Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 11

Pitirizani Kuvala “Umunthu Watsopano” Pambuyo Pobatizidwa

Pitirizani Kuvala “Umunthu Watsopano” Pambuyo Pobatizidwa

“Muvale umunthu watsopano.”​—AKOL. 3:10.

NYIMBO NA. 49 Tizikondweretsa Mtima wa Yehova

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi n’chiyani chimene nthawi zambiri chimachititsa kuti tikhale ndi makhalidwe ena ake?

 KAYA tangobatizidwa kumene kapena tinabatizidwa zaka zambiri m’mbuyomu, tonsefe timafuna kukhala ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kulamulira maganizo athu chifukwa nthawi zambiri, zimene timaganiza ndi zomwe zimachititsa kuti tikhale ndi makhalidwe amene tili nawo. Ngati nthawi zambiri timaganizira zimene thupi lathu limalakalaka, tikhoza kulankhula kapena kuchita zoipa. (Aef. 4:17-19) Koma ngati nthawi zambiri timaganizira zinthu zabwino, tikhoza kumalankhula kapena kuchita zinthu zimene zingasangalatse Atate wathu Yehova.​—Agal. 5:16.

2. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

2 Monga mmene tinaonera munkhani yapita ija, sitingapeweretu maganizo onse oipa. Koma tikhoza kusankha kuti tisamachite zimene timaganizazo. Tisanabatizidwe tiyenera kusiya kulankhula kapena kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo. Chimenechi ndi chinthu choyamba komanso chofunika kwambiri kuchita kuti tivule umunthu wakale. Komanso kuti tizisangalatsa kwambiri Yehova tiyeneranso kumvera lamulo lakuti: “Muvale umunthu watsopano.” (Akol. 3:10) Munkhaniyi tipeza mayankho amafunso awa: Kodi “umunthu watsopano” n’chiyani? Kodi tingatani kuti tivale umunthu watsopano ndipo tisauvule?

KODI “UMUNTHU WATSOPANO” N’CHIYANI?

3. Mogwirizana ndi Agalatiya 5:22, 23, kodi “umunthu watsopano” n’chiyani, nanga munthu angauvale bwanji?

3 “Umunthu watsopano” umatanthauza kuganiza komanso kuchita zinthu motsanzira Yehova. Munthu amavala umunthu watsopano akamasonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndipo amalola kuti mzimuwo uzimutsogolera pa mmene amaganizira, mmene amamvera komanso zochita zake. (Werengani Agalatiya 5:22, 23.) Mwachitsanzo, iye amakonda Yehova komanso anthu ake. (Mat. 22:36-39) Amapitirizabe kukhala wosangalala ngakhale pamene akukumana ndi mayesero. (Yak. 1:2-4) Amakhala mwamtendere ndi ena. (Mat. 5:9) Amakhala woleza mtima komanso wokoma mtima akamachita zinthu ndi ena. (Akol. 3:13) Iye amakonda komanso kuchita zabwino. (Luka 6:35) Zochita zake zimasonyeza kuti amakhulupirira kwambiri Atate wake wakumwamba. (Yak. 2:18) Amakhalabe wofatsa anthu ena akamuputa komanso amakhala wodziletsa akakumana ndi mayesero.​—1 Akor. 9:25, 27; Tito 3:2.

4. Kuti tivale umunthu watsopano n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza makhalidwe onse otchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23? Fotokozani.

4 Kuti tivale umunthu watsopano, tiyenera kukhala ndi makhalidwe otchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23 komanso m’mavesi ena a m’Baibulo. * Sikuti makhalidwewa ali ngati zovala zosiyanasiyana zomwe timavala chilichonse pa nthawi yake. Ndipotu ambiri a makhalidwewa amayendera limodzi. Mwachitsanzo, ngati timakondadi anzathu tingachite nawo zinthu moleza mtima komanso mokoma mtima. Ndipo ngati tikufunadi kukhala munthu wabwino, timafunika kukhala ofatsa komanso odziletsa.

KODI TINGAVALE BWANJI UMUNTHU WATSOPANO?

