Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 23

NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Yehova Akutiitana Kuti Tikhale Alendo Ake

Yehova Akutiitana Kuti Tikhale Alendo Ake

“Tenti yanga idzakhala pakati pawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo.”​—EZEK. 37:27.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kuti tiziyamikira Yehova chifukwa chotiitana kuti tikhale alendo mutenti yake yophiphiritsira komanso chifukwa cha mmene amatisamalirira.

1-2. Kodi Yehova amawaona bwanji atumiki ake okhulupirika?

 KODI Yehova ali ngati ndani kwa inuyo? Mwina mungayankhe kuti, ‘Yehova ndi Atate wanga, Mulungu wanga komanso mnzanga.’ Palinso mayina ena audindo omwe mungagwiritse ntchito ponena za Yehova. Komabe, kodi munayamba mwaganizirapo kuti mungakhalenso mlendo wake?

2 Mfumu Davide anayerekezera ubwenzi womwe umakhalapo pakati pa Yehova ndi atumiki ake okhulupirika ndi ubwenzi umene umakhalapo pakati pa munthu ndi alendo amene wawaitana. Iye anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale m’phiri lanu lopatulika?” (Sal. 15:1) Mawu ouziridwa amenewa akusonyeza kuti tikhoza kukhala alendo a Yehova kapena kuti anzake. Ndi mwayitu wamtengo wapatali kukhala alendo a Yehova.

YEHOVA AMAFUNA KUTI TIKHALE ALENDO AKE

3. Kodi mlendo woyamba wa Yehova anali ndani, nanga Yehova ndi mlendo wakeyo ankamva bwanji?

3 Yehova asanayambe kulenga zinthu zonse anali yekha. Koma kenako pa nthawi ina, iye analandira Mwana wake woyamba kubadwa mutenti yake yophiphiritsa. Yehova anasangalala kwambiri kulandira mlendo wakeyu. Baibulo limanena kuti Yehova “ankasangalala kwambiri” ndi Mwana wake. Nayenso mlendo wake woyambayu, ‘ankakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.’​—Miy. 8:30.

4. Kodi ndi ndaninso amene anadzakhala alendo mutenti ya Yehova?

4 Kenako Yehova analenga angelo omwe anakhalanso alendo ake. Iwo amatchedwa ‘ana a Mulungu’ ndipo Baibulo limafotokoza kuti amasangalala kukhala ndi Yehova. (Yobu 38:7; Dan. 7:10) Kwa zaka zambiri, anzake a Yehova anali kumwamba kokha komwe iye amakhala. Pambuyo pake analenga anthu padzikoli omwe anakhalanso alendo mutenti yake. Ena mwa alendo akewa anali Inoki, Nowa, Abulahamu komanso Yobu. Atumiki okhulupirikawa amafotokozedwa kuti anali anzake a Mulungu kapena kuti anthu omwe anayenda “ndi Mulungu woona.”​—Gen. 5:24; 6:9; Yobu 29:4; Yes. 41:8.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa ulosi wa pa Ezekieli 37:26, 27?

5 Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akuitana anzake kuti akhale alendo ake. (Werengani Ezekieli 37:26, 27.) Ulosi wa Ezekieli umasonyeza kuti Mulungu amafunitsitsa kuti atumiki ake okhulupirika akhale naye pa ubwenzi wabwino. Iye amalonjeza kuti adzachita nawo “pangano lamtendere.” Ulosiwu umanena za nthawi imene anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba ndi omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli, adzagwirizane n’kukhala “gulu limodzi” la nkhosa mutenti yake yophiphiritsa. (Yoh. 10:16) Nthawi imeneyo ndi inoyi.

MULUNGU AMATISAMALIRA KULIKONSE KOMWE TINGAKHALE

6. Kodi munthu angatani kuti akhale mlendo mutenti ya Yehova, nanga kodi tentiyi imapezeka kuti?

6 Kale, tenti inkakhala malo omwe munthu ankakhalamo kuti apume komanso atetezeke ku zinthu ngati mphepo, dzuwa komanso mvula. Tikadzipereka n’kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, timakhala alendo mutenti yake yophiphiritsa, timapeza chakudya chauzimu chokwanira komanso timakhala pa ubwenzi wabwino ndi ena omwe amakhalanso alendo a Yehova. (Sal. 61:4) Tenti ya Yehova sili kudera limodzi lokha. Mungathe kupita dziko lililonse mwinanso kumisonkhano ikuluikulu ndipo mukapeza anthu omwe akusangalala kukhala mutenti ya Mulungu. Tenti ya Yehova imapezeka kulikonse komwe kuli atumiki ake okhulupirika.​—Chiv. 21:3.

