa zaka zonsezi Yehova wakhala akundithandiza pogwiritsa ntchito anzangawa.” Kugwirizana ndi Akhristu okhulupirika n’kothandiza kwambiri. Yehova amagwiritsa ntchito anzanu amenewa pokuthandizani kulimbana ndi maganizo ofooketsa, monga odziona kuti muli nokhanokha.​—Miy. 17:17.

MUZITHANDIZA ENA KUONA KUTI TILI NGATI ANTHU A M’BANJA LAWO

13. Kodi abale ndi alongo onse mumpingo ali ndi udindo wotani?

13 Abale ndi alongo onse ali ndi udindo woonetsetsa kuti mumpingo muli mtendere komanso kuti aliyense aziona kuti amakondedwa. (Yoh. 13:35) Zimene timachita komanso kulankhula zingalimbikitse kwambiri ena. Mlongo wina anati: “Nditaphunzira choonadi, anthu amumpingo anakhala ngati anthu a m’banja langa. Sindikanakhala wa Mboni za Yehova abale ndi alongo akanapanda kundithandiza.” Kodi mungathandize bwanji Akhristu amene achibale awo si a Mboni kuti aziona kuti abale ndi alongo mumpingo amawakonda?

14. Kodi tingatani kuti anthu atsopano mumpingo aziona kuti ndife anzawo apamtima?

14 Muziyamba ndinu kukhala anzawo. Tingayambe ndi kulandira ndi manja awiri atsopano omwe abwera mumpingo. (Aroma 15:7) Komabe timafunikanso kuchita zina osati kungowapatsa moni mwansangala. Timafuna kuti pakapita nthawi akhale anzathu apamtima. Choncho tizichita nawo zinthu mokoma mtima komanso kusonyeza kuti timawaganizira. Popanda kuwafunsa mafunso amene angawachititse manyazi, muziyesetsa kumvetsa mavuto amene akukumana nawo. Ena angamavutike kufotokoza mmene akumvera, choncho muzikhala osamala kuti musamawakakamize kulankhula. M’malomwake muziwafunsa mokoma mtima komanso mwanzeru ndipo muzimvetsera moleza mtima akamayankha. Mwachitsanzo, mukhoza kuwafunsa mmene anaphunzirira choonadi.

15. Kodi Akhristu olimba mwauzimu angathandize bwanji ena mumpingo?

15 Anthu onse mumpingo angakhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ngati Akhristu olimba mwauzimu makamaka akulu akuwasonyeza kuti amawaganizira. Melissa yemwe anaphunzitsidwa choonadi ndi mayi ake anati: “Pa zaka zonsezi, ndimayamikira kwambiri abale amene nthawi zonse ankachita nane chidwi n’kumandithandiza ngati kuti ndi a bambo anga. Ndikamafotokoza mmene ndikumvera iwo ankandimvetsera.” M’bale wina wachinyamata dzina lake Mauricio, yemwe ankadziona kuti ali yekhayekha chifukwa choti mphunzitsi wake anasiya choonadi, anafotokoza kuti: “Akulu ankasonyeza kuti amandiganizira ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri. Iwo ankalankhula nane pafupipafupi, kuyenda nane mu utumiki, kundifotokozera mfundo zothandiza zomwe apeza pophunzira Baibulo komanso ngakhale kuchita nane masewero osiyanasiyana.” Melissa komanso Mauricio akhala akutumikira Yehova mu utumiki wanthawi zonse.

Kodi pali munthu wina mumpingo mwanu yemwe angayamikire kwambiri mutamusonyeza kukoma mtima komanso kupeza nthawi yocheza naye? (Onani ndime 16-19) *

16-17. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene tingachite kuti tithandize ena?

16 Muziwathandiza. (Agal. 6:10) Leo, yemwe akutumikira kudziko lina lakutali ndi kwawo anati: “Nthawi zambiri timangofunika kuchita zinthu zina zing’onozing’ono zosonyeza chifundo. Ndikukumbukira kuti pa nthawi ina ndinachita ngozi ya galimoto. Pamene ndinkafika kunyumba n’kuti ndili ndi nkhawa kwambiri. Koma banja lina linandiitanira kunyumba kwawo kuti ndikadye nawo chakudya. Sindikukumbukira kuti tinadya chiyani koma chomwe ndikukumbukira n’chakuti ankandimvetsera mokoma mtima ndipo pamapeto pake ndinamva bwino kwambiri.”