Tikamayesetsa kukhala ndi maganizo ngati Yesu, m’pamenenso zimakhala zosavuta kusonyeza makhalidwe amene ali nawo (Onani ndime 5, 8, 10, 12, 14)

5. Kodi kukhala ndi “maganizo a Khristu” kumatanthauza chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira mmene Yesu ankachitira zinthu? (1 Akorinto 2:16)

5 Werengani 1 Akorinto 2:16. Kuti tivale umunthu watsopano, tiyenera kukhala ndi “maganizo a Khristu.” M’mawu ena, tiyenera kuphunzira mmene Yesu amaganizira n’kumamutsanzira. Yesu amasonyeza bwino kwambiri makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Mofanana ndi galasi loyang’anira labwino, iye amasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Yehova. (Aheb. 1:3) Tikamayesetsa kukhala ndi maganizo ngati a Yesu, m’pamenenso tingathe kuchita zinthu ngati iyeyo komanso kusonyeza makhalidwe ake.​—Afil. 2:5.

6. Kodi ndi mfundo ziti zimene tiyenera kukumbukira tikamayesetsa kuti tivale umunthu watsopano?

6 Kodi tingathedi kutsanzira Yesu? Mwina tingamaganize kuti: ‘Yesu ndi wangwiro. Sindingathe kuchita zinthu ndendende ngati iyeyo.’ Ngati mumaona choncho muzikumbukira mfundo izi. Choyamba, munalengedwa kuti mukhale wofanana ndi Yehova komanso Yesu. Choncho mungathe kusankha kuti muziwatsanzira ndipo mungakwanitse pamlingo winawake. (Gen. 1:26) Chachiwiri, mzimu woyera wa Mulungu ndi wamphamvu m’chilengedwe chonse. Mothandizidwa ndi mzimuwu mungathe kuchita zinthu zimene panokha simukanakwanitsa. Chachitatu, Yehova sayembekezera kuti muzisonyeza mosalakwitsa kalikonse makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Ndipotu Atate wathu wachikondi wapereka zaka 1,000 kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli kuti adzafike pokhala angwiro. (Chiv. 20:1-3) Panopa Yehova amatiyembekezera kuti tizichita zonse zomwe tingathe komanso kumudalira kuti azitithandiza.

7. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

7 Kodi tingatsanzire Yesu pa zinthu ziti? Tikambirana mwachidule makhalidwe 4 amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Tikamakambirana khalidwe lililonse, tiona zimene tingaphunzirepo pa mmene Yesu anasonyezera makhalidwewo. Ndipo tizikambirana mafunso otithandiza kuona zimene tikuchita pa nkhani yovala umunthu watsopano.

8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chikondi?

8 Popeza amakonda kwambiri Yehova, Yesu anachita zinthu modzimana chifukwa cha Atate wakewo komanso ifeyo. (Yoh. 14:31; 15:13) Ndipotu zimene Yesu anachita ali padzikoli zinasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu. Tsiku lililonse iye ankasonyeza chikondi komanso chifundo, ngakhale pamene anthu ena ankamutsutsa. Njira yaikulu imene anasonyezera kuti amakonda anthu, ndi kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43, 44) Yesu anasonyezanso Mulungu ndi anthu chikondi chovutikira ena pololera kuti azunzidwe komanso kuphedwa ndi anthu ochimwa. Zimene anachitazi zinatipatsa mwayi woti tidzapeze moyo wosatha.

9. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yosonyeza chikondi?

9 Tinadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa chifukwa chakuti timakonda Atate wathu wakumwamba. Choncho mofanana ndi Yesu, mmene timachitira zinthu ndi anthu ziyenera kusonyeza kuti timakonda Yehova. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda kwambiri anthu? Kodi ndimachitira chifundo anthu ena, ngakhale pamene sakundilemekeza? Kodi chikondi chimandichititsa kugwiritsa ntchito nthawi ndi zinthu zanga pothandiza ena kuphunzira za Yehova? Kodi ndimafunitsitsa kuchita zimenezi ngakhale pamene anthu ambiri sakuyamikira zimene ndikuchita kapenanso akunditsutsa? Kodi pali zimene ndingachite kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yothandiza anthu kukhala ophunzira a Yesu?’​—Aef. 5:15, 16.

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda mtendere?

10 Yesu anali munthu wokonda mtendere. Anthu akamuchitira zoipa iye sankabwezera. Koma ankachitanso zoposa pamenepa. Ankayamba ndi iyeyo kuchita zinthu mwamtendere ndipo ankalimbikitsa ena kuti azithetsa kusamvana pakati pawo. Mwachitsanzo, iye anaphunzitsa kuti munthu ayenera kukhazikitsa mtendere ndi m’bale wake kuti Mulungu azivomereza kulambira kwake. (Mat. 5:9, 23, 24) Ndipo mobwerezabwereza anathandiza atumwi ake kuti asamakangane pa nkhani yakuti wamkulu ndani pakati pawo.​—Luka 9:46-48; 22:24-27.