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu okhulupirika omwe anamwalira amakhalabe alendo mutenti ya Yehova? (Onaninso chithunzi.)

7 Nanga bwanji za anthu okhulupirika omwe anamwalira? Kodi n’zomveka kunena kuti iwo adakali alendo mutenti ya Yehova? Inde. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova amawakumbukirabe ndipo kwa iyeyo ndi amoyo. Yesu anafotokoza kuti: “Zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.”​—Luka 20:37, 38.

Ngakhale anthu okhulupirika omwe anamwalira angakhalebe alendo mutenti ya Mulungu (Onani ndime 7)


UBWINO WOKHALA ALENDO A YEHOVA KOMANSO ZIMENE TIYENERA KUCHITA

8. Kodi alendo a Yehova amapindula bwanji chifukwa chokhala mutenti yake?

8 Mofanana ndi tenti yomwe munthu amatha kukhalamo kuti apume komanso kubisalamo, tikalowa mutenti ya Yehova timatetezeka ku zinthu zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi iye komanso timakhala ndi chiyembekezo. Tikapitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, Satana sangachite chilichonse chomwe chingativulaze mpaka kalekale. (Sal. 31:23; 1 Yoh. 3:8) Yehova adzapitiriza kuteteza anzake okhulupirika ku zinthu zomwe zingawavulaze mwauzimu ngakhalenso imfa.​—Chiv. 21:4.

9. Kodi Yehova amafuna kuti alendo ake azichita chiyani?

9 Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kukhala mlendo mutenti ya Yehova ndipo timasangalala kukhala naye pa ubwenzi mpaka kalekale. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kukhala alendo ake? Ngati mutaitanidwa kunyumba kwa mnzanu, mungafune kudziwa zimene iye angakonde kuti muchite. Mwachitsanzo, mwina angafune kuti muvule nsapato musanalowe m’nyumba ndipo simungakane. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingafune kudziwa zimene Yehova angakonde kuti anthu omwe akufuna kupitiriza kukhala alendo mutenti yake azichita. Kukonda Yehova kumatilimbikitsa kuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti ‘tizimusangalatsa pa chilichonse.’ (Akol. 1:10) Komanso ngakhale kuti Yehova ndi mnzathu, timazindikira kuti iye ndi Mulungu ndiponso Atate wathu ndipo ndi woyenera kuti tizimulemekeza. (Sal. 25:14) Tisamaiwale zimenezi ndipo nthawi zonse tizimupatsa ulemu waukulu. Zimenezi zingatithandize kuti tizipewa kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse. Choncho timafunitsitsa kuti ‘tiziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’​—Mika 6:8.

YEHOVA ANKACHITA ZINTHU MOPANDA TSANKHO M’CHIPULULU

10-11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti alibe tsankho pochita zinthu ndi Aisiraeli m’chipululu cha Sinai?

10 Yehova sachita zinthu mwatsankho ndi alendo ake. (Aroma 2:11) Timaona umboni wa zimenezi tikaganizira mmene ankachitira zinthu ndi Aisiraeli m’chipululu cha Sinai.

11 Atapulumutsa anthu ake ku ukapolo ku Iguputo, Yehova anasankha ansembe kuti azitumikira pachihema. Alevi ankapatsidwa ntchito zosiyanasiyana pachihema chopatulikacho. Kodi amene ankatumikira pachihema komanso anthu omwe ankakhala pafupi ndi chihemacho ankasamalidwa bwino ndi Yehova kuposa anthu ena? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova alibe tsankho.

12. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti alibe tsankho pochita zinthu ndi Aisiraeli omwe anali alendo ake? (Ekisodo 40:38) (Onaninso chithunzi.)

12 Mwisiraeli aliyense anali ndi mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova posatengera kuti ankachita utumiki winawake wapadera kapenanso ankakhala pafupi ndi chihema. Mwachitsanzo, Yehova anaonetsetsa kuti Aisiraeli onse azitha kuona zinthu zodabwitsa monga chipilala cha mtambo komanso chipilala cha moto zomwe zinkakhala pamwamba pa chihema. (Werengani Ekisodo 40:38.) Mtambo ukayamba kuyenda, ngakhale amene anali kutali kwambiri ndi chihema ankatha kuuona, kulongedza katundu komanso kuphwasula matenti n’kunyamukira limodzi ndi anzawo. (Num. 9:15-23) Onse ankatha kumva kulira kwa malipenga awiri asiliva osonyeza kuti aliyense anyamuke. (Num. 10:2) Apa n’zoonekeratu kuti kukhala pafupi ndi chihema sunali umboni wosonyeza kuti munthu ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. M’malomwake, Mwisiraeli aliyense akanatha kukhala mlendo mutenti ya Yehova ndipo iye akanamamutsogolera ndiponso kumuteteza. Masiku anonso, kaya timakhala kuti, Yehova amatikonda, kutisamalira komanso kutiteteza.