17 Tonsefe timasangalala tikamachita zinthu zokhudza kulambira monga kuchita misonkhano yadera komanso yachigawo, chifukwa timapeza nthawi yocheza ndi ena komanso kukambirana zomwe taphunzira pamisonkhanoyo. Komabe, Carol yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndikakhala pamisonkhano yadera komanso yachigawo, ndimangodzimva kuti ndili ndekhandekha.” Chifukwa chiyani? Iye anati: “Ngakhale kuti ndimakhala ndili pakati pa abale ndi alongo ambiri, nthawi zambiri iwo amakhala ndi anthu a m’banja lawo. Pa nthawi imeneyi ndi pamene ndimavutika kwambiri ndi maganizo odziona kuti ndili ndekhandekha.” Enanso zimawavuta kuti apezeke pamsonkhano wachigawo kapena wadera kwa nthawi yoyamba kungochokera pamene mkazi kapena mwamuna wawo anamwalira. Kodi mukudziwa munthu wina amene akukumana ndi vuto limeneli? Mungachite bwino kumupempha kuti adzakhale ndi banja lanu pamsonkhano wotsatira.

18. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo a pa 2 Akorinto 6:11-13, tikamachita zinthu zosangalatsa?

18 Muzichita nawo limodzi zinthu zina. Mukamachita zinthu zosangalatsa, muzichitira limodzi ndi abale ndi alongo osiyanasiyana makamaka amene amadziona kuti ali okhaokha. Timafunika ‘kuwafutukulira mitima yathu.’ (Werengani 2 Akorinto 6:11-13.) Melissa, yemwe tamutchula kale uja anati: “Tinkasangalala kwambiri anzathu akatiitanira kunyumba kwawo kapena kutitenga pa maulendo osiyanasiyana.” Kodi pali munthu wina mumpingo wanu yemwe mungamachite naye zinthu zina limodzi?

19. Kodi ndi pa nthawi iti pamene kucheza ndi Akhristu anzathu kumakhala kothandiza kwambiri?

19 Nthawi zina Akhristu anzathu akhoza kuyamikira kwambiri ngati titachita nawo zinthu limodzi. Ena zingawavute kukhala ndi achibale awo omwe si a Mboni pa nthawi ya zikondwerero zina. Enanso angamamve chisoni kwambiri pa masiku ena monga tsiku limene munthu amene ankamukonda anamwalira. Tikamapeza nthawi yocheza ndi abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto ngati amenewa, timawasonyeza kuti timawaganizira kapena kuti ‘timasamaladi za iwo.’​—Afil. 2:20.

20. Kodi mawu a Yesu a pa Mateyu 12:48-50, angatithandize bwanji tikamadziona kuti tili tokhatokha?

20 Pali zifukwa zambiri zimene zingachititse Mkhristu kuti nthawi zina azidziona ngati ali yekhayekha. Komabe tisamaiwale kuti Yehova amadziwa bwino mmene timamvera. Iye nthawi zambiri amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu potithandiza. (Werengani Mateyu 12:48-50.) Ifenso timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova watichitira tikamayesetsa kuthandiza abale ndi alongo athu. Ngakhale kuti nthawi zina tingamadzione kuti tili tokhatokha, nthawi zonse Yehova amakhala nafe.

NYIMBO NA. 46 Timakuyamikirani Yehova

^ ndime 5 Kodi nthawi zina mumalimbana ndi maganizo odziona ngati muli nokhanokha? Ngati ndi choncho, dziwani kuti Yehova amadziwa bwino mmene mumamvera ndipo amafunitsitsa kuti akuthandizeni. Munkhaniyi tikambirana zimene mungachite ngati mwayamba kukhala ndi maganizo odziona ngati muli nokhanokha. Tikambirananso mmene tingalimbikitsire Akhristu anzathu amene amadziona kuti ali okhaokha.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale amene mkazi wake anamwalira akulimbikitsidwa pamene akumvetsera Baibulo komanso zinthu zina zojambulidwa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wina ndi mwana wake asonyeza kukoma mtima popita kukaona m’bale wina wachikulire wa mumpingo mwawo