11. Kodi tingatani kuti tikhale anthu okonda mtendere?

11 Kuti tizikhala mwamtendere ndi ena, tiyenera kuchita zambiri osati kungopewa kuyambitsa mikangano. Tiyenera kuyesetsa kuti tizikhala mwamtendere ndi ena komanso kulimbikitsa abale ndi alongo kuti azithetsa kusamvana pakati pawo. (Afil. 4:2, 3; Yak. 3:17, 18) Tingadzifunse mafunso otsatirawa: ‘Kodi ndingalolere kudzimana zinthu zina kuti ndikhale pamtendere ndi ena? M’bale kapena mlongo akandikhumudwitsa, kodi ndimasunga chakukhosi? Kodi ndimadikira kuti ayambe ndi munthu winayo kukhazikitsa mtendere kapena ndimayamba ndi ineyo kuchitapo kanthu ngakhale zikuoneka kuti winayo ndi amene walakwitsa? Ngati n’koyenera, kodi ndimalimbikitsa anthu amene asemphana maganizo kuti akhalenso pamtendere?’

12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kukoma mtima?

12 Yesu anali wokoma mtima. (Mat. 11:28-30) Iye anasonyeza khalidweli pokhala wodekha komanso wololera ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri. Mwachitsanzo, mayi wa ku Foinike atamupempha kuti amuchiritsire mwana wake, poyamba iye anakana, koma mayiyo atasonyeza chikhulupiriro chachikulu, mokoma mtima anamuchiritsira mwana wakeyo. (Mat. 15:22-28) Ngakhale kuti anali wokoma mtima Yesu sankalekerera zinthu. Nthawi zina Yesu ankasonyeza kukoma mtima popereka malangizo amphamvu kwa anthu amene ankawakonda. Mwachitsanzo, pamene Petulo ankayesa kumuletsa kuti asachite chifuniro cha Yehova, Yesu anamudzudzula pamaso pa ophunzira ena. (Maliko 8:32, 33) Iye anachita zimenezi osati pofuna kumuchititsa manyazi, koma pofuna kumuphunzitsa komanso kuchenjeza ophunzira enawo kuti asakhale odzikuza. N’zosakayikitsa kuti Petulo anachita manyazi komabe malangizowo anamuthandiza.

13. Kodi tingatani kuti tizisonyeza ena kukoma mtima?

13 Kuti tisonyeze ena kukoma mtima, nthawi zina timafunika kuwapatsa malangizo mosapita mbali. Tikamachita zimenezi, tizitsanzira Yesu popereka malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu ndipo tizikhala odekha. Tisamakayikire kuti iwo akufuna kuchita zoyenera ndipo popeza amakonda Yehova komanso amatikonda, adzatsatira malangizo achikondi amene tawapatsa. Tingadzifunse mafunso awa: ‘Kodi ndimalimba mtima n’kulankhulapo ndikaona munthu amene ndimamukonda akuchita zinthu zolakwika? Ndikafunika kupereka malangizo kodi ndimalankhula mokoma mtima kapena mwaukali? Kodi cholinga changa popereka malangizo chimakhala chani? Kodi ndimapereka malangizo chifukwa chakuti munthu wandikhumudwitsa kapena chifukwa chomufunira zabwino?’

14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji ubwino?

14 Sikuti Yesu amangodziwa zimene zili zabwino koma amachitanso zabwinozo. Yesu amakonda Atate wake choncho nthawi zonse amachita zabwino ali ndi zolinga zoyenera. Munthu wabwino nthawi zonse amafunafuna njira zothandizira anthu ena, komanso kuwachitira zabwino. Kudziwa zoyenera kuchita sikokwanira koma tiyeneranso kuzichita tili ndi zolinga zabwino. Wina angafunse kuti: ‘Kodi n’zotheka kuchita zinthu zoyenera uli ndi zolinga zolakwika?’ Inde n’zotheka. Mwachitsanzo Yesu ananena za anthu ena omwe ankathandiza osauka, n’kumafunitsitsa kuti anthu ena adziwe za mphatso zimene apereka. Ngakhale kuti anthuwa ankachita ntchito zabwino, Yehova sankasangalala nazo.​—Mat. 6:1-4.