Zimene zinkachitika pachihema zimasonyeza kuti Mulungu alibe tsankho (Onani ndime 12)


MMENE YEHOVA AMASONYEZERA KUTI ALIBE TSANKHO MASIKU ANO

13. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti alibe tsankho masiku ano?

13 Ena mwa anthu a Mulungu masiku ano amakhala kufupi ndi likulu lathu kapena ofesi ya nthambi. Ndipo ena amatumikira kumeneko. Choncho iwo amachita nawo zambiri zomwe zikuchitika m’malo amenewa komanso amakumana ndi abale amene akutsogolera. Ena amatumikira ngati oyang’anira madera kapena akuchita utumiki winawake wapadera wa nthawi zonse. Koma ngati muli m’gulu la anthu ambiri omwe alibe mwayi umenewu, dziwani kuti Yehova amakuonanibe kuti ndinu mlendo wake ndipo amakonda alendo ake onse. Iye amasamalira mtumiki wake aliyense. (1 Pet. 5:7) Anthu onse a Mulungu amalandira chakudya chauzimu, malangizo komanso chitetezo chimene amafunikira.

14. Kodi ndi chitsanzo china chiti chosonyeza kuti Yehova alibe tsankho masiku ano?

14 Chitsanzo china chosonyeza kuti Yehova alibe tsankho masiku ano ndi chakuti amathandiza anthu padziko lonse kuti apeze Baibulo. Malemba Opatulika analembedwa m’zilankhulo zitatu: Chiheberi, Chiaramu ndi Chigiriki. Kodi anthu amene amalankhula bwino zilankhulo zoyambirirazi ndi amene amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kuposa ena? Ayi si choncho.​—Mat. 11:25.

15. Kodi ndi umboni winanso uti wosonyeza kuti Yehova alibe tsankho? (Onaninso chithunzi.)

15 Yehova satiitana kuti tikhale alendo ake chifukwa choti tinaphunzira kwambiri kapena timadziwa zilankhulo zoyambirira za Baibulo. Choncho iye amalola kuti anthu padziko lonse adziwe nzeru zake, kaya ndi ophunzira kapena ayi. Baibulo lomwe ndi Mawu ake lamasuliridwa m’zilankhulo zambiri ndipo anthu padziko lonse angathe kupindula ndi zimene limaphunzitsa komanso angadziwe zimene angachite kuti akhale anzake.​—2 Tim. 3:16, 17.

Kodi kupezeka kwa Baibulo m’zilankhulo zambiri kumasonyeza bwanji kuti Mulungu alibe tsankho? (Onani ndime 15)


PITIRIZANI KUKHALA ALENDO A YEHOVA

16. Mogwirizana ndi Machitidwe 10:34, 35, kodi tingatani kuti tipitirize kukhala alendo a Yehova?

16 Ndi mwayi waukulu kukhala alendo a Yehova mutenti yake yophiphiritsa. Iye amalandira alendo ake mokoma mtima, mwachikondi komanso amawasamalira bwino kwambiri. Kuwonjezera pamenepo iye ndi wopanda tsankho ndipo amalandira aliyense posatengera kumene amakhala, chikhalidwe, maphunziro ake, mtundu, msinkhu kayanso kuti ndi mwamuna kapena mkazi. Komabe ndi anthu okhawo amene amatsatira mfundo zake omwe amawalandira monga alendo ake.​—Werengani Machitidwe 10:34, 35.

17. Kodi tipeza kuti mfundo zowonjezereka zomwe zingatithandize kukhalabe alendo mutenti ya Yehova?

17 Pa Salimo 15:1, Davide anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu? Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?” Wolemba masalimoyu anauziridwanso kulemba mayankho a mafunso amenewa. Nkhani yotsatira ifotokoza zina zimene tiyenera kuchita kuti tipitirize kusangalatsa Yehova komanso kukhala anzake.

NYIMBO NA. 32 Khalani Okhulupirika kwa Yehova