15. Kodi tingatani kuti tizisonyeza kuti ndifedi munthu wabwino?

15 Tingasonyeze kuti ndifedi munthu wabwino ngati timachita zoyenera tili ndi zolinga zabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Kuwonjezera pakudziwa zoyenera kuchita, kodi ndimayesetsanso kuti ndizizichita? Kodi cholinga changa pochita zabwino chimakhala chiyani?’

KODI TINGATANI KUTI TIPITIRIZEBE KUTETEZA UMUNTHU WATHU WATSOPANO?

16. Kodi tsiku lililonse tiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

16 Tisamaganize kuti kuvala umunthu watsopano kumatha tikangobatizidwa. Timafunika kupitiriza kuteteza chovala chatsopano chokongolachi. Njira ina imene tingachitire zimenezi, ndi kuyesetsa kuti tsiku lililonse tizisonyeza makhalidwe amene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa. Tikutero chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amachita zinthu ndipo mzimu wake ndi mphamvu yogwira ntchito. (Gen. 1:2) Choncho khalidwe lililonse limene mzimu woyera umatulutsa lizitichititsa kuchitapo kathu. Mwachitsanzo, Yakobo analemba kuti: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yak. 2:26) N’chimodzimodzinso ndi makhalidwe ena amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Nthawi iliyonse imene tasonyeza makhalidwewa, timasonyeza kuti mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito mwa ife.

17. Kodi tizitani ngati talephera kusonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa?

17 Ngakhale Akhristu omwe anabatizidwa zaka zambiri m’mbuyomo, nthawi zina amalephera kusonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Chofunika kwambiri ndi kupitirizabe kuyesetsa kuti tizisonyeza makhalidwewa. Taganizirani chitsanzo ichi. Ngati chovala chimene mumachikonda chitang’ambika, kodi mumangofulumira kuchitaya? Ayi. Nthawi zambiri mumasoka pamene pang’ambikapo ngati n’zotheka. Ndipo pambuyo pake mumayesetsa kuchita zinthu mosamala. Mofanana ndi zimenezi, ngati mwalephera kusonyeza kukoma mtima, kuleza mtima kapena chikondi kwa munthu wina wake, musamataye mtima. Kupepesa mochokera pansi pamtima kungakuthandizeni kuti muyambirenso kugwirizana naye. Mukatero muziyesetsa kuti mudzachite bwino pa nkhaniyo m’tsogolo.

18. Kodi mungakhale otsimikiza za chiyani?

18 Timayamikira kwambiri chitsanzo chimene Yesu anatipatsa. Tikamatsanzira kwambiri mmene Yesu amagazinira komanso mmene amaonera zinthu, m’pamene zimakhala zosavuta kuti tizichita zinthu ngati iyeyo. Ndipo tikamayesetsa kuchita zinthu ngati iyeyo, m’pamene timachita bwino kwambiri pa nkhani yovala umunthu watsopano. Munkhaniyi tangokambirana makhalidwe 4 amene mzimu woyera umatulutsa. Bwanji osapeza nthawi yophunzira makhalidwe ena amene mzimu woyera umatulutsa komanso kuganizira mmene mukuchitira powasonyeza? Mungapeze nkhani zofotokoza makhalidwewa M’buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Pitani pa mutu wakuti “Moyo Wachikhristu” kenako “Makhalidwe Amene Mzimu Woyera Umatulutsa.” Mungakhale otsimikiza kuti mukamachita khama, Yehova adzakuthandizani kuti muvale umunthu watsopano ndiponso kuti musauvule.

NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala

^ ndime 5 Kaya moyo wathu unali wotani m’mbuyomu, tikhoza kuvala “umunthu watsopano.” Kuti tikwanitse kuchita zimenezi tiyenera kupitiriza kusintha mmene timaganizira n’kumayesetsa kutsanzira Yesu. Nkhaniyi ifotokoza zitsanzo za mmene Yesu amaganizira komanso kuchitira zinthu. Ifotokozanso zimene tingachite kuti tipitirize kumutsanzira pambuyo poti tabatizidwa.

^ ndime 4 Lemba la Agalatiya 5:22, 23, silitchula makhalidwe onse abwino amene mzimu wa Mulungu ungatithandize kukhala nawo. Kuti mumve zambiri onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June, 2020.